Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi Aisiraeli ankapeza zakudya zina m’chipululu kupatula pa mana ndi zinziri?
Pa nthawi imene Aisiraeli anali m’chipululu kwa zaka 40, chakudya chawo chachikulu chinali mana. (Eks. 16:35) Yehova anawapatsanso zinziri maulendo awiri. (Eks. 16:12, 13; Num. 11:31) Komabe, Aisiraeli anali ndi zakudya zinanso zomwe ankadya.
Mwachitsanzo, nthawi zina Yehova ankatsogolera anthu ake kuti akamange “msasa” pamalo ena pamene pankapezeka madzi ndi zakudya zachilengedwe. (Num. 10:33) Ena mwa malo ngati amenewa, anali ku Elimu “kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza.” (Eks. 15:27) Buku lina lofotokoza za zomera zotchulidwa m’Baibulo linanena kuti mtundu umenewu wa kanjedza, “womwe unkamera m’chipululu, unkapezeka m’malo ambiri . . . ndipo unkathandiza anthu mamiliyoni ambiri kupeza chakudya, mafuta ndi malo ogona.”—Plants of the Bible
Aisiraeli ayenera kuti anaimanso pamalo ena amene masiku ano amatchedwa Feiran, omwe ndi m’dera lomwe limatchedwa Chigwa cha Feiran. a Buku lina lofotokoza za malo otchulidwa m’Baibulo linanena kuti chigwachi “ndi chachitali makilomita 130 ndipo ndi chimodzi mwa zigwa zazitali kwambiri, zokongola komanso zotchuka kwambiri ku Sinai.” Bukuli linanenanso kuti: “Munthu akayenda makilomita 45 kuchokera pamene chigwachi chimakafika m’nyanja, amafika kudera la Feiran. Derali ndi lokwera mamita 610 ndipo ndi lalitali pafupifupi makilomita 5. M’derali muli mitengo yambiri ya kanjedza ndipo ndi lokongola moti anthu amalitchula kuti Edeni wa ku Sinai. Kwa zaka zambiri anthu akhala akubwera m’derali potsatira mitengo ya kanjedzayi.”—Discovering the World of the Bible
Pamene Aisiraeli ankachoka ku Iguputo, anatenga ufa wophikira mikate, zokandiramo ufawo ndipo n’kuthekanso kuti anatenga tirigu ndi mafuta. Komabe, zinthuzi sizikanatenga nthawi yaitali. Anthuwa anatenganso “nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zambirimbiri.” (Eks. 12:34-39) Koma chifukwa cha kutentha kwa m’chipululu, ziweto zambiri ziyenera kuti zinafa. Aisiraeli ayeneranso kuti anadya nyama zina ndi ndipo zina ankazipereka nsembe, mwinanso kwa milungu yabodza. b (Mac. 7:39-43) Koma Aisiraeli ayenera kuti ankawetabe ziweto. Umboni wake ndi zimene Yehova anauza anthu ake pamene anasonyeza kusowa chikhulupiriro. Iye anati: “Ana anu adzakhala abusa m’chipululu kwa zaka 40.” (Num. 14:33) N’kutheka kuti ziwetozi nthawi zina zinkawapatsa Aisiraeli mkaka ndiponso nyama ngakhale kuti sizinali zokwanira kuti anthu pafupifupi 3 miliyoni adye kwa zaka 40. c
Kodi ziwetozi zinkapeza kuti chakudya ndi madzi? d Kalelo kuyenera kuti nthawi zina kunkagwa mvula yambiri ndipo m’chipululu munkapezeka zomera zambiri. Buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, limanena kuti zaka 3,500 zapitazo, “madzi ankapezeka ambiri ku Arabia kusiyana ndi mmene zilili panopa. Kuderali kuli zigwa zambiri zouma zomwe poyamba zinali mitsinje ndipo umenewu ndi umboni woti kalelo kunkagwa mvula yambiri.” Ngakhale zinali choncho, m’chipululu simunkakhala zomera zambiri ndipo anali malo oopsa. (Deut. 8:14-16) Popanda madzi amene Yehova ankawapatsa m’njira yodabwitsa, Aisiraeli pamodzi ndi ziweto zawo akanafa.—Eks. 15:22-25; 17:1-6; Num. 20:2, 11.
Mose anauza Aisiraeli kuti Yehova anawadyetsa mana n’cholinga choti ‘adziwe kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse ochokera m’kamwa mwa Yehova.’—Deut. 8:3.
a Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1992, tsamba 24-25.
b Baibulo limatchula maulendo awiri pamene nsembe za nyama zinaperekedwa kwa Yehova m’chipululu. Koyamba ndi pamene Aisiraeli ankayamba kukhala ndi ansembe ndipo kachiwiri ndi pa Pasika. Zonsezi zinachitika mu 1512 B.C.E., chomwe ndi chaka chachiwiri kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo.—Lev. 8:14–9:24; Num. 9:1-5.
c Chakumapeto kwa zaka 40 zimene anayenda m’chipululu, Aisiraeli anatenga ziweto zambiri za mitundu imene anaigonjetsa pankhondo. (Num. 31:32-34) Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kudya mana mpaka pamene anakalowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Yos. 5:10-12.
d Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti ziweto zinkadya mana, chifukwa ankangoperekedwa mogwirizana ndi mmene munthu aliyense angadyere.—Eks. 16:15, 16.