Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu afunika kuchenjezedwa kuti Mulungu watsala pang’ono kupereka chiweruzo choopsa

Chiweruzo cha Mulungu​—Kodi Amachenjeza Anthu Mokwanira Nthawi Zonse?

Chiweruzo cha Mulungu​—Kodi Amachenjeza Anthu Mokwanira Nthawi Zonse?

TIYEREKEZE kuti katswiri wazanyengo akuona kuti mphepo yamkuntho ikubwera m’dera limene mumakhala anthu ambiri. Ndipo akudera nkhawa anthuwo choncho akuwachenjeza mwakhama kwambiri.

Panopa Yehova akuchenjezanso anthu onse padzikoli zokhudza zinthu zimene zikubwera zomwe zidzakhala zoopsa kuposa mphepo yamkuntho iliyonse. Kodi akuchenjeza bwanji anthu? Nanga tingadziwe bwanji kuti akupatsa anthu nthawi yokwanira yoti amvere chenjezoli? Kuti tiyankhe mafunsowa, choyamba tiyeni tikambirane machenjezo ena amene Yehova anapereka m’mbuyomu.

MULUNGU ANKACHENJEZA ANTHU

M’mbuyomo, Yehova ankapereka chenjezo asanapereke chiweruzo choopsa ngati “mphepo yamkuntho” kwa anthu amene sankamvera mwadala malamulo ake. (Miy. 10:25; Yer. 30:23) Nthawi iliyonse, ankachenjeza anthu nthawi idakalipo n’kuwauza zoyenera kuchita kuti apulumuke. (2 Maf. 17:12-15; Neh. 9:29, 30) Pofuna kuthandiza anthu kuti asinthe mwamsanga, nthawi zambiri iye ankauza atumiki ake okhulupirika kuti awachenjeze.​—Amosi 3:7.

Mmodzi mwa atumiki a Mulungu okhulupirikawa anali Nowa. Kwa zaka zambiri, iye ankachenjeza anthu omwe anali achiwerewere komanso achiwawa kuti kukubwera Chigumula. (Gen. 6:9-13, 17) Nowa ankawauzanso zoyenera kuchita kuti apulumuke moti Baibulo limanena kuti iye anali “mlaliki wa chilungamo.”​—2 Pet. 2:5.

Ngakhale kuti Nowa ankachenjeza anthu mwakhama, anthu sanamvere uthenga wake wochokera kwa Mulungu. Iwo anasonyeza kuti alibiretu chikhulupiriro. Zotsatira zake zinali zakuti “chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.” (Mat. 24:39; Aheb. 11:7) Pamene mapeto ankafika, iwo sakananamizira Mulungu kuti sanawachenjeze.

Nthawi zina, Yehova ankapereka chenjezo atatsala pang’ono kupereka chiweruzo. Koma ngakhale pa nthawiyo, ankaonetsetsa kuti wapereka nthawi yokwanira yoti anthuwo asinthe. Mwachitsanzo, iye ankachenjeza anthu asanabweretse miliri 10 ku Iguputo. Yehova atatsala pang’ono kubweretsa mliri wa nambala 7 wa mvula yamphamvu kwambiri ya matalala, anatuma Mose ndi Aroni kuti akachenjeze Farao ndi atumiki ake. Popeza tsiku lotsatira ndi limene chimvulacho chinayamba, kodi tinganene kuti Yehova anawapatsa nthawi yokwanira yoti apeze malo obisala? Baibulo limati: “Aliyense amene anaopa mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao anaonetsetsa kuti ziweto zake ndi antchito ake athawira m’nyumba. Koma aliyense amene sanalabadire mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.” (Eks. 9:18-21) Yehova anapereka chenjezo mokwanira moti anthu amene anamvera mwamsanga sanavutike kwambiri ndi mliriwu.

Farao ndi atumiki ake anachenjezedwanso mliri wa 10 usanayambe koma iwo sanamvere. (Eks. 4:22, 23) Kumeneku kunali kupusa chifukwa ana awo aamuna oyamba anafa. Zinalitu zomvetsa chisoni kwambiri. (Eks. 11:4-10; 12:29) Koma kodi panali nthawi yokwanira kuti amvere chenjezolo? Inde. Paja Mose anachenjeza mwamsanga Aisiraeli za mliriwu ndipo anawauza zimene angachite kuti ateteze mabanja awo. (Eks. 12:21-28) Kodi ndi anthu ochuluka bwanji amene anamvera chenjezoli? Ena amanena kuti anthu okwana 3 miliyoni, omwe akuphatikizapo Aisiraeli, “khamu la anthu” a ku Iguputo komanso amitundu ina anapulumuka ndipo anachoka ku Iguputo.​—Eks. 12:38.

Zitsanzo zimene takambiranazi zimasonyeza kuti nthawi zonse Yehova ankapereka chenjezo komanso nthawi yokwanira yoti anthu amvere chenjezolo. (Deut. 32:4) Kodi cholinga cha Mulungu pochita zimenezi chinali chotani? Mtumwi Petulo ananena kuti Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Mulungu ankakonda kwambiri anthu amene anawachenjezawo ndipo ankafuna kuti alape n’kutsatira malangizo ake chiweruzo chisanafike.​—Yes. 48:17, 18; Aroma 2:4.

ANTHU AYENERA KUMVERA CHENJEZO LA MULUNGU MASIKU ANO

Masiku anonso, anthu onse ayenera kumvera mwamsanga chenjezo limene likuperekedwa padziko lonse. Yesu ali padzikoli, anachenjeza anthu kuti dziko loipali lidzawonongedwa pa “chisautso chachikulu.” (Mat. 24:21) Iye anafotokoza ulosi wokhudza zimene zidzachitike chisautsocho chitatsala pang’ono kuyamba. Choncho ananeneratu zinthu zimene zikuchitika padzikoli masiku ano.​—Mat. 24:3-12; Luka 21:10-13.

Mogwirizana ndi ulosi umenewu, panopa Yehova akuuza anthu kuti agonjere ulamuliro wake wachikondi. Iye amafuna kuti anthu akhale ndi moyo wabwino panopa komanso adzapeze madalitso ambiri m’dziko latsopano lamtendere. (2 Pet. 3:13) Pofuna kuthandiza anthu kuti azikhulupirira malonjezo ake, Yehova akupereka uthenga wopulumutsa womwe ndi ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Uthengawu ndi umene Yesu ananeneratu kuti “udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Mulungu wakonza zoti atumiki ake oona azichitira “umboni” kapena kuti azilalikira uthenga wakewu m’mayiko oposa 240. Yehova amafuna kuti anthu ambiri amvere chenjezoli kuti adzapulumuke pa nthawi ya chiweruzo chake chachilungamo.​—Zef. 1:14, 15; 2:2, 3.

Choncho pali umboni wosonyeza kuti nthawi zonse Yehova amapereka nthawi yokwanira kuti anthu amvere machenjezo ake. Koma funso lofunika n’lakuti: Kodi anthu adzamvera chenjezo la Mulungu nthawi idakalipo? Tiyeni atumiki a Yehovafe tiziyesetsa kuthandiza anthu ambiri kuti adzapulumuke dziko loipali likamadzawonongedwa.