Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 46

Mmene Yehova Amatithandizira Kuti Tizipirira Mosangalala

Mmene Yehova Amatithandizira Kuti Tizipirira Mosangalala

“Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo.”​—YES. 30:18.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. (a) Kodi tikambirana mafunso ati? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza?

 YEHOVA angatithandize kuti tizitha kulimbana ndi mavuto amene timakuma nawo pa moyo wathu komanso kuti tizisangalala pomutumikira. Ndiye kodi amatithandiza m’njira ziti? Nanga tingatani kuti tizipindula kwambiri ndi thandizo limene amatipatsali? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhaniyi. Komabe tisanakambirane mayankho ake, tiyeni tiganizire funso ili: Kodi Yehova ndi wofunitsitsadi kutithandiza?

2 Mawu amene mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito m’kalata yake yopita kwa Aheberi angatithandize kupeza yakho. Iye analemba kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?” (Aheb. 13:6) Buku lina lofotokoza Baibulo linanena kuti mawu akuti “mthandizi,” monga mmene agwiritsidwira ntchito palembali, amanena za munthu amene akuthamanga kuti akathandize winawake yemwe akufunika thandizo. Yerekezerani kuti mukuona Yehova akuthamangira kukapulumutsa winawake yemwe ali pamavuto. N’zosakayikitsa kuti mungavomereze kuti mafotokozedwe amenewa akusonyeza kuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhala Mthandizi wathu. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupirira mayesero aliwonse mosangalala.

3. Kodi ndi zinthu zitatu ziti zomwe Yehova amagwiritsa ntchito potithandiza kupirira mosangalala mayesero omwe timakumana nawo?

3 Kodi Yehova amatithandiza kupirira mayesero athu mosangalala m’njira ngati ziti? Kuti tipeze yankho, tiyeni tiwerenge zimene zili m’buku la Yesaya. Chifukwa chiyani? Chifukwa maulosi ambiri amene Yesaya anauziridwa kulemba amakhudzanso atumiki a Mulungu masiku ano. Kuwonjezera pamenepo, nthawi zambiri Yesaya anamufotokoza Yehova m’mawu osavuta kumvetsa. Mu Yesaya chaputala 30, muli zitsanzo zangati zimenezo. Muchaputalachi, Yesaya anafotokoza pogwiritsa ntchito mawu amene amatithandiza kuona m’maganizo mwathu mmene Yehova amathandizira anthu ake (1) pomvetsera mwatcheru ndi kuyankha mapemphero athu, (2) potipatsa malangizo, komanso (3) potipatsa madalitso panopa ndiponso m’tsogolo. Tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane zinthu zitatuzi zimene Yehova amagwiritsa ntchito potithandiza.

YEHOVA AMATIMVETSERA

4. (a) Kodi Yehova anawafotokoza bwanji Ayuda a munthawi ya Yesaya, nanga anawalola kuti akumane ndi zotani? (b) Kodi Yehova anapatsa anthu okhulupirika chiyembekezo chotani? (Yesaya 30:18, 19)

4 M’mawu oyambirira muchaputala 30, Yehova amawafotokoza Ayuda monga “ana aamuna osamva” amene amawonjezera “tchimo pa tchimo.” Iye anawonjezera kuti: “Amenewa ndi anthu opanduka, . . . amene safuna kumva malamulo a Yehova.” (Yes. 30:1, 9) Popeza kuti iwo anakana kumvera, Yesaya ananeneratu kuti Yehova adzawalola kuti akumane ndi mavuto. (Yes. 30:5, 17; Yer. 25:8-11) Iwo anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Komabe, panali Ayuda ena okhulupirika ndipo Yesaya anawauza uthenga wachiyembekezo. Anawauza kuti tsiku lina Yehova adzawakomera mtima. (Werengani Yesaya 30:18, 19.) Ndipo izi ndi zomwe zinachitikadi. Yehova anawamasula ku ukapolo. Komabe, sikuti iye anawamasula nthawi yomweyo. Mawu akuti “Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima” akusonyeza kuti panafunika kudutsa nthawi kuti Ayuda okhulupirika amasulidwe. Ndipotu Aisiraeli anakhala zaka 70 ku ukapolo ku Babulo asanamasulidwe kuti abwerere kwawo ku Yerusalemu. (Yes. 10:21; Yer. 29:10) Iwo atabwerera, chisoni chomwe anali nacho chifukwa cha ukapolo chinatha ndipo anayamba kukhala mosangalala.

5. Kodi lemba la Yesaya 30:19, limatitsimikizira chiyani?

5 Masiku ano tingalimbikitsidwe kwambiri ndi mawu awa akuti: “Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako.” (Yes. 30:19) Yesaya anatitsimikizira kuti Yehova adzamvetsera mwatcheru pamene tikupempha thandizo ndipo adzayankha mofulumira mapemphero athu. Iye anawonjezera kuti: “Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.” Mawu olimbikitsawa amatikumbutsa kuti Atate wathu ndi wofunitsitsa kuthandiza aliyense amene amapempha thandizo kwa iye. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tizipirira mosangalala.

