Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 43

Tizikhala Odzipereka kwa Yehova Yekha

Tizikhala Odzipereka kwa Yehova Yekha

“Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”​NAH. 1:2.

NYIMBO NA. 51 Tadzipereka kwa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzipereka kwa Yehova yekha?

TIYENERA kukhala odzipereka kwa Yehova yekha chifukwa chakuti ndi amene anatilenga komanso kutipatsa moyo. (Chiv. 4:11) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Ngakhale kuti timakonda Yehova komanso kumulemekeza, zinthu zina zikhoza kutilepheretsa kukhala odzipereka kwa iye yekha. Koma tisanayambe kukambirana zinthuzo, tiyeni tikambirane kaye tanthauzo la kukhala odzipereka kwa Yehova yekha.

2. Malinga ndi Ekisodo 34:14, kodi munthu wodzipereka kwa Yehova yekha amatani?

2 M’Baibulo, mawu akuti kudzipereka kwa Mulungu amatanthauza kumukonda ndi mtima wonse. Munthu wodzipereka kwa Yehova yekha amalambira iyeyo basi. Ndipo salola kuti munthu wina kapena chinthu china chizikhala pamalo oyamba.​—Werengani Ekisodo 34:14.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti sitidzipereka kwa Yehova m’chimbulimbuli?

3 Sikuti timangokhala odzipereka kwa Yehova m’chimbulimbuli. Tikutero chifukwa timadzipereka pambuyo pophunzira zinthu zokhudza iyeyo komanso kukonda makhalidwe ake. Timadziwa zimene amakonda ndi zimene amadana nazo ndipo timagwirizana ndi maganizo ake. Timadziwanso cholinga chimene anatilengera ndipo timaona kuti n’chabwino. Ndipo timayamikira kuti watipatsa mwayi wokhala anzake. (Sal. 25:14) Chilichonse chimene timaphunzira chokhudza Mlengi wathuyu chimatithandiza kuti tizimukonda kwambiri.​—Yak. 4:8.

4. (a) Kodi Mdyerekezi amagwiritsa ntchito zinthu ziti pofuna kuti tisakhale odzipereka kwa Yehova yekha? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Mdyerekezi ndi wolamulira wa dzikoli ndipo amagwiritsa ntchito zinthu zam’dzikoli zimene timazilakalaka mwachibadwa kuti atikope. (Aef. 2:1-3; 1 Yoh. 5:19) Cholinga chake n’chakuti tiyambe kukonda kwambiri zinthuzo n’kusiya kukhala odzipereka kwa Yehova yekha. Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene amagwiritsa ntchito pofuna kutikopa. Choyamba, amatikopa kuti tizifuna kukhala ndi chuma ndipo chachiwiri, amatikopa kuti tisamasankhe bwino zosangalatsa.

TIZIPEWA KUKONDA NDALAMA

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisayambe kukonda ndalama?

5 Anthufe mwachibadwa timafuna kukhala ndi chakudya chokwanira, zovala zooneka bwino komanso malo okhala abwino. Komabe tiyenera kukhala osamala kuti tisayambe kukonda ndalama. Anthu ambiri am’dziko la Satanali ndi “okonda ndalama” komanso zinthu zimene angapeze chifukwa cha ndalamazo. (2 Tim. 3:2) Yesu anadziwa kuti otsatira ake akhoza kukopeka kuti ayambe kukonda ndalama. Iye anati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Mtumiki wa Yehova amene amagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake zambiri kuti apeze chuma amakhala ngati akutumikira ambuye awiri. Akatero sangakhale wodzipereka kwa Yehova yekha.

Mmene anthu ena a ku Laodikaya ankadzionera . . . ndiponso mmene Yehova ndi Yesu ankawaonera (onani ndime 6)

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anauza mpingo wa ku Laodikaya?

