Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi
“Inu Yehova, . . . mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha.”—SAL. 119:159, 160.
1, 2. (a) Kodi Yesu ankaona kuti ntchito yofunika kwambiri ndi iti, nanga n’chifukwa chiyani? (b) Kodi tingatani kuti tizigwira bwino ntchito ndi Mulungu?
YESU KHRISTU anali kalipentala komanso mphunzitsi. (Maliko 6:3; Yoh. 13:13) Iye anali waluso pa ntchito zonsezi. Pa ntchito yake ya ukalipentala, ankadziwa kugwiritsa ntchito bwino zipangizo zake moti ankapanga zinthu mwaluso kwambiri. Ndipo pa ntchito yake yophunzitsa anthu, ankagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba zimene ankazidziwa bwino kuti athandize anthu osiyanasiyana kumvetsa choonadi cha m’Mawu a Mulungu. (Mat. 7:28; Luka 24:32, 45) Ali ndi zaka 30, Yesu anasiya ukalipentala chifukwa ankaona kuti ntchito yophunzitsa anthu inali yofunika kwambiri. Iye ananena kuti chifukwa china chimene Mulungu anamutumizira padzikoli chinali choti adzalengeze uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 20:28; Luka 3:23; 4:43) Choncho pa moyo wake wonse, Yesu ankaona kuti ntchito yophunzitsa anthu ndi yofunika kwambiri ndipo ankafuna kuti anthu ena azigwira nawonso ntchito imeneyi.—Mat. 9:35-38.
2 Mwina ife si akalipentala koma tonsefe timagwira ntchito yophunzitsa anthu uthenga wabwino. Ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa timaigwira ndi Mulungu. Paja Baibulo limati ndife “antchito anzake.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 6:4) Koma timadziwanso kuti mawu onse a Yehova “ndi choonadi chokhachokha.” (Sal. 119:159, 160) N’chifukwa chake tiyenera kuyesetsa ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a choonadi.’ (Werengani 2 Timoteyo 2:15.) Choncho tiyenera kukulitsa luso lathu pogwiritsa ntchito Baibulo chifukwa ndi limene timaligwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu za Yehova, Yesu ndi Ufumu. Pofuna kutithandiza kuti utumiki wathu uziyenda bwino, gulu la Yehova lakonza zinthu zina zoti tizigwiritsa ntchito polalikira. Zinthu zimenezi timazitchula kuti Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa ndipo tiyenera kuzidziwa bwino.
3. Kodi tiyenera kuchita chiyani pa nthawi imene yatsala kuti tilalikire, nanga lemba la Machitidwe 13:48 limatithandiza bwanji pa nkhaniyi?
3 Mwina tingadzifunse kuti, N’chifukwa chiyani timazitchula kuti Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa osati polalikira? Mawu oti “kulalikira” amatanthauza kulengeza uthenga winawake koma mawu oti “kuphunzitsa” amatanthauza kufika munthu pamtima ndi uthengawo n’cholinga choti agwiritse ntchito zimene waphunzirazo. Nthawi imene yatsala kuti tilalikire ndi yochepa kwambiri. Choncho tiyenera kuigwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro a Baibulo ndiponso kuphunzitsa anthu choonadi. Kuti tichite zimenezi tiyenera kufufuza mwakhama anthu omwe ali “ndi maganizo abwino” n’kuwathandiza kuti akhale okhulupirira.—Werengani Machitidwe 13:44-48.
4. Kodi tingazindikire bwanji anthu amene ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha,’ nanga tingawapeze bwanji?
4 Kodi tingazindikire bwanji anthu omwe ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha’? Mofanana ndi mmene zinalili munthawi ya atumwi, tingapeze anthu ngati amenewa tikamalalikira. Choncho tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Mukalowa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera.” (Mat. 10:11) Sitingayembekezere kuti anthu amene alibe chidwi, amene sakonda zinthu zokhudza Mulungu kapena anthu onyada angamvetsere uthenga wabwino. Koma tiyenera kufufuza anthu oona mtima, odzichepetsa komanso amene akufunitsitsa kuphunzira choonadi. Tingayerekezere kufufuza kumeneku ndi zimene Yesu ayenera kuti ankachita pa ntchito ya ukalipentala. Iye ayenera kuti ankafufuza mtengo umene unali woyenera kuti apangire mipando, zitseko, magoli kapena zinthu zina. Akapeza mtengo woyenera ankatenga zipangizo zake n’kupangira mwaluso zimene ankafunazo. Tiyenera kuchitanso zimenezi tikamayesetsa kuphunzitsa munthu woona mtima kuti akhale wophunzira wa Yesu.—Mat. 28:19, 20.
