Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 46

Amene Mwangokwatirana Kumene, Muziika Kutumikira Yehova Pamalo Oyamba

Amene Mwangokwatirana Kumene, Muziika Kutumikira Yehova Pamalo Oyamba

“Yehova ndiye mphamvu yanga . . . mtima wanga umam’khulupirira.”​—SAL. 28:7.

NYIMBO NA. 131 “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) N’chifukwa chiyani anthu omwe angokwatirana kumene ayenera kudalira Yehova? (Salimo 37:3, 4) (b) Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?

 KODI mwatsala pang’ono kulowa m’banja, kapena mwangokwatirana kumene? Ngati ndi choncho, n’zosakayikitsa kuti mukuyembekezera kudzasangalala ndi munthu yemwe mumamukonda kwambiri. N’zoona kuti anthu amene akwatirana amakumana ndi mavuto komanso amafunika kusankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri. Zimene mumachita mukakumana ndi mavutowo komanso zosankha zanu, zingachititse kuti banja lanu lidzakhale losangalala kapena ayi. Mukamadalira Yehova, mungasankhe zochita mwanzeru, banja lanu lidzakhala lolimba komanso mudzakhala osangalala. Koma ngati simungatsatire malangizo a Mulungu, mudzakumana ndi mavuto ambiri m’banja mwanu ndipo zidzachititsa kuti musamasangalale.​—Werengani Salimo 37:3, 4.

2 Ngakhale kuti nkhaniyi ikufotokoza kwambiri za amene angokwatirana kumene, ifotokozanso mavuto amene mabanja onse angakumane nawo. Tionanso zimene tingaphunzire pa zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo. Pa zitsanzozi, tiphunzira mfundo zimene tingagwiritse ntchito pa mbali zosiyanasiyana za moyo wathu, kuphatikizapo m’banja. Tionanso zomwe tingaphunzire pa zimene mabanja ena amasiku ano anachita.

KODI ANTHU ONGOKWATIRANA KUMENE ANGAKUMANE NDI MAVUTO ATI?

Kodi ndi zosankha ziti zomwe zingalepheretse okwatirana kumene kuchita zambiri potumikira Yehova? (Onani ndime 3-4)

3-4. Kodi anthu amene angokwatirana kumene angakumane ndi mavuto ati?

3 Anthu ena angalimbikitse amene angokwatirana kumene kuti azikhala moyo womwe anthu onse amakhala nawo. Mwachitsanzo, makolo ndi achibale ena angawalimbikitse kuti ayambe kukhala ndi ana mwamsanga. Kapenanso anzawo a anthu amene angokwatirana kumenewo angawalimbikitse kuti agule nyumba ndi katundu wambiri wabwino.

4 Ngati sangasamale, anthu okwatiranawo angasankhe zinthu zomwe zingachititse kuti akhale ndi ngongole zambiri. Zikatero, mwamuna ndi mkazi angafunikire kuti azigwira ntchito maola ambiri kuti abweze ngongolezo. Ntchitoyo ingachititse kuti asamapeze nthawi yophunzira Baibulo paokha, kuchita kulambira kwa pabanja komanso kulalikira. Mwinanso iwo angamalephere kupezeka pamisonkhano kuti azigwira ovataimu n’cholinga choti azipeza ndalama zambiri kapenanso kuti ntchito isawathere. Zimenezi zingachititse kuti asakhale ndi mwayi wochita nawo zinthu zina zosangalatsa potumikira Yehova.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zomwe zinachitikira Klaus ndi Marisa?

5 Pali zitsanzo zambiri zosonyeza kuti kufunitsitsa kukhala ndi zinthu zambiri, sikuchititsa munthu kukhala wosangalala. Taganizirani zomwe Klaus ndi Marisa, omwe ndi banja, anaphunzira pa nkhani imeneyi. * Atangokwatirana kumene, onse ankagwira ntchito kwa maola ambiri kuti azikhala ndi moyo wofewa. Komabe, iwo ankaona kuti sankasangalala. Klaus ananena kuti: “Tinali ndi zonse zomwe tinkafunikira, koma tinalibe zolinga zilizonse zowonjezera utumiki wathu. Kunena zoona, palibe chomwe chinkayenda.” N’kutheka kuti inunso mwazindikira kuti kufunitsitsa kukhala ndi zinthu zambiri pa moyo sikunakuthandizeni kukhala okhutira. Ngati ndi choncho, musataye mtima. Kuganizira zitsanzo zabwino za anthu ena kungakuthandizeni pa nkhaniyi. Choyamba, tiyeni tione zimene amuna angaphunzire pa chitsanzo cha Mfumu Yehosafati.

