Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 45

Kodi Mzimu Woyera Umatithandiza Bwanji?

Kodi Mzimu Woyera Umatithandiza Bwanji?

“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—AFIL. 4:13.

NYIMBO NA. 104 Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Kodi n’chiyani chimatithandiza kupirira tsiku lililonse? Fotokozani. (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

MWINA ambirife tanenapo kuti, “Pandekha sindikanatha kupirira mavuto amene ndinakumana nawo.” N’kutheka kuti munanena mawu ngati amenewa mutakumana ndi mavuto monga matenda aakulu kapena imfa ya mnzanu. Mwina mumaona kuti munkatha kupirira tsiku lililonse chifukwa choti mzimu woyera wa Yehova unkakupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.”​—2 Akor. 4:7-9.

2 Timadaliranso mzimu woyera kuti uzitithandiza kupewa zinthu zoipa zam’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Kuwonjezera pamenepo, tiyenera kulimbana ndi “mizimu yoipa.” (Aef. 6:12) Munkhaniyi, tikambirana njira ziwiri zimene mzimu woyera umatithandizira pa mavuto amenewa. Kenako tikambirana zimene tingachite kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri.

MZIMU WOYERA UMATIPATSA MPHAMVU

3. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuti tipirire mavuto?

3 Mzimu wa Yehova umatipatsa mphamvu kuti tikwaniritse maudindo athu ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. Mtumwi Paulo anaona kuti kudalira “mphamvu ya Khristu” ndi kumene kunamuthandiza kuti azitumikirabe Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. (2 Akor. 12:9) Pa ulendo wake wachiwiri waumishonale, Paulo ankalalikira mwakhama komanso kugwira ntchito kuti azipeza zofunika pa moyo wake. Iye atafika ku Korinto ankakhala kunyumba ya Akula ndi Purisikila. Banja limeneli linkagwira ntchito yopanga matenti. Ndiye poti Paulo ankadziwa ntchitoyi, masiku ena ankagwira nawo. (Mac. 18:1-4) Mzimu woyera unapatsa Paulo mphamvu kuti azitha kugwira ntchito komanso kukwaniritsa utumiki wake.

4. Malinga ndi 2 Akorinto 12:7b-9, kodi Paulo ankalimbana ndi vuto lotani?

4 Werengani 2 Akorinto 12:7b-9. Kodi palembali, Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti ankavutika ndi “munga m’thupi”? Kunena zoona, minga ikabaya munthu n’kuthyokera m’thupi munthuyo amamva kupweteka kwambiri. Choncho Paulo ankatanthauza kuti anali ndi vuto linalake limene linkamusowetsa mtendere kwambiri. Pofotokoza za vutoli, iye anati linali ngati “mngelo wa Satana” amene ‘ankamumenya nthawi zonse.’ Satana kapena ziwanda ayenera kuti si amene anayambitsa mavuto a Paulo mwachindunji ngati kuti ankatenga minga n’kumamubaya. Koma mwina iwo ataona mungawo, kapena kuti vuto lakelo, ankafunitsitsa kuukanikizira mkati kuti uzimupweteka kwambiri. Ndiye kodi Paulo anatani?

5. Kodi Yehova anayankha bwanji mapemphero a Paulo?

5 Poyamba, Paulo ankafuna kuti Yehova achotse ‘mungawo.’ Iye ananena kuti: “Katatu konse ndinachonderera Ambuye [Yehova] kuti mungawu undichoke.” Koma mungawo sunachokebe. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sanayankhe mapemphero a Paulo? Ayi, anayankha. Kungoti sanachotse mungawo koma anamupatsa mphamvu kuti azipirira. Yehova ananena kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.” (2 Akor. 12:8, 9) Mothandizidwa ndi Mulungu, Paulo anakwanitsa kukhalabe ndi mtendere wamumtima komanso kukhala wosangalala.​—Afil. 4:4-7.

6. (a) Kodi Yehova angayankhe bwanji mapemphero athu? (b) Kodi malemba amene ali mundimeyi akukutsimikizirani za chiyani?