6. Kodi mawu a Yesaya akusonyeza bwanji kuti Yehova amamvetsera pemphero la mtumiki wake aliyense payekha?

6 Kodi n’chiyaninso chimene lembali limatitsimikizira pa nkhani ya pemphero? Yehova amamvetsera mapemphero athu aliyense payekha. N’chifukwa chiyani tikutero? Mumbali yoyamba ya Yesaya chaputala 30, Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti “iwe” ponena za anthu ake monga gulu. Koma muvesi 19, mawu akuti “iwe” amasonyeza kuti uthengawo ukupita kwa munthu aliyense payekha. Yesaya analemba kuti: “Iwe sudzaliranso”; “iye adzakukomera mtima”; “iye adzakuyankha. Monga Tate wachikondi, Yehova sauza mwana wake yemwe wafooka kuti, “Ukuyenera kukhala wolimba ngati m’bale kapena mlongo wako.” M’malomwake, iye amaganizira aliyense payekha ndipo amamvetsera pemphero la aliyense mwachidwi.​—Sal. 116:1; Yes. 57:15.

Kodi Yesaya ankatanthauza chiyani pomwe anati: “Musaleke kumukumbutsa [Yehova]”? (Onani ndime 7)

7. Kodi Yesaya ndi Yesu anasonyeza bwanji kufunika kopemphera mobwerezabwereza?

7 Tikapemphera kwa Mulungu pa nkhani yomwe ikutidetsa nkhawa, chinthu choyamba chomwe Yehova angatichitire ndi kutipatsa mphamvu kuti tipirire. Ndipo ngati mayeserowo sakutha msanga monga mmene timayembekezera, tingafunike kupitiriza kumupempha kuti atipatse mphamvu zoti tipirire. Iye amatilimbikitsa kuti tizichita zimenezi. Izi zikugwirizana ndi mawu a Yesaya akuti: “Musaleke kumukumbutsa [Yehova].” (Yes. 62:7) Kodi zimenezi zimatanthauza chiyani? Tiyenera kupemphera kwa Yehova mobwerezabwereza komwe kungakhale ngati kumukumbutsa. Mawu a Yesayawa akutikumbutsa fanizo la Yesu lokhudza kupemphera lomwe limapezeka pa Luka 11:8-10, 13. Palembali Yesu anatilimbikitsa kuti tizipempha ‘mokakamira’ komanso “tizipemphabe” mzimu woyera. Tingamupemphenso Yehova kuti atitsogolere kuti tisankhe bwino zinthu.

YEHOVA AMATITSOGOLERA

8. Mu nthawi ya Ayuda, kodi lemba la Yesaya 30:20, 21 linakwaniritsidwa bwanji?

8 Werengani Yesaya 30:20, 21. Pamene asilikali a Babulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu kwa chaka ndi hafu, mavuto omwe anthu ankakumana nawo anangofika pozolowereka ngati chakudya ndi madzi. Koma mogwirizana ndi vesi 20 ndi 21, Yehova anawalonjeza Ayudawo kuti ngati atalapa komanso kusintha zochita zawo, iye adzawapulumutsa. Potchula Yehova monga ‘Mlangizi Wamkulu,’ Yesaya analonjeza anthuwo kuti Yehova adzawaphunzitsa mmene angamamulambirire movomerezeka. Mawu amenewa anakwaniritsidwa pamene Ayuda anamasulidwa ku ukapolo. Yehova anasonyeza kuti analidi Mlangizi wawo Wamkulu, ndipo malangizo omwe ankawapatsa anathandiza kuti akwanitse kubwezeretsa kulambira koona. Ifenso masiku ano tili ndi mwayi kuti Yehova ndi Mlangizi wathu Wamkulu.

9. Kodi ndi njira imodzi iti yomwe timalandirira malangizo a Yehova masiku ano?

9 Popitiriza kulankhula mwafanizo, Yesaya akutifotokoza monga ophunzira omwe akuphunzitsidwa ndi Yehova m’njira ziwiri. Choyamba Yesaya akuti: “Maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.” Mufanizoli, Mlangizi waima kutsogolo kwa ophunzira ake. Masiku ano tili ndi mwayi waukulu kuti timalandira malangizo ake. Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji? Iye amatiphunzitsa kudzera m’gulu lake. Timayamikira kwambiri chifukwa cha malangizo omveka bwino omwe amatipatsa kudzera m’gulu lakeli. Malangizo omwe timapatsidwa pamisonkhano yampingo ndi yachigawo komanso m’mabuku athu, pulogalamu ya JW Broadcasting ndi njira zina, amatithandiza kupirira mosangalala tikakumana ndi mavuto.

