Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 48

Muzikhalabe Oganiza Bwino Mukamayesedwa

Muzikhalabe Oganiza Bwino Mukamayesedwa

“Ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse.”​—2 TIM. 4:5.

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi kukhalabe oganiza bwino kumatanthauza chiyani? (2 Timoteyo 4:5)

 NTHAWI zina mavuto omwe timakumana nawo angatilepheretse kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Ndiye kodi tingatani kuti tithe kulimbana ndi mavutowa? Tiyenera kupitiriza kukhalabe oganiza bwino, kukhala maso komanso kukhala olimba m’chikhulupiriro. (Werengani 2 Timoteyo 4:5.) Timakhalabe oganiza bwino tikamakhala odekha komanso tikamaona zinthu mmene Yehova amazionera. Tikamachita zimenezi, maganizo athu sadzasokonekera chifukwa cha mmene tikumvera.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhani yapita ija, tinakambirana mavuto atatu ochititsidwa ndi dzikoli omwe tingakumane nawo. Munkhaniyi, tikambirana mavuto atatu omwe tingakumane nawo mumpingo amene angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Mavutowa ndi (1) tikamaona kuti Mkhristu mnzathu sanatichitire zinthu mwachilungamo, (2) tikapatsidwa malangizo kapena chilango komanso (3) tikamavutika kuzolowera kusintha komwe kwachitika m’gululi. Kodi tingatani kuti tipitirizebe kukhala oganiza bwino komanso tisasiye Yehova ndi gulu lake tikakumana ndi mavuto amenewa?

TIKAMAONA KUTI MKHRISTU MNZATHU SANATICHITIRE ZACHILUNGAMO

3. Kodi tingatani ngati tikuona kuti Mkhristu mnzathu watichitira zopanda chilungamo?

3 Kodi nthawi ina munaonapo kuti Mkhristu mnzanu, mwinanso yemwe ali ndi udindo, sanakuchitireni zinthu mwachilungamo? N’zodziwikiratu kuti m’baleyo sanali ndi cholinga chokukhumudwitsani. (Aroma 3:23; Yak. 3:2) Komabe mwina zomwe anachitazo zinakukwiyitsani. Mwinanso munkalephera kugona chifukwa cha nkhaniyo. N’kutheka munadzifunsa kuti, ‘Ngati m’baleyu wachita zimenezi, kodi limenelidi ndi gulu la Mulungu?’ Izitu ndi zomwe Satana amafuna tiziganiza. (2 Akor. 2:11) Maganizo olakwikawa angachititse kuti tisiye Yehova ndi gulu lake. Ndiye ngati tikuona kuti Mkhristu mnzathu watichitira zinthu zopanda chilungamo, tingatani kuti tipitirizebe kukhala oganiza bwino n’kumapewa maganizo olakwika omwe Satana amafuna kuti tikhale nawo?

4. Kodi Yosefe anatani kuti apitirizebe kukhala woganiza bwino atachitiridwa zopanda chilungamo, nanga tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake? (Genesis 50:19-21)

4 Musamasunge chakukhosi. Yosefe ali wachinyamata, azichimwene ake sanamuchitire zinthu mwachilungamo. Ankadana naye ndipo ena mpaka ankafuna kumupha. (Gen. 37:4, 18-22) Pambuyo pake, anamugulitsa ku ukapolo. Izi zinachititsa kuti Yosefe akumane ndi mayesero aakulu kwambiri kwa zaka pafupifupi 13. Yosefe akanatha kukayikira ngati Yehova ankamukondadi. Akanathanso kumaona ngati Yehova wamusiya pamene akufunikira thandizo. Koma iye sanalole kuti zimenezi zimukhumudwitse. Anapitirizabe kukhala woganiza bwino pokhala wodekha. Pamene anali ndi mpata woti akanatha kuwabwezera abale akewo, iye sanatero koma anawasonyeza chikondi komanso anawakhululukira. (Gen. 45:4, 5) Yosefe anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa ankaganiza bwino. M’malo moganizira mavuto omwe ankakumana nawo, iye ankaganizira nkhani yofunika kwambiri yokhudza cholinga cha Yehova. (Werengani Genesis 50:19-21.) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mukachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, musamakwiyire Yehova kapena kuyamba kuona kuti wakutayani. M’malomwake, muziganizira mmene akukuthandizirani kupirira mayeserowo. Kuwonjezera pamenepo, ena akakulakwirani muziphimba zolakwa zawo ndi chikondi chanu.​—1 Pet. 4:8.

