Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 22

Nzeru Zothandiza pa Moyo Wathu

Nzeru Zothandiza pa Moyo Wathu

“Yehova amapereka nzeru.”​—MIY. 2:6.

NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tonsefe timafunika nzeru zochokera kwa Mulungu? (Miyambo 4:7)

 NGATI pa nthawi ina munkafunika kusankha zinthu pa nkhani yofunika kwambiri, n’zosakayikitsa kuti munapempha nzeru kwa Mulungu chifukwa munkadziwa kuti nzeru zake zingakuthandizeni. (Yak. 1:5) Mfumu Solomo inalemba kuti: “Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.” (Werengani Miyambo 4:7.) Koma sikuti iye ankangonena nzeru zilizonse. M’malomwake ankanena zokhudza nzeru zochokera kwa Yehova Mulungu. (Miy. 2:6) Koma kodi nzeru zochokera kwa Mulungu zingatithandize kulimbana ndi mavuto omwe timakumana nawo masiku ano? Inde zingatithandize, monga mmene tionere munkhaniyi.

2. Kodi chinthu chimodzi chomwe chingatithandize kukhala anzeru n’chiyani?

2 Chinthu chimodzi chomwe chingatithandize kukhala anzeru ndi kuphunzira komanso kutsatira mfundo zimene anthu awiri anzeru kwambiri anaphunzitsa. Choyamba tikambirana za Solomo. Baibulo limafotokoza kuti “Mulungu anapitiriza kupatsa Solomo nzeru zopanda malire ndi luso lomvetsa zinthu losaneneka.” (1 Maf. 4:29) Kenako tikambirana za Yesu, yemwe nzeru zake zinali zoposa za munthu aliyense yemwe anakhalako. (Mat. 12:42) Ponena za Yesu, ulosi unanena kuti: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru [ndi] womvetsa zinthu.”​—Yes. 11:2.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Pogwiritsa ntchito nzeru zimene Mulungu anawapatsa, Solomo ndi Yesu anapereka malangizo othandiza pa nkhani zofunika kwa tonsefe. Mu nkhaniyi tikambirana zitatu mwa nkhani zofunikazi, zomwe ndi kudziona moyenera komanso kuona moyenera ndalama ndi ntchito.

KUONA NDALAMA MOYENERA

4. Kodi Solomo ndi Yesu ankasiyana bwanji pa nkhani za chuma?

4 Solomo anali wolemera kwambiri ndipo ankakhala moyo wawofuwofu. (1 Maf. 10:7, 14, 15) Koma Yesu sanali ndi zinthu zambiri ndipo analibe nyumba yakeyake. (Mat. 8:20) Koma anthu onsewa ankaona zinthu moyenera chifukwa nzeru zawo zinkachokera kwa Yehova Mulungu.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Solomo ankaona ndalama moyenera?

5 Solomo anavomereza kuti ndalama ‘zimateteza.’ (Mlal. 7:12) Ndalama zimatithandiza kuti tipeze zinthu zofunika pa moyo komanso zinthu zina zomwe timafuna. Ngakhale kuti anali wolemera, Solomo anazindikira kuti palinso zinthu zina zofunika kwambiri kuposa ndalama. Mwachitsanzo iye analemba kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.” (Miy. 22:1) Solomo anazindikiranso kuti anthu omwe amakonda ndalama sasangalala ndi zinthu zomwe ali nazo. (Mlal. 5:10, 12) Anatichenjezanso kuti tisamadalire kwambiri ndalama chifukwa zikhoza kutha m’kanthawi kochepa.​—Miy. 23:4, 5.

Kodi timalephera kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba chifukwa cha mmene timaonera zinthu zimene tili nazo? (Onani ndime 6-7) *

6. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankaiona moyenera nkhani yokhala ndi zinthu? (Mateyu 6:31-33)

6 Yesu ankaona moyenera nkhani yokhala ndi zinthu. Ankasangalala ndi zakudya komanso zakumwa. (Luka 19:2, 6, 7) Pa nthawi ina iye anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri ndipo ichi chinali chozizwitsa chake choyamba. (Yoh. 2:10, 11) Ndipo pa tsiku lomwe anafa anavala chovala chamtengo wapatali. (Yoh. 19:23, 24) Komabe Yesu sanalole kuti kukhala ndi zinthu kukhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake. Iye anauza otsatira ake kuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri. . . . Simungathe kutumikira Mulungu ndi chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Yesu anaphunzitsa kuti tikamafunafuna Ufumu choyamba, Yehova adzaonetsetsa kuti tili ndi zonse zimene timafunikira.​—Werengani Mateyu 6:31-33.

