Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 44

Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?

Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?

“Kukoma mtima [kwa Yehova] kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.”​—SAL. 136:1.

NYIMBO NA. 108 Chikondi Chosatha cha Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova amatilimbikitsa kuti tizichita chiyani?

 YEHOVA amaona kuti khalidwe la kukoma mtima, kapena kuti chikondi chokhulupirika, ndi lofunika kwambiri. * (Hos. 6:6) Iye amafuna kuti atumiki ake azilionanso choncho. Kudzera mwa mneneri Mika, Mulungu wathu amatilimbikitsa kuti tizikhala ndi chikondi chokhulupirika. (Mika 6:8) Komabe choyamba tiyenera kudziwa kaye zimene khalidweli limatanthauza.

2. Kodi munthu amene ali ndi chikondi chokhulupirika amatani?

2 Kodi munthu amene ali ndi chikondi chokhulupirika amatani? Mawu akuti “chikondi chokhulupirika” amapezeka nthawi pafupifupi 230 mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso. Ndiye kodi amatanthauza chiyani? Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amakonda kwambiri munthu wina n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa iye zivute zitani. Chimenechi ndi chikondi chomwe nthawi zambiri Mulungu amasonyeza anthu. Komabe anthu amasonyezananso chikondichi. Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chokhulupirika. Munkhaniyi tikambirana mmene Yehova amasonyezera chikondichi kwa anthu. Ndipo munkhani yotsatira tidzakambirana mmene atumiki a Mulungu angamutsanzirire posonyezana khalidweli.

YEHOVA NDI “WODZAZA NDI KUKOMA MTIMA KOSATHA”

3. Kodi Yehova anadzifotokoza motani kwa Mose?

3 Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, Yehova anadziulula yekha kwa Mose pamene ankalengeza dzina lake ndi makhalidwe ake. Iye anati: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha [chikondi chokhulupirika] ndi choonadi. Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukira zolakwa ndi machimo.” (Eks. 34:6, 7) M’mawu okhudza mtima amenewa onena za makhalidwe ake, Yehova anaulula kwa Mose kanthu kena kapadera kokhudza chikondi chake chokhulupirika. Kodi iye anati chiyani?

4-5. (a) Kodi Yehova anadzifotokoza bwanji? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

4 Yehova sanangodzifotokoza kuti ali ndi chikondi chokhulupirika, iye anati ndi “wodzaza” ndi chikondi chokhulupirika. Ndipotu mawu amenewa amapezekanso m’malo ena 6 m’Baibulo. (Num. 14:18; Neh. 9:17; Sal. 86:15; 103:8; Yow. 2:13; Yona 4:2) M’malo onsewa, mawuwa amanena za Yehova yekha osati anthu. Kodi sizochititsa chidwi kuona kuti Yehova mwiniwakeyo amatsindika kwambiri za chikondi chake chokhulupirika? N’zosachita kufunsa kuti khalidweli ndi lofunika kwambiri kwa iye. * Mpake kuti Mfumu Davide anafuula kuti: “Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba . . . Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali! Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.” (Sal. 36:5, 7) Mofanana ndi Davide, kodi ifenso timayamikira chikondi chokhulupirika cha Mulungu?

5 Kuti timvetse bwino khalidwe la chikondi chokhulupirika, tiyeni tikambirane mafunso awiri awa: Kodi Yehova amasonyeza chikondichi kwa ndani? Nanga tingatani kuti tizipindula ndi chikondi chokhulupirika cha Yehova?

KODI YEHOVA AMASONYEZA KWA NDANI CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA?

6. Kodi Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa ndani?

6 Kodi Yehova amasonyeza kwa ndani chikondi chokhulupirika? Baibulo limasonyeza kuti anthufe timakonda zinthu zosiyanasiyana monga “ulimi,” “vinyo ndi mafuta,” “malangizo,” “kudziwa zinthu,” “nzeru” komanso zinthu zina. (2 Mbiri 26:10; Miy. 12:1; 21:17; 29:3) Komabe chikondi chokhulupirika chimasonyezedwa kwa anthu okha osati ku zinthu zina. Ndipo sikuti Yehova amasonyeza chikondichi kwa wina aliyense. M’malomwake amachisonyeza kwa anthu okhawo amene ali pa ubwenzi wabwino ndi iye. Mulungu wathu ndi wokhulupirika kwa anthu amene ndi mabwenzi ake. Iye wawakonzera zinthu zabwino m’tsogolo ndipo sadzasiya kuwakonda.

