Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ngati Zimenezi Mukuzidziwa, Ndinu Odala Mukamazichita”

“Ngati Zimenezi Mukuzidziwa, Ndinu Odala Mukamazichita”

“Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”​—YOH. 4:34.

NYIMBO: 80, 35

1. Kodi khalidwe lodzikonda la anthu a m’dzikoli lingatikhudze bwanji?

N’CHIFUKWA chiyani zimativuta kutsatira zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu? Chifukwa chimodzi n’chakuti pamafunika kudzichepetsa kuti tizichita zoyenera, koma kukhala odzichepetsa n’kovuta kwambiri m’masiku otsiriza ano. Zili choncho chifukwa masiku ano, anthu ambiri ndi “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza” komanso “osadziletsa.” (2 Tim. 3:1-3) Atumiki a Mulungufe sitisangalala anthu akamachita zinthu modzikonda, koma nthawi zina tikhoza kusirira zimene anthu oterewa amapeza chifukwa cha kudzikondako. (Sal. 37:1; 73:3) Mwina tikhoza kufika podzifunsa kuti: ‘Kodi kuchita zinthu moganizira anthu ena kuli ndi ubwino uliwonse? Kodi anthu sangasiye kundilemekeza ndikamachita zinthu “ngati wamng’ono”?’ (Luka 9:48) Ngati tingatengere khalidwe lodzikonda, tingasiye kugwirizana ndi Akhristu anzathu komanso anthu ena sangadziwe kuti ndife Akhristu. Koma tikamaphunzira za anthu otchulidwa m’Baibulo n’kumatsatira chitsanzo chawo chabwino, timadalitsidwa.

2. Kodi chitsanzo chabwino cha atumiki a Mulungu okhulupirika chingatithandize bwanji?

2 Kuti titsanzire anthu otchulidwa m’Baibulo, tiyenera kufufuza zimene zinawathandiza kuti akhale okhulupirika. Kodi ankatani kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, kuti azichita zinthu zomusangalatsa komanso kuti azipeza mphamvu yochitira zimene Mulungu amafuna? Kufufuza mwanjira imeneyi kungathandize kuti chikhulupiriro chathu chilimbe.

KUDYA CHAKUDYA CHAUZIMU

3, 4. (a) Kodi timapeza kuti malangizo ochokera kwa Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudya chakudya chauzimu kumatanthauza zambiri osati kungophunzira zinthu?

3 Timaphunzira zambiri komanso kupeza malangizo abwino m’Baibulo, m’mabuku athu, pawebusaiti yathu, pa JW Broadcasting, pamisonkhano yampingo komanso pamisonkhano ikuluikulu. Koma malinga ndi zimene Yesu ananena pa Yohane 4:34, kudya chakudya chauzimu kumatanthauza zambiri osati kungophunzira zinthu. Paja Yesu ananena kuti: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma ndi kutsiriza ntchito yake.”

4 Yesu ankaona kuti kutsatira malangizo a Mulungu kunali ngati kudya chakudya chauzimu. Kodi n’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Munthu akadya chakudya chabwino amapeza mphamvu komanso amasangalala. N’chimodzimodzinso ndi chakudya chauzimu. Tikutero chifukwa tikamachita zimene Mulungu amafuna timapeza mphamvu komanso timalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mwina inunso zakuchitikiranipo kuti tsiku lina munapita kumsonkhano wokonzekera utumiki mutatopa koma poweruka munali osangalala komanso amphamvu.

5. Kodi munthu amadalitsidwa bwanji akamachita zinthu mwanzeru?

5 Munthu akamatsatira malangizo ochokera kwa Mulungu amasonyeza kuti ndi wanzeru. (Yak. 3:13) Ndipo munthu akamachita zinthu mwanzeru amapeza madalitso ambiri. Pofotokoza za nzeru, Baibulo limanena kuti: “Zonse zimene umakonda sizingafanane nazo. . . . Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwiritsitsa adzatchedwa odala.” (Miy. 3:13-18) Nayenso Yesu ananena kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.” (Yoh. 13:17) Apa ankatanthauza kuti ophunzira ake akhoza kukhalabe osangalala akamachita zimene Yesu anawauza. Iwo ankayenera kutsatira chitsanzo chake komanso zimene ankaphunzitsa kwa moyo wawo wonse.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuchita zimene timaphunzira?