MOFANANA NDI YEHOSAFATI, MUZIDALIRA YEHOVA

6. Mogwirizana ndi malangizo opezeka pa Miyambo 3:5, 6, kodi Mfumu Yehosafati anatani atakumana ndi vuto lalikulu?

6 Amuna, kodi nthawi zina mumapanikizika chifukwa cha maudindo anu? Ngati ndi choncho, chitsanzo cha Mfumu Yehosafati chikhoza kukuthandizani. Monga mfumu, Yehosafati anali ndi udindo woonetsetsa kuti anthu onse m’dziko lake ndi otetezeka. Ndiye kodi anatani kuti akwaniritse udindo waukuluwu? Anachita zonse zomwe akanatha kuti ateteze anthu ake. Anamanga mipanda yolimba kwambiri ku Yuda komanso anasonkhanitsa asilikali oposa 1,160,000. (2 Mbiri 17:12-19) Patapita nthawi, Yehosafati anakumana ndi vuto lalikulu kwambiri. Gulu lalikulu kwambiri lankhondo la Aamoni, Amowabu komanso amuna am’dera lamapiri la Seiri anaopseza iyeyo, banja lake komanso anthu ake. (2 Mbiri 20:1, 2) Ndiye kodi Yehosafati anatani? Iye anapempha Yehova kuti amuthandize komanso kumupatsa mphamvu. Zimene anachitazi zinali zogwirizana ndi malangizo anzeru opezeka pa Miyambo 3:5, 6. (Werengani.) Pemphero la Yehosafati lochokera pansi pa mtima lopezeka pa 2 Mbiri 20:5-12, limasonyeza kuti ankadalira kwambiri Atate wake wakumwamba yemwe ndi wachikondi. Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero la Yehosafati?

7. Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero la Yehosafati?

7 Yehova analankhula ndi Yehosafati kudzera mwa Mlevi wina dzina lake Yahazieli. Yehova anati: “Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.” (2 Mbiri 20:13-17) N’zoona kuti imeneyi si njira imene anthu amagwiritsa ntchito pomenya nkhondo. Komatu malangizowa sikuti anachokera kwa munthu. Anali ochokera kwa Yehova. Yehosafati anadalira kwambiri Mulungu ndipo anachita zomwe anauzidwa. Iye ndi anthu ake atapita kukakumana ndi adani awo anaika patsogolo pa asilikali ake, osati asilikali aluso kwambiri, koma oimba omwe analibe zida zomenyera nkhondo. Yehova sanamugwiritse fuwa lamoto Yehosafati, koma anamugonjetsera adani ake.​—2 Mbiri 20:18-23.

Anthu omwe angokwatirana kumene angaike patsogolo kutumikira Yehova popemphera komanso kuphunzira Mawu ake (Onani ndime 8, 10)

8. Kodi amuna angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yehosafati?

8 Amunanu, mungaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Yehosafati. Muli ndi udindo wosamalira banja lanu, choncho mumagwira ntchito mwakhama kuti musamalire komanso kuteteza banjalo. Mukakumana ndi vuto, mwina mukhoza kuona kuti muli ndi zonse zofunika kuti mulithetse. Komabe, muzipewa chizolowezi chodzidalira. M’malomwake, muzipempha Yehova panokha kuti akuthandizeni. Kuwonjezera pamenepa, muzipemphera mochokera pansi pa mtima ndi mkazi wanu. Muzifufuza malangizo ochokera kwa Yehova pophunzira Baibulo komanso mabuku omwe gulu la Mulungu limatipatsa ndipo muzigwiritsa ntchito malangizo omwe mwapezawo. Ena sangasangalale ndi zomwe mwasankha mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo mwinanso angakuuzeni kuti ndinu opusa. Akhoza kumanenanso kuti ndalama ndi zinthu zina zomwe mungagule n’zimene zingateteze kwambiri banja lanu. Koma muzikumbukira chitsanzo cha Yehosafati. Iye anadalira Yehova ndipo zochita zake zinasonyeza zimenezi. Yehova sanasiye munthu wokhulupirikayu ndipo inunso sangakusiyeni. (Sal. 37:28; Aheb. 13:5) Kodi n’chiyaninso chimene anthu okwatirana angachite kuti azikhala moyo wosangalala?

