Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 45

Mmene Yehova Amatithandizira Kukwaniritsa Utumiki Wathu

Mmene Yehova Amatithandizira Kukwaniritsa Utumiki Wathu

Adzadziwabe kuti pakati pawo panali mneneri.”​—EZEK. 2:5.

NYIMBO NA. 67 “Lalikira Mawu”

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi tiziyembekezera chiyani, nanga tingakhale otsimikiza za chiyani?

 TIZIYEMBEKEZERA kuti tingatsutsidwe pamene tikugwira ntchito yathu yolalikira. Ndipo m’tsogolomu tikhoza kudzatsutsidwa kwambiri. (Dan. 11:44; 2 Tim. 3:12; Chiv. 16:21) Komabe tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza. N’chifukwa chiyani tikutero? Nthawi zonse Yehova wakhala akuthandiza atumiki ake kukwaniritsa utumiki womwe apatsidwa, kaya utumikiwo ukhale wovuta bwanji. Mwachitsanzo, tiyeni tione zinthu zina zomwe zinachitika pa moyo wa mneneri Ezekieli, yemwe ankalalikira kwa Ayuda omwe anali ku ukapolo ku Babulo.

2. Kodi Yehova anawafotokoza bwanji anthu a m’gawo limene Ezekieli ankalalikira, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi? (Ezekieli 2:3-6)

2 Kodi anthu a m’gawo limene Ezekieli ankalalikira anali otani? Yehova anafotokoza kuti iwo anali “a nkhope zamwano,” “amakani” ndiponso ‘opanduka.’ Iwo anali ovulaza ngati minga komanso oopsa ngati zinkhanira. Mpake kuti Yehova anauza Ezekieli mobwerezabwereza kuti: “Usaope.” (Werengani Ezekieli 2:3-6.) Ezekieli anakwanitsa kugwira ntchito yolalikira imene anapatsidwa chifukwa (1) anatumidwa ndi Yehova, (2) ankathandizidwa ndi mzimu woyera ndipo (3) ankalimbikitsidwa ndi mawu a Mulungu. Kodi zinthu zitatu zimenezi zinathandiza bwanji Ezekieli? Nanga zimatithandiza bwanji masiku ano?

EZEKIELI ANATUMIDWA NDI YEHOVA

3. Kodi ndi mawu ati omwe ayenera kuti anamulimbikitsa Ezekieli, nanga Yehova anamutsimikizira bwanji kuti amuthandiza?

3 Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndikukutumiza.” (Ezek. 2:3, 4) Mawu amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa. Chifukwa chiyani? N’zosakayikitsa kuti iye anakumbukira kuti Yehova anagwiritsanso ntchito mawu ngati omwewa pomwe ankatuma Mose ndi Yesaya monga aneneri ake. (Eks. 3:10; Yes. 6:8) Iye ankadziwanso mmene Yehova anathandizira aneneri awiriwa kulimbana ndi mavuto. Choncho pamene Yehova anamuuza kawiri kuti: “Ndikukutumiza,” mneneriyu anali ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti Yehova amuthandiza. Kuwonjezera pamenepo, m’buku la Ezekieli timapezamo kambirimbiri mawu akuti: “Yehova analankhula nane.” (Ezek. 3:16) Ndipo mobwerezabwereza iye analemba kuti, “Yehova anapitiriza kulankhula nane.” (Ezek. 6:1) Apatu Ezekieli sankakayikira kuti anatumidwa ndi Yehova. Komanso popeza anali mwana wa wansembe, bambo ake ayenera kuti anamuphunzitsa mmene Yehova nthawi zonse ankatsimikizira aneneri ake kuti awathandiza. Mwachitsanzo, Yehova anauza Isaki, Yakobo ndi Yeremiya kuti: “Ine ndili nawe.”​—Gen. 26:24; 28:15; Yer. 1:8.

