Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 20

Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudzanso Adani a Mulungu

Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudzanso Adani a Mulungu

“Anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”​CHIV. 16:16.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi buku la Chivumbulutso limafotokoza zotani zokhudza anthu a Mulungu?

 BUKU la Chivumbulutso limafotokoza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba ndipo Satana anathamangitsidwako. (Chiv. 12:1-9) Zimenezi zinachititsa kuti kumwamba zinthu ziziyenda bwino, koma zinabweretsa mavuto padzikoli. Chifukwa chiyani? Chifukwa Satana ndi wokwiya ndipo akulimbana ndi anthu omwe akutumikira Yehova mokhulupirika.​—Chiv. 12:12, 15, 17.

2. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova?

2 Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti Satana akulimbana nafe? (Chiv. 13:10) Chinthu chimodzi ndi kudziwa zomwe zichitike m’tsogolomu. Mwachitsanzo, m’buku la Chivumbulutso mtumwi Yohane anafotokoza ena mwa madalitso omwe tidzasangalale nawo posachedwapa, monga kuwonongedwa kwa adani a Mulungu. Tsopano tiyeni tione mmene buku la Chivumbulutso limafotokozera zokhudza adaniwa komanso zomwe zidzawachitikire.

ADANI A MULUNGU ANAFOTOKOZEDWA “MWA ZIZINDIKIRO”

3. Kodi ndi zizindikiro zina ziti zomwe zimatchulidwa m’buku la Chivumbulutso?

3 Mu vesi loyambirira, buku la Chivumbulutso likutiuza kuti zimene tiwerenge m’bukuli zikufotokozedwa “mwa zizindikiro.” (Chiv. 1:1) Adani a Mulungu akufotokozedwa mophiphiritsa. Timawerenga zokhudza zilombo zingapo. Mwachitsanzo, akutchula za “chilombo chikutuluka m’nyanja” ndipo chili ndi “nyanga 10 ndi mitu 7.” (Chiv. 13:1) Kenako pakubwera “chilombo china chikutuluka pansi pa dziko lapansi.” Chilombochi chinayamba kulankhula ngati chinjoka ndipo chinachititsa “moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba.” (Chiv. 13:11-13) Kenako timawerenganso za “chilombo chofiira kwambiri,” chomwe pamsana pake pali hule. Zilombo zitatuzi zikuimira adani omwe akhala akulimbana ndi Yehova ndi Ufumu wake kwa nthawi yaitali. Choncho n’zofunika kuti tiwadziwe.​—Chiv. 17:1, 3.

ZILOMBO ZIKULUZIKULU 4

‘Zinatuluka m’nyanja.’ (Dan. 7:1-8, 15-17) Zimaimira maulamuliro amphamvu padziko lonse omwe zochita zawo zakhala zikukhudza anthu a Mulungu kuyambira m’nthawi ya Danieli. (Onani ndime 4, 7)

4-5. Kodi zimene zili pa Danieli 7:15-17 zimatithandiza bwanji kudziwa tanthauzo la zizindikirozi?

4 Tisanadziwe kuti adaniwa ndi ndani, choyamba tiyenera kumvetsa tanthauzo la zizindikirozi. Chimene chingatithandize ndi kulola kuti Baibulo lidzifotokoze lokha. Zambiri mwa zizindikiro za m’buku la Chivumbulutsozi zinafotokozedwa kale m’mabuku ena a m’Baibulo. Mwachitsanzo, mneneri Danieli analota maloto ndipo anaona ‘zilombo zinayi zikuluzikulu zikutuluka m’nyanja.’ (Dan. 7:1-3) Iye anafotokoza zimene zilombozi zikuimira. Anati zikuimira “mafumu,” kapena kuti maboma 4. (Werengani Danieli 7:15-17.) Izi zikutithandiza kumvetsa kuti zilombo zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso ziyeneranso kuti zikuimira maboma a padzikoli.

5 Tsopano tiyeni tikambirane zina mwa zizindikiro zotchulidwa m’buku la Chivumbulutsozi. Tikamakambirana, tiona mmene Baibulo litithandizire kudziwa matanthauzo ake. Tiyamba ndi kukambirana zilombo zimene zatchulidwa ndipo tiziona zimene chilichonse chikuimira. Kenako tiona zimene zidzachitikire zilombozi. Ndipo pomaliza tikambirana mmene zochitika zimenezi zikutikhudzira.

