Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kusonyeza Chikondi Chifukwa Chimalimbikitsa

Pitirizani Kusonyeza Chikondi Chifukwa Chimalimbikitsa

“Chikondi chimamangirira.”​—1 AKOR. 8:1.

NYIMBO: 109, 121

1. Kodi Yesu anakambirana kwambiri za chiyani ndi ophunzira ake usiku woti aphedwa mawa lake?

USIKU woti aphedwa mawa lake, Yesu anatchula za chikondi maulendo 30. Iye anatsindika mfundo yoti ophunzira ake ayenera kukondana. (Yoh. 15:12, 17) Chikondi chawo chinayenera kukhala chapamwamba kwambiri mpaka kufika pokhala chizindikiro choti ndi Akhristu enieni. (Yoh. 13:34, 35) Chikondi choterechi si chimene munthu amachisonyeza chifukwa chongotengeka basi. Apa Yesu ankanena za chikondi chololera kuvutikira anthu ena. Paja ananena kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.”​—Yoh. 15:13, 14.

2. (a) Kodi atumiki a Mulungu masiku ano amadziwika ndi chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

2 Chikondi chimene atumiki a Yehova ali nacho masiku ano komanso mgwirizano wawo zimatsimikizira kuti ndi anthu a Mulungu. (1 Yoh. 3:10, 11) Chosangalatsa kwambiri n’chakuti atumiki a Yehova amasonyezana chikondi ngakhale kuti amasiyana mitundu, zilankhulo komanso kochokera. Koma mwina tingadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani chikondi n’chofunika kwambiri masiku ano? Nanga Yehova ndi Yesu amatilimbikitsa bwanji? Kodi tingasonyeze bwanji chikondi ngati chimene Khristu ankasonyeza?’​—1 Akor. 8:1.

CHIKONDI N’CHOFUNIKA KWAMBIRI MASIKU ANO

3. Kodi mavuto a masiku ano amakhudza bwanji anthu?

3 Popeza moyo wa masiku ano ndi ‘wodzaza ndi mavuto ndi zopweteka,’ anthu ambiri amakhala ndi nkhawa. (Sal. 90:10; 2 Tim. 3:1-5) Ndipo ambiri amaganiza kuti kuli bwino kungofa. Kafukufuku amasonyeza kuti anthu oposa 800,000 amadzipha chaka chilichonse. Choncho tingati munthu mmodzi amadzipha pa masekondi 40 alionse. N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale Akhristu ena amadzipha chifukwa chopanikizika ndi mavuto.

4. Kodi ndi anthu ati otchulidwa m’Baibulo amene anakhalapo ndi maganizo ofuna kufa?

4 Atumiki ena okhulupirika otchulidwa m’Baibulo anapanikizikapo ndi mavuto moti ankafuna atangofa. Mwachitsanzo, Yobu atavutika kwambiri ananena kuti: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16; 14:13) Nayenso Yona anakhumudwa kwambiri chifukwa cha zimene zinachitika pa utumiki wake moti ananena kuti: “Tsopano inu Yehova, chotsani moyo wanga, pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.” (Yona 4:3) Pa nthawi ina Eliya anadandaula kwambiri ndipo anapemphanso kuti afe. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova.” (1 Maf. 19:4) Koma Yehova ankaona kuti anthuwo anali amtengo wapatali ndipo ankafuna kuti akhalebe ndi moyo. Iye sanawadzudzule chifukwa choti ankafuna kufa. M’malomwake anawathandiza kusintha maganizo awo ndipo anawalimbikitsa mwachikondi kuti apitirize kumutumikira mokhulupirika.

5. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kwambiri chikondi kwa abale ndi alongo athu masiku ano?

