NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2018

Magaziniyi ili ndi nkhani zophunzira kuyambira pa December 3 mpaka 30, 2018.

Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo Mu 1918

Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse ku Europe, zinkasonyeza kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino kwa Ophunzira Baibulo komanso padziko lonse.

Tizilankhula Zoona Zokhazokha

N’chifukwa chiyani anthu amakonda kunama, nanga zotsatira zake n’zotani? Tingatani kuti tizilankhula zoona zokhazokha?

Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi

Nthawi yatsalayi tiyenera kuigwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro a Baibulo ndipo tiziphunzitsa anthu choonadi. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa tikakhala mu utumiki?

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Wandidalitsa Kwambiri Chifukwa cha Zimene Ndinasankha

Charles Molohan ali mnyamata anasankha zokatumikira ku Beteli ndipo Yehova wakhala akumudalitsa kwa zaka zambiri.

Tizikhulupirira Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wathu

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yesu yemwe ndi mtsogoleri wathu pamene zinthu zikusintha kwambiri m’gulu la Yehova masiku ano?

Tizikhalabe ndi Mtendere Wamumtima Zinthu Zikasintha

Zinthu zikasintha mosayembekezereka pa moyo wathu, tikhoza kuda nkhawa. Kodi ‘mtendere wa Mulungu’ ungatithandize bwanji pa nthawi ngati imeneyi?

Kodi Mukudziwa?

Sitefano anali Mkhristu woyamba kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti akhalebe wodekha pamene ankazunzidwa?