Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yophunzira 48

Maso Ako Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo

Maso Ako Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo

“Maso ako aziyang’ana patsogolo. Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.”MIY. 4:25.

NYIMBO NA. 77 Kuwala M’dziko Lamdima

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi tingatsatire bwanji malangizo opezeka pa Miyambo 4:25? Perekani chitsanzo.

TAGANIZIRANI zitsanzo zitatu izi. Mlongo wachikulire akukumbukira zinthu zimene ankasangalala nazo m’mbuyomo. Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto iye akuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova. (1 Akor. 15:58) Tsiku lililonse amaganizira ali m’dziko latsopano limodzi ndi anzake komanso achibale ake. Mlongo wina akukumbukira zinthu zokhumudwitsa zimene munthu wina mumpingo anamuchitira, koma anasankha kuti amukhululukire. (Akol. 3:13) M’bale wina akukumbukira zinthu zimene analakwitsa m’mbuyomo, koma panopa akuyetsetsa kuti azichita zonse zomwe angathe kuti azitumikira Yehova mokhulupirika.—Sal. 51:10.

2 Kodi Akhristu atatuwa akufanana bwanji? Onse akukumbukira zinthu zimene zinawachitikira m’mbuyomo komabe si kuti nthawi zonse amangoganizira zinthu zimenezo. M’malomwake iwo ‘akuyang’ana patsogolo.’—Werengani Miyambo 4:25.

3. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti maso anthu “aziyang’ana patsogolo?”

3 N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti maso anthu “aziyang’ana patsogolo?” Munthu amene akuyenda n’kumayang’ana kumbuyo, akhoza kupatuka panjira mosavuta. Zimenezi n’zofanana ndi zimene zingachitike pamene tikutumikira Yehova. Sitingathe kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse ngati nthawi zonse timaganizira zinthu zimene zinachitika kapena zinthu zimene tinachita m’mbuyo.—Luka 9:62.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene zingachititse kuti tiziganizira kwambiri zomwe zinachitika m’mbuyomo. Zinthu zake ndi (1) kulakalaka zakale, (2) kusunga chakukhosi ndi (3) kudziimba kwambiri mlandu. Pa chilichonse cha zinthuzi tiona mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire kuti tisamangoganizira za “zinthu zakumbuyo,” koma m’malomwake tiziyesetsa kuganizira “zakutsogolo.”—Afil. 3:13.

KULAKALAKA ZINTHU ZAKALE

N’chiyani chimene chingatilepheretse kuyang’ana pa zinthu zakutsogolo? (Onani ndime 5, 9, 13) *

5. Kodi lemba la Mlaliki 7:10, limatiuza kuti tiyenera kupewa chiyani?

5 Werengani Mlaliki 7:10. Vesili silikunena kuti n’kulakwa kudzifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino?” Kukumbukira zinthu zabwino ndi mphatso yochokera kwa Yehova. M’malomwake vesili likuti: “Usanene kuti: ‘N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’” Tinganene kuti vuto lili pa kuyerekezera mmene moyo wathu ulili panopa ndi mmene unalili m’mbuyomo, n’kumaona ngati panopa palibe chilichonse chimene chikutiyendera bwino. Baibulo lina linamasulira vesili kuti: “Usamafunse kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?’ Pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.”

Kodi Aisiraeli analakwitsa zinthu ziti atachoka ku Iguputo? (Onani ndime 6)

6. N’chifukwa chiyani si nzeru kumangoganiza kuti kale zinthu zinali bwino? Perekani chitsanzo.

6 N’chifukwa chiyani si nzeru kumangoganiza kuti kale zinthu zinali bwino? Kulakalaka zinthu zakale kungatichititse kuti tizingokumbukira zinthu zabwino zokhazokha zimene zinachitika pa moyo wathu. Kungatichititsenso kuti tiiwale mavuto amene tinkakumana nawo. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira Aisiraeli. Atangochoka ku Iguputo, mwamsanga anaiwala mavuto amene ankakumana nawo ali m’dzikoli. M’malomwake ankangoganizira za chakudya chabwino chimene ankadya. Iwo anati: “Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinali kudya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!” (Num. 11:5) Koma kodi n’zoona kuti zakudyazi zinali zaulere? Ayi si zinali zaulere chifukwa pa nthawi imene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo ankaponderezedwa kwambiri. (Eks. 1:13, 14; 3:6-9) Koma pambuyo pake iwo anaiwala mavuto onse amene ankakumana nawo n’kuyamba kulakalaka zinthu zakale. Iwo anasankha kumangoganizira zimene ankasangalala nazo m’mbuyomo, m’malo moganizira zinthu zabwino zimene Yehova anali atawachitira. Yehova sanasangalale ndi zimenezi.—Num. 11:10.

