Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhalabe ndi Mtendere Wamumtima Zinthu Zikasintha

Tizikhalabe ndi Mtendere Wamumtima Zinthu Zikasintha

“Ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi.”​—SAL. 131:2.

NYIMBO: 128, 129

1, 2. (a) Kodi Mkhristu angamve bwanji zinthu zikasintha mosayembekezereka pa moyo wake? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Mogwirizana ndi Salimo 131, kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe ndi mtendere wamumtima?

LLOYD ndi mkazi wake Alexandra atamva kuti utumiki wawo ukusintha, poyamba anadandaula kwambiri. Iwo anali atatumikira pa Beteli kwa zaka zoposa 25. Lloyd ananena kuti: “Ndinkaona kuti kutumikira pa Beteli ndi mbali yaikulu ya moyo wanga ndipo ndinkakonda kwambiri ntchito imene ndinapatsidwa. Ndinamvetsa chifukwa chake tinasinthidwa. Koma pamene milungu ndi miyezi inkapita ndinkavutika kwambiri mumtimamu. Ndinkamva ngati atitaya. Ndinkati nthawi ina kumva bwino nthawi ina osamva bwino.”

2 Zinthu zikasintha mosayembekezereka pa moyo wathu tikhoza kuchita mantha komanso kudera nkhawa zam’tsogolo. (Miy. 12:25) Mwina tingavutikenso kuti tivomereze kuti zinthu zasintha. Zimenezi zikatichitikira, kodi tingatani kuti ‘tidzitonthoze komanso kukhazika mtima wathu pansi’? (Werengani Salimo 131:1-3.) Tiyeni tikambirane za atumiki a Yehova ena otchulidwa m’Baibulo komanso amasiku ano amene anakhalabe ndi mtendere wamumtima pamene zinthu zinasintha pa moyo wawo.

“MTENDERE WA MULUNGU” UMATILIMBIKITSA KWAMBIRI

3. Kodi zinthu zinasintha bwanji pa moyo wa Yosefe?

3 Yosefe anali ndi zaka 17 pamene abale ake anamugulitsa chifukwa chomuchitira nsanje. Izi zisanachitike, iye anali mwana wokondedwa kwambiri ndi bambo ake. (Gen. 37:2-4, 23-28) Kwa zaka 13, Yosefe anakhala kapolo komanso mkaidi ku Iguputo ndipo anali kutali ndi bambo ake omwe ankawakonda kwambiri. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asataye mtima kapena kukwiya?

4. (a) Kodi Yosefe ankaganizira kwambiri za chiyani ali kundende? (b) Kodi Yehova anayankha bwanji mapemphero a Yosefe?

4 Pa nthawi imene Yosefe ankazunzika m’ndende, ayenera kuti ankaganizira kwambiri mmene Yehova ankamuthandizira. (Gen. 39:21; Sal. 105:17-19) Maloto ochokera kwa Mulungu amene Yosefe analota ali mwana ayeneranso kuti ankamutsimikizira kuti Mulungu akusangalala naye. (Gen. 37:5-11) N’zosakayikitsa kuti iye ankauza Yehova zimene zinkamupweteka mumtima mwake. (Sal. 145:18) Ndiyeno Yehova anayankha mapemphero ake ochokera mumtimawo n’kumuthandiza kudziwa kuti “anali naye” pa mavuto ake onse.​—Mac. 7:9, 10. *

5. Kodi “mtendere wa Mulungu” ungatithandize bwanji kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri pomutumikira?

5 Ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto, tikhoza kulimbikitsidwa ndi “mtendere wa Mulungu” umene umateteza maganizo athu. (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Choncho tikakhala ndi nkhawa tizipempha Mulungu kuti atipatse mtendere wake umene ungatithandize kuti tisataye mtima koma tiziyesetsabe kuchita zambiri pomutumikira. Tiyeni tikambirane za anthu ena amasiku ano amene apereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi.

MUZIPEMPHA YEHOVA KUTI AKUPATSENI MTENDERE WAMUMTIMA

6, 7. Kodi kupemphera kungatithandize bwanji kupeza mtendere wamumtima? Perekani chitsanzo.

6 Ryan ndi mkazi wake Juliette atauzidwa kuti utumiki wawo monga apainiya apadera akanthawi watha, anadandaula kwambiri. Koma Ryan anati: “Nthawi yomweyo tinapemphera kwa Yehova. Tinkadziwa kuti uwu unali mwayi wapadera wosonyeza kuti timamukhulupirira. Anthu ambiri mumpingo wathu anali atsopano. Choncho tinapempha Yehova kuti atithandize kukhala chitsanzo chabwino pa nkhani yosonyeza chikhulupiriro.”

7 Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero lawo? Ryan anena kuti: “Titangomaliza kupemphera, nthawi yomweyo tinasiya kuda nkhawa komanso kudandaula. Mtendere wa Mulungu unkateteza mtima ndi maganizo athu. Tinazindikira kuti tikhoza kugwiritsidwabe ntchito ndi Yehova tikapitiriza kukhala ndi maganizo oyenera.”

