Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 23

Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova

Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”​—MAT. 22:37.

NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Fotokozani mmene mfundo za m’Baibulo zingakhalire zofunika kwambiri zinthu zikasintha pa moyo wathu.

 PATSIKU la ukwati wawo, mkwati yemwe amakhala akuoneka bwino ndi mkwatibwi wake wokongola, amamvetsera mwatcheru nkhani ya ukwati ikamakambidwa. Sikakhala koyamba kumva mfundo zomwe zikufotokozedwazo. Koma kungoyambira tsiku limenelo kupita m’tsogolo, mfundo zimenezo zimakhala zofunika kwambiri kwa iwo. Chifukwa chiyani? Chifukwa akayamba kuzigwiritsa ntchito monga anthu amene ali pabanja.

2 N’chimodzimodzinso makolo a Chikhristu akakhala ndi mwana. N’kutheka kuti kwa zaka zambiri, iwo amakhala akumvetsera nkhani zokhala ndi malangizo okhudza kulera ana. Koma tsopano panthawiyi amafunikira kwambiri malangizo amenewa. Amakhala kuti ali ndi mwana wawowawo woti amulere. Umenewutu ndi udindo waukulu. Kunena zoona, kusintha kwa zinthu pa moyo wathu kungachititse kuti tisinthe mmene timaonera mfundo za m’Baibulo zodziwika bwino. Chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene atumiki a Yehova amawerengera komanso kuganizira mozama Malemba “masiku onse” a moyo wawo, monga mmene mafumu a Isiraeli anauzidwira.​—Deut. 17:19.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Makolo, muli ndi mwayi waukulu womwe Mkhristu angakhale nawo wophunzitsa ana anu zokhudza Yehova. Koma pali zambiri zimene muyenera kuchita kuposa pa kungowathandiza kudziwa zokhudza Mulungu wathu. Mumafunika kuwathandiza kuti azimukonda kwambiri. Ndiye kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azikonda Yehova? Munkhaniyi tikambirana mfundo 4 za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni. (2 Tim. 3:16) Tionanso mmene makolo ena a Chikhristu apindulira chifukwa chogwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo.

MFUNDO 4 ZOMWE ZINGATHANDIZE MAKOLO

Kodi zimene mumachita pofunafuna malangizo a Yehova komanso kukhala chitsanzo chabwino zingathandize bwanji ana anu? (Onani ndime 4, 8)

4. Kodi ndi mfundo imodzi iti yomwe ingathandize makolo kuti aziphunzitsa ana awo kukonda kwambiri Yehova? (Yakobo 1:5)

4 Mfundo 1: Muzifufuza malangizo a Yehova. Muzipempha Yehova kuti akupatseni nzeru zomwe mukufunikira kuti muthandize ana anu kuyamba kumukonda. (Werengani Yakobo 1:5.) Iye ndi amene angakupatseni malangizo abwino kwambiri. Tikutero pazifukwa zingapo. Taganizirani zifukwa ziwiri izi. Choyamba, Yehova ndi amene wakhala kholo kwa nthawi yaitali. (Sal. 36:9) Ndipo chachiwiri, nthawi zonse malangizo anzeru omwe amapereka amakhala othandiza.​—Yes. 48:17.

5. (a) Kodi gulu la Yehova limapereka zinthu ziti pofuna kuthandiza makolo? (b) Kodi mwaphunzira zotani muvidiyo yosonyeza mmene M’bale ndi Mlongo Amorim analerera ana awo?

5 Pogwiritsa ntchito Mawu ake komanso gulu lake, Yehova amapereka chakudya chauzimu chochuluka chomwe chingakuthandizeni kuphunzitsa ana anu kuti azimukonda. (Mat. 24:45) Mwachitsanzo, mungathe kupeza malangizo ambiri othandiza munkhani zakuti “Malangizo Othandiza Mabanja,” zomwe zinkapezeka m’magazini a Galamukani! kwa zaka zingapo ndipo pano zikupezeka pawebusaiti yathu. Komanso, mavidiyo ambiri opezeka pa jw.org amakhala ndi mbali yocheza ndi ena komanso zitsanzo zomwe zingathandize makolo kugwiritsa ntchito malangizo a Yehova akamalera ana awo. *​—Miy. 2:4-6.