7. Kodi n’chiyani chimene chinathandiza mlongo wina kuti asamalakelake zinthu zakale?

7 Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kupewa kulakalaka zinthu zakale? Taganizirani za mlongo wina yemwe anayamba kutumikira ku Beteli ya ku Brooklyn mu 1945. Patadutsa zaka anakwatirana ndi m’bale wina ndipo anatumikira limodzi pa Beteli kwa zaka zambiri. Komabe m’chaka cha 1976 mwamuna wake anayamba kudwala. Mlongoyu ananena kuti mwamuna wake atazindikira kuti watsala pang’ono kumwalira, anamupatsa malangizo omwe anamuthandiza kuti apirire umasiye wake. Iye anamuuza kuti: “Banja lathu linali losangalatsa. Anthu ambiri sakhala ndi mabanja otere.” Anamulimbikitsanso kuti: “Usamangoganizira zam’mbuyo ngakhale kuti sungalephere kuzikumbukira. Pakapita nthawi udzaziiwala. Osamaipidwa nazo ndiponso osadzimvera chisoni. Uzingosangalala kuti unapeza chimwemwe ndiponso madalitso onsewa. Kukumbukira zam’mbuyo ndi mphatso yathu yochokera kwa Mulungu.” Kodi simukuvomereza kuti amenewa anali malangizo abwino?

8. Kodi mlongo wina anapeza madalitso otani chifukwa chotsatira malangizo a mwamuna wake?

8 Mlongo wathuyu anatsatira malangizo amene mwamuna wake anamupatsa. Iye anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira ali ndi zaka 92. Zaka zingapo asanamwalire iye anati: “Kunena zoona, ndikaganizira zaka zopitirira 63 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova kwa nthawi zonse, ndimaona kuti moyo wanga wakhala wosangalatsa kwambiri.” N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Chimene chimapangitsa moyo kukhala wosangalatsadi ndi ubale wathu wachikondi ndiponso chiyembekezo chodzakhala ndi abale komanso alongo athu m’dziko lapansi la paradaiso, n’kumatumikira kosatha Mlengi wathu wamkulu, yemwe ali Mulungu woona yekha, Yehova.” * Tingaphunziretu zambiri kuchokera kwa mlongoyu yemwe ankaganizira kwambiri zimene Yehova walonjeza.

KUSUNGA CHAKUKHOSI

9. Mogwirizana ndi Levitiko 19:18, kodi ndi pa nthawi iti pamene zimakhala zovuta kukhululuka munthu wina akatilakwira?

9 Werengani Levitiko 19:18. Nthawi zambiri zimativuta kukhululuka ngati amene watilakwira ndi Mkhristu mnzathu, mnzathu wapamtima komanso wachibale wathu. Mwachitsanzo mlongo wina ananamiziridwa ndi mlongo mnzake kuti wamubera ndalama. Patapita nthawi mlongo amene ananamizira mnzake uja anazindikira kuti walakwitsa ndipo anapepesa. Koma mnzakeyo anakhumudwa kwambiri ndipo ankangoganizirabe zimene zinachitikazo. Kodi nanunso munayamba mwamvapo chonchi? Ngakhale zoterezi sizinatichitikirepo koma n’kutheka kuti ambirife munthu wina atatilakwira tinkaona kuti sitingathe kumukhululukira.

10. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize ngati tikulephera kukhululuka?

10 Kodi n’chiyani chimene chingatithandize ngati tikulephera kukhululuka? Tiyenera kukumbukira kuti Yehova amaona zinthu zonse. Iye amaona zinthu zonse zimene zikutichitikira kuphatikizapo zinthu zopanda chilungamo zimene ena angatichitire. (Aheb. 4:13) Zimamupweteka tikamavutika. (Yes. 63:9) Ndipo akulonjeza kuti adzathetsa mavuto onse omwe tikukumana nawo chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene ena atichitira.—Chiv. 21:3, 4.

11. Kodi timapindula bwanji tikamakhululukira ena?

11 Tizikumbukiranso kuti tikamakhululukira ena timamva bwino. Zimenezi ndi zimene mlongo amene ananamiziridwa kuti waba ndalama uja anazindikira. Patapita nthawi iye anakhululukira mnzake uja komanso anasiya kumukwiyira. Anazindikira kuti tikamakhululukira ena Yehovanso amatikhululukira machimo athu. (Mat. 6:14) Mlongoyu ankadziwa kuti zimene mnzake uja anamuchitira zinali zolakwika, koma anasankha kumukhululukira. Zotsatira zake mlongoyu anakhala wosangalala ndipo anaika maganizo ake onse potumikira Yehova.

