Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 47

Kodi Chikhulupiriro Chanu Chidzakhala Cholimba?

Kodi Chikhulupiriro Chanu Chidzakhala Cholimba?

“Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu.”​—YOH. 14:1.

NYIMBO NA. 119 Tiyenera Kukhala ndi Chikhulupiriro

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi tingamadzifunse funso liti?

 KODI nthawi zina mumachita mantha mukaganizira zimene zichitike m’tsogolomu monga kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga, kuukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi komanso nkhondo ya Aramagedo? Kodi mwina mumadzifunsa kuti, ‘Zochitika zochititsa manthazi zikadzayamba, ndidzakhalabe wokhulupirika?’ Ngati mumada nkhawa ndi zimenezi, kukambirana mawu a Yesu opezeka mulemba lomwe likutsogolera nkhaniyi kungakuthandizeni kwambiri. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu.” (Yoh. 14:1) Chikhulupiriro cholimba chidzathandiza kuti tikhale olimba mtima, kaya tidzakumana ndi zotani.

2. Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Tingalimbitse chikhulupiriro chathu kuti tidzathe kupirira mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolo tikaganizira zimene timachita panopa tikakumana ndi mayesero. Kuganizira zimene timachita kungatithandize kuona mbali zimene tiyenera kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Nthawi iliyonse tikapirira mayesero enaake, chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. Ndipo zimenezi zidzatithandiza kuti tidzapirire mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolo. Munkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene zinachitikira ophunzira a Yesu zomwe zinasonyeza kuti ankafunikira kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Kenako tiona zimene tingachite ngati titakumana ndi mavuto ofanana ndi amene iwo anakumana nawo komanso mmene zimenezi zingatithandizire kukonzekera za m’tsogolo.

TIZIKHULUPIRIRA KUTI MULUNGU AZITIPATSA ZOMWE TIMAFUNIKIRA

Ngati takumana ndi mavuto azachuma, chikhulupiriro chingatithandize kuti tiziikabe pamalo oyamba kutumikira Yehova (Onani ndime 3-6)

3. Mogwirizana ndi Mateyu 6:30, 33, kodi Yesu anafotokoza momveka bwino mfundo iti yokhudza chikhulupiriro?

3 Si zachilendo kuti mwamuna amafuna kupezera ana ndi mkazi wake chakudya chokwanira, zovala komanso malo okhala. Masiku ano izi sizikhala zophweka. Nthawi zina abale ndi alongo ena ntchito imawathera ndipo ngakhale atayesetsa kwambiri amalephera kupeza ina. Enanso amafunika kukana ntchito imene sigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Pa zochitika ngati zimenezi, timafunika kukhulupirira kwambiri kuti Yehova adzapatsa banja lathu zimene likufunikira. Yesu anatsindika mfundo imeneyi kwa ophunzira ake pa ulaliki wa paphiri. (Werengani Mateyu 6:30, 33.) Tikamakhulupirira kwambiri kuti Yehova sadzatisiya, tidzaika maganizo athu onse pa zinthu zokhudza Ufumu. Tikamaona mmene Yehova akutithandizira kupeza zofunika pa moyo, timakhala naye pa ubwenzi wolimba ndiponso timayamba kumukhulupirira kwambiri.

4-5. N’chiyani chinathandiza banja lina kuti lisamade nkhawa kuti lipeza bwanji zinthu zofunikira pa moyo?

4 Taganizirani mmene Yehova anathandizira banja lina ku Venezuela pomwe anthu a m’banjalo ankada nkhawa kwambiri kuti azipeza bwanji zofunika pa moyo. Pa nthawi ina banja la Castro linkalima mu famu yawo n’kumapeza ndalama zokwanira kugulira zinthu zofunika. Kenako gulu lina la achifwamba lomwe linali ndi mfuti, linawalanda malo n’kuwathamangitsa. Miguel, yemwe ndi bambo wa m’banjali, anafotokoza kuti: “Panopa timadalira kwambiri zomwe timalima pamalo ochepa omwe tinabwereka kwa munthu wina. Tsiku likamayamba ndimam’pempha Yehova kuti atithandize kupeza zomwe tikufunikira pa tsikulo.” Banjali likukumana ndi mavuto ambiri, koma popeza amakhulupirira kwambiri kuti Atate wawo wakumwamba aziwathandiza kupeza zimene amafunikira, iwo nthawi zonse amapezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Amaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba pa moyo wawo ndipo Yehova amawathandiza.

