Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 45

NYIMBO NA. 138 Imvi Ndi Chisoti cha Ulemerero

Zimene Tikuphunzira pa Mawu Omaliza a Amuna Okhulupirika

Zimene Tikuphunzira pa Mawu Omaliza a Amuna Okhulupirika

“Kodi si paja okalamba amakhala ndi nzeru, ndipo amene akhala moyo wautali si paja amamvetsa zinthu?”​—YOBU 12:12.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Kumvera Yehova Mulungu kumatithandiza kuti tipeze madalitso panopa komanso tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira zinthu kuchokera kwa achikulire?

 TONSEFE timafunikira malangizo kuti tizisankha zochita mwanzeru. Tingapeze malangizowa kwa akulu komanso Akhristu olimba mwauzimu. Ngati otipatsa malangizowo ali achikulire, tisamafulumire kuganiza kuti malangizo awo ndi achikale. Yehova amafuna kuti tiziphunzira zinthu kuchokera kwa achikulirewo. Iwo akhala ndi moyo kwa nthawi yaitali kuposa ife, zomwe zachititsa kuti adziwe zinthu zambiri, azimvetsa zinthu komanso akhale ndi nzeru.​—Yobu 12:12.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Kale, Yehova ankagwiritsa ntchito achikulire okhulupirika pofuna kulimbikitsa komanso kutsogolera anthu ake. Mwachitsanzo, iye anagwiritsa ntchito anthu ngati Mose, Davide komanso mtumwi Yohane. Iwo anakhala ndi moyo pa nthawi zosiyanasiyana ndipo zochitika pa moyo wawo zinalinso zosiyana kwambiri. Pamene moyo wawo unkapita kumapeto, iwo anapereka malangizo anzeru kwa achinyamata. Aliyense wa amuna okhulupirikawa anatsindika kufunika komvera Mulungu. Yehova anachititsa kuti mawu awo anzeru alembedwe n’cholinga choti azitithandiza masiku ano. Kaya ndife achinyamata kaya achikulire, kuphunzira malangizo a amuna amenewa kungatithandize. (Aroma 15:4; 2 Tim. 3:16) Munkhaniyi tikambirana mawu omaliza a amuna atatuwa komanso zimene tingaphunzirepo.

“MUDZAKHALA NDI MOYO KWA NTHAWI YAITALI”

3. Kodi Mose anachita zinthu ziti potumikira Mulungu?

3 Mose anatumikira Yehova modzipereka kwa moyo wake wonse. Iye anali mneneri, woweruza, mtsogoleri komanso wolemba mbiri. Mose ankadziwa zinthu zambiri. Iye anatsogolera Aisiraeli kuchoka ku ukapolo ku Iguputo ndipo anaona Yehova akuchita zinthu zambiri zodabwitsa. Yehova anamugwiritsa ntchito kuti alembe mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo, Salimo 90, komanso mwina Salimo 91. Zikuonekanso kuti iye ndi amene analemba buku la Yobu.

4. Kodi Mose analimbikitsa ndani, nanga n’chifukwa chiyani?

4 Atatsala pang’ono kufa, ali ndi zaka 120, Mose anasonkhanitsa Aisiraeli onse n’kuwakumbutsa zimene anaona Yehova akuwachitira. Ena mwa Aisiraeliwa ali achinyamata, anaona zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Yehova anachita ndiponso mmene anaweruzira Aiguputo. (Eks. 7:3, 4) Iwo anayenda pa Nyanja Yofiira madzi atagawikana ndipo anaona Yehova akuwononga magulu ankhondo a Farao. (Eks. 14:29-31) Yehova anawateteza komanso kuwasamalira m’chipululu. (Deut. 8:3, 4) Ndiyeno atsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anaona kuti uwu unali mwayi wake womaliza kuti awalimbikitse. a

5. Kodi mawu omaliza a Mose a pa Deuteronomo 30:19, 20 anatsimikizira chiyani Aisiraeli?

5 Kodi Mose ananena kuti chiyani? (Werengani Deuteronomo 30:19, 20.) Iye anakumbutsa Aisiraeli kuti tsogolo lawo linali labwino kwambiri. Yehova akanawadalitsa kuti akhale kwa nthawi yaitali m’dziko limene anawalonjeza. Dzikolo linali lokongola kwambiri komanso lachonde. Ponena za dziko limenelo, Mose ananena kuti: “[Ndi] dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu, yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu.”​—Deut. 6:10, 11.

