Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onésime ndi Géraldine

Anthu Amene Abwerera Kwawo Amapeza Madalitso Ambiri

Anthu Amene Abwerera Kwawo Amapeza Madalitso Ambiri

ABALE ndi alongo ambiri amene m’mbuyomu anapita kumayiko ena kukafuna chuma anabwerera kwawo. Kukonda Yehova komanso anthu ena n’kumene kunawachititsa kuti asamukire kumadera komwe kukufunika ofalitsa ambiri. (Mat. 22:37-39) Kodi abale ndi alongo amenewa anadzimana zinthu ziti, nanga anapeza madalitso otani? Kuti timve zambiri, tiyeni tikambirane zimene zikuchitika ku Africa, m’dziko la Cameroon.

“NDILI PAMALO ABWINO PAMENE ‘NDINGAPHE NSOMBA ZAMBIRI’”

Mu 1998 m’bale wina dzina lake Onésime, anachoka kwawo ku Cameroon kupita kudziko lina. Iye anakhala kumeneko kwa zaka 14. Tsiku lina ali kumisonkhano ya mpingo, anamva chitsanzo chokhudza ntchito yolalikira. Wokamba nkhaniyo anati, “Ngati anthu awiri akuwedza nsomba pamalo osiyana ndipo wina akupha nsomba zambiri kuposa mnzake, kodi amene akupha nsomba zochepayo sangapite kumene kuli mnzakeyo?”

Chitsanzo chimenechi chinachititsa Onésime kuganiza zobwerera kwawo ku Cameroon, kumene ntchito yosodza anthu inali yaikulu kwambiri. Komabe iye anali ndi nkhawa. Ankadera nkhawa kuti kodi akazoloweranso moyo wa kwawo atakhala kudziko lina zaka zonsezi? Kuti adziwe ngati angakazolowere, Onésime anapita ku Cameroon n’kukakhalako kwa miyezi 6. Kenako mu 2012, anasamukiratu.

Onésime anati: “Ndinkafunikira kuzolowera nyengo yotentha komanso moyo wakuno. Ku Nyumba ya Ufumu ndinkafunika kuzoloweranso kukhala pamabenchi.” Akumwetulira iye anati, “Koma ndikamamvetsera mwachidwi misonkhano, ndinkaiwala za mipando yawofuwofu imene inali m’Nyumba za Ufumu zina.”

Mu 2013, Onésime anakwatirana ndi Géraldine, amene anabwerera ku Cameroon atakhala ku France kwa zaka 9. Kodi banjali linapeza madalitso otani chifukwa choika kutumikira Yehova pamalo oyamba? Onésime anati: “Tinalowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu komanso tikutumikira pa Beteli. Chaka chathachi, anthu 20 mumpingo wathu anabatizidwa. Ndikuona kuti panopa, ndili pamalo abwino pamene ‘ndingaphe nsomba zambiri.’” (Maliko 1:17, 18) Géraldine anawonjezera kuti: “Ndapeza madalitso ambiri kuposa mmene ndinkaganizira.”

TINASANGALALA KUTHANDIZA ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA

Judith ndi Sam-Castel

Judith anasamukira ku United States koma ankafunitsitsa kuchita zambiri potumikira Yehova. Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zonse ndikapita kukaona achibale ku Cameroon, ndikamabwerera ndinkalira chifukwa ndinkasiya anthu amene ndayamba kuphunzira nawo Baibulo.” Koma Judith ankaopa kubwerera ku Cameroon. Iye anali pa ntchito ya malipiro abwino imene inkamuthandiza kupeza ndalama zolipirira bambo ake kuchipatala. Komabe Judith anadalira Yehova ndipo anabwerera kwawo. Iye anavomereza kuti ankasowa zinthu zina zimene ankasangalala nazo pa nthawi imene anali kunja. Anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kusintha ndipo woyang’anira dera ndi mkazi wake anamulimbikitsa kwambiri.