KUDZIIMBA KWAMBIRI MLANDU

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa lemba la 1 Yohane 3:19, 20?

12 Werengani 1 Yohane 3:19, 20. Nthawi zina tonsefe timadziimba mlandu. Mwachitsanzo, ena amadziimba mlandu chifukwa cha zinthu zimene ankachita asanaphunzire choonadi. Enanso amadziimba mlandu chifukwa cha zolakwa zimene anachita atabatizidwa. Ndipotu si zachilendo kumva choncho. (Aroma 3:23) N’zoona kuti timafuna kuchita zabwino, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Ngakhale kuti kudziimba mlandu sikosangalatsa, koma kumatithandiza m’njira zina. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa kudziimba mlandu n’kumene kungatithandize kuti tisinthe n’kutsimikiza mtima kuti tisadzabwerezenso zimene tinalakwitsazo.—Aheb. 12:12, 13.

13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudziimba kwambiri mlandu?

13 Komabe n’zotheka kumadziimba kwambiri mlandu. Zimenezi zikutanthauza kupitirizabe kudziimba mlandu ngakhale zitakhala kuti munthuyo analapa ndiponso Yehova anamukhululukira. Kudziimba mlandu kotereku kungakhale koopsa. (Sal. 31:10; 38:3, 4) N’chifukwa chiyani? Tiyeni tikambirane chitsanzo cha mlongo wina amene ankadziimbabe mlandu chifukwa cha machimo amene anachita m’mbuyo. Iye anati: “Ndikuona kuti palibe chifukwa chakuti ndizichitira khama potumikira Yehova, chifukwa olo nditadzipereka bwanji sindidzapulumuka.” N’kutheka kuti ambirife tingamamve ngati mmene mlongoyu ankamvera. Choncho tiyenera kusamala kuti tisamaidziimbe mlandu mopitirira muyezo. Tikutero chifukwa Satana angasangalale kwambiri ngati titasiya kutumikira Yehova ngakhale kuti Yehovayo amatikondabe komanso anatikhululukira.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:5-7, 11.

14. Kodi tingadziwe bwanji kuti Yehova amatikondabe ndipo angatikhululukire?

14 Komabe mwina tingamadzifunse kuti, ‘Kodi tingadziwe bwanji kuti Yehova amatikondabe ndipo angatikhululukire?’ Ngati mwafunsa funso limeneli ndi umboni wakuti Yehova angakukhululukireni. Zaka zambiri zapitazo Nsanja ya Olonda ina inafotokoza kuti: “Nthawi zina tingapezeke kuti tikuchita tchimo linalake mobwerezabwereza, zimenezi zingachitike chifukwa chakuti mwina sitinathetse vutolo tisanayambe kutumikira Mulungu. . . . Komabe simuyenera kutaya mtima. Musaganize kuti mwachita tchimo limene Yehova sangakukhululukireni. Zimenezi ndi zimene Satana amafuna kuti muziganiza. Kukhumudwa kapena kudzimvera chisoni mukachita tchimo linalake ndi umboni wakuti si inu munthu woipa ndipo Yehova akhoza kukukhululukirani. Muyenera kukhala odzichepetsa n’kupitiriza kupemphera kuti Mulungu akukhululukireni, akuthandizeni kuti mukhalenso ndi chikumbumtima chabwino komanso akuthandizeni kuti musadzabwerezenso kuchita tchimolo. Mofanana ndi mwana amene nthawi zonse amapita kwa bambo ake ndi vuto lomwelomwelo kuti akamuthandize, inunso muyenera kupitirizabe kupempha Yehova kuti akuthandizeni ndipo adzakuthandizani chifukwa iye ndi Mulungu wokoma mtima.”

15-16. Kodi anthu ena amamva bwanji akazindikira kuti Yehova amawakondabe komanso kuti anawakhululukira?