6 Kodi nanunso munachondererapo Yehova kuti akupulumutseni pa vuto linalake? Ngati vutolo silinathe kapena mwina linawonjezeka, kodi munaganiza kuti Yehova sakusangalala nanu? Ngati ndi choncho, kumbukirani chitsanzo cha Paulo. Yehova anayankha mapemphero ake, choncho sangalephere kuyankhanso anuwo. Mwina sangachotse vutolo koma akhoza kukupatsani mzimu woyera kuti mukhale ndi mphamvu zokuthandizani kulipirira. (Sal. 61:3, 4) N’zoona kuti mukhoza ‘kugwetsedwa pansi,’ koma Yehova sangakusiyeni.​—2 Akor. 4:8, 9; Afil. 4:13.

UMATITHANDIZA KUTI TIZITUMIKIRABE YEHOVA

7-8. (a) Kodi mzimu woyera umafanana bwanji ndi mphepo? (b) Kodi Petulo anafotokoza bwanji mmene mzimu woyera umagwirira ntchito?

7 Kodi mzimu woyera umatithandiza m’njira ina iti? Mphepo yapanyanja imene ikulowera kumene ngalawa ikupita imathandiza ngalawayo kuti ikafike bwinobwino kumene ikupitako. Mofanana ndi zimenezi, mzimu woyera ungatithandize kuti tipirire mavuto athu n’kumatumikirabe Yehova mpaka tidzalowe m’dziko latsopano.

8 Mtumwi Petulo ankadziwa kwambiri zapanyanja chifukwa anali msodzi. Choncho n’zosadabwitsa kuti anayerekezera mmene mzimu woyera umagwirira ntchito ndi mphepo yapanyanja. Iye analemba kuti: “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “motsogoleredwa” amatanthauza ‘kutengedwa’ kapena ‘kukankhiridwa kutsogolo.’​—2 Pet. 1:21.

9. Kodi Petulo ankanena za chiyani pamene anagwiritsa ntchito mawu otanthauza ‘kukankhiridwa kutsogolo’?

9 Kodi Petulo ankanena za chiyani pamene anagwiritsa ntchito mawu otanthauza ‘kukankhiridwa kutsogolo’? Luka, yemwe analemba buku la Machitidwe, anagwiritsanso ntchito mawu achigiriki omwewa pofotokoza za ngalawa imene ‘inatengedwa’ ndi mphepo. (Mac. 27:15) Katswiri wina wa mawu a m’Baibulo ananena kuti Petulo anagwiritsa ntchito mawu onena za maulendo apanyanja pofotokoza mmene mzimu woyera unathandizira anthu olemba Baibulo. Apa tingati Petulo ankanena kuti mofanana ndi mmene mphepo imakankhira nsalu za ngalawa kuti ngalawayo ikafike kumene ikupita, mzimu woyera unathandiza olemba Baibulo kuti agwire bwino ntchito yawo. Katswiri uja anati: “Olemba Baibulowo anali ngati ngalawa zimene nsalu zake zothandiza poyenda zakwezedwa.” Yehova anathandiza olembawo powapatsa mzimu wake woyera umene unali ngati mphepo. Ndiyeno olemba Baibulowo anachita mbali yawo polola kutsogoleredwa ndi mzimuwo.

CHOYAMBA: Tizikonda kuchita zinthu zokhudza kulambira

CHACHIWIRI: Tizichita zinthuzo ndi mtima wathu wonse (Onani ndime 11) *

10-11. Kodi ndi zinthu ziwiri ziti zimene tingachite kuti mzimu woyera uzitithandiza? Perekani chitsanzo.

10 N’zoona kuti masiku ano Yehova sagwiritsa ntchito mzimu woyera pothandiza anthu kuti alembe mabuku a m’Baibulo. Komabe Mulungu amagwiritsabe ntchito mzimu woyera pothandiza anthu ake. Choncho Yehova akuchitabe mbali yake. Koma kodi tingatani kuti mzimu wa Mulungu uzitithandiza? Ifenso tiyenera kumachita mbali yathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

