Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akhristu Achikulire, Yehova Amayamikira Kukhulupirika Kwanu

Akhristu Achikulire, Yehova Amayamikira Kukhulupirika Kwanu

PADZIKO LONSE, akulu amayamikira kwambiri utumiki umene apatsidwa m’gulu la Yehova. Ndipo kunena zoona amatithandiza kwambiri. Koma chaposachedwapa zinthu zina zinasintha. Akulu achikulire anapemphedwa kuti asiyire achinyamata maudindo akuluakulu amene anali nawo. Tiyeni tione zimene anapemphedwa kuchita.

Malangizo ena amene anaperekedwa anali akuti oyang’anira madera komanso alangizi a m’masukulu ophunzitsa Baibulo anafunika kusiya utumiki wawo akangokwanitsa zaka 70. Akulu amene akwanitsa zaka 80 anafunika kusiyira achinyamata maudindo monga wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi kapena wogwirizanitsa ntchito za akulu. Kodi akulu achikulirewo anamva bwanji atauzidwa zimenezi? Iwo asonyeza kuti ndi okhulupirika kwambiri kwa Yehova ndi gulu lake.

M’bale wina dzina lake Ken, yemwe anatumikira ngati wogwirizanitsa Komiti ya Nthambi kwa zaka pafupifupi 49, anati: “Ndinagwirizana kwambiri ndi mfundo imeneyi. Ndipo m’mawa wa tsiku lomwe tinalandira malangizowa, ndinali nditapempha Yehova kuti pangafunike m’bale wachinyamata kuti atumikire pa udindowu.” Maganizo amene M’bale Ken anali nawo ndi amene abale ambiri achikulire ali nawo. Koma popeza ankakonda kutumikira abale, n’zosachita kufunsa kuti poyamba anakhumudwa pang’ono.

M’bale wina dzina lake Esperandio amene anali wogwirizanitsa ntchito za akulu anati: “Ndinakhumudwabe pang’ono.” Koma kenako anati: “Kunena zoona zandithandiza kuti ndikhale ndi nthawi yambiri yopuma chifukwa ndimadwaladwala.” Chosangalatsa n’chakuti m’baleyu akutumikirabe Yehova mokhulupirika komanso kuthandiza anthu mumpingo wake.

Nanga bwanji za oyang’anira madera amene utumiki wawo unasinthanso? M’bale Allan, amene wakhala woyang’anira woyendayenda kwa zaka 38, anati: “Nditauzidwa kuti utumiki wasintha ndinazizira nkhongono.” Koma anaona kuti ndi bwino kuphunzitsa achinyamata kuti apitirize ntchitoyi ndipo iye akutumikirabe Yehova mokhulupirika.

M’bale Russell amene anali woyang’anira woyendayenda komanso mlangizi wa sukulu kwa zaka 40 ananena kuti poyamba iye ndi mkazi wake anakhumudwa. Iye anati: “Tinkakonda kwambiri utumiki wathu ndipo tinkaona kuti tidakali ndi mphamvu.” Koma M’bale Russell ndi mkazi wake akugwiritsa ntchito luso limene anaphunzira kuti athandize mumpingo umene akutumikira ndipo abale ndi alongo amayamikira kwambiri.

Koma kaya inu munamva bwanji mutauzidwa za kusinthaku, nkhani ya m’buku la 2 Samueli ikhoza kukuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera.

MUNTHU WODZICHEPETSA KOMANSO WOMVETSA ZINTHU

Taganizirani nthawi imene Abisalomu anaukira Mfumu Davide, yemwe anali bambo ake. Davide anathawa ku Yerusalemu kupita kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano ku Mahanaimu. Atafika, iye ndi anthu amene anali nawo ankasowa zinthu zofunika pa moyo. Kodi mukukumbukira zimene zinachitika?

Anthu atatu a m’deralo anabweretsa zinthu zambiri monga makama, chakudya komanso ziwiya. Mmodzi mwa anthuwo anali Barizilai. (2 Sam. 17:27-29) Abisalomu atalephera kulanda ufumu, Davide anabwerera ku Yerusalemu ndipo Barizilai anamuperekeza mpaka kumtsinje wa Yorodano. Davide anamupempha kuti apite naye ku Yerusalemu. Ndipo anamuuza kuti azikamupatsa chakudya nthawi zonse ngakhale kuti Barizilai anali “munthu wolemera kwambiri” ndipo nkhani ya chakudya sinali vuto. (2 Sam. 19:31-33) Davide ayenera kuti ankayamikira makhalidwe abwino a Barizilai komanso ankaona kuti angapereke malangizo abwino. Apatu Barizilai anapatsidwa mwayi waukulu wokakhala komanso kugwira ntchito m’nyumba yachifumu.

Koma Barizilai anali wodzichepetsa komanso womvetsa zinthu ndipo anauza Davide kuti anali ndi zaka 80. Kenako anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndingasiyanitse chabwino ndi choipa?” (2 Sam. 19:35) Barizilai ayenera kuti anali wanzeru chifukwa chokhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Ndipo akanatha kupereka malangizo abwino ngati mmene anthu achikulire anadzachitira ndi Mfumu Rehobowamu. (1 Maf. 12:6, 7; Sal. 92:12-14; Miy. 16:31) Choncho ponena kuti sangasiyanitse chabwino ndi choipa, Barizilai ayenera kuti ankanena za mavuto amene anali nawo chifukwa cha uchikulire. Paja iye ananena kuti anali ndi vuto losamva bwino nyimbo komanso kukoma kwa chakudya. (Mlal. 12:4, 5) N’chifukwa chake anapempha Davide kuti popita ku Yerusalemu atenge Chimamu, yemwe mwina anali mwana wa Barizilaiyo.​—2 Sam. 19:36-40.

