Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikhala Okoma Mtima Komanso Oganizira Ena Ngati Yehova

Tizikhala Okoma Mtima Komanso Oganizira Ena Ngati Yehova

“Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.”​—SAL. 41:1.

NYIMBO: 130, 107

1. Kodi anthu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti amakondana?

ANTHU a Mulungu amakhala ngati banja limodzi ndipo amakondana. (1 Yoh. 4:16, 21) Sikuti amangosonyeza chikondi m’zinthu zikuluzikulu zokha koma ngakhalenso m’zinthu zing’onozing’ono zimene amachita ndiponso kunena. Tikamachita zinthu mokoma mtima komanso moganizira ena timakhala kuti ‘tikutsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.’​—Aef. 5:1.

2. Kodi Yesu anatsanzira bwanji Mulungu posonyeza chikondi?

2 Yesu ankatsanzira Atate wake pa zonse zimene ankachita. Iye anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani . . . , chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mat. 11:28, 29) Tikamatsanzira Khristu pa nkhani yochita zinthu “moganizira munthu wonyozeka” timasangalatsa Atate wathu wakumwamba ndipo nafenso timakhala osangalala. (Sal. 41:1) Tiyeni tikambirane zimene tingachite posonyeza kuti timaganizira anthu a m’banja lathu, mumpingo komanso mu utumiki.

TIZICHITA ZINTHU MOGANIZIRA ANTHU A M’BANJA LATHU

3. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amamvetsa mkazi wake komanso kumuganizira? (Onani chithunzi choyambirira.)

3 Amuna ayenera kukhala patsogolo pochita zinthu moganizira anthu m’banja lawo. (Aef. 5:25; 6:4) Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti amuna ayenera kukhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino.” Mawu oti “mowadziwa bwino” akhoza kumasuliridwanso kuti “mowaganizira” kapena “mowamvetsa.” (1 Pet. 3:7) Kuti munthu achite zinthu moganizira wina, choyamba amafunika kumumvetsa. Mwachitsanzo, mwamuna womvetsa amadziwa kuti mkazi wake ndi womuthandiza choncho kusiyana naye mu zinthu zina sikuchititsa kuti akhale wotsika. (Gen. 2:18) Izi zimamuthandiza kuti aziganizira mmene akumvera mumtima mwake n’kumachita naye zinthu mwaulemu. Pofotokoza za mwamuna wake, mkazi wina wa ku Canada anati: “Amaganizira mmene ndikumvera ndipo sandinyoza kapena kunena kuti ‘Bwanji ukumva choncho?’ M’malomwake amandimvetsera ndikamalankhula. Akafuna kundithandiza kuti ndisinthe maganizo amachita zimenezo mokoma mtima.”

4. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amaganizira mkazi wake pochita zinthu ndi akazi ena?

4 Mwamuna amene amaganizira mkazi wake amakhalanso wosamala pochita zinthu ndi akazi ena. Amapewa kukopana kapena kucheza nawo mopitirira malire. Amachitanso zinthu mosamala akamacheza ndi anthu pa intaneti kapena kuonera zinthu pa intanetipo. (Yobu 31:1) Iye amakhala wokhulupirika kwa mkazi wake chifukwa choti amamukonda, amakonda Mulungu komanso amadana ndi zoipa.​—Werengani Salimo 19:14; 97:10.

5. Kodi mkazi angasonyeze bwanji kuti amaganizira mwamuna wake?

5 Mwamuna akamatsanzira Yesu Khristu, yemwe ndi mutu wake, amathandiza mkazi wake kuti ‘azimulemekeza kwambiri.’ (Aef. 5:22-25, 33) Ulemu umenewo ungathandize kuti nayenso mkaziyo azichita zinthu moganizira mwamuna wake. Mwachitsanzo, akhoza kukhala womvetsa ngati mwamunayo akufuna kuchita zinthu zina zokhudza udindo wake m’gulu la Yehova kapena ngati nkhani inayake ikumudetsa nkhawa. Mwamuna wina wa ku Britain anati: “Nthawi zina mkazi wanga akangoona mmene ndikuonekera amadziwa kuti pali nkhani inayake imene ikundidetsa nkhawa. Kenako amatsatira mfundo ya pa Miyambo 20:5 ndipo nthawi zina amadikira nthawi yoyenera kuti andifunse zimene zikundidetsa nkhawa. Ngati nkhaniyo si yachinsinsi ndimamufotokozera.”