5. Kodi tiyenera kudziwa chiyani zokhudza Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa? Perekani chitsanzo. (Onani zithunzi zoyambirira.)
5 Chipangizo chilichonse chimene Yesu ankagwiritsa ntchito popanga zinthu chinali ndi ntchito yakeyake. * Ayenera kuti anali ndi zipangizo zimene ankagwiritsa ntchito poyeza ndi kulemba matabwa, kudula, kuboola, kusema, kupala komanso kukhoma matabwawo. N’chimodzimodzinso ndi Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa. Chinthu chilichonse chili ndi ntchito yake. Choncho tiyeni tikambirane zinthuzi kuti tidziwe mmene tingazigwiritsire ntchito.
ZOTHANDIZA KUTI ANTHU ATIDZIWE
6, 7. (a) Kodi inuyo munagwiritsapo ntchito bwanji makadi? (b) Kodi timapepala toitanira anthu kumisonkhano tili ndi ntchito ziwiri ziti?
6 Makadi. Makadiwa ndi aang’ono koma amathandiza kwambiri kuti anthu atidziwe komanso adziwe za webusaiti yathu. Anthuwo akapita pawebusaitiyi akhoza kudziwa zambiri zokhudza ifeyo komanso kupempha kuti tiziphunzira nawo Baibulo. Panopa anthu oposa 400,000 apempha pa jw.org kuti aziphunzira Baibulo ndipo tsiku lililonse anthu ena mahandiredi angapo amapemphanso. Mukhoza kunyamula makadiwa mukamachita zinthu za tsiku ndi tsiku n’cholinga choti mulalikire pa mpata uliwonse umene ungapezeke.
7 Timapepala Toitanira Anthu. Timapepala timeneti tili ndi ntchito ziwiri. Paja patimapepalati pamalembedwa kuti: “Tikukupemphani kuti muziphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.” Ndiponso Mat. 5:3) Koma munthu aliyense akhoza kufika kumisonkhano yathu, kaya akuphunzira nafe kapena ayi. Munthu akafika kumisonkhanoyi amatha kumva mfundo zoona zimene timaphunzira kuchokera m’Baibulo.
amalembapo kuti munthu angaphunzire Baibulo “kumisonkhano yathu kapena ndi munthu wina.” Choncho timapepalati timathandiza anthu kuti adziwe zokhudza ifeyo komanso kuti anthu amene “amazindikira zosowa zawo zauzimu” ayambe kuphunzira Baibulo. (8. Kodi kupezeka pamisonkhano yathu, ngakhale kamodzi kokha, kumathandiza bwanji anthu? Perekani chitsanzo.