5 Pa mavuto osiyanasiyana omwe Miguel ndi mkazi wake Yurai akukumana nawo, iwo akhala akuganizira kwambiri mmene Yehova akuwasamalira. Nthawi zina Yehova wakhala akugwiritsa ntchito abale ndi alongo powapatsa zofunikira kapena kuthandiza Miguel kuti apeze ntchito. Nthawi zinanso Yehova wakhala akugwiritsa ntchito ofesi ya nthambi powapatsa zinthu zomwe akufunikira. Iye sanawasiye ngakhale pang’ono. Iwo aona kuti chikhulupiriro cha aliyense m’banja lawo chakhala chikulimba chifukwa cha zimenezi. Atafotokoza mmene Yehova anawathandizira pa nthawi ina, mwana wawo wina wamkazi dzina lake Yoselin, anati: “N’zolimbikitsa kuona mmene Yehova wakhala akutithandizira. Ndimaona kuti iye ndi mnzanga yemwe ndimamudalira.” Iye anawonjezera kuti: “Mayesero omwe takumana nawo ngati banja, atithandiza kukonzekera mayesero ovuta kwambiri omwe tidzakumane nawo m’tsogolo.”

6. Kodi mungalimbitse bwanji chikhulupiriro chanu mukamakumana ndi mavuto azachuma?

6 Kodi mukukumana ndi mavuto azachuma? Ngati ndi choncho, imeneyi ndi nthawi yovuta kwa inu. Komabe mungagwiritse ntchito nthawi imeneyi kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Mungapemphere kwa Yehova n’kuwerenga mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:25-34 komanso kuwaganizira kwambiri. Muziganizira zitsanzo za masiku ano zosonyeza mmene Yehova amathandizira anthu omwe amatanganidwa ndi zinthu za Ufumu. (1 Akor. 15:58) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri kuti Atate wanu wakumwamba adzakuthandizani ngati mmene anathandiziranso ena omwe anakumana ndi zomwe inu mukukumana nazo. Yehova amadziwa zomwe mumafunikira komanso mmene angakupatsireni zimenezo. Mukamaona kuti iye akukuthandizani pa moyo wanu, chikhulupiriro chanu chidzalimba kwambiri moti mudzakwanitsa kupirira mayesero aakulu omwe mudzakumane nawo m’tsogolo.​—Hab. 3:17, 18.

TIZIKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA ADZATITHANDIZA KUPIRIRA “MPHEPO YAMPHAMVU”

Chikhulupiriro cholimba chingatithandize kuti tipirire mphepo iliyonse yamphamvu, kaya ndi yeniyeni kapena yophiphiritsa (Onani ndime 7-11)

7. Mogwirizana ndi Mateyu 8:23-26, kodi “mphepo yamphamvu” inayesa bwanji chikhulupiriro cha ophunzira a Yesu?

7 Yesu ndi ophunzira ake atakumana ndi mphepo yamphamvu panyanja, iye anagwiritsa ntchito zomwe zinachitikazo powathandiza kuona mbali zimene ankafunika kulimbitsa chikhulupiriro chawo. (Werengani Mateyu 8:23-26.) Pamene mphepoyo komanso madzi zinkawomba botilo, Yesu anali akugona. Ophunzirawo omwe anali ndi mantha, atamudzutsa n’kumupempha kuti awapulumutse, iye anawadzudzula mokoma mtima kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?” Ophunzirawo ankafunika kuzindikira kuti sizinali zovuta kwa Yehova kuti ateteze Yesu komanso iwowo. Kodi pamenepa tikuphunzira chiyani? Chikhulupiriro cholimba chingatithandize kuti tipirire “mphepo yamphamvu,” kaya ndi yeniyeni kapena yophiphiritsa.

8-9. Kodi chikhulupiriro cha Anel chinayesedwa bwanji, nanga n’chiyani chinamuthandiza?

8 Taganizirani za mlongo wina wosakwatiwa wa ku Puerto Rico dzina lake Anel yemwe chikhulupiriro chake chinalimba kwambiri atakumana ndi mayesero aakulu. Vuto lomwe anakumana nalo ndi mphepo yamkuntho yomwe inawononga nyumba yake mu 2017. Komanso chifukwa cha mphepoyi, iye sanakhalenso pa ntchito. Anel anafotokoza kuti: “Pa nthawi yovutayi ndinkada nkhawa. Koma ndinaphunzira kudalira Yehova popemphera kwa iye komanso kuti ndisamalole nkhawa kundilepheretsa kuchita zinthu zofunika.”

