Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

M’bale Rutherford akukamba nkhani pamsonkhano wachigawo ku Cedar Point, Ohio, mu 1919

1919​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

1919​—Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

POFIKA mu 1919 nkhondo yoyamba yapadziko lonse, yomwe inamenyedwa kwa zaka 4, inali itatha. Chakumapeto kwa chaka cha 1918, mayiko anasiya kumenyana ndipo pa 18 January 1919, msonkhano wokhudza mtendere unayamba ku Paris. Pamsonkhanowu, anthu anasaina pangano la ku Versailles, lomwe linatsimikizira kuti nkhondoyi yatha. Anasaina panganoli pa 28 June 1919.

Pangano limeneli linathandiza kuti bungwe la League of Nations likhazikitsidwe. Cholinga cha bungweli chinali choti “lizilimbikitsa mgwirizano wa mayiko komanso mtendere ndi chitetezo.” Zipembedzo zambiri zimene zimati ndi zachikhristu zinkagwirizana ndi bungweli. Bungwe lina la matchalitchi a ku United States linanena kuti League of Nations ndi “bungwe landale limene Ufumu wa Mulungu ukugwiritsa ntchito polamulira dziko lapansi.” Bungwe la matchalitchili linafika potumiza nthumwi zake kumsonkhano wa ku Paris uja. Ndipo nthumwi ina inanena kuti msonkhanowu “unali chiyambi cha nthawi yatsopano padziko lonse.”

N’zoona kuti nthawi yatsopano inali ikuyamba koma osati chifukwa cha msonkhano umenewo. Mu 1919, nthawi yatsopano ya ntchito yolalikira inayamba. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anapatsa anthu ake mphamvu zowathandiza kulalikira mwakhama kuposa kale lonse. Koma poyamba zinthu zinayenera kusintha m’gulu la Ophunzira Baibulo.

ANASANKHA ZOCHITA PA NKHANI YOVUTA

Joseph F. Rutherford

Chisankho cha pa chaka cha madailekitala a Watch Tower Bible and Tract Society chinakonzedwa kuti chidzachitike Loweruka pa 4 January 1919. Pa nthawiyo, M’bale Joseph F. Rutherford amene ankatsogolera zinthu m’gulu la Yehova anali atamangidwa limodzi ndi anthu ena 7. Zifukwa zake sizinali zachilungamo ndipo anali kundende yamumzinda wa Atlanta ku Georgia m’dziko la United States. Ndiye funso linali lakuti, Kodi abale amene anamangidwawo anafunika kusankhidwanso kapena angosankha ena?

Evander J. Coward

M’bale Rutherford ali kundendeko ankadera nkhawa gulu la Yehova. Iye ankadziwa kuti abale ena angakonde kusankha munthu wina kuti akhale pulezidenti. Choncho analembera kalata anthu amene anasonkhana n’cholinga choti achite chisankhocho n’kuwauza kuti angachite bwino kusankha M’bale Evander J. Coward. M’bale Rutherford ananena kuti M’bale Coward ndi “wodekha,” “wanzeru” komanso “wokhulupirika kwa Ambuye.” Koma abale ambiri ananena kuti ndi bwino kudikira kaye kwa miyezi 6 asanachite chisankhocho. Abale oona nkhani zamalamulo amene ankaimira abale omangidwawo anavomereza zimenezi. Pa zokambiranazo, abale ena anayamba kupsa mtima.

Richard H. Barber

Koma kenako panachitika zinthu zina zimene zinathandiza kuti pakhale mtendere. Pofotokoza zimene zinachitikazo, M’bale Richard H. Barber anati kunali ngati ‘kuthira mafuta pamadzi owinduka.’ M’bale wina amene analipo ananena kuti: “Ine si loya koma ndimadziwa malamulo amene anthu okhulupirika amatsatira. Ndiye Mulungu amafuna kuti tizikhala okhulupirika. Ndikuganiza kuti tingasonyeze kukhulupirika kwathu tikachita chisankhochi n’kusankha M’bale Rutherford kuti apitirize kukhala pulezidenti.”​—Sal. 18:25.