11 Taganizirani chitsanzo ichi. Kuti mphepo izithandiza woyendetsa ngalawa, iye ayenera kuchita zinthu ziwiri. Choyamba, ayenera kuonetsetsa kuti ngalawa yake ili pamalo amene mphepo ikudutsa. Zili choncho chifukwa ngalawayo singayende ngati yangoima padoko pamene mphepo sikudutsa. Chachiwiri, akufunika kukweza nsalu za ngalawayo n’kuzitambasula bwinobwino. Zili choncho chifukwa ngakhale kuti kuli mphepo, ngalawayo singayende ngati nsalu zake sizikukankhidwa ndi mphepoyo. Ifenso tingapitirize kutumikira Yehova ngati tikuthandizidwa ndi mzimu woyera. Koma palinso zinthu ziwiri zimene timafunika kuchita kuti tizithandizidwa ndi mzimuwo. Choyamba, timafunika kuchita zinthu zimene Mulungu amatiuza kuti tizichita. Tikatero timakhala ngati tili pamalo amene mzimu wake umapezeka. Chachiwiri, tiyenera kuchita zinthuzo ndi mtima wonse kuti tikhale ngati takweza nsalu zathu n’kuzitambasula bwinobwino. (Sal. 119:2) Tikamachita zinthu ziwirizi mzimu woyera udzakhala ngati ukutikankhira kutsogolo pamene tikukumana ndi mavuto kuti tizitumikirabe Yehova mpaka kulowa m’dziko latsopano.

12. Kodi tsopano tikambirana chiyani?

12 Kufika pano, takambirana njira ziwiri zimene mzimu woyera umatithandizira. Umatipatsa mphamvu komanso kutithandiza kukhalabe okhulupirika tikamakumana ndi mavuto. Mzimu woyera umatithandizanso kupitiriza kutumikira Yehova kuti tidzapeze moyo wosatha. Tsopano tikambirana zinthu 4 zimene tiyenera kuchita kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri.

KODI TINGATANI KUTI MZIMU WOYERA UZITITHANDIZA KWAMBIRI?

13. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 3:16, 17, kodi Malemba angatithandize bwanji, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?

13 Choyamba, tiziphunzira Mawu a Mulungu. (Werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.) Mawu achigiriki omwe anawamasulira kuti “anauziridwa ndi Mulungu” amatanthauza kuti “Mulungu anapumira mpweya.” Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake kuti apumire, kapena kuti aike, mawu ake m’maganizo a anthu olemba Baibulo. Tikamawerenga Baibulo komanso kusinkhasinkha zimene tikuwerengazo, malangizo a Mulungu amalowa m’maganizo ndiponso mumtima mwathu. Kenako malangizowo amatithandiza kuti tisinthe n’kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. (Aheb. 4:12) Koma kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri, tiyenera kumapeza nthawi yophunzira Baibulo komanso kuganizira mozama zimene tikuphunzirazo. Tikatero Mawu a Mulungu azititsogolera pa zonse zimene timalankhula komanso kuchita.

14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti misonkhano yathu ili ngati malo amene “mphepo ikudutsa”? (b) Kodi tingatani kuti pamisonkhano tizikhala ngati ngalawa imene nsalu zake zakwezedwa komanso kutambasulidwa?

14 Chachiwiri, tizilambira Mulungu limodzi. (Sal. 22:22) Misonkhano yathu yachikhristu ili ngati malo amene “mphepo ikudutsa” chifukwa kumakhala mzimu wa Yehova. (Chiv. 2:29) Tikutero chifukwa cha zimene zimachitika pamisonkhanoyo. Timapempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera, timaimba nyimbo za Ufumu zokhala ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso timamvetsera malangizo a m’Baibulo omwe amaperekedwa ndi abale amene anaikidwa ndi mzimu woyera. Mzimu woyera umathandizanso alongo kukonzekera komanso kuchita mbali zimene amapatsidwa pamisonkhano. Koma kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri, tizikonzekera misonkhano komanso kuyesetsa kuyankha. Tikatero tingakhale ngati ngalawa imene nsalu zake zakwezedwa komanso kutambasulidwa.