7. Kodi m’bale wina anapindula bwanji chifukwa choona ndalama moyenera?

7 Abale ndi alongo athu ambiri zinthu zawayendera bwino chifukwa chogwiritsa ntchito nzeru zochokera kwa Mulungu pa nkhani ya ndalama. Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina yemwe sali pabanja dzina lake Daniel. Iye anati: “Ndili wachinyamata, ndinasankha kuti zinthu zofunika kwambiri kwa ine zikhale zokhudza kulambira.” Popeza kuti amakhala moyo wosalira zambiri, Daniel wakhala akugwiritsa ntchito nthawi ndi luso lake pochita zambiri m’gulu la Yehova. Iye anawonjezera kuti: “Ndinganene moona mtima kuti sindinanong’onezeko bondo chifukwa cha zimene ndinasankha. N’zoona kuti ndikanapezadi ndalama zochuluka ndikanakhala kuti ndimaziona kuti ndizofunika kwambiri pa moyo wanga. Koma sizikanandithandiza kupeza anzanga abwino omwe ndili nawo. Sizikanandithandizanso kukhala wokhutira ngati mmene zilili panopa chifukwa choti ndikuika pamalo oyamba zinthu zokhudza Ufumu. Yehova wandipatsa chimwemwe chochuluka kuposa chomwe ndikanakhala nacho chifukwa chokhala ndi ndalama zambiri.” Kunena zoona, timapindula kwambiri chifukwa choika zinthu zauzimu pamalo oyamba osati ndalama.

KUONA NTCHITO MOYENERA

8. Kodi Solomo anasonyeza bwanji kuti ankaona ntchito moyenera? (Mlaliki 5:18, 19)

8 Solomo ananena kuti chisangalalo chomwe timapeza chifukwa chogwira ntchito mwakhama ndi “mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Werengani Mlaliki 5:18, 19.) Iye analemba kuti “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.” (Miy. 14:23) Solomo ankadziwa kuti mfundo imene ananenayi ndi yoona. Tikutero chifukwa anali wakhama pantchito. Iye anamanga nyumba zambiri, analima minda ya mpesa komanso anali ndi minda ya maluwa ndiponso madamu a madzi. Anamanganso mizinda. (1 Maf. 9:19; Mlal. 2:4-6) Anachitatu khama pogwira ntchitoyi ndipo n’zosakayikitsa kuti zinamuthandiza kukhala wosangalala. Koma sikuti Solomo ankangodalira zinthu zimenezi kuti azisangalala. M’malomwake ankagwiranso ntchito zokhudzana ndi kulambira Yehova. Mwachitsanzo, kwa zaka 7 iye anatsogolera pa ntchito yomanganso kachisi wokongola woti anthu azilambiriramo Yehova. (1 Maf. 6:38; 9:1) Komabe pambuyo pake Solomo anazindikira kuti kugwira ntchito zokhudzana ndi kulambira Yehova n’kofunika kwambiri kusiyana ndi kugwira ntchito zina zonse. Analemba kuti: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake.”​—Mlal. 12:13.

9. Kodi Yesu anatani kuti asamaone ntchito yake ya ukalipentala kukhala yofunika kwambiri?

9 Yesu anali wakhama pantchito. Ali wachinyamata ankagwira ntchito yaukalipentala. (Maliko 6:3) N’zosakayikitsa kuti makolo ake ankayamikira powathandiza kupeza zofunikira zothandiza banja lawo lomwe linali lalikulu. Ndipo popeza anali wangwiro, ziyenera kuti zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri pa ntchito yake ya ukalipentala. N’zosakayikitsa kuti iye ankasangalala ndi ntchitoyi. Ngakhale kuti ankachita khama kwambiri pa ntchito yakeyi, Yesu ankapeza nthawi yotumikira Yehova. (Yoh. 7:15) Pambuyo pake atayamba utumiki wa nthawi zonse, analangiza omvetsera ake kuti: “Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha.” (Yoh. 6:27) Ndipo pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu ananena kuti: “Unjikani chuma chanu kumwamba.”​—Mat. 6:20.