6. Kodi bambo wina amaona bwanji malangizo amene iye ndi mkazi wake amalandira kuchokera ku gulu la Yehova?

6 Makolo ambiri amayamikira mmene Yehova wakhala akuwathandizira pogwiritsa ntchito gulu lake. Bambo wina dzina lake Joe anavomereza kuti: “Sizophweka kuthandiza ana atatu kuti azikonda choonadi. Nthawi zonse ine ndi mkazi wanga timapemphera kwa Yehova kuti atithandize. Nthawi zambiri timaona kuti pamene tikulimbana ndi vuto linalake, nkhani kapena vidiyo yoyenera imatuluka kuti itithandize. Nthawi zonse takhala tikudalira malangizo a Yehova kuti atithandize pa moyo wathu.” Joe ndi mkazi wake apeza kuti nkhani ndi mavidiyo amenewa zathandiza ana awo kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

7. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kukhala osamala ndi chitsanzo chimene amapereka kwa ana awo? (Aroma 2:21)

7 Mfundo 2: Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana amayang’anitsitsa zimene makolo awo amachita ndipo nthawi zambiri amatengera zimene aona. N’zoona kuti palibe kholo limene sililakwitsa zinthu. (Aroma 3:23) Ngakhale zili choncho, makolo anzeru amayesetsa kuti akhale chitsanzo chabwino kwa ana awo. (Werengani Aroma 2:21.) Ponena za ana, bambo wina anafotokoza kuti: “Iwo ali ngati thonje lomwe limangoyamwa chilichonse.” Anawonjezeranso kuti: “Zochita zawo zingasonyeze kuti tikuchita kapena sitikuchita zomwe timawaphunzitsa.” Choncho ngati tikufuna kuti ana athu azikonda Yehova, ifeyo tiyenera kusonyeza kuti timamukonda kwambiri.

8-9. Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene Andrew ndi Emma ananena?

8 Pali njira zambiri zimene makolo angaphunzitsire ana awo kukonda Yehova. Taonani zimene mbale wina wachinyamata wazaka 17 dzina lake Andrew ananena. Iye anati: “Nthawi zonse makolo anga akhala akundithandiza kuti ndiziona kufunika kwa pemphero. Madzulo alionse bambo anga ankapemphera nane ngakhale zitakhala kuti ndapemphera kale pandekha. Nthawi zonse makolo athu ankatikumbutsa kuti: ‘Mukhoza kulankhula ndi Yehova kambirimbiri.’ Zimenezi zinachititsa kuti ndiziona pemphero kukhala lofunika kwambiri, ndipo panopa ndimapemphera kwa Yehova momasuka n’kumamuona monga Atate wanga wachikondi.” Makolo, musamakayikire kuti ana anu angayambe kukonda kwambiri Yehova chifukwa choona mmene inuyo mumamukondera.

9 Taganiziraninso chitsanzo cha Emma. Bambo ake anasiya banja lawo, ndipo anasiyanso ngongole zambiri zimene mayi ake ankafunika kubweza. Emma anati: “Nthawi zambiri amayi ankavutika kupeza ndalama, koma nthawi zonse ankalankhula za mmene Yehova amasamalira komanso kuthandizira atumiki ake. zimene ankachita pa moyo wawo zimasonyezeratu kuti amakhulupirira kwambiri zimenezi. Iwo ankachita zomwe ankatiphunzitsa.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngakhale pamene akukumana ndi mavuto, makolo angaphunzitse ana awo mwa zochita zawo.​—Agal. 6:9.

10. Kodi makolo a Chiisiraeli ankakhala ndi mipata yotani yocheza ndi ana awo? (Deuteronomo 6:6, 7)

10 Mfundo 3: Muzilankhula ndi ana anu pafupipafupi. Yehova anauza Aisiraeli kuti nthawi zonse aziphunzitsa ana awo zokhudza iye. (Werengani Deuteronomo 6:6, 7.) Makolo amenewa anali ndi mipata yambiri patsiku yocheza ndi ana awo komanso kuwathandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Mwachitsanzo, mnyamata Wachiisiraeli akanatha kukhala maola ambiri akuthandiza bambo ake kudzala mbewu kapena kukolola. Ndipo mchemwali wake akanatha kukhala nthawi yaitali akuthandiza mayi ake kusoka, kuluka komanso ntchito zina zapakhomo. Choncho makolo ndi ana awo akanatha kukambirana nkhani zambiri zofunika pamene akuchitira zinthu limodzi. Mwachitsanzo, iwo akanatha kukambirana za khalidwe la Yehova la ubwino komanso mmene iye akuthandizira banja lawo.

