Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbiri Ya Moyo Wanga

“Yehova Sanandiiwale”

“Yehova Sanandiiwale”

KWATHU ndi ku Orealla mudzi wa anthu pafupifupi 2,000 ku Guyana, South America. Mudziwu uli kwa okhaokha moti kuti munthu akafikeko angafunike kuyenda pa ndege zing’onozing’ono kapena pa boti.

Ndinabadwa m’chaka cha 1983. Ndili mwana ndinali ndi moyo wathanzi, koma nditakwanitsa zaka 10 ndinayamba kumva kupweteka kwambiri thupi lonse. Patadutsa zaka pafupifupi ziwiri, nditadzuka tsiku lina ndinangoona kuti sindikutha kuyenda. Ndinkayesetsa kusuntha miyendo yanga koma sizinkatheka. Kuyambira tsiku limenelo ndinasiya kuyenda. Matendawa anachititsanso kuti ndisamakule. Panopa ndimangoonekabe ngati kamwana.

Patadutsa miyezi ingapo nditayamba kudwala komanso ndisakutha kuchoka panyumba, a Mboni za Yehova awiri anabwera kunyumba kwathu. Nthawi zambiri kukabwera alendo ndinkayesetsa kukabisala, koma pa tsikuli ndinalola kuti ndilankhule ndi azimayiwo. Pamene ankafotokoza za paradaiso ndinakumbukira zimene ndinamva ndili ndi zaka pafupifupi 5. Pa nthawi imeneyo mmishonale wina dzina lake Jethro amene ankakhala ku Suriname ankabwera m’mudzi mwathu kamodzi pamwezi kudzaphunzira Baibulo ndi bambo anga. Jethro ankachita nane zinthu mokoma mtima kwambiri ndipo ankandikonda. Komanso agogo anga ankanditenga popita kumisonkhano ina ya Mboni imene inkachitikira m’mudzi mwathu. Ndiye mmodzi wa azimayiwa dzina lake Florence atandifunsa ngati ndikufuna kuphunzira zambiri, ndinayankha kuti inde.

Florence anabweranso ndi mwamuna wake dzina lake Justus ndipo anayamba kuphunzira nane Baibulo. Ataona kuti sinditha kuwerenga anayamba kundiphunzitsa. Patapita nthawi ndinayamba kutha kuwerenga. Tsiku lina banjali linandiuza kuti awatumiza kuti azikalalikira ku Suriname. N’zomvetsa chisoni kuti ku Orealla kunalibe aliyense amene akanapitiriza kuphunzira nane Baibulo. Koma n’zosangalatsa kuti Yehova sanandiiwale.

Pasanapite nthawi ku Orealla kunafika mpainiya wina dzina lake Floyd ndipo anandipeza pamene ankalalikira kunyumba ndi nyumba. Atandiuza kuti tiziphunzira Baibulo ndinamwetulira. Iye anandifunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukumwetulira?” Ndinamuuza kuti ndinamaliza kuphunzira kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? ndipo ndinayamba kuphunzira buku lakuti Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Ndinafotokoza chifukwa chake phunziroli linaima. Floyd anamalizitsa kuphunzira nane buku la Chidziwitso koma kenako nayenso anamutumiza kuti azikalalikira kwina. Kachiwirinso ndinalibe woti azindiphunzitsa Baibulo.

Koma mu 2004 apainiya apadera awiri Granville ndi Joshua anatumizidwa ku Orealla. Iwo anandipeza pamene ankalalikira kunyumba ndi nyumba. Atandifunsa ngati ndikufuna kuphunzira, ndinamwetulira. Ndinawapempha kuti tiyambirenso kuphunzira buku la Chidziwitso. Ndinkafuna kuona ngati angandiphunzitse zofanana ndi zimene ena aja anandiphunzitsa. Granville anandiuza kuti misonkhano imachitikira m’mudzi mwathu momwemo. Ngakhale kuti sindinkachoka panyumba kwa zaka pafupifupi 10, ndinkafunitsitsa kupita nawo kumisonkhano. Choncho Granville ananditenga pa njinga ya olumala kupita nane ku Nyumba ya Ufumu.

