Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 42

Musamakayikire Kuti Munapeza Choonadi

Musamakayikire Kuti Munapeza Choonadi

“Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.”​—1 ATES. 5:21.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amasokonezeka?

 PALI zipembedzo zambirimbiri padzikoli zotchedwa za Chikhristu zomwe zimati zimalambira Mulungu movomerezeka. N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amasokonezeka. Iwo amafunsa kuti, “Kodi pali chipembedzo choona chimodzi chokha, kapena zipembedzo zonse zimasangalatsa Mulungu?” Kodi ifeyo timakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene timaphunzitsa ndi choonadi, komanso kuti njira imene a Mboni za Yehova amalambirira Mulungu ndi imene ili yovomerezeka kwa Yehova? Kodi n’zothekadi kudziwa zoona pa nkhaniyi? Tiyeni tione.

2. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 1:5, n’chifukwa chiyani mtumwi Paulo sankakayikira kuti zimene ankakhulupirira ndi choonadi?

2 Mtumwi Paulo sankakayikira ngakhale pang’ono kuti zomwe ankakhulupirira ndi choonadi. (Werengani 1 Atesalonika 1:5.) Sikuti ankakhulupirira zimenezi chifukwa chakuti zinkangomusangalatsa. M’malomwake, iye ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama kwambiri ndipo ankakhulupirira kuti “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Tim. 3:16) Ndiye kodi zimene ankaphunzira zinamuthandiza kuzindikira chiyani? M’Malemba, Paulo anapeza umboni wosatsutsika wakuti Yesu anali Mesiya yemwe Mulungu analonjeza, umboni womwe atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda ankaukana. Atsogoleri achinyengowa ankanena kuti amaphunzitsa zoona zokhudza Mulungu koma ankamukana m’zochita zawo. (Tito 1:16) Mosiyana ndi anthuwa, Paulo sankachita kusankha mbali ya Mawu a Mulungu yoti azikhulupirira. Iye ankaphunzitsa komanso kutsatira “chifuniro chonse cha Mulungu.”​—Mac. 20:27.

3. Kodi tiyenera kupeza mayankho a mafunso athu onse kuti titsimikizire kuti tili m’chipembedzo choona? (Onaninso bokosi lakuti, “ Maganizo ndi Ntchito za Yehova ‘N’zochuluka Kwambiri Moti Sitingathe Kuzifotokoza.’”)

3 Anthu ena amaona kuti chipembedzo choona chiyenera kukhala ndi yankho la funso lililonse, ngakhale mafunso amene m’Baibulo mulibe mayankho ake. Koma kodi zimenezi n’zomveka? Taganizirani chitsanzo cha Paulo. Iye analimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘azitsimikizira zinthu zonse,’ koma anavomerezanso kuti panali zambiri zomwe sankazimvetsa. (1 Ates. 5:21) Iye analemba kuti: “Tikudziwa moperewera” komanso anawonjezera kuti, “sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino.” (1 Akor. 13:9, 12) Paulo sankamvetsa zinthu zonse, chimodzimodzinso ifeyo. Komabe iye ankamvetsa zinthu zikuluzikulu zokhudza Yehova. Zimene ankadziwazo zinali zokwanira kumutsimikizira kuti zomwe ankakhulupirirazo ndi choonadi.

4. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri kuti tinapeza choonadi, nanga tikambirana zotani zokhudza Akhristu oona?

4 Chimodzi mwa zinthu zomwe zingatithandize kukhulupirira kwambiri kuti tinapeza choonadi ndi kuyerekezera njira yolambirira imene Yesu anayambitsa ndi zimene a Mboni za Yehova amachita masiku ano. Munkhaniyi tiona kuti Akhristu oona (1) amakana kulambira mafano, (2) amalemekeza dzina la Yehova, (3) amakonda choonadi komanso (4) amakondana kwambiri.

TIMAKANA KULAMBIRA MAFANO

5. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu pa nkhani yolambira Mulungu moyenera, nanga tingagwiritse ntchito bwanji zimene anaphunzitsa?

