Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 44

NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako

Zimene Tingachite Ena Akatilakwira

Zimene Tingachite Ena Akatilakwira

“Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa pochita chabwino.”​—AROMA 12:21.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona zimene tingachite ena akatilakwira n’cholinga choti zinthu zisaipe kwambiri.

1-2. Kodi zopanda chilungamo zimatikhudza bwanji tonsefe?

 YESU ananena fanizo la mkazi wina wamasiye yemwe anapempha woweruza kuti amuthandize mwachilungamo. Nkhaniyi iyenera kuti inafika pamtima ophunzira a Yesu, chifukwa chakuti pa nthawiyo anthu wamba sankachitiridwa zachilungamo. (Luka 18:1-5) Nkhaniyi ingatithandizenso masiku ano chifukwa pafupifupi tonsefe tinachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo.

2 Masiku ano zinthu zopanda chilungamo, kusankhana mitundu komanso kuponderezana ndi zofala, choncho sitidabwa anthu ena akatichitira zopanda chilungamo. (Mlal. 5:8) Akhristufe sitimayembekezera kuti m’bale kapena mlongo angatichitire zimenezi, koma izi zikhoza kuchitika. Mosiyana ndi anthu amene amatizunza kapena kutsutsa choonadi, abale ndi alongo athu samafuna kutichitira zopanda chilungamo. Kungoti iwowo si angwiro. Tingaphunzire zambiri pa zimene Yesu anachita atachitiridwa zopanda chilungamo ndi otsutsa. Ngati timaleza mtima ndi otsutsa omwe amatichitira zopanda chilungamo, tiyeneranso kumaleza mtima ndi Akhristu anzathu. Kodi Yehova amamva bwanji tikachitiridwa zopanda chilungamo, kaya ndi anthu ena kapenanso Akhristu anzathu? Kodi zimamukhudza?

3. Kodi Yehova amamva bwanji tikamachitiridwa zopanda chilungamo, nanga n’chifukwa chiyani?

3 Popeza ‘Yehova amakonda chilungamo,’ zimamukhudza anthu ena akamachitira atumiki ake zopanda chilungamo. (Sal. 37:28) Yesu anatitsimikizira kuti Yehova “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika . . . mwamsanga” komanso pa nthawi yoyenera. (Luka 18:7, 8) Posachedwa, iye adzathetsa mavuto onse ndi zopanda chilungamo zamtundu uliwonse.​—Sal. 72:1, 2.

4. Kodi Yehova amatithandiza bwanji masiku ano?

4 Pamene tikuyembekezera nthawi imene Yehova adzabweretse chilungamo, iye amatithandiza kupirira tikakumana ndi zopanda chilungamozo. (2 Pet. 3:13) Iye amatiphunzitsa mmene tingachitire zinthu mwanzeru. Kudzera mwa Mwana wake, iye amatipatsa chitsanzo chabwino cha mmene tingachitire tikakumana ndi zinthu zoterezi. Komanso amatipatsa malangizo othandiza omwe tingatsatire.

MUZISAMALA NDI MMENE MUMACHITIRA ZINTHU MUKACHITIRIDWA ZOPANDA CHILUNGAMO

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala tikachitiridwa zopanda chilungamo?

5 Ngati ena atichitira zopanda chilungamo, zingatipweteke kwambiri ndipo tingakhumudwe. (Mlal. 7:7) Atumiki okhulupirika monga Yobu ndi Habakuku anamvanso choncho. (Yobu 6:2, 3; Hab. 1:1-3) Ngakhale kuti mwachibadwa zingatipweteke, tiyenera kukhala osamala kuti tisachite zinthu mopanda nzeru.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Abisalomu? (Onaninso chithunzi.)

6 Anthu akatichitira zopanda chilungamo tingafune kubwezera mwanjira inayake. Komabe kuchita zimenezi kungangochititsa kuti zinthu zifike poipa kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Abisalomu yemwe anali mwana wa Mfumu Davide. Iye anakwiya kwambiri Aminoni yemwe anali mchimwene wake wa mayi ena atagwirira mchemwali wake Tamara. Mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, Aminoni ankayenera kuphedwa. (Lev. 20:17) Ngakhale kuti Abisalomu ankayenera kukwiya ndi zimene zinachitikazi, iye sankayenera kupha Aminoni.​—2 Sam. 13:20-23, 28, 29.

Abisalomu anakwiya chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zomwe mchemwali wake Tamara anachitiridwa (Onani ndime 6)


7. Kodi poyamba zinthu zopanda chilungamo zinamukhudza bwanji wolemba masalimo?

7 Tikamaona anthu omwe akuchita zopanda chilungamo zinthu zikuwayendera bwino, tingayambe kumaganiza kuti kuchita zoyenera n’kosathandiza. Chitsanzo ndi wolemba masalimo wina yemwe ankaona ngati anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino kusiyana ndi olungama. Iye anati: “Izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.” (Sal. 73:12) Iye anakhumudwanso kwambiri ndi zopanda chilungamo zomwe anaona moti anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kunali kothandiza. Iye anati: “Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi, zinali zopweteka kwa ine.” (Sal. 73:14, 16) Ndipotu iye anaulula kuti: “Koma ine mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera, mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.” (Sal. 73:2) Zofananazi zinachitikiranso m’bale wina dzina lake Alberto.

