Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 47

Musalole Kuti Chilichonse Chikusiyanitseni ndi Yehova

Musalole Kuti Chilichonse Chikusiyanitseni ndi Yehova

“Ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova.”​—SAL. 31:14.

NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi?

 YEHOVA amatiuza kuti timuyandikire. (Yak. 4:8) Iye amafuna kukhala Mulungu wathu, Atate wathu komanso mnzathu. Amayankha mapemphero athu komanso amatithandiza pa nthawi yovuta. Amatiphunzitsanso pogwiritsa ntchito gulu lake ndiponso amatiteteza. Koma kodi tingatani kuti tikhale naye pa ubwenzi?

2. Kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova?

2 Tingakhale pa ubwenzi ndi Yehova popemphera kwa iye komanso kuwerenga ndi kuganizira Mawu ake. Tikamachita zimenezi, timayamba kumukonda kwambiri komanso kumuyamikira. Timafunitsitsa kumumvera komanso kumutamanda monga mmene kumafunikira. (Chiv. 4:11) Tikamamudziwa kwambiri Yehova m’pamene timadaliranso kwambiri iyeyo ndi gulu limene watipatsa kuti lizitithandiza.

3. Kodi Mdyerekezi amayesa bwanji kutilekanitsa ndi Yehova, koma n’chiyani chingatithandize kuti tisasiye Mulungu wathu ndi gulu lake? (Salimo 31:13, 14)

3 Komabe Mdyerekezi amafuna kutilekanitsa ndi Yehova makamaka pamene tikukumana ndi mavuto. Kodi amachita bwanji zimenezi? Mwapang’onopang’ono, iye amafuna kutichititsa kuti tisamadalire Yehova ndi gulu lake. Komabe tingathe kupewa misampha yake. Tikamakhulupirira komanso kudalira kwambiri Yehova, sitingasiye Mulungu wathu ndi gulu lake.​—Werengani Salimo 31:13, 14.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Munkhaniyi, tikambirana mavuto atatu oyambitsidwa ndi dzikoli, omwe angachititse kuti tisamadalire kwambiri Yehova ndi gulu lake. Kodi mavutowa angatilekanitse bwanji ndi Yehova, nanga tingatani kuti mayesero a Satanawa asatisokoneze?

TIKAKUMANA NDI MAVUTO

5. Kodi mavuto omwe tikukumana nawo angachititse bwanji kuti tisamakhulupirire kwambiri Yehova ndi gulu lake?

5 Nthawi zina timakumana ndi mavuto monga kutsutsidwa ndi achibale kapena kutha kwa ntchito. Kodi mavuto amenewa angachititse bwanji kuti tilekane ndi Yehova komanso tisamakhulupirire gulu lake? Ngati tapirira vuto linalake kwa nthawi yaitali, tikhoza kufooka n’kuyamba kumaona kuti tilibe chiyembekezo. Satana amapezerapo mwayi wotichititsa kuti tizikayikira ngati Yehova amatikonda. Iye amafuna kuti tiziona kuti mavutowo akuchititsidwa ndi Yehova kapena gulu lake. Zofanana ndi zimenezi zinachitikirapo Aisiraeli ku Iguputo. Poyamba iwo ankakhulupirira kuti Yehova anatumiza Mose ndi Aroni kuti awalanditse ku ukapolo. (Eks. 4:29-31) Koma Farao atachititsa kuti mavuto awo awonjezereke, iwo anayamba kuimba mlandu Mose ndi Aroni n’kumanena kuti: “Mwatinunkhitsa pamaso pa Farao ndi atumiki ake, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.” (Eks. 5:19-21) Iwo ankaimba mlandu atumiki okhulupirika a Yehova. Zimenezitu zinali zomvetsa chisoni. Ngati mwakhala mukupirira mavuto enaake kwa nthawi yaitali, kodi mungatani kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova ndi gulu lake?

6. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Habakuku pa nkhani yopirira mavuto? (Habakuku 3:17-19)

6 Muzipemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kuti akuthandizeni. Mneneri Habakuku anakumana ndi mavuto ambiri. Pa nthawi ina, ankakayikira ngati Yehova ankamuganizira. Choncho anapemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. Iye anati: “Inu Yehova, kodi ndidzalirira thandizo koma inu osandimva kufikira liti? . . . N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa?” (Hab. 1:2, 3) Yehova anayankha pemphero la mtumiki wake wokhulupirikayu. (Hab. 2:2, 3) Ataganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ake m’mbuyomu, Habakuku anayambiranso kukhala wosangalala. Iye anatsimikiza kuti Yehova amamuganizira komanso kuti amuthandiza kupirira mayesero aliwonse. (Werengani Habakuku 3:17-19.) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukakumana ndi mavuto, muzipemphera kwa Yehova ndipo muzimuuza mmene mukumvera. Kenako muzimudalira kuti akuthandizani. Mukatero, mungakhale otsimikiza kuti Yehova akupatsani mphamvu zomwe mumafunikira kuti mupirire. Ndipo mukaona kuti wakuthandizani, mudzayamba kumukhulupirira kwambiri.

