Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tipitirize Kulimbikitsana Tsiku ndi Tsiku

Tipitirize Kulimbikitsana Tsiku ndi Tsiku

“Ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.”​—MAC. 13:15.

NYIMBO: 121, 45

1, 2. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti kulimbitsa ena n’kofunika kwambiri.

MTSIKANA wina wazaka 18 dzina lake Cristina anati: “Makolo anga samandilimbikitsa ndipo nthawi zonse amangondinyoza.  [1] Nthawi zina amandilankhula mawu opweteka kwambiri. Amakonda kunena kuti ndine wachibwana, sindidzaphunzira zinthu komanso ndine wonenepa kwambiri. Izi zimapangitsa kuti ndizidziona kuti ndine wachabechabe moti nthawi zina ndimangolira ndipo sindifuna kulankhula nawo.” Izitu zikusonyeza kuti munthu amene salimbikitsidwa amakhala wosasangalala.

2 Zimene ananena mnyamata wina dzina lake Rubén zikusonyeza kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri. Iye anati: “Kwa zaka zambiri ndakhala ndikudziona kuti ndine wosafunika. Koma tsiku lina ndili mu utumiki, mkulu amene ndinayenda naye anazindikira kuti sindikusangalala. Nditayamba kumufotokozera mavuto anga komanso mmene ndinkamvera, anamvetsera mwachidwi. Kenako anandikumbutsa za zinthu zabwino zimene ndakwanitsa kuchita. Anandikumbutsanso mawu a Yesu oti munthu aliyense ndi wofunika kuposa mpheta zambiri. Ndimakumbukirabe lemba limeneli ndipo limandikhudza mtima kwambiri. Zimene mkuluyu ananena zinandilimbikitsa kwambiri.”—Mat. 10:31.

3. (a) Fotokozani zimene mtumwi Paulo ananena pa nkhani yolimbikitsa ena. (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?

3 M’pake kuti Baibulo limatsindika kufunika koti tizilimbikitsana nthawi zonse. Mtumwi Paulo analembera Akhristu achiheberi kuti: “Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro. M’malomwake, pitirizani kudandaulirana [kapena kuti kulimbikitsana] tsiku ndi tsiku, . . . kuopera kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chingaumitse mtima wa wina wa inu.” (Aheb. 3:12, 13) Tingathe kumvetsa kuti malangizo oti tizilimbikitsanawa ndi ofunikadi, tikaganizira mmene tinamvera munthu wina atatilimbikitsa. M’nkhaniyi tikambirana mafunso awa: N’chifukwa chiyani tingati kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri? Kodi chitsanzo cha Yehova, Yesu komanso Paulo chikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yolimbikitsa ena? Nanga kodi tingatani kuti tizilimbikitsadi ena?

TONSEFE TIMAFUNIKA KULIMBIKITSIDWA

4. Kodi ndani amene amafunika kulimbikitsidwa, nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri salimbikitsa ena?

4 Munthu aliyense amafunika kulimbikitsidwa. Mwana akamakula ndi pamenenso amafunika kulimbikitsidwa. Mphunzitsi wina dzina lake Timothy Evans anati: “Ana . . . amafunika kulimbikitsidwa ngati mmene zomera zimafunira madzi kuti zikule bwino. Mwana akalimbikitsidwa amadziona kuti ndi wofunika komanso amadziwa kuti wachita zabwino.” Koma tikukhala m’nthawi yovuta. Anthu ambiri ndi odzikonda, opanda chikondi komanso sakonda kulimbikitsa ena. (2 Tim. 3:1-5) Makolo ena sayamikira ana awo chifukwa choti makolo awo sankawalimbikitsa. Komanso ogwira ntchito ambiri sayamikiridwa choncho amadandaula kuti palibe amene amawalimbikitsa akakhala kuntchito.

5. Kodi timalimbikitsa bwanji munthu?

5 Nthawi zambiri tikamalimbikitsa munthu timamuyamikira chifukwa cha zinthu zabwino zimene wachita. Timathanso kumuuza za makhalidwe abwino amene ali nawo. Tikhozanso ‘kulankhula mawu olimbikitsa’ kwa anthu amene afooka kapena akhumudwa ndi zinazake. (1 Ates. 5:14) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kulimbikitsa” amatanthauza “kuitana munthu kuti akhale nawe pafupi n’cholinga choti akuthandize komanso kukutonthoza.” Nthawi zonse tiziyesetsa kupeza mpata wouza abale ndi alongo athu mawu olimbikitsa. (Werengani Mlaliki 4:9, 10.) Kodi timagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka n’kuthandiza ena kudziwa chifukwa chake timawakonda komanso kuwayamikira? Tingathe kuchita zimenezi ngati timaganizira kwambiri mwambi wakuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.”—Miy. 15:23.

