Muzilola Kuti Yehova Azikutsogolerani
MLONGO WA KU POLAND ANASANKHA BWINO
“NDINABATIZIDWA ndili ndi zaka 15 ndipo patangopita miyezi 6 ndinayamba upainiya wothandiza. Patatha chaka chimodzi ndinayamba upainiya wokhazikika. Nditamaliza sukulu kusekondale, ndinapempha kuti ndikalalikire kudera limene kunalibe ofalitsa ambiri. Ndinkafuna kuchoka kutauni yakwathu komanso kusiyana ndi agogo anga omwe sanali a Mboni. Koma ndinakhumudwa woyang’anira dera atandiuza kuti gawo langa likhala tauni yakwathu yomweyo. Komabe ndinayesetsa kuti asadziwe zoti ndakhumudwa. Ndinangochokapo mozyolika n’kupita kunyumba kuti ndikaiganizire bwino nkhaniyi. Kenako ndinauza mnzanga amene ndinkalalikira naye kuti: ‘Zimene ndikuchitazi sizikusiyana ndi zimene Yona anachita. Koma paja Yona anapitabe ku Nineve. Nanenso nditumikira m’gawo limene andiuzali.’”
“Panopa ndachita upainiyawu kwa zaka 4 ndipo ndikuona kuti ndinachita bwino kumvera. Vuto ndi loti sindinkaona zinthu bwinobwino. Koma panopa ndikusangalala kwambiri moti mwezi wina ndinachititsa maphunziro okwana 24. Ndimathokozanso kwambiri Yehova chifukwa panopa ndayamba kuphunzira ndi agogo anga aja, ngakhale kuti poyamba ankanditsutsa.”
ZIMENE MLONGO WA KU FIJI ANACHITA
Mayi wina amene ankaphunzira Baibulo ku Fiji ankafunika kusankha zochita. Mwamuna wake anamuuza kuti apite naye kumwambo wokumbukira tsiku lomwe wachibale wake anabadwa, koma linalinso tsiku la msonkhano. Atakambirana, mwamunayo anamulola kuti apite kumsonkhano. Mayiyu anati apita kumwambowo akabwera kumsonkhanoko. Koma atabwerako anaganiza zoti asapite kumwambowo chifukwa mwina kukachitika zinthu zosagwirizana ndi Malemba.
Mwamuna wake atafika kumwambowo anauza achibale ake kuti mkazi wake abwera mochedwa chifukwa wapita kaye kumsonkhano. Koma achibalewo anati: “Amenewotu sabwera. A Mboni za Yehova sakondwerera masiku obadwa.” *
Mwamuna uja ataona kuti mkazi wake sanabweredi, anasangalala kwambiri. Anaona kuti amatsatiradi zimene amakhulupirira. Zimene mlongoyu anachitazi zinapangitsa kuti nthawi ina athe kulalikira mwamuna wakeyo komanso anthu ena. Zotsatira zake zinali zakuti mwamunayo anayamba kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana.
^ ndime 7 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2001.