ADANI A MULUNGU ANADZIWIKA

CHILOMBO CHA MITU 7

‘Chinatuluka m’nyanja’ ndipo chili ndi mitu 7, nyanga 10 komanso zisoti zachifumu 10. (Chiv. 13:1-4) Chikuimira maufumu onse omwe akhala akulamulira anthu kuyambira kale mpaka pano. Mitu 7 ikuimira maulamuliro 7 amphamvu padziko lonse omwe zochita zawo zakhala zikukhudza kwambiri anthu a Mulungu. (Onani ndime 6-8)

6. Kodi chilombo cha mitu 7 chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1-4 chikuimira chiyani?

6 Kodi chilombo cha mitu 7 chikuimira chiyani? (Werengani Chivumbulutso 13:1-4.) Chilombochi ndi chooneka ngati kambuku, zala zake zooneka ngati za chimbalangondo, pakamwa pake ngati pa mkango ndipo chili ndi nyanga 10. Zilombo 4 zotchulidwa pa Danieli 7 zilinso ndi maonekedwe ngati amenewa. Koma m’buku la Chivumbulutso, ndi chilombo chimodzi chokha chomwe chili ndi maonekedwe onsewa. Chilombochi sichikuimira boma limodzi kapena ulamuliro umodzi wa padziko lonse. Chikufotokozedwa kuti chikulamulira “anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, chinenero chilichonse ndi dziko lililonse.” Choncho chiyenera kukhala ulamuliro waukulu osati boma limodzi lokha. (Chiv. 13:7) Apa ndiye kuti chilombochi chiyenera kuti chikuimira maulamuliro onse omwe akhala akulamulira anthu mpaka pano. *​—Mlal. 8:9.

7. Kodi mutu uliwonse wa chilombo cha mitu 7 ukuimira chiyani?

7 Kodi mutu uliwonse pa mitu 7 ya chilombo ukuimira chiyani? Mfundo yotithandiza kumvetsa zimenezi ikupezeka pa Chivumbulutso 17, pomwe amafotokoza za chifaniziro cha chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13. Pa Chivumbulutso 17:10 timauzidwa kuti: “Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.” Pa maulamuliro onse omwe Satana wakhala akuwagwiritsa ntchito, 7 ndi amene ali ngati “mitu” chifukwa choti anali ndi mphamvu zambiri. Amenewa ndi maufumu omwe akhala akulamulira dziko lonse ndipo zochita zawo zakhala zikukhudza anthu a Mulungu. Pofika m’nthawi ya Yohane, maufumu 5 anali atalamulira kale omwe ndi Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya komanso Girisi. Ufumu wa nambala 6 womwe ndi wa Roma, unali ukulamulirabe pa nthawi yomwe Yohane anaona masomphenya a mu Chivumbulutso. Kodi ndi boma liti lomwe likanakhala ufumu wa nambala 7 komanso womaliza kulamulira padziko lonse?

8. Kodi mutu wa nambala 7 wa chilombo ukuimira ulamuliro uti?

8 Monga mmene tionere, maulosi a m’buku la Danieli akutithandiza kudziwa mutu wa nambala 7 wachilombo, womwenso ndi womaliza. Kodi ndi ulamuliro uti wamphamvu padziko lonse umene wakhala ukulamulira m’masiku otsiriza ano, omwe ndi ‘tsiku la Ambuye’? (Chiv. 1:10) Ulamulirowu wapangidwa ndi maboma awiri amphamvu omwe ndi United Kingdom ndi United States of America. Choncho tinganene kuti ulamuliro umenewu ndi mutu wa nambala 7 wa chilombo chotchulidwa pa Chivumbulutso 13:1-4.