8 Tiyenera kupitiriza kuitanira anthu kumisonkhano yathu kuti afike ngakhale kamodzi kokha. Zili choncho chifukwa adzatha kuona kuti ifeyo timaphunzira mfundo zoona za m’Baibulo pomwe ku zipembedzo zawo saphunzira zimenezi. (Yes. 65:13) Ray ndi mkazi wake Linda a ku United States anazindikira zimenezi zaka zingapo zapitazo. Iwo ankakhulupirira Mulungu ndipo anaganiza zoti ayambe kupita kutchalitchi kuti azikaphunzira za Mulunguyo. Choncho anayamba kupita kutchalitchi chilichonse chimene chinali mumzinda wawo. Mumzindawo munali matchalitchi komanso zipembedzo zambirimbiri. Iwo anagwirizana kuti tchalitchi chimene angasankhe kulowa chikhale ndi zinthu ziwiri. Choyamba chinali chakuti ayenera kuphunzira mfundo yatsopano popemphera mutchalitchicho ndipo chachiwiri chinali chakuti anthu ake ayenera kuoneka kuti amatumikiradi Mulungu. Patapita zaka zingapo, anamaliza matchalitchi onse koma palibe chilichonse chimene chinali ndi zinthu ziwirizi. Sanaphunzireko chilichonse ndipo anthu ake anali osadzilemekeza. Tsiku lina ataweruka kutchalitchi chomaliza chimene anapita, Linda anapita kuntchito pomwe Ray anabwerera kunyumba. Pobwerera, Ray anadutsa pa Nyumba ya Ufumu ndipo anaganiza kuti: ‘Bwanji ndikalowe umo ndione mmene zimakhalira?’ Iye anasangalala kwambiri atafika m’Nyumba ya Ufumuyo. Aliyense ankaoneka wansangala komanso wovala bwino. Ray anakhala pampando wakutsogolo ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anaphunzira. Zinafanana kwambiri ndi mmene Paulo anafotokozera munthu amene anafika koyamba pamisonkhano yachikhristu n’kunena kuti: “Zoonadi Mulungu ali pakati panu.” (1 Akor. 14:23-25) Kungoyambira tsiku limenelo, Ray ankasonkhana Lamlungu lililonse ndipo kenako anayamba kupezekanso pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Linda anayambanso kupezeka pamisonkhano ndipo banjali linayamba kuphunzira Baibulo lili ndi zaka za m’ma 70 ndipo kenako linabatizidwa.
ZOTHANDIZA KUTI TIYAMBE KUKAMBIRANA
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kugwiritsa ntchito timapepala n’kosavuta? (b) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji kapepala kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
9 Timapepala. Pali timapepala tamitundu 8 ndipo timathandiza kwambiri kuti tiyambe kukambirana ndi anthu m’njira yosavuta. Timapepalati tinayamba kutuluka mu 2013 ndipo pofika pano timapepala tokwana 5 biliyoni tasindikizidwa. Ubwino wa timapepalati ndi wakuti tinapangidwa mofanana moti ukangodziwa kugwiritsa ntchito kamodzi ndiye kuti ukhoza kugwiritsa ntchito tonse bwinobwino. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji kapepala kuti muyambe kukambirana ndi munthu?
10 Tiyerekeze kuti mukugwiritsa ntchito kapepala kakuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? Mukhoza kusonyeza munthu funso limene lili patsamba loyamba n’kumufunsa kuti: “Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi mungayankhe kuti ndi . . . ” Kenako mungamupemphe kuti asankhe yankho limodzi mwa mayankho atatuwo. Popanda kumuuza ngati wayankha molondola kapena ayi, mutsegule patsamba lachiwiri pakamutu kakuti “Zimene Baibulo Limanena” n’kumusonyeza lemba la Danieli 2:44 ndi Yesaya 9:6. Ngati n’zotheka, pitirizani kukambirana naye. Pomaliza, mumusonyeze funso lapatsamba lomaliza pansi pa kamutu kakuti “Ganizirani Mfundo Iyi” lomwe mungadzakambirane naye mukadzabweranso. Funso lake ndi lakuti, “Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumu wa Mulungu?” Mukadzakumananso mukhoza kudzakambirana naye mutu 7 wa kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, komwe timagwiritsa ntchito poyambitsa maphunziro a Baibulo.
ZOTHANDIZA KUTI MUNTHU AKHALE NDI CHIDWI
11. Kodi magazini athu amakonzedwa n’cholinga chotani, nanga tiyenera kudziwa chiyani?
11 Magazini. Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi magazini amene amafalitsidwa komanso kumasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa magazini ena onse padzikoli. Nkhani zake zoyambirira zimakonzedwa n’cholinga choti zikhale zosangalatsa kwa anthu kulikonse. Zili choncho chifukwa magaziniwa amagwiritsidwa ntchito padziko lonse. Tiziwagwiritsa ntchito kuti tithandize anthu kuchita chidwi ndi nkhani zimene n’zofunika kwambiri pa moyo. Tiyenera kudziwa kuti magaziniwa anapangidwa n’cholinga chothandiza anthu ati. Izi zingatithandize kuti tiziwagawira kwa anthu oyenera.
