Mfundo Zothandiza Pophunzira
Malifalensi a pa LAIBULALE YA PA INTANETI
Malifalensi athu angakuthandizeni kuphunzira zambiri pa nkhani zosiyanasiyana. Malifalensiwa akuphatikizapo Matanthauzo a Mawu Ena, Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, Insight on the Scriptures ndi Watch Tower Publications Index.
Mbali yofufuzira yomwe ili palaibulaleyi ingakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito malifalensiwa. Mukamalemba mukabokosi kofufuzira, zina zomwe mukufuna zimayamba kuoneka pansi pakabokosiko. Mawu akuti “Mawu” amaonekera pambali pa liwu lililonse lomwe likupezeka m’malifalensiwo.
Tayesani izi: Pakabokosi kofufuzira (A) yambani kulemba mawu akuti “Yehova.” Pa (B) sankhani mawu akuti “Yehova” omwe ali ndi mawu akuti “Mawu” pambali pake. Mukatero muona zotsatira za m’malifalensi osiyanasiyana.