Kodi tingatani kuti tipitirize kuona moyenera ntchito komanso zinthu zokhudza kulambira? (Onani ndime 10-11) *

10. Kodi ndi vuto lotani lomwe ena angakumane nalo pa nkhani ya ntchito?

10 Nzeru za Mulungu zimatithandiza kuti tiziona ntchito moyenera. Monga Akhristu, timalimbikitsidwa kuti ‘tizigwira ntchito molimbikira . . . , ntchito yabwino.’ (Aef. 4:28) Nthawi zambiri mabwana athu amaona kuona mtima komanso khama lathu ndipo angatiyamikire chifukwa cha mmene timagwirira ntchito. Mwina tili ndi zolinga zabwino, tingayambe kumagwira ntchito maola ambiri n’cholinga choti abwana athu apitirize kuona kuti a Mboni za Yehova ndi anthu abwino. Koma pasanapite nthawi yaitali, tingayambe kuzindikira kuti tayamba kunyalanyaza udindo wathu m’banja komanso zinthu zauzimu. Choncho tiyenera kusintha kuti tizikhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zofunika.

11. Kodi m’bale wina anaphunzira chiyani pa nkhani yoona ntchito moyenera?

11 M’bale wina wachinyamata dzina lake William anaona kufunika koona moyenera ntchito yomwe timagwira. Ponena za m’bale wina yemwe anamulembapo ntchito, William ananena kuti: “[M’bale ameneyu] ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yoona ntchito moyenera. Iye amalimbikira ndipo amagwira bwino ntchito yake zomwe zimachititsa kuti makasitomala ake azimukonda. Koma akamaliza kugwira ntchito pamapeto pa tsiku, amasiya chilichonse chokhudzana ndi ntchitoyo n’kuyamba kugwiritsa ntchito nthawi yake pothandiza banja lake komanso polambira Yehova. Ndipotu iye ndi mmodzi wa anthu osangalala kwambiri amene ndimawadziwa.” *

TIZIDZIONA MOYENERA

12. Kodi Solomo anasonyeza bwanji kuti ankadziona moyenera, nanga n’chiyani chinachititsa kuti asamadzionenso choncho?

12 Pa nthawi imene ankalambira Yehova mokhulupirika, Solomo ankadziona moyenera. Ali wachinyamata, Iye anavomereza modzichepetsa zimene sangakwanitse ndipo anapempha Yehova kuti azimutsogolera. (1 Maf. 3:7-9) Cha kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Solomo ankadziwanso za kuopsa kwa kunyada. Iye analemba kuti: “Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.” (Miy. 16:18) Koma n’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi, Solomo anakanika kutsatira malangizo ake omwe. Cha mkatikati mwa ulamuliro wake, modzikuza anayamba kunyalanyaza malamulo a Mulungu. Mwachitsanzo, lamulo lina linkanena kuti mfumu ya Chiheberi ‘isachulukitse akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Solomo sanamvere lamulo limeneli ndipo anakwatira akazi 700 komanso anali ndi akazi 300 a pambali, ndipo ambiri mwa iwo ankalambira milungu ina. (1 Maf. 11:1-3) N’kutheka kuti iye ankaona kuti chilichonse chili m’chimake. Mulimonse mmene zinalili, patapita nthawi Solomo anakumana ndi zotsatirapo za kusamvera Yehova.​—1 Maf. 11:9-13.

13. Kodi kuganizira chitsanzo cha Yesu cha kudzichepetsa kungatiphunzitse chiyani?

13 Yesu anapitirizabe kudziona moyenera komanso kukhala wodzichepetsa. Asanabwere padzikoli, iye anachita zinthu zambiri potumikira Yehova. Kudzera mwa Yesu “zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” (Akol. 1:16) Pa nthawi imene ankabatizidwa, zikuoneka kuti Yesu anakumbukira zinthu zimene anakwanitsa kuchita ali limodzi ndi Atate wake. (Mat. 3:16; Yoh. 17:5) Koma zimenezi sizinamuchititse kuti ayambe kunyada. Ndipotu iye sanadzionepo ngati woposa ena. Anauza ophunzira ake kuti sanabwera padzikoli “kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kupereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Komanso modzichepetsa, Yesu anavomereza kuti sakanachita chilichonse mongoganiza payekha. (Yoh. 5:19) Kumenekutu kunali kudzichepetsa kwakukulu. Apa iye anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri chimene tiyenera kutengera.

14. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu pa nkhani yodziona moyenera?