11. Kodi ndi mpata wina uti umene makolo angagwiritse ntchito kulankhula ndi ana awo?

11 Masiku ano zinthu zinasintha. M’mayiko ambiri, makolo sangakhale ali limodzi ndi ana awo kwa tsiku lonse. Mwina angakhale ali kuntchito ndipo anawo angakhale ali kusukulu. Choncho makolo amafunika kuyesetsa kuti azipeza nthawi yolankhula ndi ana awo. (Aef. 5:15, 16; Afil. 1:10) Nthawi ina yochitira zimenezi ndi pa kulambira kwa pabanja. M’bale wina wachinyamata dzina lake Alexander ananena kuti: “Nthawi zonse bambo anga amakonza zoti tichite kulambira kwa pabanja ndipo salola chilichonse kusokoneza nthawi imene timachitira zinthu limodziyi. Tikamaliza kulambirako timayamba kucheza.”

12. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wabanja ayenera kukhala ndi cholinga chiti akamachititsa kulambira kwa pabanja?

12 Ngati ndinu mutu wabanja, kodi mungatani kuti ana anu azisangalala pa kulambira kwa pabanja? Bwanji osakonza zoti muziphunzira nawo buku latsopano lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Buku limeneli lingakuthandizeni kuti muzilankhula nawo momasuka. Ngati mumafuna kuti ana anu azimasuka kukufotokozerani mmene akumvera komanso zimene zikuwadetsa nkhawa, musamagwiritse ntchito nthawi ya kulambira kwa pabanja kuti muwadzudzule kapena kuwakalipira. Ndipo muziyesetsa kuti musamakwiye ngati ana anu akufotokoza mfundo zosemphana ndi Malemba. M’malomwake, muziwayamikira chifukwa chofotokoza moona mtima mmene akumvera, ndipo muziwalimbikitsa kuti azikumasukirani. Dziwani kuti mukhoza kuthandiza ana anu moyenera pokhapokha ngati mukudziwa bwino mmene akumvera.

Kodi makolo angagwiritse ntchito bwanji zinthu zam’chilengedwe pophunzitsa ana awo makhalidwe a Yehova? (Onani ndime 13)

13. Kodi ndi mipata ina iti yomwe makolo angagwiritse ntchito pothandiza ana awo kuti azikonda Yehova?

13 Makolo, muziyesetsa kuti tsiku lililonse muzipeza mipata yothandizira ana anu kuti azikonda Yehova. Musamangodikira nthawi ya phunziro la Baibulo kuti muphunzitse ana anu zokhudza Mulungu wathu wachikondi. Taonani zimene mayi wina dzina lake Lisa ananena: “Tinkagwiritsa ntchito zolengedwa zilizonse pofuna kuthandiza ana athu kudziwa zokhudza Yehova. Mwachitsanzo, galu wathu akachita zinazake zoseketsa, tinkagwiritsa ntchito zimenezo powathandiza kudziwa kuti Mlengi wathu ndi wanthabwala komanso kuti amafuna tizisangalala.”

Makolo, kodi mumadziwa anzawo a ana anu? (Onani ndime 14) *

14. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti makolo azithandiza ana awo kusankha anzawo mwanzeru? (Miyambo 13:20)

14 Mfundo 4: Muzithandiza ana anu kupeza anzawo abwino. Mawu a Mulungu amafotokoza momveka bwino kuti anzathu angatithandize kukhala ndi makhalidwe abwino kapena oipa. (Werengani Miyambo 13:20.) Makolo, kodi mumadziwa anzawo a ana anu? Kodi munakumanapo nawo n’kucheza nawo? Kodi mungatani kuti muwathandize kuti azigwirizana ndi anthu omwe amakonda Yehova? (1 Akor. 15:33) Mungawathandize kusankha anzawo abwino poitanira kunyumba kwanu anthu omwe ndi olimba mwauzimu kuti mudzachitire limodzi zinthu zina.​—Sal. 119:63.