Alexander H. Macmillan

M’bale A. H. Macmillan, yemwenso anali kundendeko, ananena kuti tsiku lotsatira M’bale Rutherford anagogoda pakhoma la selo yake n’kumuuza kuti, “Tatulutsa dzanja lako.” Kenako M’bale Rutherford anamupatsa uthenga wa pa telegalamu. M’bale Macmillan ataona uthenga wachidulewo anazindikira nthawi yomweyo zimene unkatanthauza. Uthenga wake unali wakuti: “RUTHERFORD WISE VAN BARBER ANDERSON BULLY NDI SPILL DAILEKITALA ATATU OYAMBA MAOFESALA MONI KWA ONSE.” Tanthauzo lake linali lakuti madailekitala onse asankhidwanso ndipo M’bale Joseph Rutherford ndi William Van Amburgh apitiriza kukhala maofesala. Choncho M’bale Rutherford anapitiriza kukhala pulezidenti.

ANAMASULIDWA

Abale 8 amenewa ali kundende, Ophunzira Baibulo okhulupirika analemba chikalata chopempha kuti abalewo amasulidwe ndipo ankapempha anthu kuti asaine. Abale ndi alongo olimba mtimawa anapeza anthu oposa 700,000 omwe anasaina chikalatacho. Lachitatu pa 26 March 1919, asanakapereke chikalatacho, M’bale Rutherford limodzi ndi abale enawo anamasulidwa.

Polankhula ndi anthu amene anawalandira, M’bale Rutherford anati: “Sindikukayikira kuti zinthu zimene takumana nazozi zikutithandiza kukonzekera mavuto amene akubwera. . . . Sikuti mwamenya nkhondo n’cholinga choti abale anu angotuluka mundende ayi . . . Koma kuti muchitire umboni Choonadi ndipo Yehova wadalitsa kwambiri anthu amene achita zimenezi.”

Zimene zinachitika pa mlandu wa abale athuwa mwina zimasonyeza kuti Yehova ankatsogolera zinthu. Tikutero chifukwa chakuti pa 14 May 1919, khoti la apilo linagamula kuti: “Anthu amene akuimbidwa mlanduwa . . . sanaweruzidwe mopanda tsankho ngati mmene zinayenera kukhalira. Pa chifukwa chimenechi tasintha chigamulo moti ndi osalakwa.” Poyamba, abale amenewa anaweruzidwa kuti ndi olakwa pa milandu ikuluikulu ndipo ngati akanangowakhululukira kapena kuchepetsa chilango chawo, ndiye kuti akanakhalabe ndi mbiri yoti anapalamula. Koma tsopano analibenso mlandu uliwonse. Choncho Judge Rutherford anakhalabe woyenerera kuimira anthu a Yehova ku Khoti Lalikulu Kwambiri la ku United States ndipo anachita zimenezi kambirimbiri.

ANKAFUNITSITSA KULALIKIRA

M’bale Macmillan anati: “Zinali zosatheka kuti tingokhala n’kupinda manja kumadikira Ambuye kuti atitenge kupita nafe kumwamba. Tinazindikira kuti tiyenera kuchita zinthu zina kuti tizindikire zimene Ambuye akufuna kuti tichite.”

Koma zinali zosatheka kuti abale akulikulu angoyambiranso ntchito imene anakhala akugwira kwa zaka zambiri. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi imene anali kundende, mashini osindikizira mabuku anawonongedwa. Izi zinali zokhumudwitsa ndipo abale ena ankaganiza kuti mwina ntchito yolalikira yatha.

Koma kodi anthu anali adakali ndi chidwi chofuna kumva uthenga wa Ophunzira Baibulo? Kuti apeze yankho la funsoli, M’bale Rutherford anaganiza zoitana anthu kuti awakambire nkhani. M’bale Macmillan anati: “Tinaona kuti ngati anthu sabwera, ndiye kuti ntchito yolalikira yatha.”