MOFANANA NDI MNENERI YESAYA NDI MKAZI WAKE, MUZIIKA KUTUMIKIRA YEHOVA PAMALO OYAMBA

9. Kodi tinganene zotani zokhudza mneneri Yesaya ndi mkazi wake?

9 Mneneri Yesaya ndi mkazi wake ankaona kuti kutumikira Yehova ndi kofunika kwambiri. Yesaya anali mneneri ndipo zikuoneka kuti mkazi wake ankachita zinthu zina zokhudzana ndi uneneri chifukwa amatchulidwa kuti “mneneri wamkazi.” (Yes. 8:1-4) Monga banja, n’zoonekeratu kuti Yesaya ndi mkazi wake ankaika patsogolo kulambira Yehova pa moyo wawo. Iwo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu okwatirana masiku ano.

10. Kodi kuphunzira maulosi a m’Baibulo kungathandize bwanji okwatirana kuti akhale otsimikiza mtima kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova?

10 Anthu okwatirana masiku ano, angaike kutumikira Yehova pamalo oyamba poyesetsa kuchita zonse zomwe angathe pomutumikira. Iwo angamadalire kwambiri Yehova akamaphunzira limodzi maulosi a m’Baibulo komanso kuona mmene nthawi zonse akukwaniritsidwira. (Tito 1:2) Angaganizire zimene angachite kuti azikwaniritsa nawo maulosi ena a m’Baibulo. Mwachitsanzo, akhoza kuthandiza kukwaniritsa nawo ulosi wa Yesu wonena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Anthu okwatirana akamazindikira kwambiri kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa, m’pamenenso amafunitsitsa kwambiri kuti azichita zonse zomwe angathe potumikira Yehova.

MOFANANA NDI AKULA NDI PURISIKILA, MUZIIKA ZINTHU ZOKHUDZA UFUMU PAMALO OYAMBA

11. Kodi Purisikila ndi Akula anakwanitsa kuchita zotani, nanga n’chifukwa chiyani?

11 Mabanja a achinyamata angaphunzire zambiri kwa Purisikila ndi Akula, banja la Chiyuda lomwe linkakhala ku Roma. Iwo anamva uthenga wabwino wokhudza Yesu ndipo anakhala Akhristu. N’kutheka kuti ankasangalala ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Komabe zinthu zinasintha mwadzidzidzi pamene Mfumu Kalaudiyo inalamula kuti Ayuda onse achoke ku Roma. Taganizirani mmene izi zinakhudzira Akula ndi Purisikila. Iwo ankafunika kusamuka dera lomwe anazolowera n’kukhala ndi nyumba yatsopano komanso kumachita bizinezi yawo yopanga matenti kudera latsopano. Kodi kusintha kwa zinthu pa moyo wawo kunachititsa kuti asamaike pamalo oyamba zinthu zokhudza Ufumu? Sitikukayikira kuti mukudziwa yankho la funso limeneli. Atayamba kukhala ku Korinto, Akula ndi Purisikila anayamba kuthandiza abale mumpingo wakumeneko ndipo ankagwira ntchito limodzi ndi mtumwi Paulo powalimbikitsa. Patapita nthawi, anasamukira kumadera ena komwe kunkafunikira olalikira ambiri. (Mac. 18:18-21; Aroma 16:3-5) Anthu awiriwa ankakhala moyo wabwino ndipo ayenera kuti ankasangalala kwambiri.