5. Kodi Miqueas anatani kuti akhalebe woganiza bwino pomwe ankaona kuti wachitiridwa zopanda chilungamo?

5 Taganizirani chitsanzo cha masiku ano cha m’bale wina, yemwe ndi mkulu ku South America, dzina lake Miqueas. b Iye amakumbukira mmene anamvera pa nthawi ina, pomwe ankaona kuti abale ena audindo amuchitira zinthu mopanda chifundo. Iye anati: “Ndinali ndisanadepo nkhawa kwambiri choncho n’kale lonse. Ndinkachita mantha. Usiku sindinkagona ndipo ndinkangokhalira kulira n’kumadziona kuti ndine wachabechabe.” Koma Miqueas anapitirizabe kukhala woganiza bwino ndipo sanalole kusokonezedwa ndi mmene ankamvera. Ankapemphera pafupipafupi, kupempha Yehova kuti amupatse mzimu wake woyera ndiponso mphamvu kuti apirire. Anafufuzanso m’mabuku athu mfundo zomwe zikanamuthandiza. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngati mukuona kuti m’bale kapena mlongo wina sanakuchitireni zinthu mwachilungamo, muzikhala odekha ndipo muziyesetsa kuchotsa maganizo olakwika aliwonse omwe mungakhale nawo. N’kutheka kuti simungadziwe zomwe zinamuchititsa kulankhula kapena kuchita zimene anachitazo. Choncho muzipemphera kwa Yehova, kumupempha kuti akuthandizeni kuti muziona zinthu mmene munthu winayo akuzionera. Zimenezi zingakuthandizeni kuona kuti m’bale kapena mlongo wanuyo sanali ndi cholinga choti akuchitireni zoipa ndipo mungamukhululukire. (Miy. 19:11) Muzikumbukira kuti Yehova akudziwa zomwe zakuchitikirani ndipo adzakupatsani mphamvu zimene mukufunikira kuti mupirire.​—2 Mbiri 16:9; Mlal. 5:8.

TIKAPATSIDWA MALANGIZO KAPENA CHILANGO

6. N’chifukwa chiyani zili zofunika kuti tiziona malangizo ochokera kwa Yehova ngati njira yosonyeza kuti amatikonda? (Aheberi 12:5, 6, 11)

6 Kupatsidwa malangizo kungakhale kowawa. Tikamaganizira kwambiri ululu wake, tingayambe kuona kuti malangizowo ndi osafunika kwambiri, sitimayenera kupatsidwa kapenanso aperekedwa mopanda chifundo. Zotsatira zake zingakhale zakuti sitingamaone malangizowo ngati njira imene Yehova akutisonyezera chikondi. (Werengani Aheberi 12:5, 6, 11.) Komanso tikamalola kusokonezedwa chifukwa cha mmene tikumvera, Satana angapezerepo mwayi. Iye amafuna kuti tizikana malangizo ndipo kuposa pamenepo, amafuna kuti tisiyane ndi Yehova ndi gulu lake. Ndiye ngati mwapatsidwa malangizo, kodi mungatani kuti mukhalebe oganiza bwino?

Modzichepetsa, Petulo anavomereza malangizo omwe anapatsidwa ndipo Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri (Onani ndime 7)

7. (a) Mogwirizana ndi chithunzichi, kodi Petulo anagwiritsidwa ntchito bwanji ndi Yehova chifukwa chovomereza malangizo? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Petulo?

7 Muzivomereza malangizo ndipo muzisintha. Maulendo angapo, Yesu anadzudzula Petulo pamaso pa atumwi ena. (Maliko 8:33; Luka 22:31-34) N’kutheka kuti Petulo ankachita manyazi. Komabe iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yesu. Ankavomera malangizo ndipo ankaphunzirapo kanthu. M’kupita kwa nthawi, Yehova anadalitsa Petulo chifukwa chokhalabe wokhulupirika ndipo anamupatsa maudindo akuluakulu mumpingo. (Yoh. 21:15-17; Mac. 10:24-33; 1 Pet. 1:1) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Petulo? Tikamapewa kuganizira kwambiri kuti tachititsidwa manyazi n’kuvomera malangizo komanso kusintha, zinthu zimatiyendera bwino ifeyo komanso anthu ena. Tikatero timakhala ofunika kwambiri kwa Yehova komanso abale athu.