5 Ngakhale abale ndi alongo amene sakufuna kufa amafunikirabe kulimbikitsidwa mwachikondi chifukwa cha mavuto amene amakumana nawo. Zili choncho chifukwa ena amazunzidwa komanso kunyozedwa. Pomwe ena amavutika kuntchito chifukwa choti anzawo amawatsutsa kapena kuwajeda. Apo ayi, amakhala otopa chifukwa chogwira ntchito kwa maola ambiri kapena mopanikizika. Komanso ena amakumana ndi mavuto a m’banja monga kutsutsidwa ndi mwamuna kapena mkazi wawo amene si Mboni. Mavuto ngati amenewa amachititsa anthu ambiri mumpingo kuti azikhala otopa komanso ankhawa. Kodi ndi ndani angawathandize kuti asataye mtima?

CHIKONDI CHA YEHOVA CHIMATILIMBIKITSA

6. Kodi Yehova amalimbikitsa bwanji atumiki ake?

6 Yehova amalimbikitsa atumiki ake powatsimikizira kuti iye sadzasiya kuwakonda. Aisiraeli okhulupirika ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri pamene anamva Yehova akuwauza kuti: ‘Ndinu amtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekezani ndipo ndimakukondani. Musachite mantha chifukwa ine ndili nanu.’ (Yes. 43:4, 5) Nafenso tisamakayikire kuti Yehova amatikonda kwambiri chifukwa timamutumikira. * Mawu a Mulungu amalonjeza munthu aliyense amene amalambira Yehova kuti: “Adzakupulumutsa chifukwa ndi wamphamvu. Iye adzakondwera nawe.”​—Zef. 3:16, 17.

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi cha Yehova chimafanana ndi cha mayi? (Onani chithunzi choyambirira.)

7 Yehova analonjeza atumiki ake kuti aziwathandiza komanso kuwalimbikitsa pa mayesero alionse amene angakumane nawo. Iye anati: ‘Inu mudzayamwadi. Mudzanyamulidwa m’manja ndipo mudzasisitidwa mwachikondi mutaikidwa pamwendo. Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.’ (Yes. 66:12, 13) Zimasangalatsa kuona mmene mayi amatonthozera mwana wake pomunyamula kapena kumusisita. N’chifukwa chake Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzochi posonyeza mmene amakondera kwambiri anthu amene amamulambira. Musamakayikire kuti Yehova amakuonani kuti ndinu ofunika kwambiri ndipo amakukondani.​—Yer. 31:3.

8, 9. Kodi chikondi cha Yesu chingatilimbikitse bwanji?

8 Akhristu enieni ali ndi chifukwa chinanso chowachititsa kudziwa kuti Yehova amawakonda. Paja Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Nayenso Yesu anasonyeza kuti amatikonda pololera kufa chifukwa cha ife. Ndipotu timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira za chikondi chimene Yesu anatisonyezachi. Mawu a Mulungu amatilonjeza kuti ngakhale ‘chisautso kapena zowawa’ sizingatilekanitse ndi “chikondi cha Khristu.”​—Aroma 8:35, 38, 39.

9 Chikondi cha Khristu chimatithandiza kupirira tikamakumana ndi mavuto amene amatitopetsa, kutisokoneza maganizo kapena kutifooketsa mwauzimu. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Chikondichi chingatilimbikitse kuti tisamataye mtima ngakhale pamene takumana ndi mavuto aakulu monga ngozi zadzidzidzi, kuzunzidwa, nkhawa kapena kukhumudwa.

TIZISONYEZA CHIKONDI KWA AKHRISTU ANZATHU

Kuphunzira za Yesu kungatilimbikitse (Onani ndime 10, 11)

10, 11. Kodi ndani ali ndi udindo wolimbikitsa anthu amene akuvutika maganizo? Fotokozani.

10 Yehova amatisonyezanso chikondi kudzera mumpingo wachikhristu. Tingasonyeze kuti timayamikira chikondi chake tikamakonda abale ndi alongo athu komanso kuwalimbikitsa. (1 Yoh. 4:19-21) Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukuchitira.” (1 Ates. 5:11) Izi zikusonyeza kuti Mkhristu aliyense mumpingo, osati akulu okha, angatsanzire Yehova ndi Yesu potonthoza komanso kulimbikitsa abale ndi alongo.​—Werengani Aroma 15:1, 2.