CHILOMBO CHA NYANGA ZIWIRI NGATI MWANA WA NKHOSA

Chinatuluka “pansi pa dziko lapansi” ndipo chinayamba kulankhula “ngati chinjoka.” Chinachititsa “moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba” ndipo chinkachita zizindikiro ngati “mneneri wonyenga.” (Chiv. 13:11-15; 16:13; 19:20) Monga chilombo cha nyanga ziwiri komanso mneneri wonyenga, ulamuliro wa United Kingdom ndi America umasocheretsa anthu padzikoli komanso kuwauza kuti apange chifaniziro cha chilombo chomwe chili ndi mitu 7 ndi nyanga 10. (Onani ndime 9)

9. Kodi chilombo cha “nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa” chikuimira chiyani?

9 Pa Chivumbulutso 13 timauzidwanso kuti mutu wa nambala 7, womwe ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa United Kingdom ndi America, umachitanso zinthu ngati chilombo chomwe “chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, koma chinayamba kulankhula ngati chinjoka.” Chilombochi “chinachitanso zizindikiro zazikulu, moti chinapangitsa ngakhale moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuona.” (Chiv. 13:11-15) Pa Chivumbulutso 16 ndi 19 amachifotokoza kuti ndi “mneneri wonyenga.” (Chiv. 16:13; 19:20) Danieli anafotokoza zofanana ndi zimenezi, pomwe anasonyeza kuti ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa United Kingdom ndi America, ‘udzaononga zinthu zambiri.’ (Dan. 8:19, 23, 24) Zimenezi ndi zomwe zinachitikadi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Mabomba awiri anyukiliya omwe anachititsa kuti nkhondoyo ithe anapangidwa ndi asayansi a ku Britain ndi America. Apa zinali ngati ulamuliro wa padziko lonse wa United Kingdom ndi America ‘wachititsa moto kugwera padziko lapansi kuchokera kumwamba.’

CHILOMBO CHOFIIRA KWAMBIRI

Pamsana pake pali hule lomwe ndi Babulo Wamkulu. Chimafotokozedwa kuti ndi mfumu ya nambala 8. (Chiv. 17:3-6, 8, 11) Poyamba hulelo likulamulira chilombo cho koma pamapeto pake chikuliwononga. Huleli likuimira zipembedzo zonse zonyenga. Chilombocho masiku ano chikuimira bungwe la United Nations lomwe limalimbikitsa zofuna za maboma a padzikoli. (Onani ndime 10, 14-17)

10. Kodi “chifaniziro cha chilombo” chimaimira chiyani? (Chivumbulutso 13:14, 15; 17:3, 8, 11)

10 Kenako timawerenga za chilombo chinanso. Chimenechi chimaoneka mofanana kwambiri ndi chilombo cha mitu 7 chija, koma kusiyana kwake n’kwakuti chilombochi chimaoneka chofiira kwambiri. Chimatchulidwa kuti “chifaniziro cha chilombocho” ndipo chikufotokozedwa kuti ndi “mfumu ya 8.” * (Werengani Chivumbulutso 13:14, 15; 17:3, 8, 11.) ‘Mfumuyi’ imafotokozedwa kuti inalipo, kenako panalibe ndipo pambuyo pake inaonekeranso. Mfundo imeneyitu ikugwirizana kwambiri ndi zimene zinachitikira bungwe la United Nations, lomwe limalimbikitsa zolinga za maboma a padzikoli. Poyamba bungweli linkatchulidwa kuti League of Nations. Kenako linatha panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndipo pambuyo pake linakhazikitsidwanso n’kuyamba kudziwika kuti United Nations.

11. Kodi maulamuliro a ndale omwe ali ngati zilombo amachita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kuwaopa?

11 Pogwiritsa ntchito mfundo zabodza, zilombozi zimalimbikitsa anthu kuti azitsutsa Yehova ndi anthu ake. Mophiphiritsa, zimasonkhanitsa “mafumu a dziko lonse lapansi” ku nkhondo ya Aramagedo, yomwe ndi “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chiv. 16:13, 14, 16) Koma ife sitidzaopa chilichonse. Mwamsanga, Mulungu wathu wamkulu Yehova adzachitapo kanthu kuti apulumutse onse amene ali kumbali ya ulamuliro wake.​—Ezek. 38:21-23.

12. Kodi n’chiyani chidzachitikire zilombo zonse?

12 Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire zilombo zonse? Lemba la Chivumbulutso 19:20 limayankha kuti: “Chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wonyenga uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake. Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.” Choncho panthawi imene adzakhale akulamulira, adani a Mulungu amenewa adzaonongedwa ndipo sadzakhalakonso mpaka kalekale.