8-10. (a) Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize bwanji tikakhala ndi nkhawa? (b) Tikamayesetsa kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba, kodi iye angatidalitse bwanji?

8 Kuwonjezera pa kukhazika mtima wathu pansi, mzimu wa Mulungu ungatichititse kuganizira malemba omwe angatithandize kuti tiziikabe maganizo athu pa kutumikira Yehova. (Werengani Yohane 14:26, 27.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Philip ndi mkazi wake Mary, omwe anatumikira pa Beteli kwa zaka pafupifupi 25. M’miyezi 4 yokha, mayi ake a Philip, mayi ake a Mary komanso wachibale wawo wina anamwalira ndipo anayamba kusamalira bambo ake a Mary amene ali ndi matenda a mu ubongo.

9 Philip anati: “Ndinkaona kuti ndikupirira koma ndinkadandaulabe mumtima. Munkhani inayake yophunzira ya mu Nsanja ya Olonda ndinapeza lemba la Akolose 1:11. Ndinazindikira kuti ndinkapirira ndithu koma ndinkafunika ‘kupirira moleza mtima ndiponso mwachimwemwe.’ Lembali linandikumbutsa kuti zimene zingandithandize kukhala wosangalala ndi kuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu osati zinthu zimene zikuchitika pa moyo wanga.”

10 Philip ndi Mary ankayesetsabe kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba ndipo iye anawadalitsa kwambiri. Iwo atangochoka pa Beteli, onse anapeza anthu omwe ankafuna kuphunzira Baibulo kangapo pa mlungu. Mary ananena kuti “timaona kuti Yehova anatipatsa maphunzirowo n’cholinga choti tidziwe kuti zinthu ziyenda bwino.”

MUZICHITA MBALI YANU NDIPO YEHOVA ADZAKUDALITSANI

Kodi tingatsanzire bwanji Yosefe ngakhale pamene zinthu zasintha pa moyo wathu? (Onani ndime 11-13)

11, 12. (a) Kodi Yosefe anachita bwanji mbali yake kuti Yehova amudalitse? (b) Kodi Yosefe anadalitsidwa bwanji chifukwa chopirira?

11 Zinthu zikasintha mwadzidzidzi pa moyo wathu, tikhoza kudera nkhawa kwambiri zam’tsogolo mpaka kufika pongogwa ulesi. Zimenezi zikanatha kuchitikira Yosefe. Koma iye anayesetsa kuchita zimene akanatha kuti asangalatse Yehova ndipo anadalitsidwa. Ngakhale pamene anali kundende, Yosefe ankagwira mwakhama ntchito iliyonse imene anapatsidwa ndi mkulu wa ndende, ngati mmene ankachitira ali kwa Potifara.​—Gen. 39:21-23.

12 Tsiku lina, Yosefe anapemphedwa kuti aziyang’anira anthu awiri, amene asanamangidwe anali ndi udindo waukulu m’nyumba ya Farao. Yosefe ankachita nawo zinthu mokoma mtima choncho iwo anamuuza mavuto awo komanso maloto amene analota. (Gen. 40:5-8) Yosefe sanadziwe kuti zimene anakambirana nawozi zidzathandiza kuti mavuto akewo athe. Iye anakhalabe m’ndende zaka zina ziwiri, koma kenako anamasulidwa ndipo tsiku lomwelo anasankhidwa kukhala wolamulira wachiwiri kwa Farao.​—Gen. 41:1, 14-16, 39-41.

13. Kodi tingatani kuti Yehova azitidalitsa ngakhale pamene takumana ndi mavuto?

13 Mofanana ndi Yosefe, tikhoza kukumana ndi mavuto amene sitingawathetse. Koma ngati tingakhale oleza mtima n’kumachita zimene tingathe posangalatsa Yehova, iye adzatidalitsa. (Sal. 37:5) N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kusokonezeka maganizo n’kumada nkhawa, koma mogwirizana ndi mawu a Paulo, ‘sitingasoweretu pothawira.’ (2 Akor. 4:8) Zimene Paulo ananenazi zikhoza kutichitikira, makamaka ngati timachita khama mu utumiki.

MUZICHITA ZAMBIRI MU UTUMIKI

14-16. Kodi Filipo ankachita chiyani ngakhale kuti zinthu zinkasintha pa moyo wake?

14 Filipo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Atangopatsidwa kumene utumiki watsopano, Akhristu anayamba kuzunzidwa ku Yerusalemu pambuyo poti Sitefano waphedwa. * (Mac. 6:1-6) Koma pamene Akhristu anabalalitsidwa, Filipo sanangokhala. Iye anapita kukalalikira mumzinda wa Samariya, womwe munali anthu amene anali asanamvepo uthenga wabwino.​—Mat. 10:5; Mac. 8:1, 5.

15 Filipo anali ndi mtima wofunitsitsa kupita kulikonse kumene mzimu wa Mulungu ungamutsogolere. Choncho Yehova anamugwiritsa ntchito kupita kumalo kumene kunali kusanalalikiridwepo. Popeza Asamariya ankanyozedwa ndi Ayuda, ayenera kuti anasangalala kuona kuti Filipo analibe tsankho. N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri ankakonda kumvetsera uthenga wake.​—Mac. 8:6-8.