ANKAGANIZIRA ZA M’TSOGOLO

Kusintha kwa maudindo a achikulire masiku ano kumagwirizana ndi maganizo amene Barizilai anali nawowa. Koma posankha zosintha mautumikiwa, anaganizira za anthu ambiri osati za munthu mmodzi ngati mmene zinalili ndi Barizilai. Anaona zimene zingathandize akulu achikulire padziko lonse.

Achikulire odzichepetsawa anazindikira kuti zinthu zikhoza kudzayenda bwino m’tsogolo ngati atapereka maudindo awo kwa abale achinyamata. Ndipo nthawi zambiri akulu achikulirewo ndi amene anaphunzitsa achinyamatawo ngati mmene Barizilai akanaphunzitsira mwana wakeyo komanso mmene Paulo anaphunzitsira Timoteyo. (1 Akor. 4:17; Afil. 2:20-22) Panopa, akulu achinyamatawo afika pochita zinthu monga “mphatso za amuna” moti amathandiza ‘kumanga thupi la Khristu.’​—Aef. 4:8-12; yerekezerani ndi Numeri 11:16, 17, 29.

MULI NDI MWAYI WOTHANDIZA M’NJIRA ZOSIYANASIYANA

Anthu amene asiyira ena maudindo awo, panopa ali ndi mwayi wochita zinthu zosiyanasiyana potumikira Yehova.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Marco, yemwe anali woyang’anira woyendayenda kwa zaka 19. Iye anati: “Panopa ndimatha kuthandiza amuna amene akazi awo ndi alongo mumpingo wathu.”

M’bale Geraldo amene anali woyang’anira woyendayenda kwa zaka 28 anati: “Panopa tili ndi cholinga chothandiza ofalitsa amene afooka komanso kuti tizichititsa maphunziro a Baibulo ambiri.” Iye ndi mkazi wake athandiza anthu ambiri kuti ayambirenso kusonkhana ndipo akuchititsa maphunziro okwana 15.

M’bale Allan amene tamutchula kale uja anati: “Panopa timakhala ndi nthawi yambiri yolalikira. Timakonda kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri, m’mashopu ndiponso m’maofesi. Timakondanso kulalikira kwa anthu amene tayandikana nawo nyumba moti awiri mwa anthu amenewa anafika ku Nyumba ya Ufumu.”

Ngati ndinu m’bale wokhulupirika ndipo utumiki wanu wasintha, pali zinthu zina zambiri zimene mungachite pothandiza ena m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, popeza muli ndi luso lambiri, mungathandize achinyamata mumpingo wanu kuti nawonso akhale aluso. M’bale Russell amene tamutchula kale uja anati: “Yehova akuphunzitsa achinyamata n’kumawagwiritsa ntchito ndipo iwo akuchita bwino kwambiri. Achinyamatawa akuthandiza kwambiri chifukwa choti akugwiritsa ntchito mphamvu zawo pophunzitsa komanso kuweta mpingo.”​—Onani bokosi lakuti “ Muzithandiza Achinyamata Kuti Azichita Zambiri Mumpingo.”

YEHOVA AMAYAMIKIRA KWAMBIRI KUKHULUPIRIKA KWATHU

Ngati panopa utumiki wanu wasintha muyenera kukhala ndi maganizo oyenera. Mwathandiza kale anthu ambirimbiri pa moyo wanu ndipo mukhoza kupitiriza kuchita zimenezi. Anthu ambiri amakukondani ndipo sangasiye.

Chofunika kwambiri n’chakuti mwakhala mukusangalatsa Yehova. Iye sangaiwale “ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.” (Aheb. 6:10) Lemba limeneli limasonyeza kuti Mulungu sangaiwale zimene munachita m’mbuyomu komanso zimene mukuchita panopa. Yehova amaona kuti ndinu wofunika kwambiri moti sangaiwale zimene mwachita kale poyesetsa kumusangalatsa komanso zimene mukupitiriza kuchita.

Ngati inuyo simuli m’gulu la anthu amene anapemphedwa kuti asiye udindo winawake, nkhaniyi ikukukhudzanibe. N’chifukwa chiyani tikutero?

Ngati mumagwira ntchito limodzi ndi m’bale wachikulire amene anasiya udindo wake, akhoza kukuthandizani kwambiri ndi nzeru zimene ali nazo chifukwa chotumikira Yehova kwa zaka zambiri. Choncho mungachite bwino kumupempha malangizo komanso kufunsa maganizo ake pa zinthu zosiyanasiyana. Mungachitenso bwino kuona mmene amachitira zinthu pa utumiki wake watsopano.

Kodi ndinu wachikulire amene utumiki wanu wasintha kapena mumangodziwa anthu oterewa? Ngati zili choncho, muzikumbukira kuti Yehova amayamikira kwambiri kukhulupirika kwa anthu amene amutumikira kwa zaka zambiri ndipo akupitiriza kuchita zimenezi.