Yehova amachita zinthu zabwino zambiri kwa anthu onse kuphatikizaponso amene samulambira (Onani ndime 7) *

7. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi kwa anthu onse?

7 Yehova anasonyeza chikondi kwa anthu onse. Yesu anauza munthu wina dzina lake Nikodemo kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko [kapena kuti anthu] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”​—Yoh. 3:1, 16; Mat. 5:44, 45.

Mogwirizana ndi zimene Mfumu Davide komanso mneneri Danieli ananena, Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamudziwa, kumuopa, kumukonda komanso kusunga malamulo ake (Onani ndime 8-9)

8-9. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake? (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

8 Monga tanenera kale, Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu omwe ali pa ubwenzi wabwino ndi iye, omwe ndi atumiki ake. Timaona umboni wa zimenezi kuchokera pa zomwe Mfumu Davide komanso mneneri Danieli ananena. Mwachitsanzo, Davide anati: “Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani.” “Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale kwa anthu amene amamuopa.” Danieli analengeza kuti: ‘Inu Yehova Mulungu woona, anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu mumawasonyeza kukoma mtima kosatha.’ (Sal. 36:10; 103:17; Dan. 9:4) Mogwirizana ndi mawu ouziridwawa, Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake chifukwa amamudziwa, kumuopa, kumukonda komanso kusunga malamulo ake. Iye amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu okhawo amene amamulambira m’njira imene amaivomereza.

9 Tisanayambe kumutumikira, Yehova ankatisonyeza chikondi monga mmene amachitira ndi anthu ena onse. (Sal. 104:14) Komabe monga anthu amene timamulambira, iye amatisonyezanso chikondi chokhulupirika. Ndipotu amatsimikizira atumiki ake kuti: “Kukoma mtima kwanga kosatha sikudzachotsedwa kwa iwe.” (Yes. 54:10) Zimene zinachitika pa moyo wa Davide zinamuthandiza kudziwa kuti “Yehova adzapatula wokhulupirika wake.” (Sal. 4:3) Kodi tiyenera kuchita chiyani podziwa kuti Yehova amatipatula kapena kuti kutiona monga apadera? Wolemba masalimo anati: “Wanzeru ndani? Iye aona zimenezi, ndi kuchita chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 107:43) Poganizira malangizo ouziridwawa, tiyeni tikambirane njira zitatu zosonyeza mmene chikondi chokhulupirika cha Yehova chimathandizira atumiki ake.

KODI CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA CHA YEHOVA CHIMATITHANDIZA BWANJI?

Yehova amapereka madalitso owonjezereka kwa anthu amene amamulambira (Onani ndime 10-16) *

10. Kodi chikondi chokhulupirika cha Mulungu chomwe chidzakhalapobe mpaka kalekale chimatithandiza bwanji? (Salimo 31:7)

10 Chikondi chokhulupirika cha Mulungu chidzakhalapobe mpaka kalekale. Mfundo imeneyi yokhudza chikondi chokhulupirika ikupezeka maulendo 26 mu Salimo 136. Muvesi loyambirira timawerenga kuti: “Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino. Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” (Sal. 136:1) Pavesi lililonse, kuyambira vesi 2 mpaka 26 timapezapo mawu akuti, “pakuti kukoma mtima kwake kosatha [chikondi chokhulupirika] kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Tikamawerenga salimo limeneli timachita chidwi ndi njira zosiyanasiyana zimene Yehova amasonyezera chikondi chake chokhulupirika nthawi zonse. Mawu amene atchulidwa mobwerezabwereza akuti “pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale,” akutitsimikizira kuti chikondi cha Mulungu kwa anthu ake sichisintha. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova samafulumira kusiya kukonda atumiki ake. M’malomwake iye amakhala nawo pafupi ndipo sawasiya makamaka pamene akukumana ndi mavuto. Mmene timapindulira: Kudziwa kuti Yehova amapitirizabe kukhala nafe, kumatithandiza kukhala osangalala komanso kumatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira mavuto amene tikukumana nawo n’kupitirizabe kuyenda pa njira ya kumoyo.​—Werengani Salimo 31:7.

