Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 47

NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso

Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mkulu?

Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mkulu?

“Ngati munthu akuyesetsa kuti akhale woyangʼanira, akufuna ntchito yabwino.”​—1 TIM. 3:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi, tikambirana ena mwa makhalidwe amene munthu amafunika kukhala nawo kuti ayenerere kukhala mkulu.

1-2. Kodi “ntchito yabwino” imene akulu amagwira imaphatikizapo chiyani?

 NGATI mwakhala mukutumikira ngati mtumiki wothandiza kwa kanthawi, muyenera kuti mwayesetsa kukhala ndi makhalidwe ambiri omwe amafunika kuti munthu akhale mkulu. Kodi mungayesetse kuti mugwire nawo “ntchito yabwino” yotumikira abale ndi alongo anu monga mkulu?​—1 Tim. 3:1.

2 Kodi akulu amagwira ntchito zotani? Amatsogolera pa ntchito yolalikira, amachita khama kuphunzitsa ndi kuchita maulendo aubusa komanso amalimbikitsa mpingo ndi mawu ndiponso zochita zawo. N’chifukwa chake Baibulo limatchula amuna akhamawa kuti ndi “mphatso.”​—Aef. 4:8.

3. Kodi m’bale angatani kuti akhale mkulu? (1 Timoteyo 3:1-7; Tito 1:5-9)

3 Kodi m’bale angatani kuti akhale mkulu? Zimene zimafunika kuti munthu akhale mkulu n‘zosiyana kwambiri ndi zimene zimafunika kuti munthu apeze ntchito yolembedwa. M’dzikoli munthu amatha kulembedwa ntchito bola ngati ali ndi luso la ntchitoyo. Mosiyana ndi zimenezi, kuti mukhale mkulu pamafunika zambiri, osati kungokhala ndi luso lophunzitsa kapena kulalikira. Mumafunika kukhala ndi makhalidwe omwe afotokozedwa pa 1 Timoteyo 3:1-7 ndi Tito 1:5-9. (Werengani.) Munkhaniyi tikambirana mfundo zikuluzikulu zitatu zomwe zimafunika kuti munthu akhale mkulu. Mfundo zake ndi kukhala ndi mbiri yabwino kwa anthu onse, a mumpingo kapena ayi, kupereka chitsanzo chabwino monga mutu wabanja komanso kukhala wofunitsitsa kutumikira mumpingo.

KUKHALA NDI MBIRI YABWINO

4. Kodi ‘kukhala opanda chifukwa chotinenezera’ kumatanthauza chiyani?

4 Kuti munthu akhale mkulu, ayenera “kukhala wopanda chifukwa chomunenezera,” zomwe zikutanthauza kukhala ndi mbiri yabwino mumpingo. Kuwonjezera apo, ayenera kukhalanso ndi “mbiri yabwino kwa osakhulupirira.” Anthu osakhulupirira akhoza kumanyoza zimene mumakhulupirira koma sayenera kukayikira ngati muli woona mtima kapena wakhalidwe labwino. (Dan. 6:4, 5) Ndiye muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndili ndi mbiri yabwino kwa anthu a mumpingo komanso osakhulupirira?’

5. Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu munthu “wokonda zabwino”?

5 Munthu “wokonda zabwino,” amaona zabwino mwa ena komanso kuwayamikira chifukwa cha makhalidwe awo. Amasangalala kuchitira ena zabwino, ngakhale zoposa zimene anthu amayembekezera. (1 Ates. 2:8) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kukhala ndi khalidwe limeneli? Chifukwa chakuti nthawi zambiri amafunika kuchita maulendo aubusa komanso kusamalira abale ndi alongo awo mumpingo. (1 Pet. 5:1-3) Ngakhale kuti imeneyi ndi ntchito yaikulu, iwo amasangalala kutumikira komanso kuthandiza ena.​—Mac. 20:35.