7. Kodi achibale ake a Shirley anayesetsa kumuchititsa kuti atani, nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti asasiye kukhulupirira Yehova?

7 Muzipitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira. Taganizirani mmene kuchita zimenezi kunathandizira mlongo wina wa ku Papua New Guinea dzina lake Shirley, atakumana ndi mavuto. b Banja lake linali losauka ndipo nthawi zina linkavutika kupeza chakudya chokwanira. Wachibale wina anayesetsa kumuchititsa kuti asamadalire Yehova. Wachibaleyo anati: “Umanena kuti mzimu woyera wa Mulungu ukukuthandiza, koma apa ukukuthandiza bwanji? Banja lako lidakali losaukabe. Umangotaya nthawi ndi kulalikira.” Shirley anati: “Ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amatiganiziradi kapena ayi?’ Choncho nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Yehova n’kumuuza zonse zomwe zinali mumtima mwanga. Ndinapitiriza kuwerenga Baibulo ndi mabuku athu, kulalikira komanso kupezeka pamisonkhano.” Posakhalitsa, iye anazindikira kuti Yehova ankasamalira banja lake. Iwo sanagonepo ndi njala ndipo ankasangalala. Shirley anati: “Ndinaona kuti Yehova ankayankha mapemphero anga.” (1 Tim. 6:6-8) Ngati nthawi zonse mumachita zinthu zokhudza kulambira, inunso simudzalola kuti kukayikira kapena mavuto omwe mukukumana nawo, zikulekanitseni ndi Yehova.

ABALE AUDINDO AKAMAZUNZIDWA

8. Kodi n’chiyani chingachitikire abale omwe akutsogolera m’gulu la Yehova?

8 Kudzera m’mawailesi, m’manyuzipepala komanso pa intaneti, adani athu amafalitsa nkhani zabodza zokhudza abale omwe akutsogolera m’gulu la Yehova. (Sal. 31:13) Abale ena amangidwa komanso kuimbidwa milandu ngati zigawenga. Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso Akhristu oyambirira, pamene mtumwi Paulo anaimbidwa milandu yabodza komanso kumangidwa. Ndiye kodi iwo anatani?

9. Kodi Akhristu ena anatani Paulo atamangidwa?

9 Akhristu ena anasiya kuthandiza Paulo pamene anatsekeredwa m’ndende ku Roma. (2 Tim. 1:8, 15) Chifukwa chiyani? Kodi ankachita naye manyazi chifukwa choti anthu ena ankamuona ngati chigawenga? (2 Tim. 2:8, 9) Kapena ankaopa kuti nawonso azunzidwa? Kaya anali ndi zifukwa zotani, tangoganizani mmene Paulo anamvera. Iye anali atapirira mavuto ambiri ngakhalenso kuika moyo wake pangozi chifukwa cha iwo. (Mac. 20:18-21; 2 Akor. 1:8) Tiyeni tisamakhale ngati anthu amene anamutaya Paulo pa nthawi yomwe ankafunikira thandizo lawo. Kodi tizikumbukira chiyani abale otsogolera akamazunzidwa?

10. Kodi tizikumbukira chiyani abale omwe amatsogolera akamazunzidwa, nanga n’chifukwa chiyani?

10 Muzikumbukira chifukwa chake timazunzidwa komanso yemwe amachititsa zimenezi. Lemba la 2 Timoteyo 3:12, limati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” Choncho tisamadabwe kuona kuti Satana amalimbana kwambiri ndi abale omwe akutsogolera. Cholinga chake n’kuwachititsa kuti asiye kukhala okhulupirika komanso kuti ifeyo tichite mantha.​—1 Pet. 5:8.