15. Kodi makolo angatani kuti azithandiza ana awo kupeza anzawo abwino?

15 Taganizirani zimene bambo wina dzina lake Tony anafotokoza. Iye anafotokoza zimene amachita limodzi ndi mkazi wake pothandiza ana awo kuti akhale ndi anzawo abwino. Tony anati: “Kwa zaka zambiri, ine ndi mkazi wanga takhala tikuitanira kunyumba kwathu abale ndi alongo a misinkhu yosiyanasiyana. Timawaitanira chakudya komanso kuti adzapange nafe kulambira kwa pabanja. Imeneyi ndi njira yabwino yodziwira anthu omwe amakonda komanso kutumikira Yehova mosangalala. Kunyumba kwathu takhala ndi mwayi wolandira oyang’anira madera, amishonale komanso anthu ena. Zinthu zomwe zakhala zikuwachitikira, khama lawo komanso kudzipereka kwawo zathandiza kwambiri ana athu kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.” Choncho makolonu, muziyesetsa kuthandiza ana anu kupeza anzawo abwino.

MUSAMATAYE MTIMA

16. Kodi mungatani ngati mwana wanu wanena kuti sakufuna kutumikira Yehova?

16 Bwanji ngati pambuyo poyesetsa kumuthandiza, mmodzi wa ana anu wanena kuti sakufuna kutumikira Yehova? Zikatero musamaganize kuti mwalephera udindo wanu monga kholo. Yehova anapatsa tonsefe kuphatikizapo mwana wanuyo ufulu wosankha kumutumikira. Ngati mwana wanu wasankha kusiya kutumikira Yehova, muziyembekezera kuti tsiku lina adzabwerera. Kumbukirani fanizo la mwana wolowerera. (Luka 15:11-19, 22-24) Mnyamata ameneyu anachita zinthu zambiri zoipa, koma pamapeto pake anabwerera. Ena anganene kuti: “Limenelitu ndi fanizo chabe, kodi zingachitikedi zimenezi?” Inde zingachitike. Ndipotu izi ndi zimene zinachitikira wachinyamata wina dzina lake Elie.

17. Kodi zimene zinachitikira Elie zakulimbikitsani bwanji?

17 Pofotokoza za makolo ake, Elie ananena kuti: “Iwo anayesetsa kundithandiza kuti ndizikonda kwambiri Yehova komanso Mawu ake Baibulo. Koma ndili ndi zaka 15 ndinasiya kuwamvera.” Elie anayamba kukhala moyo wachiphamaso ndipo anakana zoti makolo ake amuthandize mwauzimu. Atachoka pakhomo pa makolo ake anayamba kuchita makhalidwe oipa. Ngakhale zinali choncho, nthawi zina ankakambirana nkhani za m’Baibulo ndi mnzake wina. Elie anati: “Ndikamakambirana kwambiri ndi mnzangayo mfundo za m’Baibulo m’pamene ndinkaganiziranso kwambiri zokhudza Yehova. Pang’ono ndi pang’ono, mbewu za choonadi zomwe zinakhazikika mumtima mwanga, zomwe makolo anga anachita khama kuzidzala, zinayamba kukula.” Patapita nthawi, Elie anabwereranso m’gulu la Yehova. * Ndiye tangoganizani mmene makolo ake anasangalalira chifukwa choti anayesetsa kumuthandiza kuyambira ali mwana kuti azikonda Yehova.​—2 Tim. 3:14, 15.

18. Kodi mumamva bwanji mukaganizira za makolo omwe amayesetsa kuthandiza ana awo kuti azikonda Yehova?

18 Makolo, mwapatsidwa mwayi wapadera wolera ana omwe ndi m’badwo watsopano wa olambira Yehova. (Sal. 78:4-6) Umenewu si udindo wophweka ndipo tikukuyamikirani mochokera pansi pamtima chifukwa choyesetsa kuthandiza ana anu. Ngati muzichita zonse zomwe mungathe powathandiza kuti azikonda Yehova, ndi kuwalera m’malangizo ake ndiponso kuwaphunzitsa kaganizidwe kake, mungakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzasangalala nanu.​—Aef. 6:4.

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”

^ Makolo a Chikhristu amakonda kwambiri ana awo. Amachita khama kuwapezera zinthu zofunika pa moyo komanso kuwathandiza kuti azisangalala. Chofunika kwambiri n’chakuti iwo amachita zonse zomwe angathe pothandiza anawo kuti azikonda kwambiri Yehova. Nkhaniyi ifotokoza mfundo 4 za m’Baibulo zomwe zingathandize makolo kuchita zimenezi.

^ Onerani vidiyo ya pa jw.org yakuti Yehova Anatithandiza Kulera Ana Athu.

^ Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2012.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pofuna kudziwa anzake a mwana wake, bambo akusewera mpira limodzi ndi mwana wakeyo ndi mnzake.