6. N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti anthu a mitundu ina agonjetse Aisiraeli?

6 Mose anachenjezanso Aisiraeli kuti iwo ankafunika kumvera malamulo a Yehova n’cholinga choti apitirizebe kukhala m’dziko lokongolalo. Mose analimbikitsa Aisiraeli kuti ‘asankhe moyo’ pomvera Yehova komanso ‘pokhala okhulupirika kwa iye.’ Koma Aisiraeli anakana kumvera Yehova. Choncho patapita nthawi, Mulungu analola kuti Asuri komanso pambuyo pake Ababulo awagonjetse n’kupita nawo ku ukapolo.​—2 Maf. 17:6-8, 13, 14; 2 Mbiri 36:15-17, 20.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Mose? (Onaninso chithunzi.)

7 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kumvera kumapulumutsa moyo. Mofanana ndi Aisiraeli omwe anali atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, ifenso tatsala pang’ono kulowa m’dziko limene Mulungu analonjeza. Posachedwapa tiona iye akusintha dzikoli kukhala Paradaiso. (Yes. 35:1; Luka 23:43) Satana ndi ziwanda zake adzachotsedwa. (Chiv. 20:2, 3) Zipembedzo zabodza sizidzasocheretsanso anthu. (Chiv. 17:16) Sipadzapezekanso maboma opondereza anthu. (Chiv. 19:19, 20) M’paradaiso simudzapezekanso anthu oukira. (Sal. 37:10, 11) Kulikonse anthu azidzatsatira malamulo olungama a Yehova, omwe amalimbikitsa mgwirizano ndi mtendere. Choncho anthu azidzakondana komanso kukhulupirirana. (Yes. 11:9) Tikuyembekezeratu zinthu zabwino kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, ngati tizimvera Yehova tidzapitiriza kukhala m’Paradaiso mpaka kalekale.​—Sal. 37:29; Yoh. 3:16.

Tikamamvera Yehova tidzakhala ndi moyo m’Paradaiso mpaka kalekale (Onani ndime 7)


8. Kodi lonjezo la moyo wosatha linathandiza bwanji mmishonale wina? (Yuda 20, 21)

8 Nthawi zonse tikamakumbukira lonjeza la Mulungu la moyo wosatha, tidzakhalabe okhulupirika kwa Yehova kaya tikumane ndi mavuto otani. (Werengani Yuda 20, 21.) Lonjezo limeneli lingatithandizenso kuti tizilimbana ndi zofooka zathu. Chitsanzo ndi m’bale wina yemwe watumikira ku Africa monga mmishonale kwa nthawi yaitali. Iye anali ndi vuto lina lomwe ankalimbana nalo ndipo anati: “Nditazindikira kuti vutoli likhoza kundilepheretsa kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale ndinayesetsa kulimbana nalo komanso kupempha Yehova ndi mtima wonse kuti andithandize. Iye anandithandizadi kuti ndithane ndi vutoli.”

“ZINTHU ZIDZAKUYENDERA BWINO”

9. Kodi Davide anakumana ndi mavuto ati pa moyo wake?

9 Davide anali mfumu yabwino komanso yokhulupirika kwa Yehova. Iye nali woimba, wandakatulo, msilikali komanso mneneri. Davide anakumana ndi mayesero ambiri. Kwa zaka zambiri iye ankakhala moyo wothawathawa pomwe Mfumu Sauli inkafuna kumupha. Atakhala mfumu, Davide anathawanso pamene mwana wake Abisalomu ankafuna kumulanda ufumu. Ngakhale kuti anakumana ndi mavuto amenewa ndiponso ankalakwitsa zinthu zina, Davide anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kwa moyo wake wonse. Yehova ananena kuti Davide anali “munthu wapamtima [pake].” Choncho malangizo a Davide ndi othandiza kwambiri.​—Mac. 13:22; 1 Maf. 15:5.