6. Kodi tonsefe tingathandize bwanji ana kuti azichita zinthu moganizira ena, nanga zimenezi zingathandize bwanji anawo?

6 Makolo akamachita zinthu moganizirana amapereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azichita zinthu moganizira ena. Mwachitsanzo, angawaphunzitse kuti asamathamangethamange m’Nyumba ya Ufumu. Angawaphunzitsenso kuti akapita kokacheza azilola kaye akuluakulu kuti atenge chakudya iwo asanatenge. Ngakhale zili choncho, ena tonse mumpingo tikhoza kuthandiza makolo pophunzitsa ana. Mwachitsanzo, mwana akatichitira zinthu zabwino tiyenera kumuthokoza. Zimenezi zingathandize anawo kuzindikira kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Mac. 20:35.

TIZICHITA ZINTHU MOGANIZIRA ANTHU MUMPINGO

7. Kodi Yesu anachita bwanji zinthu moganizira munthu wina amene anali ndi vuto losamva?

7 Pa nthawi ina pamene Yesu anali m’zigawo za Dekapole, anthu “anam’bweretsera munthu wogontha komanso wovutika kulankhula.” (Maliko 7:31-35) M’malo momuchiritsira pa gulu, Yesu ‘anapita naye pambali.’ Anachita zimenezi chifukwa chakuti mwina vuto la munthuyu linkachititsa kuti asamamasuke pa gulu. Ndiye mwina Yesu atazindikira zimenezi anaona kuti ndi bwino kumuchiritsira pambali. N’zoona kuti ifeyo sitingachiritse munthu. Koma tikhoza kuchita zinthu moganizira mavuto amene anthu akukumana nawo komanso mmene akumvera mumtima mwawo. Paja Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Yesu anazindikira mmene munthu uja ankamvera ndipo anachita zinthu momuganizira. Apatu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri.

8, 9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira achikulire komanso odwala? (Perekani zitsanzo.)

8 Tizichita zinthu moganizira achikulire komanso odwala. Akhristu amadziwika kuti amachita zinthu mwadongosolo komanso mwachikondi. (Yoh. 13:34, 35) Chikondi chimenechi chimatilimbikitsa kuti tiziyesetsa mmene tingathere kuti tithandize achikulire kapena olumala kuti azipezeka pamisonkhano komanso azilalikira. Timachita zimenezi ngakhale kuti zimene iwo angakwanitse n’zochepa. (Mat. 13:23) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Michael, amene amayenda pa njinga ya olumala. Iye amayamikira zimene anthu a m’banja lake komanso a m’kagulu kake ka utumiki amachita pomuthandiza. Michael anati: “Zimene amachita zimandithandiza kuti ndizipezeka pamisonkhano komanso mu utumiki. Ndimakonda kwambiri kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri.”

9 M’mayiko ambiri, ku Beteli kuli anthu achikulire komanso odwala. Abale amene amayang’anira zinthu amaganizira kwambiri atumiki okhulupirika amenewa ndipo amakonza zoti azilalikira pafoni kapena polemba makalata. M’bale wina dzina lake Bill, yemwe ali ndi zaka 86, amalembera makalata anthu okhala m’madera akutali ndipo anati: “Timayamikira kwambiri mwayi wolalikira polemba makalata.” Mlongo wina wazaka pafupifupi 90 dzina lake Nancy anati: “Sindiona kuti ndikungoika makalata m’maenvelopu basi koma ndikulalikira. Tikuthandiza anthu amene akufuna kudziwa choonadi.” Mlongo winanso dzina lake Ethel yemwe anabadwa mu 1921 ananena kuti: “Ndimamva ululu nthawi iliyonse moti masiku ena ngakhale kuvala kumandivuta.” Ngakhale zili choncho, amasangalala kulalikira pafoni ndipo ali ndi maulendo obwereza abwino. Mlongo wina wazaka 85 dzina lake Barbara anati: “Popeza ndimadwaladwala, zimandivuta kulowa mu utumiki. Koma kulalikira pafoni kumandithandiza kuti ndiziuza ena uthenga wabwino. Ndikuthokoza kwambiri Yehova.” Gulu lina la achikulire linalalikira maola 1,228 chaka chisanathe ndipo linalemba makalata 6,265, kuimba mafoni maulendo oposa 2,000 komanso kugawira mabuku okwana 6,315. N’zosakayikitsa kuti zimene anachitazi zinasangalatsa kwambiri mtima wa Yehova.​—Miy. 27:11.