Pokumbukira zimene zinachitika atabwerera ku Cameroon, Judith anati, “M’zaka zitatu zokha ndinasangalala kuthandiza anthu 4 kuti abatizidwe.” Judith anayamba kutumikira monga mpainiya wapadera. Panopa akutumikira limodzi ndi mwamuna wake Sam-Castel, yemwe ndi woyang’anira dera. Koma kodi zinatha bwanji ndi bambo ake a Judith aja? Iye ndi achibale ake anapeza chipatala kunja chimene chinavomera kuti chilipira opaleshoni ya bambo akewo. N’zosangalatsa kwambiri kuti opaleshoniyo inayenda bwino.

TINAONA YEHOVA AKUTITHANDIZA

Caroline ndi Victor

M’bale wina dzina lake Victor, anasamukira ku Canada. Atawerenga nkhani ina mu Nsanja ya Olonda, yokhudza maphunziro apamwamba, anaganizira za maphunziro ake. Choncho anasiya maphunziro a kuyunivesite ndipo anayamba maphunziro a ntchito yamanja omwe anali a nthawi yochepa. Iye anati: “Zimenezi zinandithandiza kuti ndipeze ntchito mwamsanga ndiponso kuchita upainiya womwe ndinkaulakalaka kwa nthawi yaitali.” Kenako Victor anakwatirana ndi Caroline ndipo anapita kukacheza ku Cameroon. Ali kumeneko anapita kukaona malo ku ofesi ya nthambi ndipo abale ena anawalimbikitsa kuti aganizire zochita utumiki ku Cameroon. Victor ananena kuti: “Panalibe chifukwa choti tikanire komanso popeza kuti tinali kale ndi moyo wosalira zambiri, tinaganiza zoyamba kutumikira ku Cameroon.” Ngakhale kuti Caroline anali ndi mavuto ena okhudza thanzi lake, iwo anaganiza zosamuka.

Victor ndi Caroline anayamba kuchita upainiya wokhazikika ku Cameroon kuti athandize anthu ambiri amene anali ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Kwa kanthawi, sankafunika kugwira ntchito chifukwa anasungira ndalama zokwanira. Koma kenako anapitanso ku Canada komwe anakagwira ntchito kwa miyezi ingapo. Zimenezi zinawathandiza kuti apeze ndalama zobwererera ku Cameroon kukapitiriza kuchita upainiya. Ndiye kodi anapeza madalitso otani? Iwo analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu, anatumikira ngati apainiya apadera ndipo panopa akuchita utumiki wa zomangamanga. Victor anati: “Chifukwa choti tinalola kusiya moyo wawofuwofu n’kuyamba utumiki wa nthawi zonse, taona Yehova akutithandiza.”

TIMASANGALALA KUTHANDIZA ANTHU KUTI ADZIPEREKE KWA YEHOVA

Stéphanie ndi Alain

M’chaka cha 2002, Alain, yemwe ankaphunzira pa yunivesite ina ku Germany, anawerenga kapepala kakuti Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji? Zimene anawerenga m’kapepalako zinamuthandiza kuti asinthe zolinga zomwe anali nazo. Mu 2006, analowa Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndipo anamutumiza kwawo ku Cameroon.

Atafika ku Cameroon, Alain anapeza ntchito yomwe ankagwira maola ochepa. Kenako anapeza ntchito ya malipiro ambiri koma ankaopa kuti ikhoza kumulepheretsa kumachita zambiri mu utumiki. Choncho atauzidwa kuti azichita utumiki wa upainiya wapadera, anavomera nthawi yomweyo. Abwana ake anamulonjeza kuti amuwonjezera malipiro koma Alain anakana ndipo anasankha kuchita upainiya wapadera. Kenako, Alain anakwatirana ndi Stéphanie, yemwe anakhalanso zaka zambiri ku France. Kodi Stéphanie atabwerera ku Cameroon anakumana ndi mavuto otani?