6 Chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, anthu ena mumpingo wa ku Laodikaya ankadzitama kuti: “Ndine wolemera, ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu.” Koma Yehova ndi Yesu ankaona kuti anthuwo anali ‘ovutika, omvetsa chisoni, osauka, akhungu, ndi amaliseche.’ Yesu anawapatsa malangizo poona kuti ankakonda kwambiri chuma moti ubwenzi wawo ndi Yehova unali utayamba kusokonekera. (Chiv. 3:14-17) Choncho tikazindikira kuti tayamba kukonda chuma, tiyenera kusintha nthawi yomweyo. (1 Tim. 6:7, 8) Kupanda kutero, mtima wathu ukhoza kugawanika ndipo Yehova sangasangalale ndi kulambira kwathu. Paja amafuna kuti anthu “azidzipereka kwa iye yekha basi.” (Deut. 4:24) Koma kodi n’chiyani chingachititse kuti tisokonezeke maganizo pa nkhani ya ndalama?

7-9. Kodi inuyo mukuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha David?

7 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi David, yemwe ndi mkulu wakhama ndipo amakhala ku United States. Iye ananena kuti ankalimbikira kwambiri pa ntchito yake moti anakwezedwa ndipo anatchuka m’dziko lawo lonse chifukwa cha luso lake. David anati: “Ndinkaona kuti zinthu zimenezi zinali umboni wakuti Yehova akundidalitsa.” Koma kodi amenewa analidi madalitso ochokera kwa Yehova?

8 David anayamba kuona zizindikiro zosonyeza kuti ntchito yake inkasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. Iye ananena kuti: “Ndikakhala kumisonkhano kapena mu utumiki ndinkangoganizira za mavuto akuntchito. Ndinkalandira ndalama zambiri koma ndinkapanikizika kwambiri kuntchito ndipo ine ndi mkazi wanga tinasiya kugwirizana.”

9 Kenako David anazindikira kuti akufunika kuonanso zinthu zimene ankaika pamalo oyamba. Iye ananena kuti: “Ndinatsimikiza mtima kuti ndisinthe zinthu pa moyo wanga.” David ankafuna kuti asinthe nthawi imene ankagwira ntchito ndipo anawafotokozera abwana ake. Atatero, abwanawo anamuchotsa ntchito. Ndiye kodi anatani? Iye anati: “Tsiku lotsatira ndinalemba fomu yofunsira upainiya wothandiza wopitirira.” Kuti azipeza zofunika pa moyo, David ndi mkazi wake anayamba kugwira ntchito yoyeretsa. Kenako m’baleyu anayamba upainiya wokhazikika ndipo patapita nthawi mkazi wake anayambanso. Iwo anasankha kuti azigwira ntchito imene anthu ambiri amainyoza koma sankaona kuti mtundu wa ntchito imene ankagwira ndi nkhani yaikulu. Ngakhale kuti ankalandira ndalama zochepa kwambiri poyerekezera ndi zimene ankalandira kale, mwezi uliwonse amakhala ndi zokwanira kuti apeze zofunika pa moyo. Chomwe akufuna ndi kuika zinthu zokhudza Yehova pamalo oyamba ndipo aona okha kuti iye amasamalira anthu amene amachita zimenezi.​—Mat. 6:31-33.

10. Kodi tingateteze bwanji mtima wathu?

10 Koma tonsefe tiyenera kuteteza mtima wathu, kaya tili ndi ndalama zambiri kapena zochepa. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kupewa kukonda chuma. Komanso tisamalole kuti ntchito yathu ikhale pamalo oyamba m’malo mwa kutumikira Yehova. Koma kodi mungadziwe bwanji ngati mwayamba kukonda chuma? Mukhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakonda kuganizira za ntchito yanga ndikakhala kumisonkhano kapena mu utumiki? Kodi ndimadera nkhawa kwambiri kuti mwina sindidzakhala ndi ndalama zokwanira m’tsogolo? Kodi nkhani za ndalama komanso chuma zimayambitsa mavuto m’banja lathu? Kodi ndingalolere kugwira ntchito imene anthu ena amainyoza ngati ingandithandize kuchita zambiri potumikira Yehova?’ (1 Tim. 6:9-12) Tikamaganizira mafunso amenewa, tizikumbukira kuti Yehova amatikonda komanso analonjeza anthu odzipereka kwa iye kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama.”​—Aheb. 13:5, 6.