5 Ali kumwamba komanso padzikoli, Yesu ankalambira Yehova yekha chifukwa chomukonda kwambiri. (Luka 4:8) Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azilambira Yehova yekha. Yesu ngakhalenso ophunzira ake okhulupirika sanagwiritsirepo ntchito zifaniziro polambira. Mulungu ndi mzimu, choncho palibe munthu amene angapange chinthu chooneka ngati iye. (Yes. 46:5) Nanga bwanji pa nkhani yopanga komanso kupemphera kwa zifaniziro za anthu omwe ena amati ndi oyera? Mulamulo lachiwiri pa Malamulo Khumi, Yehova ananena kuti: “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi . . . Usaziweramire.” (Eks. 20:4, 5) Mawu amenewa ndi omveka bwino kwa anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu.

6. Kodi ndi njira yolambirira iti yomwe a Mboni za Yehova amatsatira masiku ano?

6 Olemba mbiri amavomereza kuti Akhristu oyambirira ankalambira Mulungu yekha. Mwachitsanzo, buku lina la mbiri yakale linafotokoza kuti Akhristuwa “sanakagwirizana m’pang’ono pomwe” ndi maganizo oika zifaniziro m’malo olambirira. Masiku ano a Mboni za Yehova amatsatira njira yolambirira imene Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito. Sitipemphera kwa zifaniziro za “oyera” kapena angelo ngakhalenso kwa Yesu. Komanso sitilambira zizindikiro za dziko. Kaya anthu atichitire zotani, ndife otsimikiza kutsatira mawu a Yesu akuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira.”​—Mat. 4:10.

7. Kodi pali kusiyana kwakukulu kuti pakati pa Mboni za Yehova ndi zipembedzo zina?

7 Masiku ano, anthu ambiri amatsatira atsogoleri achipembedzo otchuka. Iwo amakonda kwambiri atsogoleri amenewa moti mpaka nthawi zina amachita zinthu ngati akuwalambira. Anthu amadzadzana m’matchalitchi awo, kugula mabuku awo komanso amapereka ndalama zambiri zothandizira matchalitchiwa. Ena amakhulupirira chilichonse chimene atsogoleriwa amanena. Amasangalala kwambiri akawaona, ngati kuti aona Yesu weniweniyo. Mosiyana ndi zimenezi, Akhristu oona sakhala ndi atsogoleri. Ngakhale kuti timalemekeza abale omwe amatsogolera, timavomereza mawu a Yesu omveka bwino akuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mat. 23:8-10) Sitilambira anthu, kaya akhale atsogoleri achipembedzo kapena andale. Ndipo sitithandiza mabungwe awo achipembedzo kapena andale komanso sitikhala kumbali ya dziko. Pa mbali zimenezi timakhala osiyana kwambiri ndi zipembedzo zina zomwe zimati ndi za Chikhristu.​—Yoh. 18:36.

TIMALEMEKEZA DZINA LA YEHOVA

Akhristu oona amasangalala kuuza ena zokhudza Yehova (Onani ndime 8-10) *

8. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amafuna kuti dzina lake lilemekezedwe komanso lidziwike kwa onse?

8 Pa nthawi ina Yesu anapemphera kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Yehova anayankha pemphero limeneli kuchokera kumwamba ndi mawu amphamvu ndipo analonjeza kuti adzalilemekeza. (Yoh. 12:28) Pa utumiki wake wonse, Yesu ankalemekeza dzina la Atate wake. (Yoh. 17:26) Choncho n’zomveka kuti Akhristu oona amasangalala kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kuuza ena za dzinali.

9. Kodi Akhristu oyambirira anasonyeza bwanji kuti ankalemekeza dzina la Mulungu?

9 Mpingo wa Chikhristu utangokhazikitsidwa kumene mu nthawi ya atumwi, Yehova “anacheukira anthu a mitundu ina . . . kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Akhristu oyambirira ankasangalala kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kuuza ena zokhudza dzinali. Iwo ankaligwiritsa ntchito akamalalikira komanso akamalemba mabuku a m’Baibulo. * Choncho anasonyezadi kuti anali anthu odziwika ndi dzina la Mulungu.​—Mac. 2:14, 21.