6 Masiku anonso tiyenera kupitiriza kugwiritsa ntchito zimene timaphunzira. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiganizire za munthu amene amakonza magalimoto. Iye akhoza kudziwa ntchito yake komanso kukhala ndi zipangizo. Koma zonsezi zikhoza kukhala zosathandiza ngati atapanda kuzigwiritsa ntchito. Ngati m’mbuyomo anagwira ntchitoyi n’kuidziwa bwino, amafunika kupitiriza kugwiritsa ntchito zinthu zimene akudziwazo kuti luso lake lisathe komanso lizimupindulira. N’kutheka kuti nafenso zinthu zina zikutiyendera bwino chifukwa chotsatira mfundo zimene tawerenga m’Baibulo. Koma kuti tikhalebe osangalala tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumapitiriza kutsatira malangizo a Yehova tsiku lililonse.

7. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze nzeru tikamaphunzira zitsanzo zabwino za m’Baibulo?

7 Tiyeni tsopano tikambirane zinthu zina zimene zingatilepheretse kukhala odzichepetsa komanso zinthu zimene zinathandiza atumiki okhulupirika akale kuti akhalabe odzichepetsa. Tikamakambirana mfundozi tiyenera kuganizira mmene tingagwiritsire ntchito mfundo iliyonse n’kuyamba kuigwiritsa ntchito mwamsanga.

TISAMADZIONE KUTI NDIFE APAMWAMBA

8, 9. Kodi nkhani ya pa Machitidwe 14:8-15 imasonyeza bwanji kuti Paulo anali wodzichepetsa? (Onani chithunzi choyambirira.)

8 Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Kodi mumaona bwanji anthu osiyanasiyana amene panopa sanaphunzire choonadi? Mtumwi Paulo ankalalikira Ayuda omwe ankadziwa zinthu zina zokhudza Mulungu. Koma ankathandizanso anthu amitundu ina amene ankalambira milungu yonyenga. Zimene anthu olambira milungu yonyengawo anachita zikanatha kumulepheretsa kukhala wodzichepetsa.

9 Mwachitsanzo, pa ulendo wake woyamba waumishonale, anthu a ku Lukaoniya anaganiza kuti Paulo ndi Baranaba anali Zeu ndi Heme, yomwe inali milungu yawo yonyenga. Kodi Paulo ndi Baranaba anasangalala kulemekezedwa chonchi? Kodi anaganiza kuti zimenezi zinali zosangalatsa chifukwa chakuti anali atazunzidwa m’mizinda imene ankachokera? Kapena kodi ankaganiza kuti kutchuka kwawo kungathandize kuti anthu ambiri amvetsere uthenga wabwino? Ayi, sankaganiza choncho. M’malomwake nthawi yomweyo anang’amba malaya awo n’kukalowa m’gulu la anthuwo ndipo anati: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.”​—Mac. 14:8-15.

10. N’chifukwa chiyani Paulo ndi Baranaba ananena kuti anali ofanana ndi anthu a ku Lukaoniya?

10 Ponena kuti anali ndi zofooka ngati anthuwo, sankatanthauza kuti ankalambiranso milungu yonyenga. Paja Paulo ndi Baranaba anali amishonale amene anapatsidwa utumiki wapadera. (Mac. 13:2) Iwo anadzozedwanso ndi mzimu woyera ndipo anali ndi chiyembekezo chapadera. Koma Paulo ndi Baranaba ankadziwa kuti anthu a ku Lukaoniya akhoza kukhalanso ndi zonsezi akayamba kutsatira uthenga wabwino.

11. Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Paulo tikamalalikira?