8-9. Kodi Bernardo anamva bwanji poyamba atapatsidwa chilango, nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe maganizo?

8 Taganizirani zomwe zinachitikira m’bale wina wa ku Mozambique, dzina lake Bernardo. Iye anachotsedwa pa udindo monga mkulu. Ndiye kodi poyamba anamva bwanji? Iye anati: “Ndinakhumudwa chifukwa sindinasangalale ndi chilango chomwe ndinapatsidwa.” Bernardo ankada nkhawa ndi mmene ena azimuonera mumpingo. Iye anavomereza kuti: “Zinanditengera miyezi ingapo kuti ndiyambirenso kuona zinthu moyenera komanso kukhulupirira Yehova ndi gulu lake.” Kodi n’chiyani chinathandiza Bernardo kuti ayambe kuona zinthu moyenera?

9 Bernardo anasintha mmene ankaganizira. Iye anafotokoza kuti: “Pa nthawi yomwe ndinali mkulu, ndinkagwiritsa ntchito lemba la Aheberi 12:7, pothandiza ena kuti aziona moyenera chilango chochokera kwa Yehova. Ndiye ndinadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi ndani amene amafunika kugwiritsa ntchito mfundo za palembali?’ Ndi atumiki onse a Yehova kuphatikizapo ineyo.” Kenako Bernardo anachita zinthu zomuthandiza kuti ayambirenso kukhulupirira Yehova ndi gulu lake. Anawonjezera zomwe ankachita pa nkhani yowerenga Baibulo komanso kuganizira kwambiri zimene wawerenga. Ngakhale kuti ankada nkhawa chifukwa cha mmene abale ndi alongo azimuonera, iye ankalalikira komanso kusonkhana nawo limodzi. Patapita nthawi, iye anaikidwanso kukhala mkulu. Ngati mofanana ndi Bernardo, nanunso mwapatsidwa chilango, musamaganizire kwambiri manyazi omwe mukumva koma muzivomereza malangizo ndiponso muzisintha. c (Miy. 8:33; 22:4) Mukamachita zimenezi, mungakhale otsimikiza kuti Yehova adzakudalitsani chifukwa chokhalabe okhulupirika kwa iye ndi gulu lake.

TIKAMAVUTIKA KUZOLOWERA KUSINTHA M’GULULI

10. Kodi ndi kusintha kotani m’gulu la Yehova komwe kunayesa kukhulupirika kwa Aisiraeli ena?

10 Kusintha kwa zinthu m’gululi kungayese kukhulupirika kwathu. Ngati sitingasamale, kusintha kotereku kungachititse kuti tisiye Yehova. Mwachitsanzo, taganizirani mmene kusintha kwa zinthu m’gulu la Yehova kunakhudzira Aisiraeli ena mu nthawi ya Mose. Chilamulo chisanakhazikitsidwe, mitu ya mabanja ndi imene inkachita zomwe ansembe ankachita. Iwo ankamanga guwa komanso kupereka nsembe kwa Yehova m’malo mwa mabanja awo. (Gen. 8:20, 21; 12:7; 26:25; 35:1, 6, 7; Yobu 1:5) Koma Chilamulo chitakhazikitsidwa, mitu ya mabanja inkafunika kusiya kuchita zimenezi. Yehova anasankha kuti anthu ochokera m’banja la Aroni ndi amene azipereka nsembe. Zinthu zitasintha choncho m’gulu la Mulungu, ngati mutu wa banja wina yemwe sanali wa m’banja la Aroni akanachita zinthu zokhudza unsembe, akanatha kuphedwa. d (Lev. 17:3-6, 8, 9) Kodi mwina ndi kusintha kumeneku komwe kunachititsa Kora, Datani, Abiramu ndi atsogoleri ena 250 kuti aukire Mose ndi Aroni? (Num. 16:1-3) Sitinganeneretu. Kaya zinthu zinali bwanji, Kora ndi anzake analephera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Kodi mungatani ngati kusintha komwe kwachitika m’gululi kwayesa kukhulupirika kwanu?

