Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yophunzira 45

Muzithandiza Ena Kuti Azimvera Malamulo a Khristu

Muzithandiza Ena Kuti Azimvera Malamulo a Khristu

“Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. . . .  ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”MAT. 28:19, 20.

NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi Mateyu 28:18-20, kodi Yesu anapereka lamulo lotani?

YESU ataukitsidwa anaonekera kwa ophunzira ake amene anasonkhana ku Galileya. Iye anali ndi mfundo yofunika kwambiri yoti awauze. Kodi mfundo yake inali yotani? Mfundo yake ikupezeka pa Mateyu 28:18-20.—Werengani.

2. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

2 Lamulo la Yesu loti tiziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake, likupitanso kwa atumiki onse a Yehova masiku ano. Choncho, tiyeni tikambirane mafunso atatu okhudza ntchito imene Yesu anatipatsayi. Funso loyamba, kuwonjezera pa kuphunzitsa ophunzira atsopanowa zimene Mulungu amafuna, kodi chinanso n’chiyani chimene tiyenera kuchita? Funso lachiwiri, kodi ofalitsa onse mumpingo angathandize bwanji ophunzira Baibulo kuti akule mwauzimu? Funso lachitatu, kodi tingathandize bwanji abale ndi alongo athu amene anasiya kulalikira kuti ayambirenso kugwira ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu?

MUZIWAPHUNZITSA KUTI AZIMVERA MALAMULO A KHRISTU

3. Kodi Yesu anapereka malangizo otani mulamulo limene anapatsa ophunzira ake?

3 Malangizo amene Yesu anapereka ndi omveka bwino. Ananena kuti tiziphunzitsa anthu zimene iyeyo analamula. Komabe, sitiyenera kuiwala mfundo yofunika yomwe anatchula. Yesu sananene kuti: ‘Muziwaphunzitsa zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.’ M’malomwake ananena kuti: Muziwaphunzitsa “kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” Kuti titsatire malangizo a Yesuwa, tiyenera kuphunzitsa ophunzira athu zimene ayenera kuchita komanso tiyenera kuwasonyeza mmene angachitire zimenezo. (Mac. 8:31) N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?

4. Kodi kusunga lamulo kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

4 “Kusunga” lamulo kumatanthauza kumvera lamulolo. Kodi tingaphunzitse bwanji munthu kuti azisunga kapena kumvera zimene Khristu analamula? Chitsanzo chotsatirachi chitithandiza kumvetsa mmene tingachitire zimenezi. Kodi munthu amene akuphunzitsa munthu wina kuyendetsa galimoto angamuphunzitse bwanji kuti azimvera malamulo a pamsewu? Choyamba asanapite pamsewu angafunike kumufotokozera malamulo a pamsewu amene ayenera kutsatira. Komabe kuti aphunzitse wophunzirayo kumvera malamulowo, ayeneranso kuchita chinthu china. Ayenera kupita ndi wophunzirayo pamsewu n’kumakamuuza zimene ayenera kuchita pamene akuyendetsa galimoto komanso kumusonyeza mmene angagwiritsire ntchito zimene anamuphunzitsa zija. Kodi tikuphunzira chiyani pachitsanzochi?

5. (a) Mogwirizana ndi Yohane 14:15 komanso 1 Yohane 2:3, kodi tiyenera kuphunzitsa ophunzira athu kuti azichita chiyani? (b) Perekani zitsanzo zosonyeza mmene tingaphunzitsire ophunzira athu kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

5 Tikamaphunzira Baibulo ndi anthu ena, timawaphunzitsa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Koma pali zinanso zimene tingachite. Tiyenera kuwaphunzitsa kuti azitsatira zimene akuphunzirazo. (Werengani Yohane 14:15; 1 Yohane 2:3.) Zochita zathu zingasonyeze ophunzira athu mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Malemba akakhala kusukulu, kuntchito kapena akamachita zosangalatsa. Tingawafotokozerenso zimene zinatichitikira kuti tiwasonyeze mmene kutsatira mfundo za m’Baibulo kunatitetezera kapena mmene kunatithandizira kusankha zinthu mwanzeru. Muzipemphera limodzi ndi ophunzira anu, kupempha Yehova kuti aziwatsogolera ndi mzimu wake woyera.—Yoh. 16:13.

6. Kodi kuphunzitsa ena kuti azisunga malamulo a Yesu kumaphatikizapo chiyani?

6 Kodi kuphunzitsa ena kuti azisunga malamulo a Yesu kumaphatikizapo chiyani? Tiyenera kuthandiza ophunzira Baibulo kuti ayambe kukhala ndi mtima wofuna kuthandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu. Ophunzira ena amachita mantha akaganizira zoyamba kugwira ntchito yolalikira. Choncho tiyenera kukhala oleza mtima kuti tiwathandize kumvetsa bwino mfundo za choonadi zomwe zingawafike pamtima n’kuwathandiza kuti azifunitsitsa kugwira nawo ntchito yolalikira. Ndiye kodi tingatani kuti tithandize ophunzira Baibulo kuti azifunitsitsa kugwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino?

7. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti azifunitsitsa kuuza ena uthenga wabwino?

7 Tingafunse wophunzira Baibulo wathu mafunso ngati awa: “Kodi moyo wanu wasintha bwanji chifukwa chotsatira mfundo zimene mukuphunzira m’Baibulo? Kodi mukuganiza kuti pali anthu enanso omwe akufunika kumva mfundo za m’Baibulozi? Ndiye kodi mungachite chiyani kuti muwathandize?” (Miy. 3:27; Mat. 9:37, 38) Mungamusonyeze timapepala timene tili m’gulu la Zinthu Zophunzitsira n’kumuuza kuti asankhepo timapepala tomwe akuona kuti achibale ake, anzake kapena anthu omwe amagwira nawo ntchito angakonde kutiwerenga. Mungamupatse wophunzirayo tina mwa timapepalato. Muziyeserera naye kuti aphunzire mmene angagawirire kapepala mwaluso kwa munthu. Wophunzirayo akadzakhala wofalitsa wosabatizidwa, tidzafunika kumalowa naye mu utumiki kuti tizimuthandiza.—Mlal. 4:9, 10; Luka 6:40.

ZIMENE ANTHU MUMPINGO ANGACHITE POTHANDIZA OPHUNZIRA BAIBULO

8. N’chifukwa chiyani wophunzira ayenera kumakonda kwambiri Mulungu komanso anthu ena? (Onaninso bokosi lakuti “ Zimene Tingachite Pothandiza Ophunzira Baibulo Athu Kuti Azikonda Kwambiri Mulungu.”)

8 Kumbukirani kuti Yesu anatilangiza kuti tiziphunzitsa ena kuti ‘azisunga zinthu zonse’ zimene analamula. N’zosachita kufunsa kuti zinthu zimenezi zikuphatikizapo malamulo awiri akuluakulu, omwe ndi akuti tizikonda Mulungu komanso tizikonda anzathu. Malamulo awiri onsewa akugwirizana ndi ntchito yathu yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mat. 22:37-39) Kodi akugwirizana bwanji? Chifukwa chachikulu chimene chimatichititsa kuti tizilalikira ndi kukonda Mulungu komanso anzathu. N’zoona kuti ophunzira Baibulo ena amachita mantha akaganizira za ntchito yolalikira. Koma ophunzira Baibulo oterewa tiyenera kuwatsimikizira kuti Yehova adzawathandiza ndipo pang’ono ndi pang’ono adzasiya kuopa anthu. (Sal. 18:1-3; Miy. 29:25) Bokosi limene lili munkhaniyi, likufotokoza zimene tingachite pothandiza wophunzira wathu kuti azikonda kwambiri Mulungu. Komanso kuwonjezera pamenepo, kodi anthu ena mumpingo angachite chiyani pothandiza wophunzira watsopanoyo kuti azikonda kwambiri Mulungu komanso anthu ena?

9. M’chitsanzo cha munthu amene akuphunzira galimoto, kodi wophunzira akuphunzira bwanji zinthu zofunika zomwe zingamuthandize pamsewu?

9 Taganiziraninso za chitsanzo cha munthu amene akuphunzira galimoto uja. Kodi amaphunzira bwanji zinthu akamayendetsa galimoto mphunzitsi wake ali momwemo? Amaphunzira akamamvetsera zimene mphunzitsi wakeyo akumuuza komanso akamaona mmene madalaivala ena akuchitira. Mwachitsanzo, angamusonyeze zimene dalaivala wina wachita popereka mpata kwa mnzake kuti akhale patsogolo. Kapenanso angamusonyeze zimene dalaivala wina wachita pochepetsa kuwala kwa magetsi a galimoto yake kuti asathobwe m’maso madalaivala ena. Zitsanzo ngati zimenezi zingathandize wophunzirayo kudziwa zomwe angachite akamayendetsa galimoto.

10. Kodi n’chiyani chingathandize wophunzira Baibulo kuti akhale wophunzira wa Yesu?

10 Mofanana ndi zimenezi, wophunzira Baibulo amene wangoyamba kumene kutumikira Yehova angaphunzire zambiri kwa atumiki ena a Yehova osati kwa mphunzitsi wake yekha. Ndiyeno kodi n’chiyani chingathandize kwambiri ophunzira Baibulo kuti akhale ophunzira a Yesu? Ndi kupezeka pamisonkhano yathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa malangizo a m’Malemba amene angalandire pamisonkhanoyi angawathandize kuti adziwe zinthu zambiri, alimbitse chikhulupiriro chawo ndiponso kuti azikonda kwambiri Mulungu. (Mac. 15:30-32) Komanso pamisonkhanoyi, mphunzitsi angathandize wophunzirayo kuti adziwane ndi abale ndi alongo amene akupirira mavuto ngati omwe iyenso akukumana nawo. Iye adzaonanso chitsanzo chabwino cha abale ndi alongo amene amakondana mumpingo. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi.

