NKHANI YOPHUNZIRA 24
Mungathe Kukwaniritsa Zolinga Zanu Zauzimu
“Tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.”—AGAL. 6:9.
NYIMBO NA. 84 Timadzipereka
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1. Kodi ambirife timakumana ndi vuto liti?
KODI munayamba mwadziikirapo cholinga chinachake chauzimu koma n’kumalephera kuchikwaniritsa? b Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Mwachitsanzo, Philip ankafuna kuti azipemphera pafupipafupi komanso mapemphero ake azikhala abwino, koma zinkamuvuta kupeza nthawi yopemphera. Erika anali ndi cholinga chakuti asamachedwe kufika pamisonkhano yokonzekera utumiki koma ankachedwa pafupifupi msonkhano uliwonse. Maulendo angapo Tomáš anayesa kukonza zoti awerenge Baibulo lonse. Iye anati: “Kungoti kuwerenga Baibulo sikunkandisangalatsa. Ndinayesapo katatu konse koma nthawi zonse ndinkangofika buku la Levitiko n’kusiya.”
2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka ngati sitinakwaniritsebe cholinga chinachake chauzimu?
2 Ngati panopa muli ndi cholinga china chomwe simunachikwaniritse, dziwani kuti si inu olephera. Kuti munthu akwaniritse ngakhale cholinga chaching’ono amafunika nthawi komanso khama. Mukamafunitsitsa kukwaniritsa cholinga chinachake mumasonyeza kuti mumaona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wamtengo wapatali komanso mukufunitsitsa kumupatsa zinthu zabwino kwambiri. Yehova amayamikira khama lanu. N’zoona kuti sayembekezera zambiri kuposa zimene mungakwanitse. (Sal. 103:14; Mika 6:8) Choncho muzikhala ndi zolinga zimene mungazikwaniritse malinga ndi mmene zilili pa moyo wanu. Ndiye mukadziikira cholinga, kodi mungatani kuti muchikwaniritse? Tiyeni tione mfundo zina zomwe zingakuthandizeni.
KUKHALA NDI MTIMA WOFUNITSITSA N’KOFUNIKA KWAMBIRI
3. N’chifukwa chiyani kukhala ndi mtima wofunitsitsa n’kofunika?
3 Timafunika kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuti tikwaniritse zolinga zauzimu. Munthu akakhala ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chake amachita khama. Mtima wofunitsitsa uli ngati mphepo imene imathandiza boti lomwe lili ndi chinsalu kuti liziyenda. Ngati mphepo itapitiriza kuomba, botilo lingakafike kumene likupita. Ndipo ngati mphepoyo ikuomba mwamphamvu, botilo lingakafike mwamsanga. Mofanana ndi zimenezi, tikakhala ofunitsitsa zimakhalanso zosavuta kukwaniritsa zolinga zathu. M’bale wina wa ku El Salvador dzina lake David, ananena kuti, “Ukakhala ndi mtima wofunitsitsa umachita khama kuti ukwaniritse cholinga chako, sulola chilichonse kukulepheretsa kukwaniritsa cholingacho.” Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhala ndi mtima wofunitsitsa?
4. Kodi tingapempherere chiyani? (Afilipi 2:13) (Onaninso chithunzi.)
4 Muzipempha Yehova kuti mukhale ndi mtima wofunitsitsa. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Yehova angakuthandizeni kukhala mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chanu. (Werengani Afilipi 2:13.) Nthawi zina timadziikira cholinga chifukwa timadziwa kuti ndi zimene tiyenera kuchita, ndipotu ndi bwino kuchita zimenezi. Koma mwina sitingakhale ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholingacho. Zimenezi ndi zimene zinachitikiranso mlongo wina wa ku Uganda dzina lake Norina. Iye anadziikira cholinga choti akhale ndi phunziro la Baibulo ngakhale kuti analibe mtima wofunitsitsa kuti akwaniritse cholingacho chifukwa ankadzikayikira kuti saphunzitsa bwino. Ndiye n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati: “Ndinayamba kupemphera kwa Yehova tsiku lililonse kuti andithandize kuti ndizifunitsitsa kwambiri kuchititsa phunziro la Baibulo. Mogwirizana ndi mapemphero anga, ndinayesetsanso kuti ndiwonjezere luso lophunzitsa. Patapita miyezi yochepa, ndinaona kuti ndayamba kufunitsitsa kuchititsa phunziro la Baibulo. Chaka chomwecho ndinayambitsa maphunziro awiri.”