10. Kodi timamva bwanji “mawu kumbuyo [kwathu]”?

10 Yesaya anatchula njira yachiwiri yomwe Yehova amatiphunzitsira ponena kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako.” Apa mneneriyu anafotokoza Yehova monga mlangizi watcheru yemwe akuyenda kumbuyo kwa ophunzira ake n’kumawalozera njira patsogolo pawo komanso kuwapatsa malangizo. Masiku ano timamva mawu a Mulungu kuchokera kumbuyo kwathu. Motani? Mawu a Mulungu analembedwa m’Baibulo kalekale ife tisanabadwe, choncho tikamawawerenga zimakhala ngati tikumva mawu a Mulungu kumbuyo kwathu.​—Yes. 51:4.

11. Kuti tizipirira mosangalala, kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

11 Kodi tingatani kuti tizipindula ndi malangizo omwe Yehova amatipatsa kudzera m’gulu lake ndi m’Mawu ake? Onani kuti Yesaya anatchula zinthu ziwiri. Choyamba iye anati, “njira ndi iyi.” Chachiwiri anati, “yendani mmenemu.” (Yes. 30:21) Si zokwanira kungodziwa “njira.” Timafunikanso ‘kuyendamo.’ Kudzera m’Mawu a Yehova, monga mmene gulu lake limawafotokozera, timadziwa zomwe Mulungu amafuna kuti tizichita. Timaphunziranso mmene tingagwiritsire ntchito zomwe timaphunzirazo. Kuti tizipirira mosangalala potumikira Yehova, timafunika kuchita zinthu ziwiri zonsezi. Tikamachita zimenezo m’pamene tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa.

YEHOVA AMATIDALITSA

12. Mogwirizana ndi Yesaya 30:23-26, kodi Yehova anadalitsa bwanji anthu ake?

12 Werengani Yesaya 30:23-26. Kodi ulosiwu unakwaniritsidwa bwanji kwa Ayuda omwe anabwerera ku Isiraeli pambuyo pomasulidwa ku ukapolo ku Babulo? Yehova anawadalitsa ndi zinthu zambiri zowathandiza kuti akhale ndi moyo komanso apitirize kumutumikira. Iye anawapatsa chakudya chambiri. Koma chofunika kwambiri n’chakuti anawapatsa chakudya chochuluka chauzimu pamene kulambira koona kunkabwezeretsedwa pang’onopang’ono. Madalitso auzimu omwe anthu a Mulungu anasangalala nawo pa nthawiyo anaposa chilichonse chomwe Mulungu anali atawapatsapo m’mbuyomo. Mogwirizana ndi vesi 26, Yehova anawathandiza kumvetsa kwambiri mawu ake. (Yes. 60:2) Madalitso amene iye anapatsa atumiki ake, anawathandiza kuti azimutumikira mosangalala ndipo anapeza mphamvu “chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.”​—Yes. 65:14.

13. Kodi ulosi wokhudza kubwezeretsedwa kwa kulambira koona wakwaniritsidwa bwanji masiku ano?

13 Kodi ulosi wonena za kubwezeretsedwa kwa kulambira koona umatikhudzanso masiku ano? Inde. Motani? Kungoyambira mu 1919 C.E., anthu mamiliyoni ambiri amasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. Iwo atsogoleredwa kudziko labwino kwambiri kuposa Dziko Lolonjezedwa la Isiraeli. Dzikoli ndi paradaiso wauzimu. (Yes. 51:3; 66:8) Kodi paradaiso wauzimuyu ndi chiyani?

14. Kodi paradaiso wauzimu ndi chiyani, nanga ndi ndani ali mmenemo masiku ano? (Onani Tanthauzo la Mawu Ena.)

14 Kungoyambira mu 1919 C.E., odzozedwa akhala akusangalala kukhala m’paradaiso wauzimu. b Pamene nthawi ikupita, a “nkhosa zina” omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli alowanso m’dziko lauzimuli ndipo akusangalala ndi madalitso a Yehova ochuluka.​—Yoh. 10:16; Yes. 25:6; 65:13.

15. Kodi paradaiso wauzimu ali kuti?

15 Kodi paradaiso wauzimu ali kuti masiku ano? Atumiki a Yehova amapezeka kulikonse padzikoli. Choncho paradaiso wauzimu yemwe amakhalamo, alinso padziko lonse. Masiku ano, kaya timakhala kuti padzikoli, tingathe kukhala m’paradaiso wauzimu ngati timayesetsa kuchita zinthu zothandiza kulambira koona.