10. Kodi timadziwa bwanji kuti ndi a Mboni za Yehova okha omwe amadziwitsa anthu za dzina lakuti Yehova?

10 Kodi a Mboni za Yehova ndi anthu odziwika ndi dzina la Mulungu? Tiyeni tione umboni wake. Masiku ano atsogoleri ambiri azipembedzo amayesetsa kubisa zoti Mulungu ali ndi dzina. Iwo akhala akuchotsa dzinali m’Mabaibulo awo ndipo nthawi zinanso amaletsa kuligwiritsira ntchito m’matchalitchi awo. * Ndiye kodi pali amene angatsutse kuti ndi a Mboni za Yehova okha omwe amalemekeza dzina la Yehova? Kuposa chipembedzo chilichonse, ifeyo ndi amene tikuthandiza kwambiri anthu kuti adziwe dzina la Mulungu. Pa nkhani imeneyi, tikuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu lakuti Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12) Tatulutsa Mabaibulo oposa 240 miliyoni a Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomwe linabwezeretsa dzina la Yehova m’malo amene omasulira Mabaibulo ena anachotsamo. Ndipo timatulutsa mabuku othandiza pophunzira Baibulo omwe amagwiritsa ntchito dzina la Yehova m’zilankhulo zoposa 1,000.

TIMAKONDA CHOONADI

11. Kodi Akhristu oyambirira anasonyeza bwanji kuti ankakonda choonadi?

11 Yesu ankakonda choonadi, chimenechi ndi choonadi chonena za Mulungu komanso chifuniro chake. Iye ankachita zinthu mogwirizana ndi choonadi komanso ankadziwitsa ena choonadicho. (Yoh. 18:37) Otsatira oona a Yesu amakondanso kwambiri choonadi. (Yoh. 4:23, 24) Ndipotu mtumwi Petulo ananena kuti Chikhristu ndi “njira ya choonadi.” (2 Pet. 2:2) Chifukwa chokonda kwambiri choonadi Akhristu oyambirira ankakana ziphunzitso zachipembedzo, miyambo komanso maganizo a anthu osemphana ndi choonadi. (Akol. 2:8) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano Akhristu oona “akuyendabe m’choonadi” poyesetsa kuti zonse zimene amakhulupirira komanso kuchita zizichokera m’Mawu a Yehova.​—3 Yoh. 3, 4.

12. Kodi chimachitika n’chiyani abale a m’Bungwe Lolamulira akazindikira kuti pakufuna kusintha kamvedwe ka choonadi pa mfundo inayake, nanga n’chifukwa chiyani amatero?

12 Anthu a Mulungu masiku ano sanena kuti nthawi zonse amamvetsa mfundo zonse za choonadi. Nthawi zina iwo amalakwitsa akamafotokoza mfundo zina za m’Baibulo kapena malangizo oyendetsera gulu la Yehova. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Baibulo limanena momveka bwino kuti munthu amamvetsa zinthu molondola nthawi ikamapita. (Akol. 1:9, 10) Yehova amaulula choonadi mwapang’onopang’ono choncho tiyenera kudikira moleza mtima kuti kuwala kwa choonadi kuwonjezeke. (Miy. 4:18) Abale a m’Bungwe Lolamulira akaona kuti pakufunika kusintha mmene timamvera mfundo inayake ya choonadi, amasintha mwamsanga. Matchalitchi ambiri omwe amati ndi a Chikhristu amasintha ziphunzitso zawo n’cholinga chofuna kusangalatsa anthu awo kapenanso kuti agwirizane ndi mmene zinthu zikuyendera m’dzikoli. Koma gulu la Yehova limasintha zinthu n’cholinga choti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso kutsatira njira yolambirira imene Yesu anayambitsa. (Yak. 4:4) Timasintha zinthu osati chifukwa cha zimene zikuchitika panopa kapena zimene anthu ambiri akufuna, koma chifukwa chomvetsa bwino mfundo za m’Malemba. Timakonda kwambiri choonadi.​—1 Ates. 2:3, 4.

TIMAKONDANA KWAMBIRI

13. Kodi ndi khalidwe lofunika liti limene Akhristu oona amasonyeza, nanga kodi limaonekera bwanji pakati pa a Mboni za Yehova?