9 Anel anafotokoza kuti kumvera kunamuthandizanso kupirira mayesero. Iye anati: “Kutsatira malangizo a gulu kunandithandiza kuti ndizichita zinthu modekha. Yehova anandithandiza pogwiritsa ntchito abale ndi alongo omwe ankandilimbikitsa mwauzimu komanso kundipatsa zinthu zomwe ndinkafunikira.” Iye anawonjezeranso kuti: “Yehova anandipatsa zinthu zochuluka kuposa zomwe ndikanapempha moti chikhulupiriro changa chinalimba kwambiri.”

10. Kodi mungatani ngati mwakumana ndi mavuto omwe ali ngati “mphepo yamphamvu”?

10 Kodi mukukumana ndi mavuto omwe ali ngati “mphepo yamphamvu” pa moyo wanu? Mwina ndi mavuto obwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe. Mwinanso ikhoza kukhala mphepo yamphamvu yophiphiritsa monga matenda aakulu omwe akuchititsani kuti mufooke moti simukudziwa zoti muchite. Nthawi zina mukhoza kumada nkhawa, koma musamalole kuti nkhawazo zikulepheretseni kudalira Yehova. Muzipemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu poganizira kwambiri mmene Yehova anakuthandizirani pa nthawi zina m’mbuyomo. (Sal. 77:11, 12) Ndipo mungakhale otsimikiza kuti iye sadzakusiyani ngakhale pang’ono, kaya panopa kapena m’tsogolo.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsimikiza mtima kuti tizimvera amene akutitsogolera?

11 Kodi n’chiyaninso china chomwe chingakuthandizeni kupirira mayesero? Monga mmene Anel anafotokozera, kumvera kungakuthandizeni. Phunzirani kukhulupirira anthu omwe Yehova ndi Yesu amawakhulupirira. Nthawi zina abale omwe amatsogolera angatipatse malangizo ooneka ngati osamveka. Komabe Yehova amadalitsa anthu omvera. Tikudziwa zimenezi chifukwa Mawu ake komanso zitsanzo za abale ndi alongo athu zimasonyeza kuti kumvera kumapulumutsa. (Eks. 14:1-4; 2 Mbiri 20:17) Muziganizira kwambiri zitsanzo zimenezi. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhale ofunitsitsa kutsatira malangizo a gulu la Yehova panopa komanso m’tsogolo. (Aheb. 13:17) Mukamatero simudzakhala ndi chifukwa choopera chimphepo chamkuntho chomwe chikubwera posachedwapa.​—Miy. 3:25.

CHIKHULUPIRIRO CHIDZATITHANDIZA KUPIRIRA ZINTHU ZOPANDA CHILUNGAMO

Tikamapemphera mochokera pansi pa mtima, chikhulupiriro chathu chidzakhala cholimba (Onani ndime 12)

12. Kodi lemba la Luka 18:1-8, limasonyeza kuti kukhala ndi chikhulupiriro n’kogwirizana bwanji ndi kupirira zinthu zopanda chilungamo?

12 Yesu ankadziwa kuti ophunzira ake adzachitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndipo zimenezi zidzayesa chikhulupiriro chawo. Pofuna kuwathandiza kupirira, iye anafotokoza fanizo lina lomwe limapezeka m’buku la Luka. Anafotokoza nkhani ya mayi wamasiye yemwe sanasiye kupempha woweruza wina wosaopa Mulungu kuti amuweruzire nkhani yake mwachilungamo. Iye sankakayikira kuti khama lake lichititsa kuti athandizidwe. Pamapeto pake woweruzayo anamuthandizadi. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova si wosalungama. Choncho Yesu ananena kuti: ‘Ndithu, kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku?’ (Werengani Luka 18:1-8.) Kenako anawonjezera kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?” Tikachitiridwa zopanda chilungamo, timafunika kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha mayi wamasiyeyu pokhala oleza mtima komanso opirira. Tikakhala ndi chikhulupiriro ngati chimenechi, sitingakayikire kuti mulimonse mmene zingakhalire Yehova adzatithandiza. Tizikhulupiriranso kuti pemphero ndi lothandiza kwambiri. Nthawi zina mapemphero athu angayankhidwe m’njira yomwe sitimayembekezera.