Patapita nthawi Granville anandilimbikitsa kuti ndilembetse mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Iye anati: “Ndiwe olumala koma umatha kulankhula. Tsiku lina udzakamba nkhani ya onse. Ndithu ndikukuuza.” Mawu ake olimbikitsawa anachititsa kuti ndisamadzikaikire.

Ndinayamba kugwira ntchito yolalikira limodzi ndi Granville. Koma misewu yambiri m’mudzi mwathu sinali yabwino moti kunali kovuta kuyendamo pa njinga ya olumala. Choncho ndinamuuza Granville kuti azinditenga mu wilibala tikamapita kolalikira. Zimenezi zinathandiza kwambiri. Mu April 2005 ndinabatizidwa. Pasanapite nthawi abale anandiphunzitsa kuti ndizisamalira mabuku komanso zokuzira mawu ku Nyumba ya Ufumu.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti mu 2007 bambo anga anamwalira pa ngozi ya boti. Banja lathu linali ndi chisoni chachikulu. Granville anapemphera nafe ndipo anatiwerengera malemba olimbikitsa kuchokera m’Baibulo. Pambuyo pa zaka ziwiri tinalinso ndi chisoni chachikulu chifukwa Granville anamwaliranso pa ngozi ya boti.

Mpingo wathu waung’onowo unali ndi chisoni kwambiri chifukwa tsopano unalibe mkulu aliyense unangokhala ndi mtumiki wothandiza mmodzi basi. Imfa ya Granville inandipweteka kwambiri chifukwa anali mnzanga wapamtima. Iye nthawi zonse ankandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso ankandithandiza kupeza zinthu zambiri zofunika pamoyo wanga. Pamisonkhano yotsatira imfayi itangochitika, ndinkawerenga ndime pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Ndinakwanitsa kuwerenga ndime ziwiri zoyambirira, kenako ndinayamba kulira ndipo misozi inkangotsika. Sindikanathanso kupitiriza moti ndinachoka papulatifomu.

Ndinayamba kusangalala pamene abale ochokera kumpingo wina anabwera ku Orealla kudzatithandiza. Komanso ofesi ya nthambi inatumiza m’bale wina yemwe anali mpainiya wapadera dzina lake Kojo. Ndimasangalala kwambiri kuti mayi anga komanso mng’ono wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa. Kenako mu March 2015 ndinaikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Patapita nthawi ndinakamba nkhani ya onse kwa nthawi yoyamba. Tsiku limeneli ndinasangalala komanso ndinali ndi chisoni chifukwa ndinakumbukira zimene Granville anandiuza zakuti: “Tsiku lina udzakamba nkhani ya onse. Ndithu ndikukuuza.”

Kudzera pa mapulogalamu a pa JW Broadcasting, ndadziwa kuti pali abale ndi alongo enanso omwe ali ndi vuto ngati langa. Koma ngakhale ali ndi vuto ngati limeneli amakwanitsa kuchita zambiri ndipo amasangalala. Inenso ndimakwanitsa kuchita zinthu zina. Ndimafunitsitsa kuchita zonse zimene ndingathe potumikira Yehova n’chifukwa chake ndinayamba upainiya wokhazikika. Ndiye mu September 2019 ndinasangalala nditamva nkhani yabwino imene sindinkaiyembekezera. Mwezi umenewo ndinaikidwa kukhala mkulu mumpingo wathu, womwe uli ndi ofalitsa pafupifupi 40.

Ndimayamikira kwambiri abale ndi alongo amene ankaphunzira nane Baibulo komanso kundithandiza kuti ndizitumikira Yehova. Koposa zonse ndimayamikira kwambiri kuti Yehova sanandiiwale.

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma pano anasiya kusindikiza.