Ngakhale kuti Paulo anamangidwa, molimba mtima Onesiforo ankamuthandiza. Masiku anonso, abale ndi alongo amathandiza Akhristu anzawo omwe amangidwa ngati mmene tikuonera pachithunzichi (Onani ndime 11-12)

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Onesiforo? (2 Timoteyo 1:16-18)

11 Muzipitiriza kuthandiza abale anu ndipo muzikhala okhulupirika kwa iwo. (Werengani 2 Timoteyo 1:16-18.) Paulo atamangidwa, Mkhristu wina dzina lake Onesiforo anachita zinthu mosiyana ndi ena. Iye “sanachite manyazi ndi maunyolo [a Paulo].” M’malomwake, iye anamufunafuna ndipo atamupeza, anayesetsa kumuthandiza. Pochita zimenezi, Onesiforo anaika moyo wake pangozi. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Tisamalole kuti kuopa anthu kutisokoneze kapena kutilepheretse kuthandiza abale athu omwe akuzunzidwa. M’malomwake, tizichita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize. (Miy. 17:17) Iwo amafunikira chikondi chathu ndi thandizo lathu.

12. Kodi tikuphunzira chiyani kwa abale ndi alongo athu a ku Russia?

12 Taganizirani mmene abale ndi alongo athu ku Russia akuthandizira Akhristu anzawo omwe amangidwa. Ena akamaimbidwa milandu kukhoti, abale ndi alongo ambiri amapita komweko posonyeza kuti ali kumbali yawo. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Abale amene amatsogolera akamanyozedwa, kumangidwa kapena kuzunzidwa, musamachite mantha. Muziwapempherera, kusamalira anthu a m’banja lawo komanso kufunafuna njira zina zowathandizira.​—Mac. 12:5; 2 Akor. 1:10, 11.

TIKAMANYOZEDWA

13. Kodi kunyozedwa kungachititse bwanji kuti tisamadalire kwambiri Yehova ndi gulu lake?

13 Achibale komanso anzathu a kuntchito kapena kusukulu, angamatinyoze chifukwa choti timalalikira kapenanso chifukwa chotsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. (1 Pet. 4:4) Iwo angamanene kuti: “Iweyotu ndi munthu wabwino, koma chipembedzo chanu chimakhwimitsa zinthu ndiponso chimayendera mfundo zachikale.” Ena angamatidzudzule chifukwa cha mmene timachitira zinthu ndi ochotsedwa, ponena kuti: “Nde munganene bwanji kuti ndinu anthu achikondi?” Mawu ngati amenewa, angachititse kuti tiyambe kukhala ndi maganizo okayikira. Mwina tingayambe kumadzifunsa kuti: ‘Kodi n’kutheka kuti Yehova akundipanikiza? Kodi gulu lakeli limakhwimitsadi kwambiri zinthu?’ Ngati mukukumana ndi zoterezi, kodi mungatani kuti mukhalebe ogwirizana ndi Yehova ndi gulu lake?

Pamene anthu omwe ankati ndi anzake a Yobu ankamunyoza, iye anakana kukhulupirira mabodza awo. M’malomwake, anali wotsimikiza kuti akhalabe wokhulupirika kwa Yehova (Onani ndime 14)

14. Kodi tizitani ena akamatinyoza chifukwa chotsatira mfundo za Yehova? (Salimo 119:50-52)

14 Muzikhala otsimikiza kuti muzitsatirabe mfundo za Yehova. Yobu ankatsatirabe mfundo za Yehova ngakhale kuti ankanyozedwa chifukwa chochita zimenezi. M’modzi wa anthu amene ankati ndi anzake, anayesa kumuchititsa kuti aziona kuti Mulungu sizinkamukhudza kuti akutsatira mfundo zake. (Yobu 4:17, 18; 22:3) Koma Yobu sanakhulupirire mabodza amenewa. Iye ankadziwa kuti mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa n’zoyenera ndipo anali wotsimikiza kuzitsatira. Sanalole kuti ena amuchititse kukhala wosakhulupirika. (Yobu 27:5, 6) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Musamalole kuti kunyozedwa kukuchititseni kuyamba kukayikira mfundo za Yehova. Muziganizira zimene zakhala zikukuchitikirani inuyo panokha. Kodi simunadzionere nokha mobwerezabwereza kuti mfundo za Yehova ndi zoona komanso kuti zimakuthandizani? Muyenera kutsimikiza kukhalabe m’gulu limene limatsatira mfundozi. Mukatero, mudzapitirizabe kutumikira Yehova kaya anthu akunyozeni chotani.​—Werengani Salimo 119:50-52.