13. Kodi maboma a m’dzikoli amachititsa kuti Akhristu azikumana ndi vuto lotani?

13 Kodi zimenezi zimatikhudza bwanji? Monga Akhristu, tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi Ufumu wake. (Yoh. 18:36) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, sitiyenera kulowerera ndale za m’dzikoli. Komabe kusalowerera ndale kungakhale kovuta kwambiri chifukwa maboma a m’dzikoli amafuna kuti tisonyeze kuti tili kumbali yawo mwa zolankhula ndi zochita zathu. Anthu amene amalolera zimenezi amalandira chizindikiro cha chilombo. (Chiv. 13:16, 17) Komatu anthu omwe alandira chizindikiro cha chilombochi, amakhala osavomerezeka kwa Yehova ndipo amataya mwayi wodzalandira moyo wosatha. (Chiv. 14:9, 10; 20:4) Choncho n’zofunika kwambiri kwa aliyense wa ife kuti asamalowerere ndale mpang’ono pomwe ngakhale maboma atatikakamiza chotani kuti tikhale kumbali yawo.

MAPETO OMVETSA CHISONI A HULE LALIKULU

14. Kodi kenako mtumwi Yohane anaona zinthu zodabwitsa ziti, zofotokozedwa pa Chivumbulutso 17:3-5?

14 Mtumwi Yohane anafotokoza kuti ‘anadabwa kwambiri’ ndi zinthu zina zomwe anaona. Kodi iye anaona chiyani? Anaona mkazi atakwera chimodzi mwa zilombo zoopsazi. (Chiv. 17:1, 2, 6) Mkaziyu akufotokozedwa kuti ndi “hule lalikulu” ndipo akutchedwa kuti “Babulo Wamkulu.” Iye anachita “dama” ndi “mafumu a dziko lapansi.”​—Werengani Chivumbulutso 17:3-5.

15-16. Kodi “Babulo Wamkulu” ndi ndani, ndipo tikudziwa bwanji?

15 Kodi “Babulo Wamkulu” ndi ndani? Mkaziyu sangaimire ulamuliro wina wake wapadzikoli chifukwa akufokozedwa kuti anachita dama ndi olamulira a m’dzikoli. (Chiv. 18:9) Ndipotu amayesetsa kuwalamulira, zomwe zili ngati kukwera pamsana pawo. Kuwonjezera pamenepa, sangaimire amalonda adyera a m’dziko la Satanali. Iwo amafotokozedwa kale kuti ndi “amalonda oyendayenda.”​—Chiv. 18:11, 15, 16.

16 M’Malemba, mawu akuti “hule” amanena za anthu omwe amati amalambira Mulungu koma n’kumalambira mafano kapena kukhala mabwenzi a dziko m’njira inayake. (1 Mbiri 5:25; Yak. 4:4) Mosiyana ndi zimenezi, anthu omwe amalambira Mulungu mokhulupirika amatchulidwa kuti “oyera” kapena “anamwali.” (2 Akor. 11:2; Chiv. 14:4) Mzinda wakale wa Babulo unali likulu la kulambira konyenga. Choncho Babulo Wamkulu ayenera kuimira kulambira konyenga kulikonse. Ndipotu iye akuimira zipembedzo zonse zonyenga.​—Chiv. 17:5, 18; onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?

17. Kodi n’chiyani chidzachitikire Babulo Wamkulu?

17 Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire Babulo Wamkulu? Lemba la Chivumbulutso 17:16, 17 limayankha kuti: “Nyanga 10 waziona zija, komanso chilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto. Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake.” Choncho Yehova adzalimbikitsa maboma kuti agwiritse ntchito chilombo chofiira, chomwe ndi bungwe la United Nations, kuti chiukire zipembedzo zonse zonyenga n’kuziwonongeratu.​—Chiv. 18:21-24.