8. Kodi m’bale wina anamva bwanji chifukwa cha zopanda chilungamo zimene zinamuchitikira?

8 Alberto ananamiziridwa kuti anaba ndalama zampingo. Zimenezi zinachititsa kuti iye asiyitsidwe kutumikira pa udindo ndipo anthu amene anamva za nkhaniyi anasiya kumulemekeza. Iye anati: “Ndinakhumudwa ndipo ndinakwiya kwambiri.” Alberto analola kuti kukhumudwako kusokoneze ubwenzi wake ndi Yehova mpaka anasiya kusonkhana kwa zaka 5. Izi zikusonyeza zomwe zingachitike ngati titakwiya kwambiri chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo.

MUZITSANZIRA YESU MUKACHITIRIDWA ZOPANDA CHILUNGAMO

9. Kodi Yesu anapirira zinthu zopanda chilungamo ziti? (Onaninso chithunzi.)

9 Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino cha zomwe tingachite tikachitiridwa zopanda chilungamo. Taganizirani zimene iye anachitiridwa ndi achibale ake komanso anthu ena. Achibale ake ankanena kuti iye wachita misala. Atsogoleri achipembedzo ankati iye amachita zinthu mogwirizana ndi ziwanda. Nawonso asilikali a Chiroma anamunyoza ndi kumuchitira nkhanza mpaka anafika pomupha. (Maliko 3:21, 22; 14:55; 15:16-20, 35-37) Koma Yesu anapirira zonsezi ndipo sanabwezere. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chakechi?

Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopirira zinthu zopanda chilungamo (Onani ndime 9-10)


10. Kodi Yesu anatani atachitiridwa zopanda chilungamo? (1 Petulo 2:21-23)

10 Werengani 1 Petulo 2:21-23. a Yesu anatisiyira chitsanzo chosonyeza zimene tiyenera kuchita ena akatichitira zopanda chilungamo. Iye ankadziwa nthawi yoyenera kukhala chete komanso yoyenera kulankhula. (Mat. 26:62-64) Iye sankayankhapo pa bodza lililonse limene anthu ankamunenera. (Mat. 11:19) Akamalankhula, sankanyoza kapena kuopseza anthu amene ankamuimba mlandu. Iye ankadziletsa chifukwa “anasiya zonse mʼmanja mwa Woweruza amene amaweruza mwachilungamo.” Yesu ankadziwa kuti Yehova ankaona zopanda chilungamo zomwe zinkamuchitikira. Iye ankakhulupirira kuti Yehova adzathana ndi zopanda chilungamozo pa nthawi yoyenera.

11. Kodi tingatani kuti tikhale osamala ndi zimene tingalankhule? (Onaninso zithunzi.)

11 Tingatsanzire Yesu poyesetsa kukhala osamala ndi zimene tingalankhule tikachitiridwa zopanda chilungamo. Zinthu zina zopanda chilungamo zimakhala zazing’ono moti tikhoza kungozinyalanyaza. Kapenanso tingasankhe kukhala chete pofuna kupewa kulankhula mawu amene angachititse kuti zinthu ziipe kwambiri. (Mlal. 3:7; Yak. 1:19, 20) Nthawi zina tingafunike kulankhulapo tikaona zinthu zopanda chilungamo kapena tikafuna kufotokoza zimene timakhulupirira. (Mac. 6:1, 2) Koma tikafuna kulankhulapo, tiyenera kuyesetsa kuchita zimenezo modekha komanso mwaulemu.​—1 Pet. 3:15. b

Tikamachitiridwa zopanda chilungamo, tingatsanzire Yesu poganizira mosamala za nthawi imene tingalankhule komanso mmene tingalankhulire (Onani ndime 11-12)


12. Kodi tingatani kuti tisiye zonse mʼmanja mwa “Woweruza amene amaweruza mwachilungamo”?

12 Tingatsanzirenso Yesu posiya zonse mʼmanja mwa “Woweruza amene amaweruza mwachilungamo.” Anthu ena akatichitira zopanda chilungamo, timadziwa kuti Yehova akudziwa zoona zake za nkhaniyo. Kudziwa kuti Yehova adzakonza zinthu, kungatithandize kuti tipirire zinthu zopanda chilungamo zimene zatichitikira. Kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova kungatithandize kuti tisapitirize kukhala okwiya. Kukwiya kungachititse kuti tichite zinthu mosaganiza bwino, tisakhale osangalala komanso tingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Sal. 37:8.

