Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mawu a Mulungu ndi amoyo”

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Lemba la Aheberi 4:12 limati “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Kodi mawu amene akutchulidwa palembali ndi ati?

Zikuoneka kuti apa mtumwi Paulo ankanena za uthenga wonena za cholinga cha Mulungu, womwe timaupeza m’Baibulo.

Nthawi zambiri timagwiritsa ntchito lemba la Aheberi 4:12 m’mabuku athu posonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu yosintha anthu ndipo izi ndi zoona. Komabe tingaphunzirenso zambiri tikaona bwinobwino nkhani yonse imene Paulo ankanena pamene ananena mawu a mulembali. Paulo ankalimbikitsa Akhristu achiheberi kuti azichita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Mfundo zina zokhudza cholinga cha Mulungucho zinalembedwa m’malemba oyera. Paulo anapereka chitsanzo cha Aisiraeli amene Mulungu anawatulutsa ku Iguputo. Iwo ankayembekezera kukalowa m’dziko “loyenda mkaka ndi uchi” limene Mulungu anawalonjeza. M’dzikoli akanakapeza mpumulo weniweni.—Eks. 3:8; Deut. 12:9, 10.

Chimenechi chinali cholinga cha Mulungu. Koma patapita nthawi, Aisiraeli anaumitsa mitima yawo ndipo sanasonyeze chikhulupiriro. Choncho ambiri analephera kukapeza mpumulo. (Num. 14:30; Yos. 14:6-10) Komabe Paulo ananena kuti “lonjezo lolowa mu mpumulo” wa Mulungu linali lidakalipobe. (Aheb. 3:16-19; 4:1) Pofuna kusonyeza kuti lonjezoli ndi la m’Malemba, Paulo anagwira mawu lemba la Genesis 2:2 ndi Salimo 95:11. N’zoonekeratu kuti “lonjezo” limeneli ndi mbalinso ya cholinga cha Mulungu. Mofanana ndi Akhristu achiheberi, nafenso tingawerenge za cholingachi komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chimenechi.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti “lonjezo lolowa mu mpumulo” wa Mulungu lidakalipo mpaka pano. Timadziwa kuti zimenezi zidzachitikadi ndipo tayamba kale kuchita zinthu zotithandiza kuti tilowe mu mpumulo umenewu. Sikuti tingalowe mu mpumulowo chifukwa chotsatira Chilamulo cha Mose kapena chifukwa cha ntchito zathu. Koma chifukwa chosonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro ndiponso chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. Anthu ambiri m’dzikoli ayamba kuphunzira Baibulo ndipo azindikira cholinga cha Mulungu. Ambiri mwa iwo anayamba kukhulupirira kwambiri Mulungu ndipo anasiya makhalidwe oipa n’kubatizidwa. Zonsezi zimatsimikizira mfundo yakuti “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” Uthenga wonena za cholinga cha Mulungu umene uli m’Baibulo watisintha kale ndipo upitiriza kutisintha.