12. (a) Kodi Galamukani! imalembedwa kuti izithandiza anthu ati, nanga cholinga chake n’chiyani? (b) Kodi inuyo mwagwiritsa ntchito bwanji magaziniyi posachedwapa?
12 Magazini ya Galamukani! imapangidwa kuti izithandiza anthu amene amadziwa zochepa zokhudza Baibulo kapena salidziwa n’komwe. Mwina sadziwa chilichonse chokhudza zimene Akhristu amakhulupirira, sadziwa kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza kapena amakayikira kuti chipembedzo n’chothandiza. Cholinga chachikulu cha Galamukani! ndi kuthandiza anthu kuti azikhulupirira zoti kuli Mulungu. (Aroma 1:20; Aheb. 11:6) Magaziniyi imathandizanso anthu kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. (1 Ates. 2:13) Mitu ya magazini a Galamukani! mu 2018 ndi yakuti: “Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala?,” “Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino” ndi “Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa.”
13. (a) Kodi Nsanja ya Olonda yogawira imalembedwa kuti izithandiza anthu ati? (b) Kodi inuyo mwagwiritsa ntchito bwanji magaziniyi posachedwapa?
13 Magazini yogawira ya Nsanja ya Olonda imafotokoza zinthu zambiri zauzimu chifukwa imalembedwa kuti izithandiza anthu amene amalemekeza Mulungu ndi Mawu ake. N’kutheka kuti anthuwa amadziwa zinthu zina za m’Baibulo koma salidziwa molondola. (Aroma 10:2; 1 Tim. 2:3, 4) Mitu ya Nsanja ya Olonda yogawira mu 2018 ndi yakuti: “Kodi Baibulo Ndi Lothandizabe Masiku Ano?,” “Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?” ndi “Kodi Mulungu Zimam’khudza Mukamavutika?”
ZOLIMBIKITSA ANTHU KUPHUNZIRA NDIPONSO KUSONKHANA
14. (a) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mavidiyo 4 amene tatchulawa? (b) Kodi mwakumana ndi zotani poonetsa mavidiyowa?
14 Mavidiyo. Pa nthawi ya Yesu, akalipentala ankangogwiritsa ntchito zipangizo zosayendera magetsi. Koma masiku ano amakhala ndi zoyendera magetsi monga zodulira, zoboolera, zopalira komanso zokhomera matabwa. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Kuwonjezera pa mabuku, panopa tili ndi mavidiyo abwino amene tingaonetse anthu. Pali mavidiyo 4 amene amapezeka pa Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa omwe ndi akuti: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? komanso Kodi a Mboni za Yehova Ndi Anthu Otani? Mavidiyo amene amakhala amaminitsi awiri okha amathandiza kwambiri pa ulendo woyamba. Koma tikhoza kugwiritsa ntchito mavidiyo otalikirapo pa ulendo wobwereza kapena ndi anthu amene ali ndi nthawi yokwanira. Tingagwiritse ntchito mavidiyowa polimbikitsa anthu kuti aziphunzira Baibulo kapena kupita kumisonkhano yathu.
15. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene munthu angakhudzidwire akaonera vidiyo m’chilankhulo chake.
15 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene anakumana ndi mzimayi wa ku Micronesia amene chilankhulo chake ndi Chiyapizi. Mlongoyo anamuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? mu Chiyapizi. Vidiyoyo itangoyamba, mzimayiyo ananena kuti, “Eti akulankhuladi chilankhulo changa. Sindikukhulupirira. Munthu wake ndi wakuchilumba chakwathu, ndadziwira mmene akulankhulira. Ndi mmenedi timalankhulira.” Kenako ananena kuti aziwerenga mabuku ndiponso kuonera mavidiyo onse achilankhulo chake amene amapezeka pa jw.org. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:8, 11.) Chitsanzo china ndi mlongo wina wa ku United States. Iye anatumizira mwana wa mchimwene wake, yemwe amakhala dziko lina, linki ya vidiyo tatchula ija m’chilankhulo chake. Mnyamatayo anaonera vidiyoyo ndipo anamulembera imelo. Iye anati: “Mfundo yakuti dziko lonse lili m’manja mwa woipayo inandichititsa chidwi kwambiri moti ndinalembetsa kuti ndiziphunzira Baibulo.” Mnyamatayo amakhala m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa.