13. N’chiyani chingatithandize kuti tizipirira tikachitiridwa zopanda chilungamo?

13 N’zoona kuti sitingathe kutsanzira Yesu ndendende. Nthawi zina tingalankhule kapena kuchita zinthu zomwe tingadzanong’oneze nazo bondo. (Yak. 3:2) Ndipo zopanda chilungamo zina zingatipweteke kapena kutidetsa nkhawa kwa moyo wathu wonse. Ngati izi ndi zimene zinakuchitikirani, dziwani kuti Yehova amadziwa mmene mukumvera. Ndipo Yesu, amene anachitiridwanso zopanda chilungamo, amamvetsa mmene mukumvera. (Aheb. 4:15, 16) Kuwonjezera pa chitsanzo cha Yesu, Yehova watipatsanso malangizo amene angatithandize ngati tachitiridwa zopanda chilungamo. Tiyeni tikambirane mavesi awiri opezeka m’buku la Aroma omwe angatithandize.

“SIYIRANI MALO MKWIYO WA MULUNGU”

14. Kodi ‘kusiyira malo mkwiyo wa Mulungu’ kumatanthauza chiyani? (Aroma 12:19)

14 Werengani Aroma 12:19. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘azisiyira malo mkwiyo wa Mulungu.’ Timasiyira malo mkwiyo wa Mulungu tikamalola kuti iye achite chilungamo pa nthawi komanso m’njira imene akuona kuti ndi yoyenera. M’bale wina dzina lake John atachitiridwa zopanda chilungamo ananena kuti: “Ndinkalimbana ndi mtima wofuna kuti ndikonze zinthu pandekha. Koma lemba la Aroma 12:19 linandithandiza kuti ndiziyembekezera Yehova.”

15. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuyembekezera Yehova kuti akonze zinthu?

15 Zinthu zimatiyendera bwino tikamayembekezera Yehova kuti akonze zinthu. Tikatero timakhala ngati tatula mtolo wofuna kuyesa kuti tikonze tokha zinthu. Yehova ndi wokonzeka kutithandiza. Zimakhala ngati iye akunena kuti, ‘Ndisiyire zinthu zopanda chilungamozo. Ndithana nazo.’ Tikamvera lonjezo lake lakuti “ndidzawabwezera ndine,” timasiya nkhaniyo m’manja mwake ndipo timakhulupirira kuti aithetsa m’njira yabwino kwambiri. Izi ndi zimene zinathandiza John yemwe tamutchula kale uja. Iye anati: “Ngati ndingayembekezere Yehova, iye angathetse vuto langalo kuposa mmene ineyo ndikanachitira.”

“PITIRIZANI KUGONJETSA CHOIPA POCHITA CHABWINO”

16-17. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti ‘tipitirize kugonjetsa choipa pochita chabwino’? (Aroma 12:21)

16 Werengani Aroma 12:21. Paulo analimbikitsanso Akhristu kuti ‘apitirize kugonjetsa choipa pochita chabwino.’ Mu ulaliki wake wapaphiri Yesu ananena kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mat. 5:44) Izi ndi zimene iyeyo anachita. Taganizirani mavuto amene Yesu anapirira pamene ankakhomereredwa pamtengo wozunzikirapo ndi asilikali a Chiroma. Kunena zoona Yesu anachitiridwa zinthu zochititsa manyazi komanso zankhanza kwambiri ndipo sitingamvetse ululu umene anamva.

17 Koma Yesu sanagonje chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene anamuchitira. M’malo motemberera asilikaliwo, iye anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.” (Luka 23:34) Tikapempherera anthu amene atilakwira, zimatithandiza kuti tisiye kusunga chakukhosi kapena kukwiya. Komanso zimatithandiza kuti tiziwaona moyenera.

18. Kodi pemphero linathandiza bwanji Alberto ndi John kuti apirire?

18 Pemphero linathandiza abale awiri omwe tawatchula kale aja kuti apirire zopanda chilungamo zomwe zinawachitikira. Alberto anati: “Ndinapempherera abale omwe anandichitira zopanda chilungamo aja. Ndinapempha Yehova maulendo angapo kuti andithandize kuti ndisiye kuwakwiyira.” N’zosangalatsa kuti Alberto anayambiranso kutumikira Yehova mokhulupirika. John anati: “Nthawi zambiri ndinkapempherera m’bale amene anandikhumudwitsa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizimuona moyenera ndipo ndisamamuweruze. Mapempherowo anandithandizanso kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima.”

19. Kodi tiyenera kumachita chiyani pamene tili m’dziko loipali? (1 Petulo 3:8, 9)

19 M’dziko loipali, tizikumanabe ndi zinthu zopanda chilungamo. Ndiye kaya tikumana ndi zotani, tiyeni tisasiye kupemphera kwa Yehova kuti atithandize. Tizitsanziranso mmene Yesu anachira zinthu atachitiridwa zopanda chilungamo ndipo tipitirize kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa.​—Werengani 1 Petulo 3:8, 9.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

a M’machaputala 2 ndi 3 a kalata yake yoyamba, mtumwi Petulo anafotokoza nthawi zingapo pomwe Akhristu anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo ndi mabwana awo ankhanza kapena amuna awo osakhulupirira.​—1 Pet. 2:18-20; 3:1-6, 8, 9.