4. Kodi ndi mawu olimbikitsa ati omwe anapatsa mphamvu Ezekieli?

4 Kodi Aisiraeli analandira bwanji uthenga umene Ezekieli ankalalikira? Yehova anati: “A nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvera, chifukwa iwo safuna kundimvera.” (Ezek. 3:7) Pokana kumvera Ezekieli, anthuwo ankakana Yehova. Mawu amenewa anathandiza Ezekieli kudziwa kuti kukana kumvetsera kwa anthuwo, sikunkatanthauza kuti iye walephera utumiki wake wa uneneri. Yehova anatsimikiziranso Ezekieli kuti zinthu zimene ankalalikira zikadzakwaniritsidwa, iwo “adzadziwabe kuti pakati pawo panali mneneri.” (Ezek. 2:5; 33:33) N’zosakayikitsa kuti mawu olimbikitsa amenewa anamuthandiza kukhala ndi mphamvu zoti akwaniritsire utumiki wake.

MASIKU ANONSO TIMATUMIDWA NDI YEHOVA

Mofanana ndi Ezekieli, anthu sangamvetsere uthenga wathu ndipo angamatitsutse, koma timadziwa kuti Yehova ali nafe (Onani ndime 5-6)

5. Mogwirizana ndi Yesaya 44:8, kodi timapeza bwanji mphamvu?

5 Nafenso timapeza mphamvu chifukwa choti tinatumidwa ndi Yehova. Iye amatilemekeza potitchula kuti “mboni” zake. (Yes. 43:10) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Monga mmene Yehova anauzira Ezekieli kuti: “Usaope,” Yehova akutiuzanso kuti: “Musachite mantha.” N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa anthu amene amatitsutsa? Mofanana ndi Ezekieli, tatumidwa ndi Yehova ndipo iye amatithandiza.​—Werengani Yesaya 44:8.

6. (a) Kodi Yehova amatitsimikizira bwanji kuti adzatithandiza? (b) Kodi timapeza kuti mphamvu?

6 Yehova amatitsimikizira kuti adzatithandiza. Mwachitsanzo, Yehova asananene kuti “Inu ndinu mboni zanga,” ananena kuti: “Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe. Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza. Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.” (Yes. 43:2) Tikamachita utumiki wathu, nthawi zina timakumana ndi mavuto omwe ali ngati madzi osefukira komanso mayesero omwe ali ngati moto. Ngakhale zili choncho, Yehova amatithandiza kuti tipitirizebe kulalikira. (Yes. 41:13) Mofanana ndi munthawi ya Ezekieli, anthu ambiri masiku ano amakananso uthenga wathu. Timazindikira kuti kukana kwawo kumvetsera, sizitanthauza kuti talephera kugwira bwino ntchito yathu yolalikira. Timalimbikitsidwa komanso kupeza mphamvu podziwa kuti Yehova amasangalala tikapitiriza kulengeza uthenga wake mokhulupirika. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake.” (1 Akor. 3:8; 4:1, 2) Mlongo wina yemwe wachita upainiya kwa nthawi yaitali ananena kuti: “Ndimasangalala podziwa kuti Yehova amadalitsa khama lathu.”

EZEKIELI ANATHANDIZIDWA NDI MZIMU WA MULUNGU

Ezekieli akuona masomphenya a galeta la Yehova la kumwamba zomwe zikumuthandiza kukhala wotsimikiza kuchita utumiki wake (Onani ndime 7)

7. Kodi nthawi zonse Ezekieli ankamva bwanji akaganizira masomphenya omwe anaona? (Onani chithunzi chapachikuto.)

7 Ezekieli anaona mmene mzimu wa Mulungu ulili wamphamvu. M’masomphenya, iye anaona mzimu woyera ukuthandiza angelo amphamvu komanso ukuyendetsa mawilo akuluakulu a galeta lakumwamba. (Ezek. 1:20, 21) Kodi Ezekieli anatani ataona zimenezi? Iye analemba zomwe zinachitika kuti: “Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.” Chifukwa cha mantha, Ezekieli anagwa pansi. (Ezek. 1:28) Nthawi zonse Ezekieli akaganizira masomphenya ochititsa chidwiwa ankalimbikitsidwa ndipo ankakhulupirira kuti mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, angathe kukwaniritsa utumiki wake.