12. N’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kudziikira zolinga zotumikira Yehova?

12 Anthu okwatirana masiku ano, angatsanzire Purisikila ndi Akula pomaika pamalo oyamba zinthu zokhudza Ufumu pa moyo wawo. Nthawi yabwino kwambiri yokambirana zimene adzachite pa moyo wawo, ndi pamene ali pachibwenzi. Iwo akasankhira limodzi zomwe akufuna kuchita potumikira Yehova n’kumayesetsa kukwaniritsa zomwe asankhazo, amakhala ndi mwayi waukulu woona mmene Yehova akuwathandizira pa moyo wawo. (Mlal. 4:9, 12) Taganizirani chitsanzo cha Russell ndi Elizabeth. Russell ananena kuti, “Tili pachibwenzi, tinakambirana zenizeni zomwe tinkafuna kuchita potumikira Yehova.” Elizabeth ananena kuti, “Tinakambirana zimenezi n’cholinga choti m’tsogolo tikadzafunika kusankha pa nkhani zosiyanasiyana, zisadzatisokoneze pa zimene tinasankha zokhudza kutumikira Yehova.” Mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili pa moyo wawo, Russell ndi Elizabeth anasamukira ku Micronesia komwe kunkafunikira olalikira ambiri.

Anthu omwe angokwatirana kumene angaike patsogolo kutumikira Yehova pokhala ndi zolinga zowonjezera utumiki (Onani ndime 13)

13. Mogwirizana ndi Salimo 28:7, kodi chidzachitike n’chiyani tikamadalira Yehova?

13 Mofanana ndi Russell ndi Elizabeth, mabanja ambiri asankha kuti asamatanganidwe ndi zinthu zina n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yambiri yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Ufumu. Okwatirana akakhala ndi zolinga zotumikira Yehova n’kumayesetsa kuzikwaniritsa limodzi, pamakhala zotsatira zabwino zambiri. Iwo amadzionera okha mmene Yehova akuwasamalirira, amamudalira kwambiri ndiponso amapeza chimwemwe chenicheni.​—Werengani Salimo 28:7.

MOFANANA NDI MTUMWI PETULO NDI MKAZI WAKE, MUZIKHULUPIRIRA MALONJEZO A YEHOVA

14. Kodi mtumwi Petulo ndi mkazi wake anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira lonjezo lopezeka pa Mateyu 6:25, 31-34?

14 Anthu omwe ali pabanja angaphunzireponso kanthu pa chitsanzo cha mtumwi Petulo ndi mkazi wake. Patapita pafupifupi miyezi 6 kapena chaka kuchokera pa nthawi yoyamba imene anakumana ndi Yesu, mtumwi Petulo ankafunika kusankha zochita pa nkhani yofunika kwambiri. Petulo ankapeza zofunika pa moyo kudzera muntchito yausodzi. Choncho pamene Yesu anamuitana kuti amutsatire, iye ankafunika kuganiziranso za banja lake. (Luka 5:1-11) Petulo anasankha kuti aziyenda limodzi ndi Yesu pa ntchito yolalikira. Pamenepatu anasankha mwanzeru. Ndipo tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuganizira kuti mkazi wake anagwirizana ndi zomwe iye anasankhazi. Baibulo limasonyeza kuti Yesu ataukitsidwa, mkazi wa Petulo ankayenda limodzi ndi mwamuna wake pa maulendo ena. (1 Akor. 9:5) N’zosakayikitsa kuti chitsanzo chake chinathandiza kuti Petulo akhale ndi ufulu wolankhula n’kulemba malangizo ouziridwa othandiza mabanja a Chikhristu. (1 Pet. 3:1-7) N’zodziwikiratunso kuti Petulo ndi mkazi wake ankakhulupirira lonjezo la Yehova loti adzawasamalira akamaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo.​—Werengani Mateyu 6:25, 31-34.

15. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Tiago ndi Esther?

15 Ngati mwakwatirana m’zaka zaposachedwapa, kodi mungatani kuti mupitirize kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri pa utumiki wanu? Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kuganizira zimene mabanja ena anachita. Mwachitsanzo, mungawerenge nkhani zakuti, “Anadzipereka Ndi Mtima Wonse.” Nkhani zimenezi zinathandiza Tiago ndi Esther, banja la ku Brazil, kuti azifunitsitsa kukatumikira komwe kukufunika olalikira ambiri. Tiago anafotokoza kuti: “Titaona mmene Yehova akuthandizira atumiki ake masiku ano, tinkafuna kuti ifenso tione Yehova akutitsogolera komanso kutisamalira.” Choncho iwo anasamukira ku Paraguay, komwe akhala akutumikira m’dera la Chipwitikizi kuyambira mu 2014. Esther anati: “Limodzi mwa mavesi amene ine ndi mwamuna wanga timakonda ndi Aefeso 3:20. Mobwerezabwereza, takhala tikuona mawu amenewa akukwaniritsidwa pamene tikutumikira Yehova.” M’kalatayi, yomwe analembera Akhristu a ku Efeso, Paulo analonjeza kuti Yehova adzatipatsa zochuluka kuposa zomwe timapempha. Zimenezitu ndi zoona.