5. Kodi tingaganizire chiyani kuti tikhale ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chathu?
5 Muziganizira zimene Yehova wakuchitirani. (Sal. 143:5) Mtumwi Paulo anaganizira mozama mmene Yehova anamusonyezera kukoma mtima kwake kwakukulu ndipo izi zinamulimbikitsa kuti azichita khama pomutumikira. (1 Akor. 15:9, 10; 1 Tim. 1:12-14) Mofanana ndi zimenezi, inunso mukamaganizira kwambiri zimene Yehova wakuchitirani, mudzakhala ofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chanu. (Sal. 116:12) Taganizirani zimene zinathandiza mlongo wina wa ku Honduras kuti akwaniritse cholinga chake chokhala mpainiya wokhazikika. Iye anati: “Ndinaganizira mmene Yehova amasonyezera kuti amandikonda. Anandithandiza kuti ndikhale m’gulu la anthu ake, amandisamalira komanso amanditeteza. Kuganizira zimenezi kunandithandiza kuti ndizimukonda kwambiri komanso ndikhale wofunitsitsa kuchita upainiya.”
6. Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti tizifunitsitsa kukwaniritsa cholinga chathu?
6 Muziganizira madalitso amene mungapeze chifukwa chokwaniritsa cholinga chanu. Taonani zomwe zinathandiza Erika, yemwe tamutchula kale uja, kukwaniritsa cholinga chake choti azisunga nthawi. Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndinkamanidwa zambiri chifukwa chofika mochedwa pamsonkhano wokonzekera utumiki. Koma kufika mwamsanga kukanandithandiza kuti ndizipereka moni kwa abale ndi alongo komanso kucheza nawo. Ndikanamamvetseranso malangizo omwe akanandithandiza kuti ndizisangalala komanso ndiziwonjezera luso langa lolalikira.” Erika ankaganizira madalitso amene akanapeza chifukwa chosunga nthawi ndipo anakwaniritsa cholinga chake. Kodi ndi madalitso otani omwe inunso mungaganizire? Ngati cholinga chanu n’chokhudza kuwerenga Baibulo kapena kupemphera, muziganizira mmene kukwaniritsa cholingacho kungakuthandizireni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. (Sal. 145:18, 19) Ngati cholinga chanu n’choti mukhale ndi khalidwe lina lake, muziganizira mmene khalidwelo lingakuthandizireni kuti muzigwirizana ndi ena. (Akol. 3:14) Bwanji osalemba penapake zifukwa zonse zimene zikukuchititsani kufuna kukwaniritsa cholinga chanu? Mukatero muzibwereramo pafupipafupi kuti muziona zifukwazo. Tomáš, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndikakhala ndi zifukwa zambiri zokwaniritsira cholinga chinachake, m’pamenenso ndimayesetsa kuti ndichikwaniritse.”
7. N’chiyani chinathandiza Julio ndi mkazi wake kukwaniritsa cholinga chawo?
7 Muzicheza ndi anthu omwe angamakulimbikitseni. (Miy. 13:20) Taganizirani zomwe zinathandiza Julio ndi mkazi wake kuti akwaniritse cholinga chawo choti azichita zambiri pa ntchito yolalikira. Iye anati: “Tinasankha kumacheza ndi anthu omwe ankatilimbikitsa ndipo tinkakambirana nawo za cholinga chathu. Ambiri mwa anzathuwo anali atakwaniritsa kale cholinga ngati chathuchi ndipo akanatha kutipatsa malangizo othandiza. Anzathuwo ankatifunsa mmene zomwe tinakonza zoti tikwaniritse cholinga chathucho zikuyendera ndipo ankatilimbikitsa ngati pakufunika kutero.”
TIKAMAONA KUTI TILIBE MTIMA WOFUNITSITSA
8. N’chiyani chingachitike ngati titamafuna kukwaniritsa cholinga pa nthawi yokhayo imene tikuona kuti tili ndi mtima wofunitsitsa kutero? (Onaninso chithunzi.)
