Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthawi Ili Bwanji?

Nthawi Ili Bwanji?

KODI mumatani mukafuna kudziwa nthawi? Mwina mumangoyang’ana wotchi yanu. Nanga ngati munthu wina wakufunsani nthawi, kodi mumaitchula bwanji? Pali njira zosiyanasiyana zotchulira nthawi.

Mwachitsanzo, pakapita ola limodzi ndi maminitsi 30 kuchokera pa 12 koloko masana, ena amati nthawi ili 1:30. Koma m’madera ena anthu amati nthawi ili 13:30. Amatchula chonchi chifukwa chakuti amawerengera maola 24 osati 12. Koma m’mayiko ena, nthawi yomweyi angaitchule kuti “hafu 2,” kutanthauza kuti kwatsala maminitsi 30 kuti ikwane 2 koloko.

Popeza mumawerenga Baibulo, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi anthu otchulidwa m’Baibulo ankatchula bwanji nthawi?’ Panali njira zingapo zimene ankatchulira nthawi. M’malemba Achiheberi, Baibulo limanena za m’mawa, masana ndi madzulo. (Gen. 8:11; 19:27; 43:16; Deut. 28:29; 1 Maf. 18:26) Koma nthawi zina Baibulo limatchula nthawi yeniyeni.

Kalelo anthu ankaika alonda m’malo osiyanasiyana, makamaka usiku. Kudakali zaka zambiri Yesu asanabadwe, Aisiraeli anagawa usiku m’zigawo zitatu zomwe ankazitchula kuti nthawi za ulonda. (Sal. 63:6) Mwachitsanzo, lemba la Oweruza 7:19 limanena za “ulonda wapakati pa usiku.” Pofika nthawi ya Yesu, Ayuda anali atatengera zimene Agiriki ndi Aroma ankachita. Iwo ankagawa usiku mu nthawi za ulonda zokwana 4.

Nthawi zimenezi zimatchulidwa kwambiri m’mabuku a Uthenga Wabwino. Mwachitsanzo, Baibulo limati Yesu anayenda panyanja kupita kumene kunali boti la ophunzira ake pa nthawi ya “ulonda wachinayi m’bandakucha.” (Mat. 14:25) Nayenso Yesu anatchula nthawi za ulonda ponena kuti: “Iwo ndi odala ndithu ngati atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri kapenanso wachitatu!”​—Luka 12:38.

Yesu anatchula nthawi 4 zonse za ulonda pamene anauza ophunzira ake kuti: “Khalani maso, pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa.” (Maliko 13:35) Ulonda woyamba, womwe ndi wamadzulo, unkayamba dzuwa litangolowa kufika m’ma 9 koloko usiku. Wachiwiri unkayamba m’ma 9 koloko mpaka pakati pa usiku. Wachitatu, womwe umatchulidwanso kuti “atambala akulira,” unkayamba pakati pa usiku kufika m’ma 3 koloko m’bandakucha. N’kutheka kuti nthawi imeneyi ndi imene tambala analira pa tsiku limene Yesu anagwidwa. (Maliko 14:72) Ulonda wachinayi, womwe ndi wam’mawa, unkayamba m’ma 3 koloko m’bandakucha mpaka pamene dzuwa latuluka.

Choncho ngakhale kuti kalelo kunalibe mawotchi, anthu anali ndi njira zawo zotchulira nthawi ya masana kapena usiku.