15. Kodi tingatani kuti mzimu woyera uzitithandiza mu utumiki?

15 Chachitatu, tizigwira nawo ntchito yolalikira. Tikamagwiritsa ntchito Baibulo polalikira ndi kuphunzitsa anthu, timakhala kuti tikulola mzimu woyera kuti uzitithandiza. (Aroma 15:18, 19) Koma kuti mzimu wa Mulungu uzitithandiza kwambiri, tiyenera kumalalikira mwakhama komanso tiziyesetsa kugwiritsa ntchito Baibulo. Kuti zizikuyenderani bwino mu utumiki, mungagwiritsenso ntchito zitsanzo zopezeka mu Ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

16. Tchulani njira yaikulu yopezera mzimu woyera.

16 Cha nambala 4, muzipemphera kwa Yehova. (Mat. 7:7-11; Luka 11:13) Njira yaikulu yopezera mzimu woyera ndi kupempha Yehova kuti atipatse. Palibe chimene chingalepheretse kuti mapemphero athu afike kwa Yehova kapena kuti iyeyo atipatse mzimu wake. Ngakhale Satana kapena kukhala m’ndende sizingalepheretse zinthu zimenezi. (Yak. 1:17) Koma kodi tiyenera kumapemphera bwanji kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambirane fanizo lokhudza pemphero lopezeka m’buku la Luka. *

TIZIPEMPHERA MOSALEKEZA

17. Kodi fanizo la Yesu pa Luka 11:5-9, 13, likutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya pemphero?

17 Werengani Luka 11:5-9, 13. Fanizo la Yesu limasonyeza mmene tingapempherere kuti tilandire mzimu woyera. Mufanizoli, munthu analandira zimene ankafuna chifukwa cha “kukakamira kwake.” Iye sanaope kukapempha thandizo kwa mnzake ngakhale kuti unali usiku. (Onani lifalensi ya pa Luka 11:8 mu Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya July 2018.) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kugwirizana pakati pa fanizoli ndi pemphero? Iye anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani.” Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Kuti tilandire mzimu woyera, tiyenera kupempha Mulungu mosalekeza.

18. Malinga ndi fanizo la Yesu, n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatipatsa mzimu woyera?

18 Fanizoli likusonyezanso chifukwa chimene Yehova angatipatsire mzimu woyera. Munthu wamufanizoli ankafuna kusamalira bwino mlendo wake yemwe anafika usiku. Iye ankafuna kumupatsa chakudya koma analibe kalikonse. Ndiye Yesu ananena kuti mnzakeyo anapereka chakudyacho chifukwa choti munthuyo anakakamira kupempha. Kodi mfundo ya Yesu inali yotani? Ngati munthu yemwe si wangwiro anathandiza mnzake chifukwa choti anakakamira, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wokoma mtima? Iye adzaperekanso mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha mosalekeza. Choncho tikamachonderera Yehova kuti atipatse mzimu woyera tisamakayikire kuti adzatipatsa.​—Sal. 10:17; 66:19.

19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zoti tikhoza kutumikirabe Yehova mokhulupirika?

19 Tisamakayikire kuti tikhoza kutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale kuti Satana akuyesetsa kutisokoneza. Tikutero chifukwa chakuti mzimu woyera umatithandiza m’njira ziwiri. Choyamba, umatipatsa mphamvu kuti tizipirira mavuto. Chachiwiri, umakhala ngati ukutikankhira kutsogolo kuti tizitumikirabe Yehova mpaka kukalowa m’dziko latsopano. Choncho tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri.

NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa

^ ndime 5 Nkhaniyi ikusonyeza mmene mzimu woyera wa Mulungu ungatithandizire kuti tizipirira. Ifotokozanso zimene tingachite kuti mzimu woyera uzitithandiza kwambiri.

^ ndime 16 Pa olemba mabuku a Uthenga Wabwino onse, Luka ndi amene anasonyeza kwambiri kuti Yesu ankakonda kupemphera.​—Luka 3:21; 5:16; 6:12; 9:18, 28, 29; 18:1; 22:41, 44.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: CHOYAMBA: M’bale ndi mlongo afika pa Nyumba ya Ufumu. Tingati ali pamalo amene mzimu wa Yehova umapezeka chifukwa choti asonkhana ndi Akhristu anzawo. CHACHIWIRI: Iwo akonzekera misonkhano n’cholinga choti ayankhe. Timafunika kutsatira mfundo ziwiri ngati zimenezi pochita zinthu zina zimene zatchulidwa munkhaniyi: kuphunzira Mawu a Mulungu, kugwira ntchito yolalikira ndiponso kupemphera kwa Yehova.