Anthu omwe angokwatirana kumene angaike patsogolo kutumikira Yehova popempha malangizo kwa anthu olimba mwauzimu (Onani ndime 16)

16. Kodi mabanja a achinyamata angapemphe malangizo kwa ndani akamadziikira zolinga pa moyo?

16 Mabanja a achinyamata masiku ano angapindule pa chitsanzo cha ena omwe aphunzira kudalira Yehova. N’kutheka kuti mabanja ena akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri. Bwanji osawapempha malangizo omwe angakuthandizeni kuti mukwaniritse zolinga zanu? Imeneyi ndi njira ina yomwe mungasonyezere kuti mukudalira Yehova. (Miy. 22:17, 19) Akulu nawonso angathandize mabanja a achinyamata kuti akhale ndi zolinga zowonjezera utumiki komanso kuzikwaniritsa.

17. Kodi n’chiyani chinachitikira Klaus ndi Marisa, nanga tikuphunzira chiyani pa zimene zinawachitikirazo?

17 Komabe nthawi zina, zomwe tasankha kuti tichite powonjezera utumiki wathu, sizingachitike mmene timaganizira. Taganizirani chitsanzo cha Klaus ndi Marisa, omwe tawatchula kale aja. Patatha zaka zitatu kuchokera pamene anakwatirana, iwo anachoka kwawo n’kudzipereka kuti akathandize pa ntchito ya zomangamanga kunthambi ya ku Finland. Komabe, iwo anauzidwa kuti sadzaloledwa kukhala kumeneko kwa miyezi yoposa 6. Poyamba anakhumudwa ndi zimenezi. Koma patapita nthawi yochepa, iwo anaitanidwa kuti akalowe sukulu yophunzira chinenero cha Chiarabu ndipo panopa akusangalala kutumikira m’dziko lina m’dera lomwe amalankhula chinenerochi. Pokumbukira zomwe zinachitika, Marisa ananena kuti: “Sizikhala zophweka kusiya zinthu zomwe unazolowera n’kumakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova azikuthandiza. Koma ndakhala ndikuona Yehova nthawi zonse akutithandiza m’njira imene sitimayembekezera. Zimene zatichitikirazi zandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova.” Monga mmene chitsanzo cha banjali chikusonyezera, mungakhale otsimikiza kuti Yehova nthawi zonse adzakudalitsani kwambiri ngati mumamudalira ndi mtima wonse.

18. Kodi anthu okwatirana angatani kuti apitirize kudalira Yehova?

18 Ukwati ndi mphatso yochokera kwa Yehova. (Mat. 19:5, 6) Iye amafuna kuti anthu okwatirana azisangalala ndi mphatso imeneyi. (Miy. 5:18) Ngati ndinu banja lachinyamata, bwanji osaganizira bwinobwino zimene mukuchita pa moyo wanu? Kodi mukuchita zonse zomwe mungathe posonyeza kuti mumayamikira mphatso zimene Yehova wakupatsani? Muzimuuza Yehova m’pemphero zimene mukufuna kuchita. Muzifufuza m’Mawu ake mfundo zomwe zingakuthandizeni mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Kenako muzigwiritsa ntchito malangizo amene Yehova wakupatsani. Mukamaika patsogolo kutumikira Yehova m’banja mwanu, mungakhale otsimikiza kuti mudzakhala ndi moyo wosangalala komanso wabwino kwambiri.

NYIMBO NA. 132 Tsopano Ndife Thupi Limodzi

^ ndime 5 Zinthu zina zomwe timasankha pa moyo wathu, zimakhudza nthawi komanso mphamvu zomwe tingagwiritse ntchito potumikira Yehova. Makamaka anthu amene angokwatirana kumene, amafunika kusankha zochita pa zinthu zomwe zingakhudze moyo wawo wonse. Nkhaniyi ithandiza okwatirana kuti azisankha zochita mwanzeru kuti azikhala ndi moyo wosangalala.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa.