Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 43

Yehova “Adzakulimbitsani”

Yehova “Adzakulimbitsani”

“[Yehova] adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.” —1 PET. 5:10.

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi atumiki a Mulungu akale ankapeza bwanji mphamvu?

 NTHAWI zambiri Baibulo limafotokoza za amuna omwe anali ndi chikhulupiriro cholimba. Koma si nthawi zonse pamene iwo ankadzimva choncho. Mwachitsanzo, nthawi zina Mfumu Davide ankadziona kuti anali ‘wamphamvu ngati phiri,’ koma nthawi zina ‘ankasokonezeka,’ kapena kuti kuchita mantha. (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali ndi mphamvu zapadera mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, ankadziwa kuti popanda kuthandizidwa ndi Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:​5, 6; 16:17) Amuna okhulupirikawa ankakhala ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova ndi amene ankawapatsa mphamvuzo.

2. N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo ananena kuti akakhala wofooka m’pamenenso ankakhala wamphamvu? (2 Akorinto 12:​9, 10)

2 Mtumwi Paulo nayenso ankadziwa kuti ankafunika kupatsidwa mphamvu ndi Yehova. (Werengani 2 Akorinto 12:​9, 10.) Mofanana ndi tonsefe, Paulo ankakumananso ndi mavuto monga matenda. (Agal. 4:​13, 14) Nthawi zina iye ankavutikanso kuchita zinthu zoyenera. (Aroma 7:​18, 19) Ndipo nthawi zina ankada nkhawa kapena kuchita mantha. (2 Akor. 1:​8, 9) Komabe, pamene Paulo ankakhala wofooka m’pamenenso ankakhala wamphamvu. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Yehova ankamupatsa mphamvu zimene ankafunikira kuti apirire mavuto ake.

3. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

3 Yehova amalonjeza kuti nafenso akhoza kutipatsa mphamvu. (1 Pet. 5:10) Koma sitingayembekezere kulandira mphamvuzi titangokhala. Mwachitsanzo, injini imathandiza kuti galimoto iyende. Komabe, dalaivala amafunika kuchitapo kanthu kuti iyende. Mofanana ndi zimenezi, Yehova ndi wokonzeka kutipatsa mphamvu zimene timafunikira. Komabe tiyenera kuchitapo kanthu kuti tilandire mphamvuzo. Ndiye kodi Yehova watipatsa zinthu ziti kuti tipeze mphamvu? Nanga tiyenera kuchita chiyani kuti tilandire mphamvuzo? Kuti tipeze mayankho a mafunsowa, tiyeni tikambirane mmene Yehova anaperekera mphamvu kwa mneneri Yona, Mariya yemwe anali mayi ake a Yesu komanso mtumwi Paulo. Tionanso mmene Yehova akupitirizira kupereka mphamvu kwa atumiki ake masiku ano.

MUNGAPEZE MPHAMVU POPEMPHERA KOMANSO KUPHUNZIRA MAWU A MULUNGU

4. Kodi tingatani kuti Yehova azitipatsa mphamvu?

4 Njira imodzi imene tingapezere mphamvu kuchokera kwa Yehova ndi kupemphera. Poyankha mapemphero athu, Yehova angatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7) Tingalimbikitsidwenso tikamawerenga Mawu ake komanso kuwaganizira. (Sal. 86:11) Paja Mawu a Yehova opezeka m’Baibulo “ndi amphamvu.” (Aheb. 4:12) Mukamapemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake, mudzapeza mphamvu zokuthandizani kupirira, kukhalabe osangalala komanso kukwanitsa kuchita utumiki wovuta. Tiyeni tione mmene Yehova anaperekera mphamvu kwa mneneri Yona.

5. N’chifukwa chiyani mneneri Yona ankafunika kupatsidwa mphamvu?

5 Mneneri Yona ankafunika kupatsidwa mphamvu. Iye anathawa utumiki wovuta umene Yehova anamupatsa. Chifukwa cha zimenezi, panyanja panachita mphepo yamkuntho ndipo iye komanso anthu omwe anakwera nawo chombo anatsala pang’ono kufa. Ataponyedwa m’nyanja, mosayembekezereka anapezeka ali m’mimba mwa chinsomba chachikulu. Kodi mukuganiza kuti Yona anamva bwanji ali m’mimbamo, momwe munali mdima waukulu? Kodi iye ankaona kuti basi afera momwemo? Kapena kodi ankaona kuti Yehova wamutaya? Yona ayenera kuti ankachita mantha kwambiri.

Mofanana ndi mneneri Yona, kodi tingatani kuti tipezenso mphamvu tikakumana ndi mayesero? (Onani ndime 6-9)

6. Mogwirizana ndi Yona 2:​1, 2, 7, kodi n’chiyani chinathandiza Yona kupezanso mphamvu ali m’mimba mwa chinsomba?

6 Kodi Yona anatani kuti apeze mphamvu pamene anali yekhayekha m’mimba mwa chinsomba? Chinthu chofunika chomwe anachita ndi kupemphera. (Werengani Yona 2:​1, 2, 7.) Ngakhale kuti Yona sanamvere Yehova, sankakayikira kuti iye amvetsera pemphero lake losonyeza kudzichepetsa komanso kulapa. Yona ankaganiziranso Malemba. N’chifukwa chiyani tikutero? M’pemphero lake lopezeka pa Yona chaputala 2, muli mawu ambiri omwe amapezekanso m’buku la Masalimo. (Mwachitsanzo, yerekezerani Yona 2:​2, 5 ndi Salimo 69:1; 86:7.) N’zoonekeratu kuti Yona ankadziwa bwino malembawa. Ndipo kuganizira malemba pa nthawi yovutayi, kunamutsimikizira kuti Yehova amuthandiza. Kenako Yehova anamupulumutsa ndipo iye anali wokonzeka kukagwira ntchito imene anamutuma.—Yona 2:10–3:4.

7-8. Kodi m’bale wina wa ku Taiwan anapeza bwanji mphamvu atakumana ndi mavuto?

7 Nkhani ya Yona ikhoza kutithandiza pamene takumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Taiwan, dzina lake Zhiming, b yemwe akudwala matenda aakulu. Kuwonjezera pamenepo, anthu a m’banja lake amamutsutsa kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma iye amapeza mphamvu kuchokera kwa Yehova popemphera komanso kuphunzira Mawu ake. Iye anati: “Nthawi zina mavuto akayamba ndimachita mantha moti maganizo anga sakhala m’malo ndipo zimakhala zovuta kuphunzira pandekha.” Koma iye amadalira Yehova kuti amuthandize. Anawonjezeranso kuti: “Choyamba, ndimapemphera kwa Yehova. Kenako ndimaika mahedifoni n’kumamvetsera nyimbo za Ufumu. Nthawi zina ndimaimba nawo chapansipansi mpaka maganizo anga atakhazikika. Kenako ndimayamba kuphunzira.”

8 Kuphunzira payekha kwamuthandiza Zhiming m’njira imene sankayembekezera. Mwachitsanzo, atapangidwa opaleshoni yaikulu, nesi anamuuza kuti maselo ake ofiira ndi ochepa ndipo afunika kuikidwa magazi. Asanapangidwe opaleshoniyo, Zhiming anawerenga nkhani yokhudza mlongo wina yemwe anapangidwanso opaleshoni ngati yomweyo. Maselo ofiira a mlongoyo anatsika kwambiri kuposa ake. Koma mlongoyo sanavomere kuikidwa magazi ndipo anachira bwinobwino. Nkhani imeneyi inathandiza Zhiming kuti akhalebe wokhulupirika.

9. Kodi mungatani ngati mwafooka ndi mayesero omwe mwakumana nawo? (Onaninso chithunzi.)

9 Mukamakumana ndi mayesero, kodi mumakhala ndi nkhawa kwambiri moti mumalephera kupemphera kwa Yehova? Kapena mumafooka kwambiri moti mumalephera kuphunzira panokha? Muzikumbukira kuti Yehova amamvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Choncho ngakhale mutangopemphera mwachidule, musamakayikire kuti iye akupatsani zimene mukufunikira. (Aef. 3:20) Ngati mukulephera kuwerenga komanso kuphunzira panokha chifukwa cha mavutowo, mungayese kumvetsera zinthu zochita kujambulidwa monga Baibulo kapena mabuku athu ena. Kumvetsera nyimbo kapena kuonera vidiyo pa jw.org kukhozanso kukuthandizani. Mukamapemphera kwa Yehova komanso kugwiritsa ntchito zinthu zimene watipatsa, mumakhala mukumulola kuti akupatseni mphamvu.

ABALE NDI ALONGO ANGAKUTHANDIZENI KUPEZA MPHAMVU

10. Kodi abale ndi alongo athu amatithandiza bwanji kupeza mphamvu?

10 Yehova akhoza kutipatsa mphamvu pogwiritsa ntchito abale ndi alongo. Iwo akhoza ‘kutithandiza ndi kutilimbikitsa’ tikamakumana ndi mayesero kapena tikapatsidwa utumiki winawake wovuta. (Akol. 4:​10, 11) Timafuna kuti anzathu atithandize, makamaka “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Tikafooka, Akhristu anzathu angatithandize kupeza zimene tikufunikira, kutithandiza kuti tisamade nkhawa komanso kuti tipitirizebe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Tiyeni tikambirane mmene ena anathandizira Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu, kupezanso mphamvu.

11. N’chifukwa chiyani Mariya ankafunika kupatsidwa mphamvu?

11 Mariya ankafunika kulimbikitsidwa. Iye anachita mantha atauzidwa ndi mngelo Gabirieli kuti achite utumiki wovuta. Mariya sanali pabanja, koma mngeloyo anamuuza kuti adzakhala ndi pakati. Iye anali asanalerepo mwana, koma ankafunika kusamalira mwana yemwe adzakhale Mesiya. Komanso popeza anali asanagonepo ndi mwamuna, kodi akanamufotokozera bwanji Yosefe, yemwe ankayembekezera kukhala naye pabanja?—Luka 1:​26-33.

12. Mogwirizana ndi Luka 1:​39-45, kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu zimene ankafunikira?

12 Kodi Mariya anapeza bwanji mphamvu kuti akwaniritse utumiki wovutawu? Iye anadalira ena kuti amuthandize. Mwachitsanzo, anapempha Gabirieli kuti amufotokozere zambiri zokhudza utumikiwu. (Luka 1:34) Pambuyo pake, iye anapita kwa wachibale wake, dzina lake Elizabeti, yemwe ankakhala “kudera lamapiri” la Yuda. Ulendo umenewu unali wothandiza kwambiri. Elizabeti anayamikira Mariya ndipo mouziridwa ndi Yehova, anamufotokozera ulosi wokhudza mwana yemwe adzabadweyo. (Werengani Luka 1:​39-45.) Mariya ananena kuti Yehova ‘wamuchitira zamphamvu ndi dzanja lake.’ (Luka 1:​46-51) Yehova anapatsa mphamvu Mariya pogwiritsa ntchito Gabirieli ndi Elizabeti.

13. Kodi chinachitika n’chiyani mlongo wina wa ku Bolivia atapempha Akhristu anzake kuti amuthandize?

13 Mofanana ndi Mariya, inunso Yehova angakupatseni mphamvu kudzera mwa Akhristu anzanu. Mlongo wina wa ku Bolivia, dzina lake Dasuri, ankafunikiranso mphamvu ngati zimenezi. Bambo ake atadwala matenda aakulu ndiponso kugonekedwa m’chipatala, Dasuri anayesetsa kuwasamalira. (1 Tim. 5:4) Kuchita zimenezi sikunali kophweka. Iye anati: “Nthawi zambiri ndinkangoona ngati sindikwanitsa.” Poyamba, iye sanapemphe ena kuti amuthandize. Iye anati: “Sindinkafuna kuvutitsa abale. Ndinkaganiza kuti Yehova ndi amene angandithandize. Koma ndinazindikira kuti zimene ndinkachitazo zinali ngati ndikulimbana ndi vutolo pandekha.” (Miy. 18:1) Dasuri anaganiza zolembera anzake n’kuwadziwitsa mmene zinthu zinalili. Iye anati: “Sindingathe kufotokoza mmene Akhristu anzanga anandilimbikitsira. Ankabweretsa chakudya kuchipatala ndipo ankandiwerengera malemba olimbikitsa. Zimakhala zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti sitili tokha. Tili m’banja lalikulu la Yehova limene ndi lofunitsitsa kutithandiza, kulira nafe limodzi komanso kutilimbikitsa kuti tipitirize kutumikira Yehova.”

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kulola kuti akulu azitithandiza?

14 Yehova amatipatsanso mphamvu pogwiritsa ntchito akulu. Iwo ali ngati mphatso zimene Yehova amazigwiritsa ntchito potilimbikitsa komanso kutitsitsimula. (Yes. 32:​1, 2) Choncho mukakhala ndi nkhawa, muzifotokozera akulu mavuto anu. Muzivomera akamafuna kukuthandizani ndipo muziyamikira. Yehova akhoza kuwagwiritsa ntchito kuti akupatseni mphamvu.

CHIYEMBEKEZO CHANU CHIKHOZA KUKUPATSANI MPHAMVU

15. Kodi Akhristu onse ali ndi chiyembekezo chotani?

15 Malonjezo a m’Baibulo amatipatsa chiyembekezo komanso mphamvu kuti tipitirize kutumikira Yehova. (Aroma 4:​3, 18-20) Akhristufe tili ndi chiyembekezo chamtengo wapatali chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi kapena mu Ufumu wakumwamba. Chiyembekezo chathu chimatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira mayesero, tizilalikira uthenga wabwino komanso tizichita bwino utumiki uliwonse mumpingo. (1 Ates. 1:3) Chiyembekezo chimenechi ndi chomwenso chinapatsa mphamvu mtumwi Paulo.

16. N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo ankafunika kupatsidwa mphamvu?

16 Paulo ankafunika kupatsidwa mphamvu. M’kalata imene analembera Akhristu a ku Korinto, iye anadziyerekezera ndi chiwiya chadothi chomwe chimakhala chosalimba. Iye ‘ankapanikizidwa,’ ‘kuthedwa nzeru,’ ‘kuzunzidwa’ ndiponso ‘kugwetsedwa pansi.’ Nthawi zina, ngakhale moyo wake weniweniwo unkakhala pangozi. (2 Akor. 4:​8-10) Paulo analemba mawu amenewa paulendo wake wachitatu waumishonale. Ndipo pamene ankalemba mawu amenewa sankadziwa kuti akumananso ndi mavuto ena aakulu. Iye anazunzidwa ndi gulu lachiwawa, anamangidwa, ngalawa inamuswekera ndiponso anatsekeredwa m’ndende.

17. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 4:​16-18, n’chiyani chinathandiza Paulo kupirira mayesero?

17 Kuganizira za chiyembekezo chake kunkamuthandiza Paulo kuti apeze mphamvu zoti apirire. (Werengani 2 Akorinto 4:​16-18.) Iye anauza Akhristu a ku Korinto kuti ngakhale munthu wake “wakunja akutha,” sadzabwerera m’mbuyo. Paulo ankaganizira kwambiri zam’tsogolo. Iye ananena kuti chiyembekezo chake chokakhala ndi moyo wosatha kumwamba chinali chaulemerero waukulu ndipo chinkaposa mavuto alionse amene akanakumana nawo. Paulo ankaganizira chiyembekezo chimenechi ndipo chinamuthandiza kuti azikhala “watsopano tsiku ndi tsiku.”

18. Kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji Tihomir ndi banja lake kupezanso mphamvu?

18 M’bale wina wa ku Bulgaria dzina lake Tihomir, amapezanso mphamvu chifukwa cha chiyembekezo chake. Zaka zingapo zapitazo, mng’ono wake dzina lake Zdravko, anafa pangozi yapamsewu. Zimenezi zitangochitika, Tihomir ankavutika kwambiri ndi chisoni. Kuti apirire, iye ndi anthu a m’banja lake amayerekezera zimene zidzachitike anthu akamadzaukitsidwa. Iye anati: “Mwachitsanzo, timakambirana malo amene tidzakumane ndi Zdravko, chakudya chimene tidzamuphikire, anthu amene tidzawaitane pakaphwando kathu koyamba ndiponso zimene tidzamuuze zokhudza masiku otsiriza.” Tihomir ananena kuti kuganizira kwambiri za chiyembekezo chawo kumapatsa mphamvu banja lake kuti lipitirize kupirira komanso kuyembekezera nthawi imene Yehova adzaukitse mchimwene wake.

Muziganizira mmene moyo wanu udzakhalire m’dziko latsopano (Onani ndime 19) c

19. Kodi mungatani kuti muzikhulupirira kwambiri malonjezo a Yehova? (Onaninso chithunzi.)

19 Kodi mungatani kuti chiyembekezo chanu chikhale champhamvu? Mwachitsanzo, ngati mukuyembekezera moyo wosatha padziko lapansi, muziwerenga ndiponso kuganizira zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Paradaiso. (Yes. 25:8; 32:​16-18) Muziganizira mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano. Muziyerekezera muli m’dzikolo. Kodi mukuonamo ndani? Nanga mukumva zinthu zotani? Mumtima mwanu mukumva bwanji? Kuti mukhale ndi zinthu zambiri zoziganizira, muziyang’ana zithunzi zam’mabuku athu zosonyeza Paradaiso kapena kuonera mavidiyo a nyimbo monga zakuti, Dziko Latsopano Lomwe Likubwera, Dziko Latsopano Lili Pafupi kapena Ganizirani Nthawiyo. Tikamaganizira kwambiri za chiyembekezo chathu cha dziko latsopano, mavuto athu adzaoneka kuti ndi “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Chiyembekezo chimene Yehova wakupatsani chingakuthandizeni kuti mupirire mayesero.

20. Kodi tingapeze bwanji mphamvu ngakhale pamene tikuona kuti tafooka?

20 Ngakhale titaona kuti tafooka, “ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu.” (Sal. 108:13) Yehova wapereka kale zinthu zomwe zingatithandize kuti tipeze mphamvu. Choncho ngati tikufuna kuti atithandize kuti tichite bwino utumiki wathu, tipirire mayesero kapena tikhalebe osangalala, tiyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima ndiponso kufufuza malangizo ake pophunzira Baibulo patokha. Tizilolanso kuti abale ndi alongo atilimbikitse. Nthawi zonse tiziganizira za chiyembekezo chathu. Tikatero tidzalandira ‘mphamvu zazikulu chifukwa cha mphamvu zake zaulemerero, kuti tithe kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.’—Akol. 1:11.

NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako

a Nkhaniyi ithandiza anthu amene akukumana ndi mavuto aakulu kapenanso amene apatsidwa utumiki umene akuona kuti sangaukwanitse. Tionanso mmene Yehova angatithandizire komanso zimene tingachite kuti atithandize.

b Mayina ena asinthidwa.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo amene ali ndi vuto losamva akuganizira malonjezo a m’Baibulo ndipo akuonera vidiyo ya nyimbo kuti imuthandize kuganizira mmene moyo wake udzakhalire m’dziko latsopano.