11 Koma abale ndi alongo amene akudwala matenda amaganizo angafunike thandizo la kuchipatala. (Luka 5:31) Akulu komanso anthu ena mumpingo ayenera kukumbukira kuti iwo si madokotala a matenda ngati amenewa. Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zofunika zimene aliyense mumpingo akhoza kuchita. Tonsefe tiyenera ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni, kuthandiza ofooka komanso kukhala oleza mtima kwa onse.’ (1 Ates. 5:14) Mkhristu aliyense ayenera kusonyeza chikondi, kukhala womvetsa, kukhala woleza mtima komanso kulankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa. Kodi inuyo mumayesetsa kulimbikitsa anthu? Tikadziwa njira yoyenera yothandizira anthu oterewa m’pamene tingawathandize bwino.

12. Perekani chitsanzo cha munthu amene analimbikitsidwa chifukwa cha chikondi cha abale ndi alongo.

12 Kodi tingatani kuti tilimbikitse mwachikondi anthu amene akuvutika maganizo? Mlongo wina wa ku Europe anati: “Nthawi zina ndimafuna nditadzipha. Koma ndili ndi anzanga ambiri amene ndimawadalira. Abale ndi alongo mumpingo wathu ndi amene amandithandiza kuti ndisachite zimenezi. Nthawi zonse amandisonyeza chikondi komanso kundilimbikitsa. Ngakhale kuti ndi anthu ochepa okha amene amadziwa za matenda anga, mpingo wonse umandilimbikitsa. Banja lina lili ngati makolo anga auzimu. Amandisamalira kwambiri ndipo amakhala okonzeka kundithandiza nthawi iliyonse, kaya masana kapena usiku.” N’zoona kuti si tonse amene tingathandize anthu m’njira imeneyi. Koma tikamalimbikitsa anzathu amene akuvutika maganizo tikhoza kuwathandiza kwambiri. *

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZILIMBIKITSA ENA MWACHIKONDI

13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilimbikitse anthu ena?

13 Muzimvetsera bwino. (Yak. 1:19) Munthu wachikondi amamvetsera kuti adziwe mmene mnzake akumvera mumtima. Ndi bwino kufunsa mafunso mwanzeru kuti mudziwe zimene zili mumtima mwa munthu amene akuvutika. Mukatero mudzatha kumumvetsa munthuyo komanso kumulimbikitsa. Nkhope yanu iyenera kusonyeza kuti mukumudera nkhawa ndipo mukufuna kumuthandiza. Ngati akufuna kufotokoza mwatsatanetsatane zinthu zina, tingachite bwino kumumvetsera moleza mtima popanda kumudula mawu. Mukamamumvetsera moleza mtima mudzazindikira zimene zikumudetsa nkhawa. Mukatero, munthuyo amayamba kukukhulupirirani ndipo zingakhale zosavuta kuti akumvetsereni mukamamuuza mfundo zolimbikitsa. Mukamasonyeza kuti mumamuganizira komanso kumukonda mudzatha kumulimbikitsa kwambiri.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kupezera ena zifukwa?

14 Tizipewa kupezera anthu zifukwa. Tikamapezera zifukwa anthu amene akuvutika maganizo, mavuto awo akhoza kukula kwambiri ndipo zimene tinganene powalimbikitsa sizingawathandize. Paja Baibulo limanena kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.” (Miy. 12:18) N’zoona kuti anthufe sitilankhula mwadala “mawu olasa ngati lupanga” kwa anthu amene akuvutika maganizo. Koma ngakhale zitachitika mwangozi, kulankhulidwa ndi “mawu olasa ngati lupanga” n’kopweteka kwambiri. Kuti tilimbikitse anzathu mwachikondi, tiyenera kukhala omvetsa n’kumaganizira mmene tikanamvera zikanakhala kuti vutolo lagwera ifeyo.​—Mat. 7:12.

15. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingagwiritse ntchito polimbikitsa anthu?

