Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi n’zoona kuti kunali munthu wotchedwa Moredekai?

MYUDA wina dzina lake Moredekai anachita zambiri mu nkhani yofotokozedwa m’buku la m’Baibulo la Esitere. Iye anali mmodzi wa Ayuda omwe anali akapolo, yemwe ankagwira ntchito kunyumba yachifumu ku Perisiya. Panthawi imene zimenezi zinkachitika, kunali kumayambiriro kwa zaka za m’ma 400 B.C.E., “m’masiku a [Mfumu] Ahasiwero.” (Masiku ano mfumuyi imadziwika kuti Sasta Woyamba) Moredekai analepheretsa chiwembu chofuna kupha mfumu. Poyamikira zimenezi, mfumuyo inakonza zoti iye alemekezedwe anthu onse akuona. Pambuyo pa imfa ya Hamani yemwe anali mdani wa Moredekai komanso Ayuda onse, mfumu inaika Moredekai kukhala nduna yaikulu. Chifukwa cha udindowu, Moredekai anakhazikitsa lamulo lomwe linathandiza kuti Ayuda asaphedwe mu ufumu wa Perisiya.​—Esitere 1:1; 2:5, 21-23; 8:1, 2; 9:16.

Olemba mbiri ena omwe anakhalapo kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, ankanena kuti nkhani ya m’buku la Esitere ndi yongopeka ndipo kunalibe munthu wotchedwa Moredekai. Komabe mu 1941, ofukula zinthu zakale anapeza zinthu zomwe zingakhale umboni wotsimikizira kuti nkhani ya m’Baibulo ya Moredekai ndi yoona. Kodi iwo anapeza zotani?

Ofufuza anapeza dzina lakuti Marduka (m’Chichewa Moredekai) pazolembedwa za pamwala za ku Perisiya. Iye anali ndi udindo m’boma, ndipo n’kutheka kuti anali wowerengera chuma ku Susani. Arthur Ungnad, yemwe ndi katswiri wa mbiri ya Kum’mawa, ananena kuti “kupatula pa Baibulo, ndi zolemba pamwala umenewu zokha zomwe zimatchulanso za Moredekai.”

Kungochokera pamene Arthur ananena zimenezi, akatswiri akhala akumasulira zolembedwa pamiyala zambiri za ku Perisiya. Ina mwa miyalayi anaipeza m’mabwinja a nyumba yosungiramo zinthu pafupi ndi mpanda wa mzinda. Miyala imeneyi inalembedwa pa nthawi ya Sasta Woyamba. Zolembedwazi zili m’chilankhulo cha Chielami ndipo zili ndi mayina angapo opezeka m’buku la Esitere. a

Mmene dzina lakuti Moredekai (Marduka) limaonekera pa zolemba za pamiyala za ku Perisiya

Miyala ingapo imatchula za dzina la Marduka, yemwe anali mlembi kunyumba yachifumu ku Susani pa nthawi ya ulamuliro wa Sasta Woyamba. Mwala wina umanena kuti Marduka anali womasulira. Zimenezi zikugwirizana ndi zomwe Baibulo limanena zokhudza Moredekai. Iye anali munthu waudindo m’khoti la Mfumu Ahasiwero (Sasta Woyamba) ndipo ankalankhula zilankhulo zosachepera ziwiri. Nthawi zambiri Moredekai ankakhala pageti kunyumba yachifumu ku Susani. (Esitere 2:19, 21; 3:3) Pagetili panali nyumba imene munkagwira ntchito anthu audindo panyumba yachifumuyi.

Pali kufanana kochititsa chidwi pakati pa Marduka wotchulidwa pamiyalayi ndi Moredekai wotchulidwa m’Baibulo. Anakhalapo pa nthawi yofanana, pamalo ofanana ndiponso ankagwira ntchito pamaudindo ofanana. Kufanana kumeneku kukusonyeza kuti zimene ofukula zakale apeza zingakhale zikunena za Moredekai wotchulidwa m’buku la Esitere.

a Mu 1992, pulofesa wina dzina lake Edwin M. Yamauchi analemba maina 10 opezeka pamiyalayi, omwenso amapezeka m’buku la Esitere.