14 Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azidziona moyenera. Pa nthawi ina iye anawalimbikitsa kuti: “Tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu [Mulungu] amaliwerenga.” (Mat. 10:30) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri makamaka ngati nthawi zina timadziona molakwika. Amasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba amachita nafe chidwi ndipo ndife ofunika kwambiri kwa iye. Sitiyenera kuganiza kuti iye akulakwitsa potilola kuti tizimulambira komanso kutiona kuti ndife oyenera kudzalandira moyo wosatha.

Kodi kulephera kudziona moyenera kungachititse kuti tisapeze madalitso ati? (Onani ndime 15) *

15. (a) Kodi Nsanja ya Olonda ina inatilimbikitsa kuti tizidziona bwanji? (b) Mogwirizana ndi chithunzi chimene chili patsamba 24, kodi sitingapeze madalitso ati chifukwa cholephera kudziona moyenera?

15 Zaka 15 zapitazo, Nsanja ya Olonda ina inatilimbikitsa kuti tizidziona moyenera. Inanena kuti: ‘Indedi, sitiyenera kuganiza kuti ndi ofunika kwambiri mpaka kuyamba kunyada. Komanso tisamachite kudzitsitsa monyanyira n’kumadziona ngati ndife opanda ntchito. Cholinga chathu chiyenera kukhala kumadziona m’njira yoyenera poganizira zinthu zimene tingachite ndiponso zimene sitingathe kuchita. Mlongo wina anafotokoza mfundo imeneyi motere: “Ndimadziwa kuti sindine munthu woipitsitsa kuposa wina aliyense. Koma pa nthawi yomweyomweyo ndimadziwanso kuti sindine munthu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense. Pa zinthu zina ndimachita bwino, koma pa zinthu zina sindichita bwino. Ndipotu umu ndi mmene aliyense alili.”’ * Kodi mwaona phindu limene lingakhalepo ngati titamayesetsa kuti tizidziona moyenera?

16. N’chifukwa chiyani Yehova amatipatsa malangizo anzeru?

16 Kudzera m’Mawu ake, Yehova amatipatsa malangizo anzeru. Amatikonda ndipo amafuna kuti tizisangalala. (Yes. 48:17, 18) Chinthu chanzeru chimene tiyenera kusankha, ndi kuika zimene Yehova amafuna pamalo oyamba pa moyo wathu, zomwe zimachititsa kuti tipeze chimwemwe chochuluka. Tikatero tidzapewa mavuto ambiri omwe anthu ambiri amakumana nawo chifukwa choganizira kwambiri ndalama, ntchito komanso zokhudza iwowo. Tiyeni tonsefe titsimikize mtima kuti tikhale anzeru komanso tizisangalatsa mtima wa Yehova.​—Miy. 23:15.

NYIMBO NA. 94 Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake

^ Solomo ndi Yesu anali anthu anzeru kwambiri. Yehova Mulungu ndi amene anawapatsa nzeruzi. Munkhaniyi tiona malangizo omwe Solomo ndi Yesu anapereka okhudza kudziona moyenera, komanso kuona moyenera ndalama ndi ntchito. Tionanso mmene Akhristu anzathu apindulira chifukwa chogwiritsa ntchito malangizo anzeru opezeka m’Baibulo amenewa.

^ Onani nkhani yakuti “Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala ndi Ntchito Yanu” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2015.

^ Onani nkhani yakuti “Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Osangalala” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2005.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: John ndi Tom ndi achinyamata awiri omwe ali mumpingo umodzi. Nthawi zambiri John amakhala akusamalira galimoto yake. Tom amanyamula ena pa galimoto yake akamalowa mu utumiki komanso popita kumisonkhano.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: John akugwira ovatayimu. Sakufuna kukhumudwitsa abwana ake. Nthawi zonse amavomera abwana ake akamupempha kuti agwire ovatayimu. Madzulo omwewo Tom, yemwe ndi mtumiki wothandiza, wapita ndi mkulu wina ku ulendo wa ubusa. Nthawi ina m’mbuyomu Tom anapempha abwana ake kuti masiku ena mkati mwa mlungu, aziweluka mofulumira kuti azikachita zinthu zina zokhudza kulambira Yehova

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: John akungoganizira zofuna zake. Tom, yemwe amaika zinthu zauzimu pamalo oyamba osati zofuna zake, wapeza anzake ambiri pamene akuthandiza nawo kukonza Nyumba ya Msonkhano.