16 Mzimu wa Mulungu unatsogolera Filipo kuti apite kumizinda ya Asidodi ndi Kaisareya, yomwe inali ndi anthu amene sanali Ayuda. (Mac. 8:39, 40) Patapita zaka 20 kuchokera pamene Filipo anayamba kulalikira ku Samariya, zinthu zinasinthanso pa moyo wake. Iye anakhala ndi ana n’kukhazikika. Ngakhale kuti zinthu zinkasintha pa moyo wake, Filipo sanasiye kulalikira mwakhama ndipo iye ndi banja lake anadalitsidwa kwambiri ndi Yehova.​—Mac. 21:8, 9.

17, 18. Kodi kugwira mwakhama ntchito yolalikira kungatithandize bwanji zinthu zikasintha pa moyo wathu?

17 Anthu ambiri amene amachita utumiki wa nthawi zonse amaona kuti zinthu zikasintha pa moyo wawo, kupitiriza kulalikira mwakhama kumawathandiza kuti akhalebe ndi maganizo oyenera. Osborne ndi mkazi wake Polite, omwe ndi a ku South Africa, atachoka pa Beteli ankaganiza kuti sizingatenge nthawi kuti apeze ntchito komanso nyumba. Koma Osborne anati: “Sizinayende mmene tinkaganizira. Sitinapeze ntchito msanga.” Polite ananena kuti: “Panapita miyezi itatu tisanapeze ntchito ndipo tinalibe ndalama. Zinali zovuta kwambiri.”

18 Kodi n’chiyani chinawathandiza kupirira? Osborne ananena kuti: “Kulalikira limodzi ndi mpingo kunatithandiza kwambiri kuti tisamadandaule komanso kuti tiziona zinthu moyenera. Tinasankha zoti tizitanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira m’malo momangoda nkhawa ndipo zimenezi zinatithandiza kukhala osangalala. Tinafufuza kwambiri ntchito ndipo kenako tinaipeza.”

MUZIYEMBEKEZERA YEHOVA MOLEZA MTIMA

19-21. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe ndi mtendere wamumtima? (b) Kodi kusintha kwa zinthu pa moyo wathu kungatithandize bwanji?

19 Zitsanzo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti tikamayesetsa kuchita zimene zimasangalatsa Yehova n’kumamuyembekezera ndi mtima wonse, tikhoza kukhalabe ndi mtendere wamumtima. (Werengani Mika 7:7.) N’kutheka kuti zinthu zimene zasintha pa moyo wathu zingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Polite, yemwe tamutchula kale uja, ataganizira zimene zamuchitikira ananena kuti: “Kusinthidwa utumiki kwandithandiza kuti ndiphunzire kudalira Yehova, ngakhale pamene zinthu sizikuyenda bwino. Panopa ndili pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova.”

20 Mary, yemwe tamutchula kale uja, akusamalirabe bambo ake achikulirewo kwinaku akuchita upainiya. Iye anati: “Ndazindikira kuti ndikayamba kuda nkhawa, ndiyenera kusiya zimene ndikuchita, kupemphera kenako n’kupuma pang’ono. Mfundo yaikulu imene ndaphunzira ndi yoti ndiyenera kusiya zinthu m’manja mwa Yehova ndipo ndikuona kuti mfundo imeneyi idzakhala yofunika kwambiri m’tsogolomu.”

21 Lloyd ndi Alexandra, omwe tawatchula kumayambiriro aja, ananena kuti zinthu zimene zinasintha pa moyo wawo zija zinayesa kwambiri chikhulupiriro chawo kuposa mmene ankayembekezera. Koma iwo anati: “Chikhulupiriro chathu chikayesedwa zimasonyeza ngati chili cholimba kapena ayi komanso ngati chingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto. Zimathandizanso kuti tikhale anthu abwino kwambiri.”

Zinthu zikasintha mosayembekezereka tikhoza kupeza madalitso osayembekezereka (Onani ndime 19-21)

22. Kodi chingachitike n’chiyani tikamayesetsa kuchita zimene tingathe kuti tizisangalatsa Yehova?

22 Zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu chifukwa cha matenda, udindo watsopano m’banja kapena ngati utumiki wathu wasintha. Zikatero, musamakayikire kuti Yehova amakuganizirani ndipo adzakuthandizani. (Aheb. 4:16; 1 Pet. 5:6, 7) Komanso muziyesetsa kuchita zimene mungathe kuti muzisangalatsa Yehova. Muzipemphera kwa iye ndiponso kusiya zinthu m’manja mwake. Mukamachita zimenezi, mudzakhalabe ndi mtendere wamumtima ngakhale kuti zinthu zasintha pa moyo wanu.

^ ndime 4 Yosefe atatuluka mundende, anaona kuti Yehova anamulimbikitsa pomupatsa mwana wamwamuna. Iye anapatsa mwanayo dzina lakuti Manase ndipo anati: “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse.”​—Gen. 41:51, mawu am’munsi.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Kodi Mukudziwa?” m’magaziniyi.