13 Akhristu oyambirira ankadziwika ndi makhalidwe ambiri abwino koma khalidwe lofunika kwambiri linali chikondi. Yesu ananena kuti: “Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Masiku ano a Mboni za Yehova amakondana komanso amakhala ogwirizana padziko lonse. Ndife osiyana ndi zipembedzo zina zonse chifukwa timachita zinthu ngati a m’banja limodzi ngakhale kuti timachokera m’mayiko komanso m’zikhalidwe zosiyanasiyana. Umboni wakuti timakondana kwambiri timauona pamisonkhano yathu yampingo, yadera komanso yachigawo. Zimenezi zimatithandiza kutsimikizira kwambiri kuti tikulambira Yehova m’njira imene iyeyo amaivomereza.

14. Mogwirizana ndi Akolose 3:12-14, kodi ndi njira yofunika kwambiri iti imene tingasonyezerane chikondi chochokera pansi pa mtima?

14 Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tikhale okondana kwambiri.’ (1 Pet. 4:8) Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timakondana ndi kukhululukirana komanso kulolerana. Timayesetsanso kukhala ochereza komanso owolowa manja kwa onse mumpingo, ngakhalenso amene atilakwira. (Werengani Akolose 3:12-14.) Chikondi chimenechi ndi khalidwe lofunika kwambiri limene limadziwikitsa Akhristu oona.

“CHIKHULUPIRIRO CHIMODZI”

15. Kodi timatsanzira Akhristu oyambirira pa nkhani ya kulambira m’njira zinanso ziti?

15 Timayesetsanso kutsatira njira yolambirira imene mpingo woyambirira wa Chikhristu unkatsatira. Mwachitsanzo, m’gulu lathu muli oyang’anira oyendayenda, akulu komanso atumiki othandiza, zomwenso zinkachitika mu nthawi ya atumwi. (Afil. 1:1; Tito 1:5) Mmene timaonera nkhani ya kugonana ndi ukwati, kulemekeza kupatulika kwa magazi komanso kufunitsitsa kuteteza mpingo kwa anthu ochimwa osalapa, timatengera mmene zinkachitikira mumpingo wa Chikhristu woyambirira.​—Mac. 15:28, 29; 1 Akor. 5:11-13; 6:9, 10; Aheb. 13:4.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zili pa Aefeso 4:4-6?

16 Yesu anafotokoza kuti ambiri azidzanena kuti ndi ophunzira ake, koma si onse omwe adzakhale ophunzira ake enieni. (Mat. 7:21-23) Ndiponso Malemba anachenjezeratu kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri ‘adzaoneka ngati odzipereka kwa Mulungu.’ (2 Tim. 3:1, 5) Koma Baibulo limatiuza mosapita m’mbali kuti pali “chikhulupiriro chimodzi” chimene Mulungu amavomereza.​—Werengani Aefeso 4:4-6.

17. Ndi ndani masiku ano amene akutsatira Yesu ndipo ali m’chipembedzo choona?

17 Kodi ndi ndani amene ali m’chipembedzo choona masiku ano? Munkhaniyi taona zimene umboni ukusonyeza. Taona njira yolambirira imene Yesu anaphunzitsa yomwe Akhristu oyambirira ankatsatira. Yankho loonekeratu ndi lakuti ndi a Mboni za Yehova okha. Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala mmodzi wa anthu a Yehova komanso kudziwa choonadi chokhudza iye ndi chifuniro chake. Choncho tiyeni tipitirize kugwira mwamphamvu choonadi.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana zokhudza kulambira koona kumene Yesu anakhazikitsa komanso zimene ophunzira ake ankachita potsatira kulambira koonako. Tionanso umboni wakuti masiku ano a Mboni za Yehova amatsatira kulambira koona kumeneko.

^ ndime 10 Mwachitsanzo, mu 2008, Papa Benedict wa 16 analamula kuti dzina la Mulungu “lisamagwiritsidwe ntchito kapena kutchulidwa” m’Matchalitchi a Katolika, poimba nyimbo kapenanso m’mapemphero.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Gulu la Yehova latulutsa Baibulo la Dziko Latsopano m’zilankhulo zoposa 200 n’cholinga chakuti anthu aziwerenga Baibulo lomwe lili ndi dzina la Mulungu m’chilankhulo chawo.