TIZISANKHA ZOSANGALATSA MOSAMALA

11. Kodi zosangalatsa zingasokoneze bwanji munthu?

11 Yehova amafuna kuti tizikhala osangalala pa moyo wathu. Paja Mawu ake amanena kuti “kwa munthu palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.” (Mlal. 2:24) Zosangalatsa zimene timasankha zimatithandiza kuchita zimenezi. Koma vuto ndi lakuti m’dzikoli zosangalatsa zambiri zikhoza kutisokoneza. Zimachititsa kuti makhalidwe a anthu alowe pansi kapena kuti anthu azilekerera kapena kukonda zinthu zimene Mawu a Mulungu amaletsa.

Kodi ndani amakonza zosangalatsa zimene mumakonda? (onani ndime 11-14) *

12. Malinga ndi 1 Akorinto 10:21, 22, n’chifukwa chiyani tiyenera kusankha zosangalatsa mosamala?

12 Akhristufe timafuna kudzipereka kwa Mulungu yekha choncho sitingayerekeze kudya “patebulo la ziwanda” uku tikudyanso “patebulo la Yehova.” (Werengani 1 Akorinto 10:21, 22.) Nthawi zambiri kudyera limodzi ndi munthu kumasonyeza kuti mumagwirizana. Choncho tikamasankha zosangalatsa zolimbikitsa chiwawa, kukhulupirira mizimu, chiwerewere kapena makhalidwe ena oipa timakhala ngati tikudyera limodzi ndi adani a Mulungu chakudya chimene iwowo aphika. Zimenezi zikhoza kutisokoneza ifeyo komanso kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova.

13-14. Malinga ndi Yakobo 1:14, 15, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala kuti zosangalatsa zisasokoneze maganizo athu? Perekani chitsanzo.

13 N’chifukwa chiyani tikunena kuti zosangalatsa zili ngati chakudya? Munthu amatha kusankha chakudya chimene akufuna kudya. Koma akangomeza, zinthu zimangochitika zokha moti chakudyacho chimakhala mbali ya thupi lake. Chakudya chabwino chingachititse munthu kukhala wathanzi koma ngati si chabwino chingamudwalitse. Koma nthawi zina zotsatira zake sizionekera msanga.

14 N’chimodzimodzi ndi zosangalatsa. Munthu akhoza kusankha zimene akufuna kusangalala nazo. Koma pambuyo posangalala nazo, zinthu zimangochitika zokha ndipo zimakhudza maganizo ndi mtima wake. Zosangalatsa zabwino zimatitsitsimula koma ngati si zabwino zimatisokoneza. (Werengani Yakobo 1:14, 15.) Ngati sitisankha bwino, mwina zotsatira zake sizingaonekere msanga koma pakapita nthawi zidzaonekera. N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti: “Musanyengedwe, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho. Pakuti amene akufesa ndi cholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera m’thupi lakelo.” (Agal. 6:7, 8) Choncho tiyenera kupeweratu zosangalatsa zomwe zimalimbikitsa zinthu zimene Yehova amadana nazo.​—Sal. 97:10.

15. Kodi Yehova watipatsa mphatso iti kuti tizisangalala?

15 Atumiki a Yehova ambiri amakonda kuonera zinthu za pa JW Broadcasting® zomwe zimakhala zolimbikitsa kwambiri. Mlongo wina dzina lake Marilyn anati: “JW Broadcasting yandithandiza kwambiri kuti ndizikhala ndi maganizo oyenera ndipo chilichonse chimene amaikapo chimakhala chabwino. Ndikamasowa wocheza naye kapena ndikakhumudwa ndimangofufuza nkhani yolimbikitsa kapena pulogalamu ya kulambira kwa m’mawa n’kuyamba kuonera. Zimenezi zimandithandiza kuona kuti ndili pafupi ndi Yehova komanso gulu lake. Kunena zoona, JW Broadcasting yasintha kwambiri moyo wanga.” Kodi inuyo mumapindula ndi mphatso yochokera kwa Yehova imeneyi? Pa JW Broadcasting pamapezeka mapulogalamu a mwezi ndi mwezi, mavidiyo, zinthu zongomvetsera komanso nyimbo zosangalatsa.