10. N’chifukwa chiyani Davide anapereka malangizo kwa mwana wake Solomo?

10 Taganizirani malangizo omwe Davide anapereka kwa mwana wake Solomo yemwe anadzakhala mfumu m’malo mwake. Yehova anasankha Solomo kuti apitirize kulimbikitsa kulambira koyera komanso kuti amange kachisi yemwe akanalemekeza Mulungu. (1 Mbiri 22:5) Pogwira ntchitoyi, Solomo akanakumana ndi mavuto. Ndiye kodi Davide anamupatsa malangizo otani? Tiyeni tione.

11. Mogwirizana ndi 1 Mafumu 2:2, 3, kodi Davide anapereka malangizo otani kwa Solomo, nanga zotsatira zake zinali zotani? (Onaninso chithunzi.)

11 Kodi Davide ananena kuti chiyani? (Werengani 1 Mafumu 2:2, 3.) Davide anauza mwana wake kuti ngati angamvere Yehova, zinthu zidzamuyendera bwino. Ndipo kwa zaka zambiri zinthu zinkamuyendera bwino Solomo. (1 Mbiri 29:23-25) Iye anamanga kachisi wokongola ndipo analemba mabuku ena a m’Baibulo. Mawu ake amapezekanso m’malo ena m’Malemba. Iye anatchuka kwambiri chifukwa anali ndi nzeru komanso chuma. (1 Maf. 4:34) Koma mogwirizana ndi mawu a Davide, zinthu zikanamuyendera bwino Solomo ngati akanapitiriza kumvera Yehova Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti patapita nthawi, Solomo anayamba kulambira milungu ina. Yehova anasiya kumukonda ndipo anasiya kumupatsa nzeru zoti azilamulira anthu mwachilungamo.​—1 Maf. 11:9, 10; 12:4.

Mawu omaliza amene Davide anauza Solomo angatithandize kudziwa kuti tikamamvera Yehova, iye adzatipatsa nzeru kuti tizisankha bwino zochita (Onani ndime 11-12) b


12. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Davide?

12 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Zinthu zimatiyendera bwino tikakhala omvera. (Sal. 1:1-3) N’zoona kuti Yehova sanatilonjeze kutipatsa chuma ndi ulemerero ngati Solomo. Koma tikamamumvera, iye adzatipatsa nzeru zomwe zingatithandize kuti tizisankha bwino zochita. (Miy. 2:6, 7; Yak. 1:5) Mfundo zake zingatithandize pa nkhani zokhudza ntchito, maphunziro, zosangalatsa komanso ndalama. Tikamatsatira malangizo ake tidzakhala naye pa ubwenzi komanso tidzapeza moyo wosatha. (Miy. 2:10, 11) Tingapezenso anzathu abwino. Komanso tingapeze malangizo amene angatithandize kukhala ndi banja losangalala.