6. Kodi tingasonyeze kuti ndife ‘ochereza’ m’njira ziti? (Aheberi 13:2, 16; onaninso chithunzi.)

6 Mungasonyeze kuti ndinu “wochereza” mukamachitira zabwino anthu ena, kuphatikizapo amene si anzanu apamtima. (1 Pet. 4:9) Pofotokoza za munthu wochereza, buku lina linanena kuti: “Chitseko cha nyumba yake komanso cha mtima wake, chimakhala chotsegula ngakhale kwa anthu osawadziwa.” Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mbiri yanga pa nkhani yolandira alendo ndi yotani?’ (Werengani Aheberi 13:2, 16.) Munthu wochereza amagawana zimene ali nazo ndi alendo kuphatikizapo osauka komanso anthu amene amatumikira Yehova mwakhama monga oyang’anira madera ndiponso amene abwera kudzakamba nkhani kuchokera kumipingo ina.​—Gen. 18:2-8; Miy. 3:27; Luka 14:13, 14; Mac. 16:15; Aroma 12:13.

Banja la Chikhristu likulandira bwino woyang’anira dera ndi mkazi wake (Onani ndime 6)


7. Kodi mkulu angasonyeze bwanji kuti si “wokonda ndalama?”

7 Asakhale wokonda ndalama.’ Zimenezi zikutanthauza kuti saika maganizo ake onse pa chuma. Kaya ndi wolemera kapena wosauka, amayesetsa kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba pa moyo wake. (Mat. 6:33) Amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zake potumikira Yehova, kusamalira banja lake komanso kutumikira mpingo. (Mat. 6:24; 1 Yoh. 2:15-17) Mungadzifunse kuti, ‘Kodi maganizo anga ndi otani pa nkhani ya ndalama? Kodi ndimakhala wokhutira ndi zinthu zofunika, kapena ndimangoganizira zopeza chuma ndi ndalama zambiri?’​—1 Tim. 6:6, 17-19.

8. Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu “wosachita zinthu mopitirira malire” komanso “wodziletsa”?

8 Ngati ndinu munthu “wosachita zinthu mopitirira malire” komanso “wodziletsa,” mumadziikira malire pa zonse zimene mumachita pa moyo wanu. Simuchita zinthu mopitirira malire pa nkhani ya kudya, kumwa, kuvala ndi kudzikongoletsa komanso zosangalatsa. Simutengera moyo wa anthu a m’dzikoli. (Luka 21:34; Yak. 4:4) Mumakhala wodekha ngakhale pamene ena akuputani. Simumwa “mowa mwauchidakwa” komanso anthu ena sakudziwani monga munthu amene amamwa kwambiri mowa. Mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndimasonyeza kuti ndine munthu wosachita zinthu mopitirira malire komanso wodziletsa?’

9. Kodi munthu “woganiza bwino” komanso ‘wadongosolo’ amatani?

9 Ngati ndinu munthu “woganiza bwino,” mumasankha zochita pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Mumaganizira mozama mfundozi, ndipo zimenezi zimakuthandizani kuti mukhale wanzeru komanso womvetsa zinthu. Simusankha zinthu mopupuluma. M’malomwake mumaonetsetsa kuti mwadziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. (Miy. 18:13) Izi zimakuthandizani kusankha zinthu mogwirizana ndi maganizo a Yehova. Munthu “wochita zinthu mwadongosolo” amachita zinthu moyenera komanso pa nthawi yake. Amakhala wodalirika ndipo amatsatira malangizo. Makhalidwe amenewa angathandize kuti mukhale ndi mbiri yabwino. Tiyeni tikambirane makhalidwe amene Baibulo limanena kuti mkulu ayenera kukhala nawo kuti azisonyeza chitsanzo chabwino monga mutu wa banja.

KUKHALA MUTU WA BANJA WABWINO

10. Kodi mwamuna amene ‘amayang’anira bwino banja lake’ amatani?

10 Ngati muli ndi banja ndipo mukufuna kukhala mkulu, banja lanu liyeneranso kupereka chitsanzo chabwino. Choncho muyenera kukhala “mwamuna woyang’anira bwino banja lake.” Muyenera kukhala ndi mbiri yakuti mumakonda komanso kusamalira bwino banja lanu. Mwachitsanzo, muyenera kutsogolera pa zinthu zonse zokhudza kulambira. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ngati munthu sadziwa kuyangʼanira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?”​—1 Tim. 3:5.