16-17. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi nthawi imene timagwiritsa ntchito pochita zosangalatsa, nanga tingachite bwanji zimenezi?

16 Tiyenera kusamala osati pongosankha mtundu wa zosangalatsa komanso kuchuluka kwa nthawi imene timachitira zosangalatsazo. Kupanda kutero, tikhoza kumawononga nthawi yambiri podzisangalatsa tokha osati potumikira Yehova. Anthu ena zimawavuta kudziletsa pa nkhani imeneyi. Mlongo wina wazaka 18 dzina lake Abigail anati: “Kuonera TV kumandithandiza kuti maganizo akhale m’malo pambuyo potanganidwa tsiku lonse. Koma ndikapanda kusamala, ndikhoza kuwononga nthawi yambiri ndikuonera TV.” M’bale wina wachinyamata dzina lake Samuel anati: “Nthawi zina ndimangokhalira kuonera timavidiyo ta pa intaneti. Poyamba, ndimaganiza kuti ndingoonera kavidiyo kamodzi basi koma kenako ndimapezeka kuti ndaonera kwa maola atatu kapena 4.”

17 Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhala odziletsa? Choyamba, mungachite bwino kudziwa nthawi imene mumagwiritsa ntchito pochita zosangalatsazo. Mukhoza kulemba nthawi imene mumachita zimenezi pa mlungu umodzi. Mwachitsanzo, mungalembe nthawi imene mumaonera TV, kufufuza zinthu pa intaneti kapena kusewera magemu pafoni yanu. Mukapeza kuti mukugwiritsa ntchito nthawi yambiri mungachite bwino kulemba ndandanda. Pandandandayo, mulembe kaye nthawi imene muzichita zinthu zofunika kwambiri, kenako n’kulemba nthawi imene mungamachite zosangalatsa. Mukatero, mupemphe Yehova kuti azikuthandizani kutsatira ndandanda yanuyo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikhala ndi nthawi komanso mphamvu zokwanira zophunzirira Baibulo, kuchita kulambira kwa pa banja, kupita kumisonkhano komanso kulalikira ndi kuphunzitsa anthu. Zingakuthandizeninso kuti musamadziimbe mlandu chifukwa chowononga nthawi yambiri pa zosangalatsa.

PITIRIZANI KUKHALA ODZIPEREKA KWA YEHOVA YEKHA

18-19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzipereka kwa Yehova yekha?

18 Mtumwi Petulo atamaliza kulemba zokhudza mapeto a dziko la Satanali komanso za dziko latsopano limene likubwera, ananena kuti: “Okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.” (2 Pet. 3:14) Tikamamvera malangizowa, kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhala oyera mwauzimu, timasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Yehova yekha.

19 Satana ndi anthu am’dzikoli adzayesetsabe kutisokoneza kuti tisamaike Yehova pamalo oyamba. (Luka 4:13) Koma kaya tikumane ndi zotani, sitiyenera kusintha n’kumaona kuti zinthu zina ndi zofunika kwambiri. Yehova ndi amene ayenera kukhala pamalo oyamba choncho tiyeni tiziyesetsa kukhalabe odzipereka kwa iye yekha.

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

^ ndime 5 Tonsefe timakonda kwambiri kutumikira Yehova. Koma kodi ndife odzipereka kwa iye yekha? Yankho la funsoli lingadalire zinthu zimene timasankha pa moyo wathu. Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene zingatithandize kudziwa ngati ndife odzipereka kwa Yehova yekha kapena ayi.

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Sitingakonde kudya chakudya choipitsidwa chomwe chaphikidwa m’khitchini yauve. Ndiye palibe chifukwa choonera zosangalatsa zomwe zaipitsidwa ndi zinthu zachiwawa, kukhulupirira mizimu kapena chiwerewere