8-9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Yehova atalamula Ezekieli kuti aimirire? (b) Kodi Yehova anapitiriza bwanji kupatsa mphamvu Ezekieli kuti akalalikire gawo lovuta?

8 Yehova analamula Ezekieli kuti: “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndikulankhule.” Mawu amenewa komanso mzimu wa Mulungu zinapatsa mphamvu Ezekieli zoti athe kudzuka. Iye analemba kuti: “Mzimu unalowa mwa ine ndipo unandiimiritsa.” (Ezek. 2:1, 2) Pambuyo pa zimenezi komanso pautumiki wake wonse, Ezekieli ankatsogoleredwa ndi “dzanja” la Mulungu, kapena kuti mzimu wake woyera. (Ezek. 3:22; 8:1; 33:22; 37:1; 40:1) Mzimu wa Mulungu unapatsa mphamvu Ezekieli yoti athe kugwira ntchito imene anapatsidwa, yolalikira kwa anthu a m’gawo lake omwe anali “amakani ndi osamva.” (Ezek. 3:7) Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndachititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo. Ndachititsa chipumi chako kukhala ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi. Usawaope, ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo.” (Ezek. 3:8, 9) Apa zinali ngati Yehova akuuza Ezekieli kuti ‘usafooke chifukwa cha kuuma mitima kwawo, ineyo ndikulimbitsa.’

9 Pambuyo pake mzimu wa Mulungu unatengera Ezekieli kugawo limene ankafunika kukalalikira. Iye analemba kuti: “Dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu.” Mneneriyu zinamutengera mlungu wathunthu kuti amvetse uthenga umene ankafunika kukalalikira n’cholinga choti athe kukalalikira mochokera pansi pa mtima. (Ezek. 3:14, 15) Kenako Yehova anamutsogolera kuchigwa komwe “mzimu unalowa mwa [iye].” (Ezek. 3:23, 24) Tsopano Ezekieli anali wokonzeka kuyamba utumiki wake.

MASIKU ANONSO TIMATHANDIZIDWA NDI MZIMU WA MULUNGU

Monga mmene zinalili ndi Ezekieli, kodi n’chiyani chimatithandiza kukwaniritsa utumiki wathu masiku ano? (Onani ndime 10)

10. Kodi timafunikira chiyani pogwira ntchito yathu yolalikira, nanga n’chifukwa chiyani?

10 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizigwira ntchito yathu yolalikira? Kuti tiyankhe funsoli, taganizirani zimene zinachitikira Ezekieli. Asanayambe ntchito yake yolalikira, mzimu wa Mulungu unamupatsa mphamvu zimene ankafunikira. Ifenso masiku ano tingathe kugwira ntchitoyi pokhapokha ngati tikuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa Satana ali pa nkhondo yolimbana nafe n’cholinga chofuna kutilepheretsa kugwira ntchito yolalikirayi. (Chiv. 12:17) N’kuona kwa anthu, zingaoneke ngati sitingapambane pa nkhondo yolimbana ndi Satanayi. Koma kudzera muntchitoyi, timamugonjetsa. (Chiv. 12:9-11) Motani? Tikamagwira nawo ntchitoyi timasonyeza kuti sitimaopa njira zimene Satana amagwiritsa ntchito potiopseza. Nthawi iliyonse imene talalikira timakhala kuti tagonjetsa Satana. Ndiye kodi tingati chiyani poona kuti tikupitirizabe kulalikira ngakhale adani athu amatitsutsa? Tinganene kuti mzimu woyera umatipatsa mphamvu ndipo Yehova amasangalala nafe.​—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:14.