6. N’chifukwa chiyani Satana amafuna kutikhumudwitsa? Perekani chitsanzo.

6 Satana amafuna kutikhumudwitsa n’cholinga choti tifooke pa zinthu zauzimu komanso pa zinthu zina. Lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Satana anachititsa kuti Yobu akumane ndi mavuto ambirimbiri n’cholinga choti afooke, koma Yobu sanafooke. (Yobu 2:3; 22:3; 27:5) Tingalimbane ndi zochita za Mdyerekezi tikamayesetsa kulimbikitsa anthu a m’banja lathu komanso a mumpingo wathu. Tikamachita zimenezi, tonse tingamaone kuti panyumba pathu komanso ku Nyumba ya Ufumu ndi malo osangalatsa komanso otetezeka.

ZITSANZO ZA M’BAIBULO ZIMENE TINGATENGERE

7, 8. (a) Tchulani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kuti Yehova amaona kuti kulimbikitsa ena n’kofunika. (b) Kodi makolo angatsanzire bwanji Yehova? (Onani chithunzi patsamba 4.)

7 Yehova. Wamasalimo anaimba kuti: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Sal. 34:18) Pamene Yeremiya anafooka komanso kuchita mantha, Yehova anamulimbikitsa. (Yer. 1:6-10) Komanso kodi mukuganiza kuti mneneri Danieli anamva bwanji pamene Mulungu anatumiza mngelo kukamulimbikitsa? Mngeloyo anatchula Danieli kuti “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 10:8, 11, 18, 19) Nanunso mungathe kulimbikitsa ofalitsa, apainiya komanso abale ndi alongo amene akufooka chifukwa cha uchikulire.

8 Paja Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kumwamba kwa zaka zambirimbiri. Komabe pamene Yesu anali padzikoli, Yehova sanaganize kuti Mwana wakeyu sankafunika kuyamikiridwa komanso kulimbikitsidwa. M’malomwake Yesu atangoyamba kumene utumiki wake komanso chakumapeto kwa utumikiwo, Yehova analankhula kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” (Mat. 3:17; 17:5) Apa Mulungu anayamikira Mwana wakeyu komanso anamutsimikizira kuti akuchita zabwino. Yesu ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva Atate wake akunena zimenezi kawiri konse. Komanso usiku woti Yesu afa mawa, Yehova anatumiza mngelo kuti akamulimbikitse chifukwa anali ndi nkhawa kwambiri. (Luka 22:43) Makolo, muzitsanzira Yehova polimbikitsa ana anu ndiponso muziwayamikira akachita zabwino. Komanso muziwathandiza kwambiri ngati akukumana ndi mayesero kusukulu.

9. Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi atumwi ake?

9 Yesu. Usiku umene Yesu anayambitsa mwambo wa Chikumbutso, anaona kuti atumwi ake anali ndi kamtima kodyada. Iye anadzichepetsa n’kusambitsa mapazi awo koma iwo ankakanganabe kuti wamkulu ndani. Komanso Petulo ankadzidalira kwambiri. (Luka 22:24, 33, 34) Komabe Yesu anayamikira atumwi ake okhulupirika chifukwa chokhalabe naye pa nthawi ya mayesero ake. Anawauzanso kuti adzachita zambiri kuposa zimene iye anachita komanso anawatsimikizira kuti Mulungu amawakonda. (Luka 22:28; Yoh. 14:12; 16:27) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndimatsanzira Yesu poyamikira ana anga ndiponso anthu ena pa zimene achita bwino kapena ndimangoganizira zolakwa zawo?’

10, 11. N’chiyani chikusonyeza kuti mtumwi Paulo ankaona kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri?

10 Mtumwi Paulo. M’makalata ake, Paulo analemba zinthu zabwino zokhudza Akhristu anzake. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti ena anayenda nawo kwa zaka zambiri ndipo ankadziwa zolakwa zawo. Mwachitsanzo, Paulo anati Timoteyo anali ‘mwana wake wokondedwa ndi wokhulupirika’ amene angasamaledi za ena moona mtima. (1 Akor. 4:17; Afil. 2:19, 20) Mtumwiyu anayamikiranso Tito m’kalata yake yopita kumpingo wa Korinto. Iye anati Tito anali ‘mnzake komanso wogwira naye ntchito pothandiza Akorintowo.’ (2 Akor. 8:23) Timoteyo ndi Tito ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri atamva zimene Paulo ananenazi.