13. Kodi n’chiyani chinathandiza Carmen kuti zinthu zimuyendere bwino?

13 Carmen amene amakhala ku Mozambique ankaganiza kuti maphunziro apamwamba ndi amene angamuthandize kuti zinthu zizimuyendera bwino. Iye anapita kuyunivesite kukaphunzira za mapulani a zomangamanga. Iye analemba kuti, “Ndinkasangalala ndi zimene ndinkaphunzira koma zinkandiwonongera nthawi komanso mphamvu. Ndinkakhala kusukulu kuyambira hafu pasiti 7 m’mawa mpaka 6 koloko madzulo. Ndinkalephera kupezeka pamisonkhano ndipo ubwenzi wanga ndi Yehova unayamba kuchepa. Mumtimamu ndinazindikira kuti ndinkatumikira ambuye awiri.” (Mat. 6:24) Carmen anapempherera nkhaniyi kwa Yehova ndipo anafufuza m’mabuku athu. Iye anawonjezera kuti: “Nditapatsidwa malangizo ndi abale olimba mwauzimu komanso mayi anga, ndinasankha kuchoka kuyunivesite n’kukayamba utumiki wa nthawi zonse. Ndimaona kuti ndinasankha zinthu mwanzeru ndipo ndimasangalala kuti ndinachita zimenezi.”

14. Kodi mfundo yayikulu mu uthenga wa Mose ndi Davide inali yotani?

14 Mose ndi Davide ankakonda Yehova ndipo ankaona kuti kumumvera n’kofunika kwambiri. Mawu awo omaliza analimbikitsa anthu ena kuti atengere chitsanzo chawo chabwino pokhalabe okhulupirika kwa Yehova Mulungu. Iwo anachenjezanso kuti onse amene amasiya Yehova, nayenso amasiya kuwakonda ndipo sangapeze madalitso omwe anawalonjeza. Malangizo awo ndi othandizabe masiku ano. Patapita zaka zambiri, mtumiki winanso wa Yehova anasonyeza kuti kukhala wokhulupirika kwa Yehova n’kofunika kwambiri.

“CHIMENE CHIMANDISANGALATSA KWAMBIRI”

15. Kodi mtumwi Yohane anaona zinthu ziti pa moyo wake?

15 Yohane anali mtumwi amene Yesu ankamukonda kwambiri. (Mat. 10:2; Yoh. 19:26) Iye anayenda ndi Yesu pa utumiki wake, anaona zodabwitsa zimene ankachita ndipo anali naye pa nthawi yovuta kwambiri. Analiponso pamene ankaphedwa ndipo anamuona ataukitsidwa. Anaonanso pamene mpingo wa Chikhristu unkakula mpaka pamene uthenga wabwino “unalalikidwa padziko lonse.”​—Akol. 1:23.

16. Kodi ndi ndani amene akhala akupindula ndi makalata a Yohane?

16 Chakumapeto kwa moyo wake, Yohane anali ndi mwayi wolemba nawo Mawu ouziridwa a Mulungu. Iye analemba zinthu zochititsa chidwi zopezeka mu “chivumbulutso chimene Yesu Khristu anapereka.” (Chiv. 1:1) Yohane analembanso buku la Uthenga Wabwino lomwe limadziwika ndi dzina lake. Iye analembanso makalata atatu ouziridwa. Kalata yachitatu inali yopita kwa Mkhristu wina wokhulupirika dzina lake Gayo, yemwe ankamuona ngati mwana wake. (3 Yoh. 1) N’kutheka kuti pa nthawiyo panali anthu ambiri amene Yohane ankawaona ngati ana ake auzimu. Zimene wachikulire wokhulupirikayu analemba, zakhala zikulimbikitsa otsatira onse a Yesu mpaka pano.

17. Mogwirizana ndi 3 Yohane 4, kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti munthu akhale wosangalala?

17 Kodi Yohane analemba kuti chiyani? (Werengani 3 Yohane 4.) Yohane analemba kuti munthu amakhala wosangalala akamamvera Mulungu. Pamene ankalemba kalata yake yachitatu, anthu ena anali atayamba kufalitsa zinthu zabodza zimene zinachititsa kuti mumpingo anthu asamagwirizane. Koma ena anapitiriza ‘kuyendabe mʼchoonadi.’ Iwo ankamvera Yehova ndipo anapitiriza “kuyenda motsatira malamulo.” (2 Yoh. 4, 6) Akhristu okhulupirikawa anasangalatsa Yohane komanso Yehova.​—Miy. 27:11.

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yohane?