15 Tizilimbikitsa anthu ndi Mawu a Mulungu. (Werengani Aroma 15:4, 5.) M’Baibulo muli mfundo zambirimbiri zimene tingazigwiritse ntchito polimbikitsa munthu. Paja mawu ake ndi ochokera kwa “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza.” Tilinso ndi zinthu zambiri zotithandiza pophunzira Baibulo. Tingathe kugwiritsa ntchito zinthu monga Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Mabuku ngati amenewa angatithandize kupeza malemba amene ali ndi mfundo zothandiza kuti tipirire vuto lililonse. Tikamawagwiritsa ntchito bwino tikhoza kukhala okonzeka kulimbikitsa moyenera anthu amene akuvutika.

16. Kodi timafunika kusonyeza makhalidwe ati polimbikitsa anthu amene akuvutika maganizo?

16 Tiyenera kukhala achifundo komanso odekha. Munthu wachikondi amasonyeza makhalidwe amenewa pamene akulimbikitsa mnzake. Paja nayenso Yehova ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse” ndipo amasonyeza “chifundo chachikulu” kwa atumiki ake. (Werengani 2 Akorinto 1:3-6; Luka 1:78; Aroma 15:13) Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Iye analemba kuti: “Tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira ana ake. Choncho popeza timakukondani kwambiri, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeniyeniyo, chifukwa tinakukondani kwambiri.” (1 Ates. 2:7, 8) Tikamakhala achifundo komanso odekha, Yehova akhoza kutigwiritsa ntchito poyankha mapemphero a anthu amene ali ndi nkhawa.

17. Kodi tiyenera kupewa maganizo ati kuti tizilimbikitsa abale ndi alongo athu?

17 Tisamaganize kuti Akhristu anzathu sangalakwitse chilichonse. Tiyenera kuona abale ndi alongo athu moyenera. Munthu akamaganiza kuti Akhristu anzake sangalakwitse kalikonse ndiye kuti akuyembekezera zinthu zosatheka ndipo akhoza kukhumudwa. (Mlal. 7:21, 22) Tizikumbukira kuti Yehova sayembekezera kuti atumiki ake achite zimene sangakwanitse. Tikamamutsanzira, tidzakhala ololera ngati ena alakwitsa zinazake. (Aef. 4:2, 32) M’malo mowachititsa kuganiza kuti akulephera kuchita zinthu zina, ndi bwino kuwayamikira pa zomwe akuchita. Tikamatero tidzawalimbikitsa kwambiri. Tikamayamikira abale ndi alongo athu timawalimbikitsa ndiponso kuwathandiza kuti azisangalala ndi utumiki wawo.​—Agal. 6:4.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikitsa anzathu mwachikondi?

18 Mtumiki wa Yehova aliyense ndi wofunika kwambiri kwa iye komanso kwa Yesu amene anapereka moyo wake monga dipo. (Agal. 2:20) Tonse timakonda kwambiri abale ndi alongo athu ndipo timafuna kuwathandiza mwachikondi komanso mwachifundo. Koma kuti zimenezi zitheke tiyenera kuyesetsa kutsatira “zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.” (Aroma 14:19) Tonsefe tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene tizidzakhala popanda chokhumudwitsa m’Paradaiso. Sipadzakhalanso zinthu zokhumudwitsa monga matenda, nkhondo, kuzunzidwa, mavuto a m’banja komanso imfa imene tinatengera kwa Adamu. Pamene zaka 1,000 zizidzatha, anthu onse adzakhala ali angwiro. Anthu amene adzapambane mayesero omaliza ndi amene Yehova Mulungu adzawalola kukhala ana ake padziko lapansi ndipo adzapeza “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Tiyeni tonse tiziyesetsa kulimbikitsana mwachikondi komanso kuthandizana kuti tidzalandire madalitso amenewa.

^ ndime 12 Kuti mupeze mfundo zothandiza munthu amene akufuna kudzipha onani nkhani za mu Galamukani! zakuti: “Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?” (April 2014); “Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?” (January 2012); “N’chifukwa Chiyani Anthu Amatopa Nawo Moyo?” komanso yakuti “Mutha Kupeza Thandizo” (November 8, 2001).