15. Kodi n’chifukwa chiyani Brizit ankanyozedwa?

15 Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina wa ku India, dzina lake Brizit. Iye ankanyozedwa ndi achibale ake chifukwa cha chikhulupiriro chake. Atangobatizidwa kumene mu 1997, mwamuna wake yemwe sanali wa Mboni, ntchito inamuthera. Choncho mwamunayo anaganiza kuti iye limodzi ndi banja lake azikakhala ndi makolo ake omwe ankakhala mumzinda wina. Zimenezi zinachititsa kuti Brizit akumane ndi mavuto ena aakulu. Popeza mwamuna wake sanali pa ntchito, iye ankafunika kuti azigwira ntchito masiku onse kuti azithandiza banja lawo. Kuwonjezera pamenepo, mpingo wapafupi unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 350. N’zomvetsa chisoni kuti achibale a mwamuna wake anayamba kumutsutsa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Zinthu zinafika povuta kwambiri moti banja la Brizit linasamukanso. Ndiye kenako mosayembekezereka, mwamuna wake anamwalira. Kenakonso mwana wake wamkazi anamwalira ndi khansa ali ndi zaka 12 zokha. Zinthu zinaipanso kwambiri pomwe achibale ake a Brizit anayamba kumuimba mlandu kuti ndi yemwe wachititsa zonsezo. Iwo ankanena kuti zikanakhala kuti iye si wa Mboni za Yehova, mavuto onsewo sakanachitika. Komabe, iye anapitiriza kudalira Yehova komanso kukhalabe m’gulu lake.

16. Kodi Brizit anadalitsidwa bwanji chifukwa choti sanasiye Yehova ndi gulu lake?

16 Popeza kuti Brizit ankakhala kutali ndi mpingo, woyang’anira dera anamulimbikitsa kuti azilalikira m’dera lakwawo komweko komanso azichitira misonkhano m’nyumba yake. Poyamba iye ankaona kuti zimenezi n’zovuta kwambiri komabe anatsatira malangizowo. Ankalalikira uthenga wabwino kwa ena, kuchita misonkhano m’nyumba yake komanso ankachita kulambira kwa pabanja ndi ana ake. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Brizit anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri ndipo anthu ambiri omwe ankaphunzira nawo anabatizidwa. Mu 2005, anayamba upainiya wokhazikika. Iye anadalitsidwa chifukwa chodalira Yehova komanso kukhalabe wokhulupirika ku gulu lake. Panopa ana ake akutumikira Yehova mokhulupirika ndipo tsopano m’dera lawo muli mipingo iwiri. Brizit samakayikira kuti Yehova anamupatsa mphamvu kuti athe kupirira mavuto omwe anakumana nawo komanso kunyozedwa ndi achibale ake.

PITIRIZANI KUKHALA OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA NDI GULU LAKE

17. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

17 Satana amafuna tizikhulupirira kuti Yehova amatisiya tikakumana ndi mavuto komanso kuti kukhala m’gulu lake, kumangowonjezera mavutowo. Amafunanso kuti tizichita mantha abale omwe akutsogolera gulu la Mulungu akamanyozedwa, kuzunzidwa kapenanso kuikidwa m’ndende. Ndiponso amafuna kuti kunyozedwa kutichititse kusiya kukhulupirira mfundo za Yehova ndi gulu lake. Komabe ife timadziwa bwino misampha yake yoipa ndipo sitipusitsidwa. (2 Akor. 2:11) Tiyeni titsimikize mtima kuti tizikana mabodza a Satana n’kumakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Tizikumbukira kuti Yehova sadzatisiya ngakhale pang’ono. (Sal. 28:7) Choncho tisalole chilichonse kutilekanitsa ndi Yehova.​—Aroma 8:35-39.

18. Kodi tikambirana chiyani munkhani yotsatira?

18 Munkhaniyi, takambirana mavuto ochititsidwa ndi dzikoli omwe tingakumane nawo. Koma nthawi zina mavuto amene tingakumane nawo mumpingo, angachititsenso kuti tisiye kudalira Yehova ndi gulu lake. Ndiye kodi tingatani kuti tilimbane ndi mavuto amenewa? Tikambirana zimenezi munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 118 “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”

a Kuti tizipirira mokhulupirika masiku otsiriza ano, tiyenera kupitiriza kudalira Yehova ndi gulu lake. Mdyerekezi amagwiritsa ntchito mayesero pofuna kuwononga chidaliro chimenechi. Munkhaniyi, tikambirana zinthu zitatu zimene iye amagwiritsa ntchito komanso zimene tingachite kuti asatigonjetse.

b Mayina ena asinthidwa.