8 Kunena zoona, tonsefe masiku ena timaona kuti sitikufuna kuchita zinazake. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingakwaniritse cholinga chathu? Ayi. Mwachitsanzo, mphepo ndi imene ingachititse boti kuti likafike kumene likupita. Komabe nthawi zina mphamvu ya mphepo ingakhale yosiyasiyana ndipo masiku ena singakhalepo n’komwe. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti woyendetsa botilo sangakafike kumene akupita? Osati kwenikweni. Mwachitsanzo, maboti ena omwe ali ndi chinsalu amakhalanso ndi injini kapena zopalasira. Woyendetsa botilo angathe kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti akafike kumene akupita. Mtima wathu wofunitsitsa tingauyerekeze ndi mphepo. Masiku ena tingamafunitsitse kukwaniritsa cholinga chathu kusiyana ndi ena ndipo masiku enanso sitingamafune n’komwe kukwaniritsa cholinga chathu. Choncho ngati titamafuna kukwaniritsa cholinga chathu potengera mmene tikumvera, sitingachikwaniritse n’komwe. Koma mofanana ndi woyendetsa boti uja, yemwe amapeza njira zina kuti akafike kumene akupita, tikhoza kukwaniritsabe cholinga chathu ngakhale ngati nthawi zina sitingakhale ndi mtima wofunitsitsa kutero. N’zoona kuti zimenezi sizingakhale zophweka koma zotsatirapo zake zimakhala zabwino kwambiri. Tisanakambirane zimene tingachite, tiyeni tikambirane funso lomwe lingakhalepo.
9. Kodi tiyenera kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chinachake ngakhale pamene tikuona kuti tilibe mtima wofunitsitsa kutero? Fotokozani.
9 Yehova amafuna kuti tizimutumikira mosangalala komanso mofunitsitsa. (Sal. 100:2; 2 Akor. 9:7) Ndiye kodi tiyenera kuyesetsa kupitiriza kukwaniritsa cholinga chinachake chauzimu ngakhale pamene tilibe mtima wofunitsitsa kutero? Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye anati: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.” (1 Akor. 9:25-27) Paulo ankadzikakamiza kuchita zoyenera ngakhale pamene ankaona kuti sakufuna kuchita zimenezo. Kodi Yehova ankasangalala ndi zimene Paulo ankachita pomutumikira? Inde. Ndipotu iye anamudalitsa chifukwa cha khama lake.—2 Tim. 4:7, 8.
10. Kodi timadalitsidwa bwanji tikamayesetsa kukwaniritsa cholinga ngakhale pamene tilibe mtima wofunitsitsa kutero?
10 Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala akationa tikuyesetsa kukwaniritsa cholinga chathu ngakhale pamene tilibe mtima wofunitsitsa kutero. Iye amasangalala chifukwa amadziwa kuti ngakhale kuti si nthawi zonse pamene timachita zinthuzo chifukwa chakuti zimatisangalatsa, timazichita chifukwa chakuti timamukonda iyeyo. Monga mmene Yehova anadalitsira Paulo ifenso adzatidalitsa chifukwa cha khama lathu. (Sal. 126:5) Ndipo tikamaona mmene Yehova akutidalitsira tingayambe kukhala ndi mtima wofunitsitsa. Mlongo wina wa ku Poland dzina lake Lucyna, ananena kuti: “Nthawi zina sindimafuna kupita mu utumiki makamaka ndikatopa. Komabe ndikapita, chimwemwe chimene ndimapeza chimakhala chosaneneka.” Tiyeni tione zimene tingachite tikamamva kuti tilibe mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chathu.
11. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuti tikhale odziletsa?
