NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa December 2-29, 2019.

1919​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

Mu 1919, Yehova anathandiza anthu ake kuti alalikire kwambiri kuposa m’mbuyo monse. Koma choyamba, zinthu zinafunika kusintha m’gulu.

Chiweruzo cha Mulungu​—Kodi Amachenjeza Anthu Mokwanira Nthawi Zonse?

Panopa Yehova akuchenjeza anthu onse padzikoli zokhudza zinthu zimene zikubwera zomwe zidzakhala zoopsa kuposa mphepo yamkuntho iliyonse. Kodi akuchenjeza bwanji anthu?

Tizitumikira Yehova Mwakhama Kumapeto kwa ‘Masiku Otsirizawa’

Kodi ndi zinthu ziti zimene zidzachitike kumapeto kwa “masiku otsiriza”? Ndipo kodi Yehova amafuna tizitani pamene tikuyembekezera zinthu zimenezi?

Tidzakhalebe Okhulupirika pa “Chisautso Chachikulu”

Kodi Yehova adzafuna kuti tidzatani pa nthawi ya “chisautso chachikulu”? Kodi tingakonzekere bwanji panopa kuti tidzakhalebe okhulupirika?

Kodi Yehova Adzakuthandizani Kuchita Chiyani?

Kale, Yehova anapatsa atumiki ake mtima wofuna kuchita zambiri komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tizimutumikira masiku ano?

Tizikhala Odzipereka kwa Yehova Yekha

Onani zinthu ziwiri zimene zingatithandize kudziwa ngati ndife odzipereka kwa Yehova yekha kapena ayi.