15 Atumiki ambiri a Yehova amalimbikitsidwa chifukwa chodziwa kuti Yehova amawakondabe komanso kuti ndi wofunitsitsa kuwakhululukira. Mwachitsanzo, zaka zapitazo m’bale wina analimbikitsidwa atawerenga zimene zinachitikira munthu wina munkhani zakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” Munkhaniyo mlongo wina ananena kuti zinkamuvuta kukhulupirira kuti Yehova angamukonde chifukwa cha zinthu zoipa zimene zinachitika pa moyo wake. Iye anavutikabe ndi maganizo amenewa ngakhale kuti panali patapita zaka zambiri kuchokera pamene anabatizidwa. Komabe kuganizira kwambiri za nsembe ya Yesu kunamuthandiza kuti azikhulupirira kuti Yehova amamukonda. *

16 Kodi nkhani ya mlongoyu inamuthandiza bwanji m’baleyu? Iye analemba kuti: “Ndili mwana, ndinayesetsa kuti ndisiye kuonera zolaula. Koma posachedwapa ndinapezeka kuti ndaoneranso zolaula. Ndinapempha akulu a kumpingo kwathu kuti andithandize ndipo ndikuyesetsa kuti ndithetse vutoli. Akuluwo ananditsimikizira kuti Mulungu ndi wachikondi komanso wachifundo. Koma nthawi zina ndimaonabe kuti ndine wosafunika ndipo Yehova sangandikonde. Nditawerenga nkhani ya mlongoyu, ndinazindikira kuti ndikamaganiza kuti Mulungu sangandikhululukire, ndiye kuti ndikutanthauza kuti nsembe ya Mwana wake siyokwanira kuphimba machimo anga. Nkhani imeneyi ndinaisunga kuti nthawi iliyonse imene ndayamba kudziona ngati wosafunika ndiziiwerenga n’kumaganizira mozama zimene ndawerengazo.”

17. Kodi mtumwi Paulo anachita chiyani kuti asamadziimbe kwambiri mlandu?

17 Nkhani ngati zimenezi zimatikumbutsa mtumwi Paulo. Asanakhale Mkhristu ankachita zinthu zambiri zoipa. Paulo ankakumbukira zimene anachitazo koma sankangoganizira zimenezo nthawi zonse. (1 Tim. 1:12-15) Iye ankaona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anam’patsa iyeyo payekha. (Agal. 2:20) Choncho Paulo sankangodziimba mlandu, koma ankayesetsa kuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova.

MUZIGANIZIRA MADALITSO AMENE MUDZAPEZE M’DZIKO LATSOPANO

Tiyeni tipitirize kuganizira madalitso amene tidzapeze m’tsogolo (Onani ndime 18-19) *

18. Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi?

18 Kodi taphunzira chiyani pa zinthu zitatu zimene takambirana munkhaniyi? (1) Kukumbukira zinthu zabwino ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Koma kaya moyo wathu unali wabwino bwanji m’mbuyomo, tizikumbukira kuti moyo wabwino kwambiri tidzakhala nawo m’dziko latsopano. (2) Anthu ena angatikhumudwitse koma tikasankha kukhululuka, maganizo athu onse amakhala pa kutumikira Yehova. (3) Kudziimba kwambiri mlandu kungatilepheretse kuti tizitumikira Yehova mosangalala. Choncho mofanana ndi Paulo tizikhulupirira kuti Yehova anatikhululukira.

19. Kodi tikudziwa bwanji kuti m’dziko latsopano sitidzadziimbanso mlandu chifukwa cha zolakwa zimene tinachita m’mbuyomo?

19 Tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. M’dziko latsopano sitidzadziimbanso mlandu chifukwa cha zinthu zimene tinachita m’mbuyomo. Baibulo limanena kuti nthawi imeneyo: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso.” (Yes. 65:17) Taganizirani mfundo iyi: Ena a ife takalamba tikutumikira Yehova, koma m’dziko latsopano tidzakhalanso anyamata. (Yobu 33:25) Choncho tisamaganizire kwambiri zinthu zakale. M’malomwake, tiziganizira kwambiri za dziko latsopano ndi kuchita zonse zimene tingathe kuti tidzapezekemo.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

^ ndime 5 Sikulakwa kuganizira zinthu zimene zinachitika pa moyo wathu m’mbuyomu. Koma tikamaganizira kwambiri zinthu zimenezi, zingatilepheretse kuti tizichita zambiri potumikira Yehova panopa komanso tingaiwale malonjezo abwino amene Yehova watilonjeza. Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene tiyenera kupewa zomwe zingatichititse kuti tiziganizira zinthu zimene zinachitika m’mbuyo. Tikambirananso mmene mfundo za m’Baibulo komanso zitsanzo za abale ndi alongo athu zingatithandizire kupewa zinthu zitatu zimenezi.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Tikamalakalaka zinthu zakale, kusunga chakukhosi komanso kudziimba kwambiri mlandu timakhala ngati tikukoka katundu wolemera amene angatilepheretse kuyenda bwino panjira yopita ku moyo.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Tikamapewa zinthu zimenezi timapepukidwa ndipo timakhala osangalala komanso timapeza mphamvu. Tikatero maganizo athu adzakhala pa madalitso amene tidzapeze m’tsogolo.