11 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala odziletsa. Kudziletsa kumaphatikizapo mmene tikumvera komanso zochita zathu. Nthawi zambiri mawuwa amanena za kuyesetsa kuti tisachite zinazake zoipa. Kudziletsa kumafunikanso kuti tichite zabwino makamaka ngati zimene tikufuna kuchitazo zili zovuta kapena tilibe mtima wofunitsitsa kuzichita. Kumbukirani kuti kudziletsa ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa choncho muzipempha mzimu woyera kwa Yehova kuti ukuthandizeni kukhala ndi khalidwe lofunikali. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) David, yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza mmene pemphero linamuthandizira. Iye ankafunitsitsa kuti nthawi zonse asamaphonye kuphunzira payekha. Iye anati: “Ndinkapempha Yehova kuti andithandize kukhala wodziletsa. Iye anandithandiza kuti ndikhale ndi pulogalamu yabwino yophunzira pandekha komanso ndisamadumphedumphe.”
12. Kodi mfundo ya pa Mlaliki 11:4, ingatithandize bwanji kukwaniritsa zolinga zauzimu?
12 Musamadikire kuti zinthu zikhale bwino. M’dzikoli palibe nthawi imene zinthu zonse zingatiyendere bwino. Ngati tingadikire kuti zinthu zikhale bwino, sitingakwaniritse cholinga chathu. (Werengani Mlaliki 11:4.) M’bale wina dzina lake Dayniel ananena kuti: “Palibe nthawi imene zinthu zonse zimakhala kuti zilibwino. Choncho sitiyenera kudikira. Timangofunika kuyambapo.” M’bale wina wa ku Uganda dzina lake Paul, anatchulanso chifukwa china chimene sitiyenera kuchitira zinthu mozengereza. Iye anati: “Tikayambapo ngakhale pamene zinthu sizili bwino, Yehova amatithandiza.”—Mal. 3:10.
13. Kodi kuyamba ndi kukwaniritsa zolinga zing’onozing’ono n’kothandiza bwanji?
13 Muziyamba mwapang’onopang’ono. Nthawi zina sitingakhale ndi mtima wofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chathu chifukwa chakuti cholingacho chikuoneka chovuta. Ngati umu ndi mmene zilili ndi inuyo, kodi mungayambe ndi zinthu zing’onozing’ono pokwaniritsa cholingacho? Ngati cholinga chanu ndi chakuti mukhale ndi khalidwe linalake, bwanji osayamba ndi kusonyeza khalidwelo m’njira zing’onozing’ono? Ngati cholinga chanu ndi choti muwerenge Baibulo lonse, bwanji osayamba ndi kumawerenga kwa nthawi yochepa? Tomáš, amene tamutchula kumayambiriro uja, ankavutika kukwaniritsa cholinga chake choti pakamatha chaka akhale atawerenga Baibulo lonse. Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndinkawerenga zinthu zambiri pakanthawi kochepa. Choncho ndinaganiza kuti ndiyesenso, koma pa nthawiyi ndinakonza kuti ndiziwerenga ndime zochepa tsiku lililonse komanso kuganizira mozama zomwe ndawerengazo. Nditachita zimenezi ndinayamba kumasangalala ndikamawerenga Baibulo.” Tomáš atayamba kusangalala akamawerenga Baibulo, anawonjezera nthawi imene ankaliwerenga. Pamapeto pake anawerenga Baibulo lonse. c
MUSAMAFOOKE NGATI MWAKUMANA NDI ZOLEPHERETSA
14. Kodi tingakumane ndi zolepheretsa ziti?
14 Komabe ngakhale titayesetsa kukhala odziletsa kapena kukhala ndi mtima wofunitsitsa, tingakumanebe ndi zolepheretsa. Mwachitsanzo, “zinthu zosayembekezereka” zingatiwonongere nthawi yomwe timafunika kukwaniritsa cholinga chathu. (Mlal. 9:11) Tingakumane ndi vuto lomwe lingachititse kuti tifooke komanso tisakhale ndi mphamvu. (Miy. 24:10) Popeza ndife ochimwa, nthawi zina tingachite zinthu zimene sizingatithandize kukwaniritsa cholinga chathu. (Aroma 7:23) Kapenanso mwina tingamadzimve kuti tatopa. (Mat. 26:43) Ndiye n’chiyani chingatithandize tikakumana ndi zolepheretsa?