18 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kukhala okhulupirika kumachititsa kuti tizisangalala. (1 Yoh. 5:3) Mwachitsanzo, timakhala osangalala tikadziwa kuti tikusangalatsa Yehova. Iye amasangalala akaona tikukana mayesero n’kumatsatira mfundo za choonadi. (Miy. 23:15) Angelo nawonso amasangalala kumwamba. (Luka 15:10) Ifenso timasangalala tikamaona Akhristu anzathu akukhalabe okhulupirika akamakumana ndi mayesero. (2 Ates. 1:4) Dzikoli likadzawonongedwa tidzasangalala podziwa kuti tinakhalabe okhulupirika kwa Yehova m’dziko lolamuliridwa ndi Satana.

19. Kodi mlongo wina dzina lake Rachel anafotokoza zotani pa nkhani yophunzitsa ena choonadi? (Onaninso chithunzi.)

19 Timakhalanso osangalala kwambiri tikamaphunzitsa ena choonadi. Rachel, yemwe amakhala ku Dominican Republic amaona kuti kuphunzitsa ena zokhudza Mulungu ndi mwayi wamtengo wapatali. Pofotokoza za anthu omwe wakhala akuwaphunzitsa, iye anati: “Ndimasangalala kwambiri ndikamaona anthu amene ndawaphunzitsa akuyamba kukonda Yehova, kumudalira komanso kusintha moyo wawo kuti azimusangalatsa. Ndimaona kuti zonse zimene ndakhala ndikuchita powaphunzitsa ndi zochepa ndikayerekezera ndi chisangalalo chimene ndimakhala nacho.”

Timasangalala tikamaphunzitsa ena kuti azikonda komanso kumvera Yehova (Onani ndime 19)


MMENE MAWU OMALIZA A AMUNA OKHULUPIRIKA AMATITHANDIZIRA

20. Kodi timafanana bwanji ndi Mose, Davide ndi Yohane?

20 Mose, Davide ndi Yohane anakhala ndi moyo pa nthawi yosiyana kwambiri ndi yathu. Komabe timafanana nawo pa zinthu zambiri. Onsewa ankatumikira Mulungu woona ngati ifeyo. Mofanana ndi iwowo, timapemphera kwa Yehova komanso timamudalira kuti azitithandiza ndi kutipatsa malangizo. Ndipotu mofanana ndi amunawa timakhulupirira kuti Yehova amadalitsa anthu omwe amamumvera.

21. Kodi anthu omwe amatsatira malangizo a amuna okhulupirika monga Mose, Davide ndi Yohane adzapeza madalitso otani?

21 Tiyeni tizitsatira malangizo a amuna achikulirewa ndipo tizimvera malamulo a Yehova. Tikatero zinthu zonse zomwe timachita zizitiyendera bwino. Tidzakhala ndi moyo “kwa nthawi yaitali” kapena kuti mpaka kalekale. (Deut. 30:20) Tidzasangalala podziwa kuti tikusangalatsa Atate wathu wakumwamba, yemwe amakwaniritsa malonjezo ake m’njira imene sitimayembekezera.​—Aef. 3:20.

NYIMBO NA. 129 Tipitirizebe Kupirira

a Aisiraeli ambiri omwe anaona zodabwitsa zimene Yehova anachita pa Nyanja Yofiira, sanakalowe m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:22, 23) Yehova analamula kuti anthu a zaka 20 kapena kuposa pamenepo adzafera m’chipululu. (Num. 14:29) Koma Yoswa, Kalebe, anthu ambiri a fuko la Levi ndi ena onse amene anali asanakwanitse zaka 20 anakhalabe ndi moyo ndipo anaona Yehova akukwaniritsa lonjezo lake pamene Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano n’kukalowa m’dziko la Kanani.​—Deut. 1:24-40.

b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Kumanzere: Davide akupereka malangizo omaliza kwa mwana wake Solomo. Kumanja: Abale ndi alongo akulandira malangizo a Yehova pa Sukulu ya Utumiki Waupainiya.