Stéphanie anati: “Ndinayamba kukumana ndi mavuto ena ang’onoang’ono okhudza thanzi langa koma ndinapeza thandizo ndipo mavutowo anatha.” Banjali linapeza madalitso chifukwa cha kupirira kwawo. Alain anafotokoza kuti: “Titapita kukalalikira kumudzi wina wakutali wotchedwa Katé, tinapeza anthu ambiri amene ankafuna kuphunzira Baibulo. Kenako tinayamba kuphunzira ndi anthuwa pafoni. Awiri mwa anthuwa anabatizidwa ndipo kuderali kunakhala kagulu ka ofalitsa.” Stéphanie anawonjezera kuti: “Palibe chimene chimasangalatsa kwambiri kuposa kuthandiza anthu kuti adzipereke kwa Yehova. Kutumikira kuno kwatipatsa mwayi woti tizisangalala ndi madalitso amenewa nthawi ndi nthawi.” Panopa Alain ndi Stéphanie akutumikira mudera.

“TINACHITA ZIMENE TINKAYENERA KUCHITA”

Léonce ndi Gisèle

Gisèle anabatizidwa ali kusukulu ya zachipatala kuti Italy. Iye anachita chidwi ndi apainiya ena amene anamuphunzitsa Baibulo, omwe ankakhala moyo wosalira zambiri moti nayenso ankafuna kuchita zambiri mu utumiki. Choncho Gisèle anayamba upainiya okhazikika kwinaku akumaliza maphunziro ake.

Gisèle ankafuna kubwerera kwawo ku Cameroon kuti akachite zambiri potumikira Yehova koma anali ndi nkhawa. Iye ananena kuti, “Ndinafunika kutaya mwayi umene boma linandipatsa wokhala m’dziko la Italy. Ndinafunikanso kusiyana ndi anzanga komanso achibale omwe ankakhala m’dzikolo.” Ngakhale zinali choncho, m’mwezi wa May 2016, Gisèle anabwerera kwawo ku Cameroon. Patapita nthawi, iye anakwatirana ndi Léonce. Ndipo ofesi ya nthambi ya ku Cameroon inawapempha kuti asamukire kutauni ya Ayos, kumene kunkafunika ofalitsa ambiri.

Kodi moyo unali bwanji ku Ayos? Gisèle anafotokoza kuti: “Kawirikawiri magetsi ankazima kwa milungu ingapo ndipo sitinkatha kutchaja mafoni athu, moti nthawi zambiri ankangokhala ozima. Ndinaphunzira kuphika pankhuni ndipo usiku tinkatenga mawilibala ndi matochi kupita kukatunga madzi kuchitsime chifukwa pa nthawiyi kunkakhala anthu ochepa.” Kodi n’chiyani chinathandiza Gisèle ndi mwamuna wake kuti apirire? Gisèle anati: “Tinatha kupirira chifukwa choti mzimu wa Yehova unkatithandiza, ine ndi mwamuna wanga tinkathandizana ndiponso achibale ndi anzathu ankatilimbikitsa komanso kutithandiza potipatsa ndalama.”

Kodi Gisèle amasangalala kuti anabwerera kwawo? Iye ananena kuti, “Inde ndimasangalala kwambiri. Poyamba tinkakumana ndi mavuto ena komanso zokhumudwitsa. Koma titangothana ndi zimenezo, ine ndi mwamuna wanga timaona kuti tinachita zimene tinkayenera kuchita. Timadalira kwambiri Yehova ndipo timaona kuti tili naye pa ubwenzi.” Léonce ndi Gisèle analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ndipo pano akutumikira ngati apainiya apadera akanthawi.

Mofanana ndi asodzi amene amafunika kulimba mtima kuti aphe nsomba zambiri, anthu amene amabwerera kwawo amakhala ofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti athandize anthu a mitima yabwino amene akufuna kumva uthenga wa Ufumu. Mosakayikira Yehova sadzaiwala khama ndi chikondi zimene ofalitsawa anasonyeza pa dzina lake. (Neh. 5:19; Aheb. 6:10) Ngati mukukhala m’dziko lina ndipo m’dziko lanu mukufunika ofalitsa Ufumu ambiri, kodi mungabwerere kwanu? Ngati mungachite zimenezi, Yehova adzakudalitsani kwambiri.—Miy. 10:22.