15. Kodi tikakumana ndi zolepheretsa, zimasonyeza kuti ndife olephera? Fotokozani. (Salimo 145:14)
15 Tizikumbukira kuti tikakumana ndi zolepheretsa sizitanthauza kuti ndife olephera. Baibulo limanena kuti tingakumane ndi mavuto mobwerezabwereza. Komabe limafotokoza momveka bwino kuti tingathe kukwaniritsa cholinga chathu, makamaka ngati tikuthandizidwa ndi Yehova. (Werengani Salimo 145:14.) Philip, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Sindimaganizira kwambiri za nthawi imene ndalephera kukwaniritsa cholinga changa. M’malomwake, ndimaganizira za nthawi imene ndayesetsa kuti ndichikwaniritsenso.” David, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndimayesetsa kuti ndiziona zolepheretsa ngati mwayi wanga woti ndimusonyeze Yehova mmene ndimamukondera.” Mukamayesetsa kuti mukwaniritse zolinga zanu ngakhale pali zolepheretsa, mumamusonyeza Yehova kuti mukufuna kumamusangalatsa. Iye amasangalala akaona kuti mukupitirizabe kuyesetsa kukwaniritsa cholinga chanu.
16. Kodi zolepheretsa zingatiphunzitse chiyani?
16 Muziphunzirapo kathu mukakumana ndi zolepheretsa. Muziganizira chimene chakulepheretsani kukwaniritsa cholinga chanu ndiyeno muzidzifunsa kuti, ‘Kodi pali zomwe ndikufunika kusintha kuti zimenezi zisadzachitikenso?’ (Miy. 27:12) Nthawi zina zolepheretsa zingasonyeze kuti tinadziikira cholinga chomwe sitikanatha kuchikwaniritsa. Ngati umu ndi mmenenso zilili ndi inu, muziganiziranso ngati cholingacho chikugwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. d Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephera chifukwa simunakwaniritse cholinga chimene simukanatha kuchikwaniritsa.—2 Akor. 8:12.
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira zomwe takwaniritsa kale?
17 Muziganizira zomwe mwakwanitsa kale kuchita. Baibulo limanena kuti “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.” (Aheb. 6:10) Choncho inunso musamaiwale zomwe mwachita. Muziganizira zolinga zomwe mwazikwaniritsa kale kaya ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, kuuza ena zokhudza iye kapena kubatizidwa. Monga mmene mwakhala mukukwaniritsira zolinga zanu m’mbuyomu, mungapitirizenso kukwaniritsa cholinga chanu panopa.—Afil. 3:16.
18. Kodi tizikumbukira kuchita chiyani pamene tikuyesetsa kuti tikwaniritse cholinga chathu? (Onaninso chithunzi.)
18 Mothandizidwa ndi Yehova, inunso mungathe kukwaniritsa cholinga chanu mofanana ndi woyendetsa boti yemwe amasangalala akafika kumene akupita. Koma kumbukirani kuti oyendetsa boti ambiri amasangalalanso ndi ulendo wawo. Inunso mukayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu chauzimu, muzisangalala ndi mmene Yehova akukuthandizirani komanso kukudalitsirani. (2 Akor. 4:7) Ndipo ngati simungafooke mudzapeza madalitso ambiri.—Agal. 6:9.
NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu
a Nthawi zambiri timalimbikitsidwa kuti tizidziikira zolinga zauzimu. Koma bwanji ngati tinadziikira kale cholinga china chomwe tikuvutika kuchikwaniritsa? Nkhaniyi ifotokoza zinthu zina zomwe zingatithandize kuti tikwaniritse zolinga zathu.
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Cholinga chauzimu ndi chilichonse chomwe mungayesetse kuti muzichichita bwino kapena kuchikwaniritsa n’cholinga choti muzitumikira Yehova mokwanira ndiponso muzimusangalatsa. Mwachitsanzo, mukhoza kukhala ndi cholinga chofuna kukulitsa khalidwe linalake, kapena kuti muzichita bwino pambali inayake yokhudza kulambira monga kuwerenga Baibulo, kuphunzira panokha kapena kulalikira.
c Onani buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, tsamba 10-11, ndime 5.
d Kuti mudziwe zambiri onani nkhani yakuti “Musadzipanikize Ndipo Mudzakhala Achimwemwe,” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008.