Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukonzanso Ubwenzi Wanu ndi Yehova

Kukonzanso Ubwenzi Wanu ndi Yehova

CHAKA chilichonse nkhosa zambiri za mtengo wapatali zimabwezeretsedwa mumpingo. Taganizirani “chisangalalo chochuluka” chomwe chimakhala kumwamba munthu wina akabwerera kwa Yehova. (Luka 15:7, 10) Ngati mwabwezeretsedwa, musamakayikire kuti Yesu, angelo komanso Yehova amasangalala kwambiri kukuonani kuti mwayambiranso kukhala kumbali ya choonadi. Komabe, pamene mukuyesetsa kukonzanso ubwenzi wanu ndi Yehova mungakumane ndi mavuto. Kodi ena mwa mavuto amenewa ndi ati, nanga n’chiyani chingakuthandizeni?

KODI MAVUTO AKE NDI ATI?

Pambuyo pobwezeretsedwa mumpingo, ambiri amalimbanabe ndi maganizo ofooketsa. Mwina mukumvetsa mmene Mfumu Davide ankamvera. Ngakhale pambuyo pokhululukidwa machimo ake iye ananena kuti: “Zolakwa zanga zandikulira.” (Sal. 40:12; 65:3) Munthu akabwerera kwa Yehova, akhoza kupitiriza kudziimba mlandu kapena kuchita manyazi kwa zaka zambiri. Chitsanzo ndi Isabelle yemwe anali wochotsedwa kwa zaka 20. * Iye anati, “Zinkandivuta kuvomereza kuti Yehova anandikhululukira.” Ngati munthu ali ndi maganizo ofooketsa, ndi zosavuta kuti akhalenso wofooka mwauzimu. (Miy. 24:10) Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni.

Enanso amada nkhawa kuti sakwanitsa kuchita zonse zimene zimafunika kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Atabwezeretsedwa, Antoine ananena kuti: “Ndinkaona kuti ndinaiwala zambiri zimene ndinkachita ndili wa Mboni.” Chifukwa cha zimenezi, ena zingawavute kuti ayambirenso kuchita zonse zimene angathe potumikira Yehova.

Mwachitsanzo, munthu wina amene nyumba yake yawonongeka kwambiri ndi mphepo yamkuntho, angamaone kuti pakufunika nthawi komanso mphamvu zochuluka kuti aimangenso. Mofanana ndi zimenezi, ngati ubwenzi wanu ndi Yehova wawonongeka chifukwa chochita tchimo lalikulu, mungamaone kuti pakufunika kuchita khama kwambiri kuti muubwezeretse. Komabe mungathandizidwe kuchita zimenezi.

Yehova amatiuza kuti: “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.” (Yes. 1:18) Mwachita kale zambiri kuti “mukhalenso pa ubwenzi wabwino” ndi Yehova. Iye amakukondani chifukwa chakuti mwayesetsa kuchita zimenezi. Tangoganizani, mwam’patsa Yehova yankho loti azipereka kwa Satana yemwe amamunyoza.​—Miy. 27:11.

Kubwerera kwa Yehova kwakuthandizani kuti mumuyandikire ndipo iyenso akulonjeza kuti adzakuyandikirani. (Yak. 4:8) Komabe, pamafunika zambiri kuposa pakungodziwika kuti mwabwezeretsedwa mumpingo. Muyenera kupitiriza kukulitsa chikondi chanu pa Yehova, yemwe ndi Atate wanu komanso Mnzanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

MUZIDZIIKIRA ZOLINGA ZIMENE MUNGAZIKWANIRITSE

Muziyesetsa kudziikira zolinga zimene mungazikwaniritse. N’kutheka kuti mukukumbukira mfundo zoyambirira zimene munaphunzira zokhudza Yehova komanso malonjezo ake a m’tsogolo. Koma muyeneranso kumachita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse monga kulalikira uthenga wabwino komanso kusonkhana ndi abale ndi alongo anu. Taganizirani zolinga zotsatirazi.

Muzilankhula ndi Yehova pafupipafupi. Atate wanu amadziwa kuti mukamangodziimba mlandu nthawi zonse, zingakhale zovuta kuti muzipemphera kwa iye. (Aroma 8:26) Komabe “Limbikirani kupemphera” ndipo muzimuuza Yehova kuti mukufunitsitsa kukhala nayenso pa ubwenzi. (Aroma 12:12) Andrej ananena kuti: “Ndinkadziimba mlandu kwambiri ndipo ndinkachita manyazi. Koma nthawi iliyonse imene ndapemphera, ndinkamva bwino komanso ndinkapeza mtendere wamumtima.” Ngati simukudziwa zomwe mungatchule popemphera, muziganizira mapemphero a Mfumu Davide amene anapemphera atalapa, opezeka mu Salimo 51 ndi 65.

Muziphunzira Baibulo nthawi zonse. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso muzikonda kwambiri Yehova. (Sal. 19:7-11) Felipe anati: “Chimene chinachititsa kuti poyambapo ndifooke n’kukhumudwitsa Yehova, ndi kusakhala ndi pulogalamu yowerenga komanso kuphunzira Baibulo pandekha. Sindinkafuna kumukhumudwitsanso choncho ndinaonetsetsa kuti ndiziphunzira Baibulo pandekha nthawi zonse.” Inunso mukhoza kuchita chimodzimodzi. Ngati mukufuna kudziwa mmene mungasankhire nkhani zoti muziphunzira panokha, mukhoza kupempha mnzanu wolimba mwauzimu kuti akuthandizeni.

Muziyesetsa kuti muyambirenso kugwirizana ndi abale ndi alongo anu. Anthu ena amene abwezeretsedwa amada nkhawa kuti mwina abale ndi alongo ena anawakwiyira. Larissa anati: “Ndinkachita manyazi kwambiri. Ndinkaona kuti ndinakhumudwitsa abale ndi alongo anga. Ndinavutika ndi maganizo amenewa kwa nthawi yayitali.” Dziwani kuti akulu ndi Akhristu ena olimba amafunitsitsa kukuthandizani kuti mukonzenso ubwenzi wanu ndi Yehova. (Onani bokosi lakuti, “ Kodi Akulu Angachite Zotani?”) Iwo amasangalala kuti munabwerera mumpingo ndipo amafuna kuti zinthu zizikuyenderani bwino.​—Miy. 17:17.

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muyambenso kugwirizana ndi Akhristu anzanu? Muzichita nawo zonse zimene abale ndi alongo akuchita monga kupezeka pamisonkhano ndiponso kulalikira nthawi zonse. Kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji? Felix anati: “Abale ndi alongo ankafunitsitsa nditabwerera mumpingo choncho ndinaona kuti amandikonda. Iwo anandithandiza kuti ndizidzimva kuti ndabwereranso m’banja la Yehova, iye anandikhululukira komanso ndingapitirize kumutumikira.​—Onani bokosi lakuti “ Kodi Mungachite Zotani?

MUSAFOOKE

Satana apitiriza kukutumizirani “mphepo zamkuntho” zambiri n’cholinga choti akufooketseni pamene mukukonzanso ubwenzi wanu ndi Yehova. (Luka 4:13) Choncho konzekerani panopa poyesetsa kulimbitsa ubwenziwu.

Ponena za nkhosa zake, Yehova akulonjeza kuti: “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna, zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa.” (Ezek. 34:16) Iye wathandiza anthu ambiri kukhalanso naye pa ubwenzi. Choncho musamakayikire kuti akufunitsitsa kukuthandizani inunso kuti mupitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba kwambiri.

^ ndime 4 Mayina munkhaniyi asinthidwa.