11-12. Ngati munthu akufuna kukhala mkulu, kodi banja lake liyenera kukhala lotani? (Onaninso chithunzi.)

11 Ngati ndinu bambo, muyenera kukhala ‘woti ana anu amakumverani ndi mtima wonse.’ Muyenera kuwaphunzitsa mwachikondi. N’zoona kuti mofanana ndi ana onse, iwo azikonda kuseka kapena kusewera. Koma chifukwa chakuti mumawaphunzitsa bwino, iwo angakhale omvera, aulemu ndiponso a khalidwe labwino. Komanso muzichita zimene mungathe pothandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, azitsatira mfundo za m’Baibulo ndiponso aziyesetsa kuti abatizidwe.

12 Ayenera kukhala ndi “ana okhulupirira ndiponso osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.” Ngati mwana wa m’bale wachita tchimo lalikulu, kodi zimenezi zingakhudze bwanji bambo ake? Ngati bamboyo sankaphunzitsa kapena kulangiza mwanayo ndiye kuti sangayenerere kukhala mkulu.​—Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1996, tsamba 21, ndime 6-7.

Mitu ya mabanja imaphunzitsa ana awo mmene angagwirire ntchito zosiyanasiyana potumikira Yehova komanso kuthandiza abale ndi alongo awo (Onani ndime 11)


KUSAMALIRA MPINGO

13. Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu “wololera” komanso ‘wosamva zake zokha’?

13 Abale amene amasonyeza makhalidwe abwino amathandiza kwambiri mumpingo. Munthu “wololera” amalimbikitsa mtendere. Kuti mukhale ololera, muyenera kumamvetsera ena komanso kukhala okonzeka kuyendera maganizo awo. Ngati muli pa zokambirana, kodi mumakhala wokonzeka kuyendera mfundo zimene ambiri akuona kuti n’zoyenera ngati sizikuphwanya mfundo za m’Baibulo? Mawu akuti “asakhale womva zake zokha,” akutanthauza kuti munthu sakakamira kuti anthu ena azichita zimene iyeyo akuona kuti n’zoyenera. Amazindikira ubwino wokhala ndi alangizi ambiri. (Gen. 13:8, 9; Miy. 15:22) Sayeneranso kukhala “wokonda kukangana” kapena “wa mtima wapachala.” M’malo mokhala wankhanza kapena wokonda kukangana, ayenera kukhala wofatsa komanso wochita zinthu mosamala. Munthu wokonda mtendere amayamba ndi iyeyo kuchita zinthu mwamtendere ngakhale zinthu zitavuta kwambiri. (Yak. 3:17, 18) Mukamalankhula mokoma mtima, mukhoza kufewetsa mitima ya anthu ena ngakhalenso otsutsa.​—Ower. 8:1-3; Miy. 20:3; 25:15; Mat. 5:23, 24.

14. Kodi mawu akuti “asakhale woti wangobatizidwa kumene” ndiponso “wokhulupirika” amatanthauza chiyani?

14 Kuti m’bale akhale mkulu, “asakhale woti wangobatizidwa kumene.” Ngakhale kuti sizidalira kuti munthu akhale woti anabatizidwa zaka zambiri m’mbuyomo, pamafunika nthawi ndithu kuti akule mwauzimu. Mofanana ndi Yesu, muyenera kukhala wodzichepetsa komanso kukhala wokonzeka kugwira ntchito iliyonse imene Yehova angakupatseni. (Mat. 20:23; Afil. 2:5-8) Mungasonyeze kuti ndinu “wokhulupirika” potsatira mfundo zolungama za Yehova komanso malangizo amene gulu limatipatsa.​—1 Tim. 4:15.