13. Kodi pemphero linathandiza bwanji banja lina lomwe linachitiridwa zinthu zopanda chilungamo?

13 Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Vero yemwe amakhala ku Democratic Republic of Congo. Vero, mwamuna wake yemwe si wa Mboni komanso mwana wawo wamkazi wazaka 15 anathawa kwawo pamene gulu la asilikali linabwera kudzaukira mudzi wawo. Ali pa ulendowu, iwo anafika pa lodibuloko ina pomwe asilikali anawagwira n’kuwaopseza kuti awapha. Vero atayamba kulira mwana wake ankamutonthoza popemphera mokweza akutchula mobwerezabwereza dzina la Yehova. Atamaliza kupempherako mkulu wa asilikaliwo anamufunsa kuti: “Mtsikana iwe, ndani anakuphunzitsa kupemphera?” Iye anayankha kuti: “Mayi anga ndi amene anandiphunzitsa pogwiritsa ntchito chitsanzo cha pemphero lopezeka pa Mateyu 6:9-13.” Mkulu wa asilikaliyo ananena kuti, “Mtsikana, pita mumtendere limodzi ndi makolo ako ndipo Yehova Mulungu wanu akutetezeni.”

14. Kodi n’chiyani chingayese chikhulupiriro chathu, nanga n’chiyani chingatithandize kupirira?

14 Zochitika ngati zimenezi zimatithandiza kuona kuti pemphero ndi lofunika kwambiri. Koma bwanji ngati mapemphero athu sanayankhidwe mofulumira kapena m’njira yodabwitsa kwambiri? Mofanana ndi mayi wamasiye wotchulidwa m’fanizo la Yesu uja, muzipitiriza kupemphera n’kumakhulupirira kuti Mulungu sadzakusiyani. Iye adzayankha mapemphero anu pa nthawi yoyenera komanso m’njira inayake. Muzimupemphabe Yehova kuti akupatseni mzimu wake woyera. (Afil. 4:13) Muzikumbukira kuti posachedwapa Yehova adzakudalitsani kwambiri moti mudzaiwala mavuto onse omwe munakumana nawo. Mukamakhalabe okhulupirika n’kumapirira mayesero mothandizidwa ndi Yehova, mudzalimbitsa chikhulupiriro chanu pokonzekera zomwe mukumane nazo m’tsogolo.​—1 Pet. 1:6, 7.

CHIKHULUPIRIRO CHINGATITHANDIZE KUTI MAVUTO ASATIFOOKETSE

15. Mogwirizana ndi Mateyu 17:19, 20, kodi ophunzira a Yesu anakumana ndi vuto lotani?

15 Yesu anauza ophunzira ake kuti chikhulupiriro chingawathandize kuti asafooke akakumana ndi mavuto. (Werengani Mateyu 17:19, 20.) Pa nthawi ina, iwo analephera kutulutsa chiwanda ngakhale kuti m’mbuyomo anali atakwanitsapo kuchita zimenezi. Kodi vuto linali chiyani? Yesu anafotokoza kuti iwo ankafunikira chikhulupiriro chowonjezereka. Iye anawauza kuti ngati akanakhala ndi chikhulupiriro chokwanira, akanatha kulimbana ndi mavuto aakulu ngati mapiri. Ifenso masiku ano tingathe kukumana ndi mavuto ofanana ndi amenewa.

Ngati tili ndi chisoni chachikulu, chikhulupiriro chidzatithandiza kuti tizichitabe zambiri potumikira Yehova (Onani ndime 16)

16. Kodi chikhulupiriro chinathandiza bwanji Geydi kupirira, mwamuna wake ataphedwa?

16 Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina wa ku Guatemala dzina lake Geydi. Mwamuna wake Edi anaphedwa pamene iwo ankapita kunyumba pochokera kumisonkhano. Ndiye kodi chikhulupiriro chathandiza bwanji Geydi kupirira imfa ya mwamuna wake? Iye anati: “Pemphero limandithandiza kuti ndizitulira Yehova nkhawa zanga ndipo ndimakhala ndi mtendere wamumtima. Ndimaona kuti Yehova anandisamalira pogwiritsa ntchito anthu a m’banja langa komanso a mumpingo. Kuchita zambiri potumikira Yehova kumandithandiza kuchepetsako ululu komanso kuti ndisamadere nkhawa zamawa. Mayesero omwe ndakumana nawowa andithandiza kuona kuti kaya ndidzakumana ndi zotani m’tsogolomu, ndidzakwanitsa kupirira ndi thandizo la Yehova, Yesu komanso gulu la Mulungu.”