11 Pa nthawi ina Paulo ndi Baranaba anaika moyo wawo pachiswe n’kupitanso kumadera kumene anazunzidwa. Mwachitsanzo, anapita ku Lusitara n’cholinga choti akalimbikitse ophunzira atsopano kuti akhalebe okhulupirika. Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti anatsutsidwa kwambiri ku Lusitara komweko. (Mac. 14:19-22) Ali ku Efeso, Paulo anakumana ndi gulu la anthu olusa. Koma lemba la Machitidwe 20:1, 2 limati: “Chipolowe . . . chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa ndi kutsanzikana nawo, ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya. Iye anayendayenda m’madera akumeneko ndi kulimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri, kenako anafika ku Girisi.” Izi zikusonyeza kuti Paulo ankaona kuti kulimbikitsa ena n’kofunika kwambiri.

TIZIYESETSA KULIMBIKITSANA

12. Kodi misonkhano yathu imathandiza bwanji kuti tizilimbikitsana?

12 Chifukwa china chimene Atate wathu wakumwamba anakonzera zoti tizisonkhana n’choti amafuna kuti tizilimbikitsana. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Mofanana ndi Akhristu oyambirira, nafenso timasonkhana kuti tiphunzire komanso tilimbikitsidwe. (1 Akor. 14:31) Cristina amene tamutchula kale uja anati: “Ndimakonda misonkhano chifukwa ndimalimbikitsidwa komanso abale ndi alongo amandisonyeza chikondi. Nthawi zina ndimapita ku Nyumba ya Ufumu ndili ndi nkhawa. Koma alongo amabwera pamene ndili, kundikumbatira n’kundiuza kuti ndikuoneka bwino. Amandiuzanso kuti amandikonda ndipo amaona kuti ndimachita bwino zinthu zambiri. Zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri ndipo nkhawa zija zimatha.” Zimakhalatu zosangalatsa kwambiri tonse tikamayesetsa ‘kulimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.

13. N’chifukwa chiyani nawonso anthu amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali amafunika kulimbikitsidwa?

13 Ngakhalenso anthu amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali amafunika kulimbikitsidwa. Taganizirani chitsanzo cha Yoswa. Iye anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. Koma Mulungu anauza Mose kuti amulimbikitse. Anati: “Uike Yoswa kukhala mtsogoleri ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa, chifukwa ndiye adzawolotsa anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.” (Deut. 3:27, 28) Yoswa anali atatsala pang’ono kutenga udindo waukulu wotsogolera Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Pa ntchito yakeyi anakumana ndi mavuto angapo ndipo pa nthawi ina gulu lake la nkhondo linagonjetsedwa. (Yos. 7:1-9) Ndiyetu m’pake kuti ankafunika kulimbikitsidwa. Choncho tiyeni nafenso tizilimbikitsa akulu komanso oyang’anira madera chifukwa amagwira ntchito yaikulu yosamalira nkhosa za Mulungu. (Werengani 1 Atesalonika 5:12, 13.) Woyang’anira dera wina anati: “Nthawi zina abale amatilembera kalata yothokoza kuti asangalala ndi mlungu wapadera. Timasunga makalata amenewa n’kumawawerenga tikakhumudwa ndi zinazake. Kunena zoona makalatawa amatilimbikitsa kwabasi.”

Ana amakula bwino tikamawalimbikitsa mwachikondi (Onani ndime 14)

14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti kuyamikira munthu komanso kumulimbikitsa kumathandiza kuti atsatire mosavuta malangizo?

14 Makolo achikhristu komanso akulu amaona kuti munthu akayamikiridwa komanso kulimbikitsidwa zimakhala zosavuta kuti atsatire malangizo a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Paulo atayamikira Akorinto chifukwa chotsatira malangizo ake, Akorintowo ayenera kuti anapitiriza kuchita zabwino. (2 Akor. 7:8-11) M’bale wina dzina lake Andreas ali ndi ana awiri ndipo anati: “Kulimbikitsa ana kumawathandiza kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso akule bwino. Kumawathandizanso kuti atsatire malangizo a m’Baibulo. Ngakhale kuti ana athu amadziwa kale zoyenera kuchita, kuwalimbikitsa kumathandiza kuti asavutike kuchita zoyenerazo.”

KODI TINGATANI KUTI TIZILIMBIKITSADI ENA?

15. Tchulani njira ina imene tingalimbikitsire ena.

15 Muziyamikira ena chifukwa cha khama limene amasonyeza komanso chifukwa cha makhalidwe awo abwino. (2 Mbiri 16:9; Yobu 1:8) Yehova ndi Yesu amayamikira kwambiri zimene tonsefe timachita pothandiza kuti zinthu zokhudza Ufumu ziziyenda bwino. Iwo amaona kuti zimene tachita kapena kupereka ndi zamtengo wapatali ngakhale zitakhala zochepa chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu. (Werengani Luka 21:1-4; 2 Akorinto 8:12.) Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena achikulire amachita khama kwambiri kuti azipezeka pa misonkhano komanso kupita mu utumiki nthawi zonse. Tiyenera kumayamikira komanso kulimbikitsa abale ndi alongo amenewa.

16. Mpata woyamikira ena ukapezeka, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuzengereza?

16 Mpata woyamikira ena ukapezeka, musalephere kuwayamikira. Tikaona kuti munthu wachita chinachake choyenera kumuyamikira, tisangokhala chete. Taganizirani zimene zinachitika Paulo ndi Baranaba ali ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Atsogoleri a sunagoge anawauza kuti: “Amuna inu, abale athu, ngati muli ndi mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, lankhulani.” Zitatero Paulo anakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri. (Mac. 13:13-16, 42-44) Choncho tikaona kuti tingathe kuuza munthu wina mawu olimbikitsa, tisamazengereze. Ndipotu tikakhala ndi chizolowezi cholimbikitsa ena, nafenso anthu azitilimbikitsa.—Luka 6:38.

17. Tikamayamikira munthu, tingatani kuti timulimbikitse kwambiri?

17 Muziyamikira kuchokera mumtima ndipo muzitchula chimene mukuyamikiracho. N’zoona kuti kuuza munthu mawu akuti, ‘mwachita bwino’ kungamulimbikitse. Koma zimene Yesu anauza Akhristu a mpingo wa Tiyatira zimasonyeza kuti munthu amalimbikitsidwa kwambiri ngati tatchula zenizeni zimene wachita bwinozo. (Werengani Chivumbulutso 2:18, 19.) Mwachitsanzo, makolo akamayamikira ana awo chifukwa choti akuchita bwino pa zinthu zokhudza kulambira, angatchule zimene anawo akuchita bwino. Komanso ngati tikulimbikitsa mayi amene akulera yekha ana, tingatchule zabwino zimene akuchita zomwe zimatichititsa chidwi ifeyo. Kuchita zimenezi kungalimbikitse kwambiri munthu amene tikulankhula nayeyo.

18, 19. Kodi tingathandize bwanji anthu amene akufunika kulimbikitsidwa?

18 Paja Yehova anauza Mose kuti alimbikitse Yoswa. Koma sikuti angachitenso kutiuza ifeyo zoti tinene kwa munthu amene akufunika kulimbikitsidwa. Komabe Yehova amasangalala akamva tikuuza Akhristu anzathu kapena anthu ena mawu olimbikitsa. (Miy. 19:17; Aheb. 12:12) Mwachitsanzo, tingauze m’bale amene wakamba nkhani kuti nkhani yake yatipatsa malangizo amene timafuna. Tingamuuzenso mmene nkhaniyo yatithandizira kumvetsa lemba linalake. Mlongo wina analemba kalata yothokoza mlendo amene anakamba nkhani pa msonkhano. Iye anati: “Ngakhale kuti tinalankhulana kwa nthawi yochepa, munazindikira vuto langa ndipo munandilimbikitsa kwambiri. Ndikuona kuti mawu okoma mtima amene munanena pokamba nkhani yanu komanso amene munandiuza, ndi mphatso yochokera kwa Yehova.”

19 Tikamayesetsa kutsatira malangizo a Paulo tingathe kupeza njira zosiyanasiyana zolimbikitsira ena. Iye anati: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.” (1 Ates. 5:11) Tonsefe tidzasangalatsa kwambiri Yehova tikapitiriza kulimbikitsana tsiku ndi tsiku.

^ [1] (ndime 1) Mayina ena tawasintha.