15. Kodi mkulu ayenera kukhala waluso kwambiri pophunzitsa? Fotokozani.

15 Malemba amanena momveka bwino kuti woyang’anira ayenera kukhala “wodziwa kuphunzitsa.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kukhala waluso kwambiri pokamba nkhani? Ayi. Akulu ambiri oyenerera, si aluso kwambiri pophunzitsa. Komabe amaphunzitsa mogwira mtima mu utumiki ndi pa maulendo aubusa. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:28, 29 komanso Aefeso 4:11.) Ngakhale zili choncho, muyenera kuyesetsa kuti mukhale ndi luso lophunzitsa. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

16. Kodi mungatani kuti mukhale mphunzitsi waluso? (Onaninso chithunzi.)

16 “Wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika.” Kuti mukhale mphunzitsi wogwira mtima, muyenera kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa komanso kupereka malangizo. Muyenera kuphunzira mwakhama Baibulo komanso mabuku athu. (Miy. 15:28; 16:23) Mukamaphunzira, muziona mmene mabuku athu akufotokozera Malemba n’cholinga choti muziwagwiritsa ntchito m’njira yoyenera. Ndipo mukamaphunzitsa muziyesetsa kuwafika pamtima anthu. Mukhoza kuwonjezera luso lanu lophunzitsa mukamapempha malangizo kwa akulu amene ali ndi luso. (1 Tim. 5:17) Akulu ayenera kukhala oti angathe “kulimbikitsa” abale ndi alongo awo ndiponso “kudzudzula” pakafunika kutero. Koma pochita zinthu zonsezi, nthawi zonse akuluwo ayenera kukhala okoma mtima. Mukakhala odekha komanso achikondi, n’kumaphunzitsa pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, mudzakhala mphunzitsi waluso chifukwa muzitsanzira Yesu yemwe ndi Mphunzitsi Waluso.​—Mat. 11:28-30; 2 Tim. 2:24.

Mtumiki wothandiza ali ndi mkulu waluso ndipo akuona mmene angagwiritsire ntchito Baibulo pophunzitsa. Mtumiki wothandizayo akuyeserera nkhani yake uku akudziyang’ana pagalasi (Onani ndime 16)


PITIRIZANI KUYESETSA KUTI MUKHALE MKULU

17. (a) Kodi n’chiyani chingathandize mtumiki wothandiza pamene akuyesetsa kuti akhale mkulu? (b) Kodi akulu ayenera kukumbukira chiyani akamaganizira m’bale woti akhale mkulu? (Onani bokosi lakuti, “ Muzikhala Odzichepetsa Mukamaona Ngati M’bale Akuyenera Kukhala Mkulu.”)

17 Pambuyo poona makhalidwe ofunika kuti munthu akhale mkulu, atumiki othandiza ena akhoza kumaona kuti sangakwanitse kukhala mkulu. Koma kumbukirani kuti Yehova komanso gulu lake, sayembekezera kuti muzisonyeza makhalidwewa popanda kulakwitsa chilichonse. (1 Pet. 2:21) Ndipo mzimu wa Yehova, womwe ndi wamphamvu, ndi umene ungakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwewa. (Afil. 2:13) Kodi pali khalidwe linalake lomwe mukufuna kuti muzilisonyeza kwambiri? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Muziphunzira zambiri zokhudza khalidwelo ndiponso kufunsa akulu ena kuti azikuthandizani.

18. Kodi atumiki othandiza onse akulimbikitsidwa kuchita chiyani?

18 Tiyeni tonse, kuphatikizapo akulu, tipitirize kusonyeza makhalidwe amene takambirana munkhaniyi. (Afil. 3:16) Ngati ndinu mtumiki wothandiza, yesetsani kuti mukhale mkulu. Muzipempha Yehova kuti akuphunzitseni n’cholinga choti muzichita zambiri pomutumikira komanso kutumikira abale ndi alongo anu. (Yes. 64:8) Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukhale mkulu.

NYIMBO NA. 101 Tizichita Zinthu Mogwirizana