11. Kodi mzimu woyera ungatithandize bwanji, nanga tingatani kuti tipitirizebe kuulandira?

11 Kodi tingalimbikitsidwenso bwanji podziwa kuti Yehova mophiphiritsa analimbitsa nkhope ndi chipumi cha Ezekieli? Mzimu wa Mulungu ungatipatse mphamvu kuti tithe kulimbana ndi vuto lililonse lomwe tingakumane nalo pa utumiki wathu. (2 Akor. 4:7-9) Ndiye kodi tingatani kuti nthawi zonse tizilandira mzimu wa Mulungu? Tiyenera kupemphera kwa Mulungu mosalekeza tili ndi chikhulupiriro kuti iye amva mapemphero athu. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pemphanibe, . . . Pitirizani kufunafuna, . . . Gogodanibe.” Poyankha mapempherowo, Yehova adzapereka “mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”​—Luka 11:9, 13; Mac. 1:14; 2:4.

EZEKIELI ANALIMBIKITSIDWA NDI MAWU A MULUNGU

12. Mogwirizana ndi Ezekieli 2:9–3:3, kodi mpukutu unachokera kuti, nanga munalembedwa chiyani?

12 Sikuti Ezekieli anangothandizidwa ndi mzimu woyera koma analimbikitsidwanso ndi mawu a Mulungu. M’masomphenya, iye anaona dzanja litanyamula mpukutu. (Werengani Ezekieli 2:9–3:3.) Kodi mpukutuwo unachokera kuti? Nanga munalembedwa chiyani? Kodi unalimbikitsa bwanji Ezekieli? Tiyeni tione. Mpukutuwo unachokera kumpando wa Mulungu. N’kutheka kuti Yehova anagwiritsa ntchito mmodzi mwa angelo 4 omwe anaona aja kuti amupatse mpukutuwo. (Ezek. 1:8; 10:7, 20) Mumpukutumo munali mawu a Mulungu, uthenga wachiweruzo womwe Ezekieli ankafunika kukauza Aisiraeli opanduka omwe anali ku ukapolo. (Ezek. 2:7) Uthengawo unalembedwa mbali zonse za mpukutuwo.

13. Kodi Yehova anauza Ezekieli kuti achite chiyani ndi mpukutuwo, nanga n’chifukwa chiyani unali wotsekemera?

13 Yehova anauza mneneri wakeyu kuti adye mpukutu umene anamupatsa “kuti mimba [yake] ikhute.” Ezekieli anamvera ndipo anadya mpukutu wonsewo. Kodi mbali ya masomphenya imeneyi inkatanthauza chiyani? Ezekieli ankafunika kumvetsa uthenga wonse umene ankafunika kukalengeza. Uthengawo unkafunika umufike pamtima. Kenako panachitika chinthu china chochititsa chidwi. Ezekieli anazindikira kuti mpukutuwo “unali wotsekemera ngati uchi.” (Ezek. 3:3) Chifukwa chiyani? Chifukwa kulankhula moimira Yehova kunali kokoma kapena kuti kosangalatsa kwa iye. (Sal. 19:8-11) Iye ankayamikira kuti Yehova wamuvomereza kutumikira monga mneneri wake.

14. N’chiyani chinathandiza Ezekieli kukhala wokonzeka kuvomera utumiki womwe anapatsidwa?

14 Pambuyo pake Yehova anauza Ezekieli kuti: “Usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza, ndipo umve ndi makutu ako.” (Ezek. 3:10) Pomupatsa malangizowa, iye anamuuza kuti asunge mawu a mumpukutuwo mumtima mwake komanso kuwaganizira. Kuchita zimenezi kunathandiza Ezekieli kulimbikitsa chikhulupiriro chake. Kunamuthandizanso kuti akalengeze kwa anthu uthenga wamphamvu womwe anatumidwa. (Ezek. 3:11) Kumvetsa komanso kukhulupirira uthengawo kunachititsa Ezekieli kukhala wokonzeka kuvomera utumiki womwe anapatsidwa.​—Yerekezerani ndi Salimo 19:14.

MASIKU ANONSO MAWU A MULUNGU AMATILIMBIKITSA

15. Kuti tizipirira, kodi tiyenera kusunga chiyani “mumtima” mwathu?

15 Kuti tizipirira pa utumiki wathu, timafunika kupitiriza kulimbikitsidwa ndi mawu a Mulungu. Timafunika ‘kusunga mumtima’ zonse zimene Yehova amatiuza. Masiku ano Yehova amalankhula nafe kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Kodi tingatani kuti Mawu a Mulungu azikhudza maganizo athu, mmene timamvera komanso zolinga zathu?