11 Kodi ifeyo tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Paulo? Choyamba, sitiyenera kufuna kapena kulola kuti anthu azitilemekeza mopitirira malire chifukwa cha zimene timachita mothandizidwa ndi Yehova. Aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimaona bwanji anthu amene ndimawalalikira? Kodi mwina ndayamba kutengera mtima watsankho n’kumanyoza anthu amtundu wina?’ Chosangalatsa n’chakuti a Mboni za Yehova padziko lonse akhala akuyesetsa kulalikira m’gawo lawo lonse kuti mwina angapeze anthu amene angamvetsere uthenga wabwino. Nthawi zina amaphunzira zilankhulo komanso zikhalidwe za anthu amene ena amawanyoza. Abale ndi alongo amene amachita zimenezi sayenera kudziona kuti ndi apamwamba kuposa anthuwo. Koma ayenera kuyesetsa kuwamvetsa anthuwo n’cholinga choti aziwafika pamtima.

TIZITCHULA ANTHU ENA M’MAPEMPHERO ATHU

12. Kodi Epafura anasonyeza bwanji kuti sanali wodzikonda?

12 Tingasonyezenso kuti ndife odzichepetsa tikamatsatira malangizo ochokera kwa Mulungu akuti tizipempherera anthu amene ali ndi “chikhulupiriro chofanana ndi chathu.” (2 Pet. 1:1) Izi n’zimene Epafura ankachita. Munthu ameneyu amangotchulidwa katatu kokha m’Baibulo ndipo maulendo onsewa amapezeka m’makalata a Paulo. Paulo atamangidwa ku Roma, analembera Akhristu a ku Kolose kuti Epafura ‘ankawapempherera mwakhama nthawi zonse.’ (Akol. 4:12) Epafura ankawadziwa bwino abalewo ndipo ankawakonda kwambiri. Ngakhale kuti anamangidwa limodzi ndi Paulo, iye ankaganizira za anthu ena ndipo ankawathandiza. (Filim. 23) Apatu anasonyeza kuti sanali wodzikonda. Kupempherera Akhristu anzathu n’kothandiza kwambiri makamaka tikamatchula mayina awo m’mapemphero athu.​—2 Akor. 1:11; Yak. 5:16.

13. Kodi mungatsanzire bwanji Epafura mukamapemphera?

13 Kodi ndi anthu ati amene mungawatchule m’mapemphero anu? Mofanana ndi Epafura, abale ndi alongo amapempherera anthu ena mumpingo wawo. Mwachitsanzo, amapempherera mabanja amene ali ndi maudindo akuluakulu, amene ayenera kusankha zochita pa nkhani zovuta kapena amene akukumana ndi mayesero. Ambiri amapempherera anthu amene mayina awo amapezeka pa jw.org munkhani zakuti “Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira.” (Pitani pamene alemba kuti MALO A NKHANI > ZOKHUDZANA NDI MALAMULO.) Ndi bwinonso kuganizira anthu amene aferedwa, amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi kapena nkhondo komanso amene akumana ndi mavuto azachuma. Kunena zoona pali abale ndi alongo ambirimbiri amene tifunika kuwapempherera ndipo kuchita zimenezi kungawathandize kwambiri. Tikamapempherera anthu ngati amenewa timasonyeza kuti timaganizira zofuna za ena osati zathu zokha. (Afil. 2:4) Yehova amamva mapemphero ngati amenewa.

TIZIKHALA ‘OFULUMIRA KUMVA’

14. Kodi Yehova wapereka chitsanzo chotani pa nkhani yomvetsera anthu akamalankhula?

14 Chinthu china chimene chimasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndi zimene timachita anthu ena akamatilankhula. Paja lemba la Yakobo 1:19 limanena kuti tiyenera ‘kukhala ofulumira kumva.’ Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. (Gen. 18:32; Yos. 10:14) Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya pa Ekisodo 32:11-14. (Werengani.) Ngakhale kuti Yehova akanatha kuchita zinthu popanda kumva maganizo a Mose, anamupatsa mpata kuti afotokoze zimene ankaganiza. Anthu ambiri sangataye nthawi kumvetsera maganizo a munthu yemwe nthawi zina maganizo ake sakhala olondola ndipo sangatsatire zimene wanena. Koma Yehova amamvetsera moleza mtima anthu amene amapemphera kwa iye mwachikhulupiriro.

15. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yolemekeza anthu?

