Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

1921​—Zomwe Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

1921​—Zomwe Zinachitika Zaka 100 Zapitazo

“KODI ndi ntchito yofunika iti imene mukuona kuti tikufunika tiigwire mofulumira m’chakachi?” Limeneli ndi funso limene linali mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1921, lopita kwa Ophunzira Baibulo akhama pa nthawiyo. Poyankha funsoli, nsanjayo inatchula mawu a pa Yesaya 61:1, 2, omwe anawakumbutsa ntchito yolalikira yomwe anapatsidwa. Lembali limati: “Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa . . . , wandituma kuti ndikalengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima, ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu.”

ALALIKI OLIMBA MTIMA

Ophunzira Baibulowa ankafunika kukhala olimba mtima kuti akwanitse kugwira ntchito yolalikira yomwe anapatsidwayi. Iwo ankafunika kulengeza “uthenga wabwino” kwa ofatsa, komanso kulengeza za “tsiku lobwezera” kwa anthu oipa.

M’bale J.  H.  Hoskin, yemwe ankakhala ku Canada, ankalalikira mopanda mantha ngakhale kuti ankatsutsidwa. Cha kumayambiriro kwa chaka cha 1921, iye anakumana ndi m’busa wa Tchalitchi cha Methodist. M’bale Hoskin anayamba kukambirana naye pomuuza kuti: “Ndikufuna kuti tikambirane mwamtendere zokhudza Baibulo. Ndipo ngakhale zitakhala kuti sitikugwirizana pa zinthu zina, timalize kukambiranaku bwinobwino ndipo tipitirize kukhala mabwenzi.” Koma izi si zomwe zinachitika. M’bale Hoskin anati: “Tinangokambirana kwa maminitsi ochepa ndipo m’busayo analowa m’nyumba ndi kumenyetsa chitseko mwamphamvu moti ndinkangoona ngati galasi lalikulu la pachitsekopo ligwa n’kusweka.”

M’busayo anakalipa kuti: “Bwanji osapita kumakalalikira anthu omwe si Akhristu?” M’bale Hoskin sanayankhe chilichonse koma pamene ankachoka pakhomopo cha mumtima anangoti, ‘Ndimaona ngatitu amene ndikuyankhula nayeyu si Mkhristu.’

Pamene m’busayo ankalalikira m’tchalitchi chake tsiku lotsatira, ananena zinthu zambiri zabodza zokhudza M’bale Hoskin. M’baleyu ananena kuti, “M’busayo anachenjeza anthu a m’chipembedzo chakewo powauza kuti ndinali munthu wabodza kwambiri m’tawuni yonseyo ndipo ndinkangofunika kuwomberedwa basi.” Koma zimenezi sizinamufooketse ndipo anapitirizabe kulalikira kwa anthu ambiri. Iye anati: “Ndinkasangalala kwambiri kugwira ntchito yolalikira m’dera limeneli. Ena anafika pondiuza kuti, ‘Ndikudziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu.’ Ndipo ankandifunsa ngati angandithandize pa zinthu china kuti ndisamasowe chilichonse.”

PHUNZIRO LAUMWINI KOMANSO PHUNZIRO LA BANJA

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa Malemba, Ophunzira Baibulo ankaika njira zosiyanasiyana zophunzirira Baibulo m’magazini imene panopa imadziwika kuti Galamukani! Mwachitsanzo, m’magaziniyi munkakhala mafunso amene makolo ankayenera kukambirana ndi ana awo. Makolowo ankafunika “kuwafunsa mafunsowa n’kumawathandiza kuti afufuze mayankho ake m’Baibulo.” Mafunso ena monga lakuti, “Kodi m’Baibulo muli mabuku angati?” ankathandiza anawo kudziwa zinthu zina zosavuta zokhudza Baibulo. Pomwe mafunso ena monga lakuti, “Kodi Mkhristu woona aliyense aziyembekezera kuti adzazunzidwa?” ankawakonzekeretsa kuti azilalikira molimba mtima.

M’magaziniyi munkakhalanso mbali imene inkathandiza anthu amene amadziwa kale mfundo zina za m’Baibulo. Mbaliyi inkakhala ndi mafunso omuthandiza munthu kuganizira zimene akuphunzira ndipo mayankho ake ankachokera m’buku la Chingelezi lakuti Studies in the Scriptures. Anthu ambiri ankapindula ndi njira zophunzirira Baibulozi. Koma magazini ya December 21, 1921 inanena kuti njira zophunzirirazi zidzasiya kuikidwa m’magaziniyi. Chifukwa chiyani?

BUKU LATSOPANO

Buku lakuti Zeze wa Mulungu

Kakhadi komuuza wophunzira zimene ayenera kuwerenga

Kakhadi ka mafunso

Abale amene ankatsogolera anazindikira kuti anthu amene akuphunzira Baibulo ankafunika kumaphunzira mfundo zoyambirira za choonadi m’njira yotsatirika. Choncho buku lakuti Zeze wa Mulungu linatulutsidwa mu November 1921. Anthu amene asonyeza chidwi ankapatsidwa bukuli ndipo ankaligwiritsa ntchito pophunzira Baibulo paokha. Kuphunzira mwa njira imeneyi, kunkathandiza anthu kudziwa “cholinga cha Mulungu chomwe ndi kudzapereka moyo wosatha kwa anthu.” Koma kodi njira yophunzirirayi inkachitika bwanji?

Munthu amene walandira bukuli, ankapatsidwanso kakhadi komudziwitsa masamba amene ayenera kuwerenga mlungu umenewo. Mlungu wotsatira, ankapatsidwanso kakhadi kena kokhala ndi mafunso a zimene anawerengazo ndipo kumapeto kwa khadilo ankalembako masamba amene ayenera kuwerenga mlungu winawo.

Mlungu uliwonse kwa milungu 12, wophunzira ankalandira kakhadi kuchokera kumpingo umene anali nawo pafupi. Nthawi zambiri amene ankakapereka makhadiwa anali anthu amene pazifukwa zina sakanatha kulalikira khomo ndi khomo kapenanso achikulire. Mwachitsanzo, Anna K. Gardner wa ku Millvale, Pennsylvania, U.S.A., ananena kuti: “Buku la Zeze wa Mulungu litatulutsidwa mchemwali wanga Thayle, yemwe ankavutika kuyenda, anali ndi ntchito yotumiza timakhaditi kwa ophunzira mlungu uliwonse.” Munthu akamaliza kuphunzira bukuli, ankayenderedwa n’cholinga chofuna kumulimbikitsa kupitirizabe kuphunzira Baibulo.

Thayle Gardner ali panjinga ya olumala

ANKAYEMBEKEZERA NTCHITO YAMBIRI

Chakumapeto kwa chakacho, M’bale J. F. Rutherford anatumiza kalata kumipingo yonse. Iye anati, “M’chaka chimenechi ntchito yokolola yachitika kwambiri kuposa zaka zonse m’nyengo yokololayi.” Poganizira zakutsogolo iye anawonjezera kuti: “Koma pali ntchito yambiri yoti igwiridwe. Tiyeni tilimbikitse ena kuti agwire nawo ntchito yabwinoyi.” N’zosakayikitsa kuti Ophunzira Baibulo pa nthawiyo anatsatira malangizowa. M’chaka cha 1922, iwo anadzagwira ntchito yolengeza za Ufumu mopanda mantha kuposa kale.