16. Kodi tiyenera kumachita chiyani ndi Mawu a Mulungu, nanga tingatani kuti azikhazikika mumtima mwathu?

16 Mofanana ndi chakudya chimene tikadya chimagayika n’kutipatsa mphamvu, kuphunzira ndi kuganizira mozama Mawu a Mulungu kumatipatsanso mphamvu mwauzimu. Ili ndi phunziro lomwe tiyenera kumakumbukira tikamaganizira za mpukutu. Ponena za Mawu ake, Yehova amafuna kuti ‘mimba zathu zikhute’ ndi Mawuwo, kutanthauza kuti tiyenera kumawamvetsa bwino. Tingachite zimenezo popemphera, kuwawerenga komanso kuwaganizira mozama. Choyamba timapemphera pokonzekeretsa mtima wathu kuti tilandire maganizo a Mulungu. Kenako timawerenga Baibulo n’kuima kaye kuti tiganizire mozama zimene tawerengazo. Kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani? Tikamaganizira kwambiri zimene tawerenga, m’pamenenso mtima wathu wophiphiritsa umamvetsa kwambiri Mawu a Mulungu.

17. N’chifukwa chiyani zili zofunika kumaganizira mozama zomwe tawerenga m’Baibulo?

17 N’chifukwa chiyani zili zofunika kuwerenga Baibulo komanso kuganizira mozama zomwe tawerengazo? Kuchita zimenezi kumatipatsa mphamvu zomwe timafunikira kuti tizitha kulalikira uthenga wa Ufumu panopa ndiponso kuti tidzathe kulengeza uthenga wamphamvu wachiweruzo m’tsogolo. Komanso kuganizira makhalidwe abwino amene Yehova ali nawo kumathandiza kuti ubwenzi wathu ndi iye ukhale wolimba kwambiri. Zotsatira zake n’zakuti tidzasangalala ndi chinthu china chokoma kapena kuti chosangalatsa kwambiri, chomwe ndi mtendere wamumtima ndi kukhala wokhutira.​—Sal. 119:103.

TIMALIMBIKITSIDWA KUTI TIZIPIRIRA

18. Kodi anthu a m’gawo lathu adzafunika kuzindikira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Mosiyana ndi Ezekieli, ifeyo si aneneri. Komabe ndife otsimikiza kupitirizabe kulalikira uthenga umene Yehova anachititsa kuti ulembedwe m’Mawu ake mpaka pamene adzaone kuti uthengawu walalikidwa mokwanira. Nthawi ya chiweruzo ikadzafika, anthu a m’gawo lathu sadzakhala ndi chifukwa chonenera kuti sanachenjezedwe kapenanso kuti Mulungu ankawanyalanyaza. (Ezek. 3:19; 18:23) M’malomwake, iwo adzazindikira kuti uthenga umene tinkawalalikira unali wochokera kwa Mulungu.

19. Kodi n’chiyani chimatipatsa mphamvu kuti tikwaniritse utumiki wathu?

19 Kodi n’chiyani chimatipatsa mphamvu kuti tikwaniritse utumiki wathu? Ndi zinthu zitatu zomwe zinathandizanso Ezekieli. Timapitirizabe kulalikira chifukwa timadziwa kuti tatumidwa ndi Yehova, timathandizidwa ndi mzimu wake woyera komanso timalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu. Mothandizidwa ndi Yehova, timalimbikitsidwa kupitirizabe kuchita utumiki wathu komanso kupirira “mpaka pa mapeto.”​—Mat. 24:13.

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

a Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zomwe zinathandiza mneneri Ezekieli kuti akwanitse kugwira ntchito yolalikira imene anapatsidwa. Kuona mmene Yehova anathandizira mneneri wakeyu kutithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti Yehova angatithandizenso ifeyo kuti tizikwaniritsa utumiki wathu.