ZOTHANDIZA POPHUNZITSA CHOONADI
16. Fotokozani cholinga cha kabuku kalikonse: (a) Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. (b) Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. (c) Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
16 Timabuku. Kodi mungaphunzire bwanji Baibulo ndi munthu amene sawerenga bwino kapena palibe mabuku m’chilankhulo chake? Tili ndi kabuku kothandiza kwambiri pa nkhaniyi komwe ndi kakuti, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. * Kabuku kamene kangatithandize kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Mukhoza kusonyeza munthu mitu 14 imene ili patsamba lomaliza n’kumuuza kuti asankhe umene wamusangalatsa. Ndiyeno mungayambe kuphunzira naye pa mutu umenewo. Kodi munayamba mwagwiritsapo ntchito njira imeneyi pa ulendo wobwereza? Kabuku kachitatu kamene katchulidwa pa Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa ndi kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? Kabukuka kanapangidwa n’cholinga choti kazithandiza anthu kudziwa za gulu lathu. Kuti mudziwe mmene mungakagwiritsire ntchito pa phunziro la Baibulo, onani Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2017.
17. (a) Kodi buku lililonse limene timaphunzira ndi anthu lili ndi cholinga chotani? (b) Kodi anthu onse amene abatizidwa ayenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
17 Mabuku. Mukayamba kuphunzira ndi munthu pogwiritsa ntchito timabuku, mukhoza kusintha nthawi iliyonse n’kuyamba kugwiritsa ntchito buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Bukuli lingathandize munthu kudziwa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo. Akamaliza kuphunzira bukulo tikhoza kuphunzira naye buku lakuti “Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?” ngati munthuyo wayamba kutsatira zimene akuphunzira. Bukuli limathandiza munthu kuti adziwe mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo tsiku ndi tsiku. Tisaiwale kuti anthu ayenera kumaliza mabuku onse awiriwa ngakhale kuti abatizidwa. Zimenezi zingawathandize kuti akhazikike bwinobwino m’choonadi.—Werengani Akolose 2:6, 7.
18. (a) Kodi lemba la 1 Timoteyo 4:16 limatilimbikitsa kuchita chiyani pa nkhani yophunzitsa choonadi, nanga zotsatira zake ndi zotani? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani pogwiritsa ntchito Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa?
18 A Mbonife tapatsidwa udindo wothandiza anthu kudziwa “choonadi cha uthenga wabwino” chimene chingawathandize kudzapeza moyo wosatha. (Akol. 1:5; werengani 1 Timoteyo 4:16.) Tapatsidwanso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa zimene zimatithandiza kukwaniritsa udindo wathuwo. (Onani bokosi lakuti “ Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa.”) Tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito mwaluso zinthu zimenezi. Wofalitsa aliyense angasankhe chinthu chimene akufuna kugwiritsa ntchito ndi munthu amene wasonyeza chidwi komanso nthawi imene akufuna kuchigwiritsira ntchito. Koma cholinga chathu si kungogawira mabuku ndipo sitiyenera kugawira buku kwa munthu amene alibe chidwi. M’malomwake cholinga chathu ndi kuphunzitsa anthu oona mtima, odzichepetsa komanso amene akufunitsitsa kuphunzira. Anthu oterewa ndi omwe ali ‘ndi maganizo abwino amene angawathandize kudzapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48; Mat. 28:19, 20.
^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Mmisiri wa Matabwa” ndiponso bokosi lakuti “Zipangizo za Mmisiri wa Matabwa” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2010.
^ ndime 16 Ngati munthu satha kuwerenga, mungamupatse kabuku kakuti Mverani Mulungu kuti azitsatira pamene mukuphunzira naye. Kabuku kameneka kali ndi zithunzi zambiri.