Utumiki wawo utasintha, Akohati anatumikira mofunitsitsa monga oimba, alonda a pageti kapenanso osamalira nyumba zosungiramo katundu (Onani ndime 11)

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Akohati ena?

11 Muzichita zinthu mogwirizana ndi kusintha komwe kwachitika m’gululi. Pa nthawi yomwe ankadutsa m’chipululu, Akohati anali ndi utumiki wapadera kwambiri. Nthawi iliyonse Aisiraeli akamasamuka kupita malo ena, Akohati ena ankanyamula likasa n’kumayenda patsogolo pa anthu onse. (Num. 3:29, 31; 10:33; Yos. 3:2-4) Umenewutu unali mwayi waukulu. Komabe zinthu zinasintha Aisiraeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa. Likasa silinkafunikanso kumanyamulidwa pafupipafupi. Choncho pa nthawi imene Solomo ankalamulira, Akohati ena anapatsidwa utumiki woimba, ena ankatumikira monga alonda a pageti ndipo ena ankasamalira nyumba zosungiramo zinthu. (1 Mbiri 6:31-33; 26:1, 24) Palibe paliponse pomwe pamasonyeza kuti Akohati anadandaula kapena kumafuna kupatsidwa udindo wapamwamba chifukwa choti m’mbuyomo ankachita utumiki wapadera. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Muzigwirizana ndi mtima wonse ndi kusintha kulikonse komwe kumachitika m’gulu la Yehova, ngakhale komwe kwakhudza utumiki wanu. Muzisangalala ndi utumiki uliwonse womwe mwapatsidwa. Muzikumbukira kuti utumiki wanu si umene umasonyeza kuti ndinu ofunika kwambiri. Yehova amaona kuti ndinu ofunika chifukwa choti ndinu omvera osati chifukwa chakuti muli pa utumiki winawake.​—1 Sam. 15:22.

12. Kodi Zaina anamva bwanji atauzidwa kuti asiye kutumikira pa Beteli?

12 Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina wa ku Middle East, dzina lake Zaina, yemwe utumiki wake womwe ankaukonda kwambiri unasintha. Iye anauzidwa kuti azikachita upainiya wapadera atatumikira pa Beteli kwa zaka zoposa 23. Zaina anati: “Ndinakhumudwa kwambiri utumiki wanga utasintha. Ndinkangodziona ngati wachabechabe moti ndinkangokhalira kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndinalakwitsa pati?’” N’zomvetsa chisoni kuti abale ndi alongo ena mumpingo, ankawonjezera ululu wake pomuuza kuti: “Zikanakhala kuti mumachita bwinobwino zonse, gulu silikanakutayani chonchi.” Kwa nthawi ndithu, Zaina anakhala wokhumudwa moti ankalira usiku uliwonse. Komabe iye anati: “Ndinayesetsa kuti ndisamakayikire kuti Yehova amandikonda komanso kuti ndisamakayikire gulu lake.” Kodi Zaina anatani kuti akhalebe woganiza bwino?

13. Kodi Zaina anatani kuti asiye kukhala ndi maganizo olakwika?

13 Zaina anayesetsa kuti asakhale ndi maganizo olakwika. Kodi anachita bwanji zimenezi? Anawerenga m’mabuku athu nkhani zomwe zinkakhudza kwambiri vuto lakeli. Iye anapeza nkhani yomwe inamuthandiza ya mutu wakuti, “Mungathe Kupitirizabe Polefulidwa!” mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2001. Nkhaniyi imafotokoza kuti n’kutheka kuti wolemba Baibulo Maliko ankalimbananso ndi maganizo ngati omwewa pamene utumiki wake unasintha. Zaina anati: “Chitsanzo cha Maliko chinali ngati mankhwala omwe anandithandiza kuti ndiyambirenso kumva bwino.” M’malo momadzipatula kapena kumangodzimvera chisoni, iye ankachita zinthu ndi anzake. Pamapeto pake, anaona kuti mzimu wa Yehova umagwira ntchito m’gulu lake ndipo abale otsogolera amamuganizira kwambiri. Iye anazindikiranso kuti gululi liyenera kuchita zinthu zomwe zingathandize kwambiri kuti ntchito ya Yehova ipite patsogolo.