11. Mogwirizana ndi Salimo 86:5, kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azikhululuka?

11 Chikondi chokhulupirika chimamuchititsa Mulungu kuti azikhululuka. Yehova akaona kuti munthu wochimwa walapa ndipo wasintha, chikondi chokhulupirika chimamuchititsa kuti amukhululukire. Ponena za Yehova, wolemba masalimo Davide anati: “Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu, kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.” (Sal. 103:8-11) Chifukwa cha zinthu zopweteka zimene zinamuchitikira pa moyo wake, Davide ankamvetsa bwino mmene munthu amamvera akakhala kuti akuvutika ndi chikumbumtima. Koma iye anaphunzirapo kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka.” Kodi n’chiyani chimachititsa kuti Yehova azikhululuka? Yankho likupezeka pa Salimo 86:5. (Werengani.) Mogwirizana ndi mfundo ya palembali yomwe Davide anatchula m’pemphero, Yehova amakhululuka chifukwa chikondi chokhulupirika chomwe amasonyeza n’chachikulu.

12-13. Ngati tikuvutika kwambiri mumtima chifukwa cha zinthu zimene tinalakwitsa m’mbuyo, kodi n’chiyani chingatithandize?

12 Kumva chisoni chifukwa cha zoipa zimene tachita n’koyenera komanso ndi kwabwino. Kungatithandize kuti tilape n’kusiya zoipa zimene timachitazo. Komabe atumiki ena a Mulungu amadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zinthu zimene analakwitsa m’mbuyo. Iwo amaona kuti Mulungu sangawakhululukire ngakhale atalapa bwanji. Ngati inunso mukuvutika ndi maganizo oterewa, kudziwa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake kungakuthandizeni.

13 Mmene timapindulira: Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kumasangalalabe kutumikira Yehova tili ndi chikumbumtima chabwino. Zimenezi n’zotheka chifukwa “magazi a Yesu Mwana wake akutiyeretsa ku uchimo wonse.” (1 Yoh. 1:7) Ngati mwafooka chifukwa cha zinthu zina zimene munalakwitsa, muzikumbukira kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira munthu wochimwa amene walapa. Taonani zimene Davide ananena zokhudza kugwirizana kumene kulipo pakati pa chikondi chokhulupirika ndi kukhululuka. Iye anati: “Monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi, kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa. Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.” (Sal. 103:11, 12) Inde, Yehova ndi wofunitsitsa ‘kukhululuka ndi mtima wonse.’​—Yes. 55:7.

14. Kodi Davide anafotokoza kuti chikondi chokhulupirika cha Mulungu chimatiteteza bwanji?

14 Chikondi chokhulupirika cha Mulungu chimatiteteza mwauzimu. Popemphera kwa Yehova, Davide anati: “Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso. Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa. . . . Wokhulupirira Yehova amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.” (Sal. 32:7, 10) Mofanana ndi mipanda imene inkateteza mizinda kalelo, chikondi chokhulupirika cha Yehova chimatitchinga n’kumatiteteza ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye. Kuwonjezera pamenepo, chikondi chimenechi chimamuchititsa kuti atikokere kwa iye.​—Yer. 31:3.

15. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chikondi chokhulupirika cha Yehova ndi malo othawirako komanso achitetezo?

15 Davide anagwiritsa ntchito mawu abwino pofotokoza mmene Mulungu amatetezera anthu ake. Iye anati: “Mulungu ndiye malo anga okwezeka ndiponso achitetezo, Mulungu wandisonyeza kukoma mtima kosatha.” Ndipo ponena za Yehova, Davide anawonjezera kuti: “Iye amandisonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndipo ndiye malo anga achitetezo, malo anga okwezeka ndi wopereka chipulumutso, chishango changa ndi malo anga othawirako.” (Sal. 59:17; 144:2) N’chifukwa chiyani ponena za chikondi chokhulupirika cha Yehova, Davide anatchulanso za malo othawirako ndi achitetezo? Kaya timakhala kuti padzikoli, ngati tili atumiki ake, Yehova adzatipatsa zonse zimene timafunikira kuti titeteze ubwenzi wathu ndi iye. Mawu olimbikitsawa akupezekanso mu Salimo 91. Wolemba salimoli anati: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo.’” (Sal. 91:1-3, 9, 14) Nayenso Mose anatchula za malo othawirako. (Sal. 90:1) Ndipotu chakumapeto kwa moyo wake, Mose anatchulanso mfundo ina yokhazika mtima pansi. Iye analemba kuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja [ake] amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Kodi mawu akuti ‘uli m’manja ake amene adzakhalapo mpaka kalekale,’ akutiuza chiyani za Yehova?