15 Yehova anadzichepetsa kuti amvetsere anthu monga Abulahamu, Rakele, Mose, Yoswa, Manowa, Eliya komanso Hezekiya. Choncho aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Ngati Yehova anamvetsera anthuwa, kuli bwanji ineyo? Kodi inenso ndimayesetsa kulemekeza abale ndi alongo n’kumawamvetsera akamalankhula ndiponso kutsatira maganizo awo omwe ndi othandiza? Nanga pali munthu wina mumpingo kapena m’banja langa amene akufunika kwambiri kuti ndizimumvetsera? Kodi ndiyenera kuchita chiyani?​—Gen. 30:6; Ower. 13:9; 1 Maf. 17:22; 2 Mbiri 30:20.

“MWINA YEHOVA AONA” MAVUTO ANGA

Davide anati: “Musiyeni anyoze.” Kodi mukanakhala inu mukanatani? (Onani ndime 16, 17)

16. Kodi Mfumu Davide anatani Simeyi atamunyoza?

16 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti tikhale odziletsa ena akatiputa. (Aef. 4:2) Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi tingachipeze pa 2 Samueli 16:5-13. (Werengani.) Pa nthawi ina, Davide ndi atumiki ake ananyozedwa komanso kugendedwa ndi Simeyi, yemwe anali wachibale wa Mfumu Sauli. Ngakhale kuti Davide anali ndi mphamvu, anadziletsa kuti asabwezere. Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti adziletse? Tingapeze yankho la funsoli mu Salimo 3.

17. Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti akhale wodziletsa, nanga tingamutsanzire bwanji?

17 Mawu apamwamba pa Salimo 3 amasonyeza kuti salimoli ndi nyimbo ya Davide imene analemba pa nthawi imene “anali kuthawa mwana wake Abisalomu.” Vesi 1 ndi 2 limafotokoza zinthu zimene zili m’chaputala 16 cha buku la 2 Samueli. Lemba la Salimo 3:4 limasonyeza kuti Davide ankadalira kwambiri Yehova. Iye anati: “Ndidzafuulira Yehova mokweza, ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.” Ifenso tiyenera kupemphera tikakhala pa mavuto. Tikatero Yehova amatipatsa mzimu woyera umene ungatithandize kuti tipirire. Kodi pali vuto lina limene mukukumana nalo ndipo mukufunika kudziletsa? Kapena kodi pali munthu winawake amene amadana nanu popanda chifukwa yemwe mukufunika kumukhululukira? Kodi mukukhulupirira kuti Yehova akuona mavuto anu ndipo angakudalitseni?

‘NZERU NDI YOFUNIKA KWAMBIRI’

18. Kodi kutsatirabe malangizo ochokera kwa Mulungu kungatithandize bwanji?

18 Munthu akamachita zinthu zoyenera amadalitsidwa. N’chifukwa chake lemba la Miyambo 4:7 limanena kuti “nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.” N’zoona kuti munthu amapeza nzeru akadziwa zinthu n’kuzimvetsa koma amasonyeza kuti ndi wanzerudi akamasankha zochita mwanzeru. Paja ngakhale nyerere zimasonyeza kuti ndi zanzeru chifukwa zimasungiratu chakudya choti zidzadye m’tsogolo. (Miy. 30:24, 25) Khristu amatchedwa “nzeru za Mulungu” ndipo nthawi zonse amachita zinthu zosangalatsa Atate wake. (1 Akor. 1:24; Yoh. 8:29) Yehova amasiyanitsa anthu amene amangodziwa zoyenera kuchita ndi amene amachita zoyenerazo. Iye amadalitsa anthu odzichepetsa amene amapirira n’kumachita zimene akudziwa kuti n’zoyenera. (Werengani Mateyu 7:21-23.) Choncho tiyeni tipitirize kuchita zinthu zimene zingatithandize kuti aliyense mumpingo azitumikira Mulungu modzichepetsa. Kutsatira zinthu zimene timadziwa kuti n’zoyenera kumatenga nthawi ndipo pamafunika kuleza mtima. Koma zimasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndipo zimathandiza kuti tikhale osangalala panopa mpaka muyaya.