Nyuzipepala inalengeza za nkhani ya M’bale Rutherford yakuti “Chiyembekezo cha Anthu Amene Ali pa Mavuto” mumzinda wa Los Angeles ku California, mu 1919

Anakonza zoti akambe nkhaniyi pa 4 May 1919, mumzinda wa Los Angeles ku California. Tsikuli litafika, M’bale Rutherford anayesetsa kuti akambe nkhaniyo ngakhale kuti ankadwala kwambiri. Mutu wake unali wakuti, “Chiyembekezo cha Anthu Amene Ali pa Mavuto.” Anthu pafupifupi 3,500 anafika ndipo ambiri anabwezedwa chifukwa choti malo anatha. Ndipo tsiku lotsatira, anthu 1,500 anafika kudzamvetseranso nkhaniyo. Apa tsopano abale anazindikira kuti anthu anali adakali ndi chidwi.

Zimene abale anachita pambuyo pa zimenezi zinathandiza kukonzekera ntchito yolalikira imene a Mboni za Yehova akugwirabe mpaka pano.

ANAKONZEKERA NTCHITO YAMBIRI

Nsanja ya Olonda ya August 1, 1919 inanena kuti chakumayambiriro kwa mwezi wa September padzakhala msonkhano waukulu ku Cedar Point, Ohio. M’bale Clarence B. Beaty, yemwe anali wachinyamata ndipo ankakhala ku Missouri, ananena kuti: “Aliyense ankalakalaka kufika pamsonkhanowu.” Pamsonkhanowu panafika abale ndi alongo oposa 6,000 ndipo anali ambiri kuposa amene ankayembekezera. Chosangalatsa kwambiri pamsonkhanowu chinali chakuti anthu oposa 200 anabatizidwa m’nyanja ya Erie, yomwe inali pafupi.

Chikuto cha magazini yoyambirira ya The Golden Age ya October 1, 1919

Pa 5 September 1919, lomwe linali tsiku la 5 la msonkhanowu, M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Uthenga Wopita kwa Antchito Anzathu.” Munkhaniyi, analengeza kuti kwatuluka magazini yatsopano yotchedwa The Golden Age. * Ananena kuti m’magaziniyi muzipezeka “nkhani zochititsa chidwi zimene zangochitika kumene ndipo izifotokoza tanthauzo la zinthuzo pogwiritsa ntchito Malemba.”

Ophunzira Baibulo onse analimbikitsidwa kuti azilalikira molimba mtima pogwiritsa ntchito magaziniyi. Kalata yofotokoza kagwiridwe ka ntchitoyi inanena kuti: “Munthu aliyense wobatizidwa ayenera kukumbukira kuti ndi mwayi waukulu kutumikira Mulungu. Ndipo ayenera kugwiritsa ntchito bwino mpata umene tili nawo panopa wochitira umboni padziko lonse.” Zotsatira zake zinali zosangalatsa kwambiri. Pofika mu December, abale ndi alongo akhama anali atapeza anthu oposa 50,000 amene analembetsa kuti azilandira magazini yatsopanoyi.

M’bale Rutherford akukamba nkhani pamsonkhano wachigawo ku Cedar Point, Ohio, mu 1919

Pofika kumapeto kwa 1919, anthu a Yehova anali atalimbikitsidwa komanso okonzeka bwino. Pa nthawiyi, maulosi ambiri onena za masiku otsiriza anali atakwaniritsidwa. Mwachitsanzo, anthu a Yehova anali atayengedwa komanso kuyeretsedwa mogwirizana ndi ulosi wa pa Malaki 3:1-4. Iwo anali atamasulidwanso mu ukapolo wophiphiritsira wa “Babulo Wamkulu” ndipo Yesu anali atasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” * (Chiv. 18:2, 4; Mat. 24:45) Apa tsopano Ophunzira Baibulo anali okonzeka kuti agwire ntchito imene Yehova ankafuna kuti aziigwira.

^ ndime 22 Mu 1937, magazini ya The Golden Age anaisintha dzina n’kukhala Consolation ndipo mu 1946 inasinthanso n’kukhala Galamukani!