14. Kodi Vlado anavutika kuzolowera kusintha kuti komwe kunachitika m’gulu la Yehova, nanga n’chiyani chinamuthandiza?

14 Vlado amene ndi mkulu wa zaka 73 wa ku Slovenia, ankavutika maganizo mpingo wawo utaphatikizidwa ndi mpingo wina komanso Nyumba yawo ya Ufumu itatsekedwa. Iye anati: “Sindinkamvetsa chifukwa chake Nyumba ya Ufumu yokongolayi inatsekedwa. Ndinakhumudwa chifukwa tinali titangoikonzanso kumene. Ndine kalipentala ndipo ndinathandiza kukonza nawo zinthu zina zatsopano m’nyumbayi. Komanso tinafunika kusintha zina ndi zina chifukwa cha kuphatikizidwa kwa mipingoyi, zomwe zinali zovuta kwa ofalitsa achikulirefe.” Kodi n’chiyani chinathandiza Vlado kutsatirabe malangizo omwe anaperekedwa? Iye anafotokoza kuti: “Kuchita zinthu mogwirizana ndi kusintha kumene kumachitika m’gulu la Yehova, nthawi zonse kumabweretsa madalitso. Kusintha kumeneku kukutithandiza kukonzekera kusintha kwakukulu komwe kudzachitike m’tsogolo.” Kodi inunso mukuvutika chifukwa choti mipingo yanu yaphatikizidwa kapena utumiki wanu wasintha? Dziwani kuti Yehova amamvetsa mmene mukumvera. Mukamachita zinthu mogwirizana ndi kusinthako komanso kupitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake limene akuligwiritsa ntchito, mudzadalitsidwa kwambiri.​—Sal. 18:25.

MUZIKHALABE OGANIZA BWINO PA ZINTHU ZONSE

15. Kodi tingatani kuti tikhalebe oganiza bwino tikakumana ndi mavuto mumpingo?

15 Pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli, tiziyembekezera kuti tingakumane ndi mavuto mumpingo. Mavuto amenewa angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Choncho tiyenera kukhalabe oganiza bwino. Ngati Mkhristu mnzanu wakuchitirani zinthu zopanda chilungamo, muzipewa kukwiya. Mukapatsidwa malangizo kapena chilango musamaganizire kwambiri zoti muchita manyazi. Muzingomvera malangizowo ndipo muzisintha. Ngati kusintha komwe kwachitika m’gululi kwakukhudzani, muzivomereza ndi mtima wonse ndipo muzitsatira malangizo omwe aperekedwa.

16. Kodi mungatani kuti musasiye kukhulupirira Yehova ndi gulu lake?

16 Ngati kukhulupirika kwanu kwayesedwa, mungathebe kupitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake. Koma kuti mukwanitse kuchita zimenezi, muyenera kukhalabe oganiza bwino, zomwe zikutanthauza kukhala odekha, kuona zinthu moyenera komanso kumaziona mmene Yehova amaonera. Khalani otsimikiza kuti muziphunzira za anthu otchulidwa m’Baibulo omwe anapirira mavuto ofanana ndi anu ndipo muziganizira chitsanzo chawo. Muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni ndipo musamasiye kuchita zinthu ndi mpingo. Ndiye kaya mukumana ndi zotani, Satana sadzatha kukulekanitsani ndi Yehova kapena gulu lake.​—Yak. 4:7.

NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu

a Kukhulupirika kwathu kwa Yehova ndi gulu lake kungayesedwe makamaka tikamakumana ndi mavuto mumpingo. Nkhaniyi ifotokoza atatu mwa mavutowa komanso zimene tingachite kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake.

b Mayina ena asinthidwa.

c Mungapeze mfundo zina zothandiza munkhani yakuti, “Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2009, tsamba 30.

d Chilamulo chinkanena kuti mutu wa banja yemwe akufuna kuti aphe nyama yoti adye, azitengera nyamayo kuchihema, kupatulapo ngati akukhala kutali ndi chihemacho.​—Deut. 12:21.