16. Kodi anthufe tinadalitsidwa m’njira ziwiri ziti? (Salimo 136:23)

16 Yehova akakhala malo athu othawirako, timamva kuti ndife otetezeka. Komabe nthawi zina tikhoza kufooka n’kumalephera kusiya kumva choncho. Ndiye kodi Yehova angatichitire zotani pa nthawi ngati imeneyo? (Werengani Salimo 136:23.) Pang’onopang’ono, iye adzatinyamula m’manja ake n’kutithandiza kuti tikhalenso olimba. (Sal. 28:9; 94:18) Mmene timapindulira: Kudziwa kuti tingadalire Mulungu kuti azitithandiza, kumatikumbutsa kuti anthufe tinadalitsidwa m’njira ziwiri. Choyamba, tili ndi malo achitetezo othawirako posatengera kumene timakhala. Ndipo chachiwiri, Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri.

SITIKAYIKIRA KUTI YEHOVA AZITISONYEZABE CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA

17. Chifukwa chakuti Mulungu ali ndi chikondi chokhulupirika, kodi sitikayikira chiyani? (Salimo 33:18-22)

17 Monga mmene taonera, tikamakumana ndi mayesero tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzachitapo kanthu potipatsa zimene timafunikira kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa iye. (2 Akor. 4:7-9) Mneneri Yeremiya anati: “Chifukwa cha kukoma mtima kosatha kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe, ndipo chifundo chake sichidzatha.” (Maliro 3:22) Sitingakayikire kuti Yehova adzapitirizabe kutisonyeza chikondi chokhulupirika chifukwa wolemba masalimo amatitsimikizira kuti, “diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa, amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.”​—Werengani Salimo 33:18-22.

18-19. (a) Kodi nthawi zonse tiyenera kumakumbukira chiyani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Kodi tisamaiwale mfundo iti? Tisanayambe kumutumikira, Yehova ankatisonyeza chikondi monga mmene amachitira ndi anthu onse. Koma titayamba kumutumikira, iye anayambanso kutisonyeza chikondi chokhulupirika. Chifukwa cha chikondi chimenechi iye amatiika m’manja mwake n’kumatiteteza. Nthawi zonse, sadzatisiya ndipo adzakwaniritsa zinthu zabwino zonse zimene anatilonjeza. Yehova amafuna kuti tikhale anzake mpaka kalekale. (Sal. 46:1, 2, 7) Choncho kaya tikumane ndi mayesero otani, adzatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika.

19 Taona mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kwa atumiki ake. Komabe iye amayembekezera kuti ifenso tizisonyezana chikondi chokhulupirika. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Nkhani yotsatira idzayankha funso lofunikali.

NYIMBO NA. 136 Yehova “Akufupe Mokwanira”

^ ndime 5 Kodi chikondi chokhulupirika n’chiyani? Kodi Yehova amasonyeza kwa ndani chikondi chokhulupirika? Nanga anthu amene amasonyezedwa chikondichi chimawathandiza bwanji? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa ndipo nkhani imeneyi komanso yotsatira zifotokoza khalidwe lofunikali.

^ ndime 1 Dziwani kuti mawu akuti kukoma mtima kosatha omwe agwiritsidwa ntchito m’Malemba a munkhaniyi angamasuliridwenso kuti chikondi chokhulupirika.

^ ndime 4 Mfundo yakuti Mulungu ndi wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ikupezekanso m’Malemba ena.​—Onani Nehemiya 13:22; Salimo 69:13; 106:7; ndi Maliro 3:32.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yehova amasonyeza chikondi chake kwa anthu onse kuphatikizapo atumiki ake. Tizithunzi tomwe tili m’mwamba mwa chithunzi chosonyeza gulu la anthu, tikuonetsa mmene Mulungu amasonyezera chikondi. Njira yaikulu ndi kupereka mwayi wopindula ndi nsembe ya dipo.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Kuwonjezera pa chikondi chimene amasonyeza anthu onse, anthu amene amakhala atumiki ake n’kumakhulupirira nsembe ya dipo, Yehova amawasonyeza chikondi chokhulupirika. Zina mwa njira zimene amawasonyezera chikondichi, zasonyezedwa mutizithunzi ting’onoting’ono.