17. Kodi tingatani ngati takumana ndi vuto langati phiri?

17 Kodi muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene mumamukonda? Yesetsani kulimbitsa chikhulupiriro chanu choti akufa adzaukitsidwa powerenga nkhani za m’Baibulo za anthu omwe anaukitsidwa. Kodi zikukupwetekani chifukwa choti wachibale wanu anachotsedwa mumpingo? Muziphunzira Mawu a Mulungu n’cholinga choti mutsimikizire kuti chilango cha Yehova chimakhala chabwino nthawi zonse. Kaya mwakumana ndi vuto lotani, muziona kuti umenewo ndi mwayi woti mulimbitse chikhulupiriro chanu. Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Musamadzipatule, m’malomwake muzichita zinthu limodzi ndi abale ndi alongo anu. (Miy. 18:1) Muzichita zinthu zomwe zingakuthandizeni kupirira ngakhale pamene mukumva kupweteka mukakumbukira zomwe zinakuchitikirani. (Sal. 126:5, 6) Musamasiye kupezeka pamisonkhano, kugwira nawo ntchito yolalikira komanso kuwerenga Baibulo. Ndiponso muziganizira kwambiri zinthu zabwino zomwe Yehova adzakupatseni m’tsogolomu. Mukamaona mmene Yehova akukuthandizirani, mudzayamba kumukhulupirira kwambiri.

“TIWONJEZERENI CHIKHULUPIRIRO”

18. Kodi mungatani ngati mwazindikira kuti chikhulupiriro chanu si cholimba kwenikweni?

18 Ngati mayesero omwe mwakumana nawo m’mbuyomu kapena panopa akusonyeza kuti chikhulupiriro chanu si cholimba kwenikweni, musataye mtima. Muziona kuti umenewo ndi mwayi woti mulimbitse chikhulupirirocho. Inunso muzipempha zomwe ophunzira a Yesu anapempha, pamene anati: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.” (Luka 17:5) Komanso muziganizira zitsanzo za anthu omwe takambirana munkhaniyi. Mofanana ndi Miguel ndi Yurai, muzikumbukira nthawi iliyonse imene Yehova anakuthandizani. Mofanana ndi mwana wa Vero komanso Anel, muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima, makamaka mukakumana ndi vuto lalikulu. Ndipo mofanana ndi Geydi, muzikumbukira kuti Yehova angakuthandizeni pogwiritsa ntchito achibale komanso anzanu. Mukamalola kuti Yehova akuthandizeni kupirira mayesero amene mukukumana nawo panopa, mungakhale otsimikiza kuti adzakuthandizaninso kupirira mayesero amene mungadzakumane nawo m’tsogolo.

19. Kodi Yesu sankakayikira chiyani, nanga inuyo mungakhale otsimikiza za chiyani?

19 Yesu anathandiza ophunzira ake kuzindikira mbali zimene ankafunika kuwonjezera chikhulupiriro chawo koma sankakayikira kuti Yehova adzawathandiza kupirira mayesero alionse omwe angadzakumane nawo m’tsogolo. (Yoh. 14:1; 16:33) Iye ankakhulupirira kuti khamu lalikulu lidzapulumuka chisautso chachikulu chifukwa cha chikhulupiriro. (Chiv. 7:9, 14) Kodi inuyo mudzakhala m’gulu la anthu opulumuka? Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, mungadzapulumuke ngati panopa mumagwiritsa ntchito mpata uliwonse womwe wapezeka kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu.​—Aheb. 10:39.

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

^ ndime 5 Tikuyembekezera mwachidwi kuti dziko loipali liwonongedwa posachedwapa. Koma mwina nthawi zina tingamakayikire ngati chikhulupiriro chathu chidzakhalebe cholimba pa nthawiyo. Munkhaniyi tikambirana zitsanzo za anthu ena komanso mfundo zomwe zingatithandize kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu panopa.