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene wophunzira angaone mumpingo, nanga zingamuthandize bwanji?

11 Wophunzira Baibulo amene akulera yekha ana, akuona mlongo amene akuleranso yekha ana. Iye akuchita chidwi kwambiri poona khama limene mlongoyo amachita kuti azifika ku Nyumba ya Ufumu ndi ana ake aang’onoang’ono. Wophunzira wina amene akuvutika kusiya kusuta fodya, akudziwana ndi wofalitsa yemwe anali ndi vuto ngati lomwelo koma anasiya kusuta. Wofalitsayo akuuza wophunzirayo mmene kukonda kwambiri Yehova kunamuthandizira kuti azimvera malamulo ake. (2 Akor. 7:1; Afil. 4:13) Wofalitsayo atauza wophunzirayo mmene anasiyira kusuta, akunena kuti, “Inunso mungasiye kusuta.” Zimenezi zikumulimbikitsa kwambiri ndipo akukhulupirira kuti angasiyedi. Mtsikana wina amene akuphunzira Baibulo akuona mlongo wachitsikana yemwe akuoneka kuti amasangalala kukhala wa Mboni. Wophunzirayu ataona zimenezi, akufunitsitsa kudziwa chimene chimachititsa mlongoyu kuti azisangalala nthawi zonse.

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti aliyense mumpingo ali ndi udindo wothandiza ophunzira Baibulo?

12 Ophunzira Baibulo akadziwana ndi ofalitsa okhulupirika osiyanasiyana, angatengere chitsanzo chawo pa nkhani yomvera lamulo la Khristu lakuti tizikonda Mulungu ndi anthu ena. (Yoh. 13:35; 1 Tim. 4:12) Komanso monga tanenera kale, wophunzira Baibulo angaphunzire zambiri kuchokera kwa ofalitsa amene akulimbana ndi mavuto ofanana ndi amene iyenso akulimbana nawo. Zitsanzo zimenezi zingathandize wophunzirayo kuona kuti n’zotheka kuti nayenso asinthe n’kukhala wophunzira wa Khristu. (Deut. 30:11) Aliyense mumpingo angathandize m’njira zosiyanasiyana kuti ophunzira Baibulo afike pokhala ophunzira a Khristu. (Mat. 5:16) Kodi inuyo mumatani kuti mulimbikitse ophunzira Baibulo omwe abwera kumisonkhano?

MUZITHANDIZA AMENE ANASIYA KULALIKIRA KUTI AYAMBIRENSO

13-14. Kodi Yesu anachita chiyani ndi atumwi ake pa nthawi imene anali achisoni?

13 Tiyenera kuthandiza abale ndi alongo athu amene anasiya kulalikira kuti ayambirenso kutsatira lamulo limene Khristu anatipatsa loti tizilalikira ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. Zimene Yesu anachita ndi atumwi ake omwe anali achisoni, zikutithandiza kudziwa zimene nafenso tingachite masiku ano.

14 Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa atumwi ake “onse anathawa ndi kumusiya yekha.” (Maliko 14:50; Yoh. 16:32) Ndiye kodi Yesu anachita chiyani pa nthawiyi pamene atumwi ake anafooka? Yesu atangoukitsidwa, anauza otsatira ake ena kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga [kuti ndaukitsidwa].” (Mat. 28:10a) Yesu sanasiye ophunzira akewo. Ngakhale kuti iwo anamusiya, iye anapitirizabe kuwatchula kuti “abale anga.” Mofanana ndi Yehova, Yesu anali wachifundo komanso wokhululuka.—2 Maf. 13:23.

15. Kodi timamva bwanji tikaganizira abale ndi alongo athu amene anasiya kulalikira?

15 Mofanana ndi Yesu, ifenso timadera nkhawa anthu amene anasiya kulalikira. Iwo ndi abale ndi alongo athu ndipo timawakonda. Timakumbukirabe ntchito yaikulu imene anachita potumikira Yehova. Ndipo ena a iwo agwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri. (Aheb. 6:10) Timawasowa kwambiri abale ndi alongo amenewa. (Luka 15:4-7) Ndiye potsanzira Yesu, kodi tingasonyeze bwanji kuti timawadera nkhawa?

16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadera nkhawa abale ndi alongo athu amene anasiya kusonkhana komanso kulalikira?

16 Tiziwaitanira kumisonkhano. Njira imodzi imene Yesu analimbikitsira atumwi ake omwe anali ndi chisoni aja, inali kuwaitanira kumsonkhano. (Mat. 28:10b; 1 Akor. 15:6) Masiku anonso, tingalimbikitse amene anasiya kulalikira kuti azibwera kumisonkhano ngati anasiya kusonkhana. Tikudziwa kuti tingafunike kuwaitanira mobwerezabwereza. Mosakayikira, Yesu anasangalala ataona kuti ophunzira ake abwera kumsonkhano umene anawaitanira.—Yerekezerani ndi Mateyu 28:16 komanso Luka 15:6.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu amene anasiya kusonkhana komanso kulalikira wabwera kumisonkhano?

17 Tiziwalandira ndi manja awiri. Yesu atakumana ndi ophunzira akewo, anawathandiza kuti akhale omasuka. Iye sanayembekezere kuti ophunzirawo apite kwa iye koma iyeyo anapita kwa iwo n’kuyamba kulankhula nawo. (Mat. 28:18) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu amene anasiya kusonkhana komanso kulalikira wabwera ku Nyumba ya Ufumu? Tiyenera kuyamba ndi ifeyo kumulandira ndi manja awiri. Mwina poyamba tingamade nkhawa kuti ‘tiyambira pati.’ Koma popanda kumuchititsa manyazi, tikhoza kungomuuza kuti tasangalala kumuonanso.

18. Kodi tingalimbikitse bwanji ofalitsa amene anasiya kulalikira?

18 Tiziwalimbikitsa. N’kutheka kuti ophunzira a Yesu ankaganiza kuti sangakwanitse kugwira ntchito imene anawapatsa yolalikira padziko lonse. Koma Yesu anawalimbikitsa powauza kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.” (Mat. 28:20) Kodi zimenezi zinathandiza ophunzirawo? Inde. Tikutero chifukwa choti pasanapite nthawi, iwo anayamba kugwira mwakhama ntchito ‘yophunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.’ (Mac. 5:42) Ofalitsa amene anasiya kulalikira amafunikiranso kulimbikitsidwa. Mwina akhoza kumachita mantha kuti ayambirenso kulalikira. Tingawalimbikitse powatsimikizira kuti sadzilalikira okha, akakonzeka tingathe kupita nawo limodzi mu utumiki. Mosakayikira, iwo angayamikire kwambiri powathandiza kuti ayambirenso kugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino. Tikamasonyeza abale ndi alongo athu amene anasiya kulalikira kuti timawaganizira, angayambirenso kugwira ntchitoyi. Ndipo zimenezi zingachititse kuti onse mumpingo asangalale.

TIYENERA KUTSIRIZA NTCHITO IMENE YESU ANATIPATSA

19. Kodi tikufunitsitsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

19 Kodi tiyenera kupitiriza kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu mpaka liti? Mpaka mapeto a nthawi ino. (Mat. 28:20) Kodi tikwanitsa kugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa imene Yesu anatipatsayi mpaka nthawi imeneyo? Inde, tikufunitsitsa kuchita zimenezi. Timasangalala kugwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso ndalama zathu pofufuza anthu amene ali ndi “maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.” (Mac. 13:48) Tikamachita zimenezi, timakhala tikutengera chitsanzo cha Yesu. Paja iye anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yoh. 4:34; 17:4) Ifenso tikufunitsitsa kutsiriza ntchito imene Yesu anatipatsa. (Yoh. 20:21) Ndipo tikufuna kuti enanso kuphatikizapo amene anasiya kulalikira, apitirize nafe kugwira ntchitoyi.—Mat. 24:13.

20. Mogwirizana ndi Afilipi 4:13, n’chifukwa chiyani tikunena kuti tingakwanitse kugwira ntchito imene Yesu anatilamula?

20 Kunena zoona, si zophweka kugwira ntchito imene Yesu anatilamula. Komabe sitikhala tokha pogwira ntchitoyi chifukwa Yesu analonjeza kuti adzakhala nafe. Tikamagwira ntchito yophunzitsa anthu timakhala “antchito anzake a Mulungu” komanso “otsatira Khristu.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 2:17) Choncho, tingakwanitse kugwira ntchito imeneyi. Timasangalala kugwira ntchito imeneyi ndipo timaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza ena kuti azichitanso chimodzimodzi.—Werengani Afilipi 4:13.

NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba

^ ndime 5 Yesu anauza otsatira ake kuti aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake komanso kuti aziwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene anawalamula. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tizitsatira malangizo a Yesuwa. Mfundo zina za munkhaniyi zachokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2004, tsamba 14-19.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo akuchititsa phunziro la Baibulo ndipo akufotokozera wophunzira zimene zingamuthandize kuti azikonda kwambiri Mulungu. Kenako, wophunzirayo akuchita zinthu zitatu zimene mphunzitsi wake anamuuza.