“Ntchitoyi Ndi Yaikulu”
PA NTHAWI ina Mfumu Davide anaitana akalonga ake, nduna za panyumba ya mfumu komanso amuna amphamvu kumsonkhano wofunika kwambiri ku Yerusalemu. Oitanidwawo anasangalala atamva chilengezo chapadera. Yehova anasankha Solomo, mwana wa Davide, kuti amange nyumba yaikulu yoti anthu azilambiriramo Mulungu woona. Mulungu anauza Davide mapulani onse a nyumbayo ndipo Davideyo anafotokozera Solomo. Davide anati: “Ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa chinyumba chachikuluchi, si cha munthu ayi, koma ndi cha Yehova Mulungu.”—1 Mbiri 28:1, 2, 6, 11, 12; 29:1.
Kenako Davide anafunsa kuti: “Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5) Kodi inuyo mukanakhalapo mukanathandiza pa ntchitoyi? Aisiraeli anayesetsa mmene akanathera kuti athandize pa ntchitoyo. Iwo “anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 29:9.
Patapita zaka zambirimbiri, Yehova anakhazikitsa kachisi wamkulu kuposa amene Solomo anamanga. Kachisiyu amatchedwa kachisi wamkulu wauzimu ndipo ndi njira yothandiza anthu kuti azimulambira kudzera mu nsembe ya Yesu. (Aheb. 9:11, 12) Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuti agwirizanenso naye? Iye amachita zimenezi kudzera mu ntchito yolalikira. (Mat. 28:19, 20) Ntchitoyi ikuthandiza kuti chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri aziphunzitsidwa Baibulo, anthu masauzande ambiri azibatizidwa komanso mipingo mahandiredi ambiri izikhazikitsidwa.
Zonsezi zikuchititsa kuti mabuku ambiri azisindikizidwa komanso pazimangidwa Nyumba za Ufumu ndiponso Malo a Misonkhano ambiri. Kunena zoona ntchito yolalikira ndi yaikulu ndipo ikuthandiza anthu.—Mat. 24:14.
Chifukwa chokonda Yehova komanso anzawo, anthu a Mulungu masiku ano amayesetsanso kupereka zinthu zawo kuti zikhale “mphatso kwa Yehova.” Iwo amadziwanso kuti ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwachangu. Zimasangalatsa kwambiri ‘tikamalemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali’ komanso tikamaona zinthuzo zikugwiritsidwa ntchito bwino kuti zithandize pa ntchito yofunika kwambiriyi.—Miy. 3:9.