18. Kodi tingatani kuti tionetsetse kuti sitikutenga nawo mbali m’zochita za Babulo Wamkulu?

18 Kodi zimenezi zikutikhudza bwanji? Kulambira kwathu kuyenera kukhala “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yak. 1:27) Sitiyenera kulola kuti tikhudzidwe ndi ziphunzitso zabodza, maholide a zipembedzo, makhalidwe oipa komanso zamizimu zomwe zimachokera ku Babulo Wamkulu. Tiyenera kupitiriza kuitana anthu kuti ‘atuluke mwa iye’ n’cholinga choti asagawane naye machimo ake.​—Chiv. 18:4.

KUWERUZA MDANI WAMKULU WA MULUNGU

CHINJOKA CHACHIKULU CHOFIIRA

Satana anapereka ulamuliro kwa chilombo. (Chiv. 12:3, 9, 13; 13:4; 20:2, 10) Monga mdani wamkulu wa Mulungu, Satana adzaponyedwa kuphompho kwa zaka 1000. Pambuyo pake adzaponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.” (Onani ndime 19-20)

19. Kodi “chinjoka chachikulu chofiira” ndi ndani?

19 Buku la Chivumbulutso limafotokozanso za “chinjoka chachikulu chofiira.” (Chiv. 12:3) Chinjokachi chinamenyana ndi Yesu ndi angelo ake. (Chiv. 12:7-9) Chinapita kukaukira anthu a Mulungu komanso chinapereka ulamuliro kwa zilombo, kapena kuti maboma a anthu. (Chiv. 12:17; 13:4) Kodi chinjoka chimenechi ndi ndani? Ndi “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana.” (Chiv. 12:9; 20:2) Iye ndi amene amatsogolera adani onse a Yehova.

20. Kodi n’chiyani chidzachitikire chinjoka?

20 Kodi n’chiyani chidzachitikire chinjoka? Lemba la Chivumbulutso 20:1-3 limafotokoza kuti mngelo adzaponyera Satana kuphompho, zomwe zidzakhale ngati waikidwa m’ndende. Akadzamangidwa, iye ‘sadzatha kusocheretsanso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1000.’ Pamapeto pake Satana ndi ziwanda zake adzawonongedwa, zomwe zili ngati kuponyedwa “m’nyanja yamoto ndi sulufule.” (Chiv. 20:10) Tangoganizani mmene zinthu zidzakhalire padzikoli popanda Satana ndi ziwanda zake. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri.

21. N’chifukwa chiyani tingakhale osangalala ndi zimene timawerenga m’buku la Chivumbulutso?

21 Timalimbikitsidwa kwambiri chifukwa chomvetsa tanthauzo la zizindikiro zomwe zili m’buku la Chivumbulutso. Sikuti tangokwanitsa kudziwa adani a Yehova, koma taonanso zimene zidzawachitikire. Kunena zoona, “wodala ndi munthu amene amawerengera ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu.” (Chiv. 1:3) Koma kodi adani onse a Mulungu akadzawonongedwa, ndi madalitso otani omwe anthu okhulupirika adzasangalale nawo? Tikambirana zimenezi munkhani yomaliza pa nkhani zitatuzi.

NYIMBO NA. 23 Yehova Wayamba Kulamulira

^ Buku la Chivumbulutso limagwiritsa ntchito zizindikiro potithandiza kudziwa adani a Mulungu. Buku la Danieli limatithandiza kumvetsa tanthauzo la zizindikirozi. Munkhaniyi tiyerekezera maulosi ena m’bukuli ofanana ndi omwe ali m’buku la Chivumbulutso. Izi zitithandiza kudziwa adani a Mulungu. Kenako tikambirana zomwe zidzawachitikire.

^ Chinthu china chomwe chikusonyeza kuti chilombo cha mitu 7 chikuimira maulamuliro onse a padzikoli n’chakuti chili ndi “nyanga 10.” Nthawi zambiri nambala ya 10 m’Baibulo imaimira kukwanira kwa chinthu.

^ Mosiyana ndi chilombo choyamba chija, chifaniziro chake chilibe ‘zisoti zachifumu’ panyanga zake. (Chiv. 13:1) Zimenezi zili choncho chifukwa ‘chatuluka mwa mafumu 7 aja’ ndipo chimadalira mafumuwo kuti achipatse ulamuliro.​—Onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Chilombo Chofiira Kwambiri Chomwe Chimatchulidwa M’chaputala 17 cha Chivumbulutso Chimaimira Chiyani?