Kodi aliyense wa ife angathandize bwanji kuti paradaiso wauzimu akhale wokongola? (Onani ndime 16-17)

16. Kodi tingatani kuti tipitirize kuona kukongola kwa paradaiso wauzimu?

16 Kuti tikhalebe m’paradaiso wauzimuyu, mwa zina tiyenera kupitiriza kuyamikira kuti tili mumpingo wapadziko lonse wa Chikhristu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero poyang’ana zabwino mwa abale ndi alongo athu, osati zimene amalakwitsa. (Yoh. 17:20, 21) N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Taganizirani chitsanzo ichi: Tikamayenda malo enaake okongola, timayembekezera kuona mitengo yosiyanasiyana. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso paradaiso wauzimu amaoneka bwino chifukwa chakuti muli anthu osiyanasiyana omwe amayerekezeredwa ndi mitengo. (Yes. 44:4; 61:3) Tiyenera kumaganizira kwambiri za kukongola kwa “nkhalango” yonseyi, osati zofooka za “mitengo” imene ili pafupi nafe. Tisamalole kuti zofooka zathu kapena za ena, zichititse kuti tisamaone kukongola kwa gulu la padziko lonse la mpingo wa Chikhristu lomwe ndi logwirizana.

17. Kodi aliyense wa ife angachite chiyani kuti azilimbikitsa mgwirizano mumpingo?

17 Kodi ifeyo patokha tingatani kuti tizilimbikitsa mgwirizano mumpingo? Tizikhala anthu obweretsa mtendere. (Mat. 5:9; Aroma 12:18) Nthawi iliyonse yomwe tachita zinthu zolimbikitsa mtendere mumpingo, timawonjezera kukongola kwa paradaiso wauzimu. Timakumbukira kuti Yehova ndi amene wakokera kwa iye aliyense yemwe ali m’paradaisoyu. (Yoh. 6:44) Tangoganizani mmene Yehova amasangalalira akationa kuti tikuyesetsa kulimbikitsa mtendere ndi mgwirizano pakati pa atumiki ake, omwe amawaona kuti ndi amtengo wapatali.​—Yes. 26:3; Hag. 2:7.

18. Kodi tiyenera kumaganizira kwambiri chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Kodi tingatani kuti tizipindula mokwanira ndi madalitso omwe timalandira monga atumiki a Mulungu? Tiziganizira kwambiri zomwe timaphunzira m’Mawu a Mulungu komanso m’mabuku athu othandiza pophunzira Baibulo. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe omwe angachititse kuti ‘tizikonda abale’ komanso ‘tikhale ndi chikondi chenicheni pakati pathu.’ (Aroma 12:10) Tikamaganizira kwambiri madalitso omwe talandira panopa, timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndipo kuganizira kwambiri madalitso omwe Yehova watisungira m’tsogolomu, kungatichititse kuti tizikhulupirira kwambiri kuti tidzamutumikira mpaka kalekale. Zonsezi zingatithandize kuti tizimutumikira mosangalala panopa.

TIKHALE OTSIMIKIZA KUTI TIZIPIRIRA

19. (a) Mogwirizana ndi Yesaya 30:18, kodi tingakhale otsimikiza za chiyani? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tizipirira mosangalala?

19 Yehova “adzanyamuka” m’malo mwa ife pamene azidzawononga dziko loipali. (Yes. 30:18) Ndife otsimikiza kuti Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amaweruza mwachilungamo,” sadzalola kuti dziko lolamuliridwa ndi Satanali likhalepobe kuposa nthawi imene analiikira. (Yes. 25:9) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene tsiku lachipulumutso la Yehova lidzafike. Koma panopa ndife otsimikiza kuti tipitiriza kuona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kupemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwatsatira komanso kuganizira madalitso athu. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatithandiza kuti tizipirira mosangalala pamene tikumulambira.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

a Nkhaniyi ifotokoza zinthu zitatu zimene Yehova amachita pothandiza atumiki ake kuti azipirira mavuto mosangalala. Tiphunzira zinthu zimenezi pokambirana Yesaya chaputala 30. Kukambirana chaputalachi kutikumbutsa kufunika kopemphera kwa Yehova, kuphunzira Mawu ake komanso kuganizira mozama madalitso amene timapeza panopa ndiponso amene tidzapeze m’tsogolo.

b TANTHAUZO LA MAWU ENA: “Paradaiso wauzimu” ndi mkhalidwe wotetezeka womwe timalambiriramo Yehova mogwirizana. Mumkhalidwe umenewu, tili ndi chakudya chambiri chauzimu chomwe si chosokonezedwa ndi mabodza a chipembedzo komanso tili ndi ntchito yabwino yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo timakhala mwamtendere ndi abale ndi alongo athu, omwe amatithandiza kupirira mosangalala mavuto omwe timakumana nawo. Timalowa m’paradaiso wauzimuyi tikayamba kulambira Yehova movomerezeka komanso tikamayesetsa kumutsanzira.