10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira abale ndi alongo athu kumisonkhano?

10 Tizichita zinthu moganizira ena kumisonkhano. Timafuna kuti misonkhano yathu izithandiza kwambiri abale ndi alongo. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kuchita zinthu mowaganizira. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timawaganizira? Njira imodzi ndi kufika kumisonkhano mofulumira n’cholinga choti tisasokoneze anthu. N’zoona kuti nthawi zina tikhoza kuchedwa pa zifukwa zosiyanasiyana. Koma ngati nthawi zambiri timachedwa, tiyenera kuganizira zimene tingachite kuti tisinthe. Tizikumbukiranso kuti amene amatiitanira kumisonkhanoyi ndi Yehova ndi Mwana wake. (Mat. 18:20) Ndiye tiyenera kuwalemekeza kwambiri.

11. N’chifukwa chiyani abale amene ali ndi nkhani ayenera kutsatira malangizo a pa 1 Akorinto 14:40?

11 Kuti tichite zinthu moganizira abale ndi alongo athu, tiyenera kutsatira malangizo akuti: “Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Abale amene apatsidwa nkhani angatsatire malangizowa posunga nthawi. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti akuganizira amene akambe nkhani yotsatira komanso mpingo wonse. Tikutero chifukwa chakuti abale ena amachokera kutali ndipo ena amayenera kukwera basi pobwerera kwawo. Palinso ena omwe ali ndi mwamuna kapena mkazi yemwe si Mboni ndipo sangasangalale ngati angafike mochedwa kunyumba.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira kwambiri akulu? (Onani bokosi lakuti “ Tizichita Zinthu Moganizira Amene Amatitsogolera.”)

12 Tiyenera kuganizira kwambiri abusa amene amagwira ntchito mwakhama mumpingo komanso amatsogolera bwino mu utumiki. (Werengani 1 Atesalonika 5:12, 13.) Muyenera kuti mumayamikira kwambiri mmene akulu amakuthandizirani. Ngati zili choncho, mungasonyeze kuyamikira kwanuko pochita zinthu mogwirizana nawo. Paja iwo “amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu.”​—Aheb. 13:7, 17.

TIZICHITA ZINTHU MOGANIZIRA ANTHU MU UTUMIKI

13. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikakhala mu utumiki?

13 Yesaya analosera za Yesu kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima sadzachizimitsa.” (Yes. 42:3) Yesu ankakonda anthu komanso kuganizira mavuto awo. Ankamvetsa anthu amene anali ngati bango lophwanyika kapena chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima. Chifukwa cha zimenezi, ankachita nawo zinthu mowaganizira, mokoma mtima komanso moleza mtima. Ngakhale ana ankamasukanso kucheza naye. (Maliko 10:14) N’zoona kuti sitingafanane ndi Yesu pa nkhani ya nzeru komanso kuphunzitsa bwino. Koma tiyenera kuchita zinthu moganizira anthu amene timawapeza mu utumiki. Tiyenera kuganizira mmene tingawalankhulire, nthawi imene tiyenera kuwapeza komanso kutalika kwa nthawi imene tingakambirane nawo.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala polankhula ndi anthu mu utumiki?

14 Mmene tingawalankhulire. Masiku ano anthu ambiri ndi “onyukanyuka ndi otayika” chifukwa choponderezedwa ndi anthu amalonda, andale komanso achipembedzo. (Mat. 9:36) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri alibe chiyembekezo ndipo sakhulupirira anthu. Choncho tiyenera kusankha bwino mawu n’kuwalankhula mokoma mtima komanso mwachifundo. Anthu ambiri amakopeka ndi uthenga wathu osati chifukwa choti timadziwa Baibulo kapena timafotokoza bwino mfundo basi, koma chifukwa choti timachita zinthu mowaganizira.

15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu mu utumiki?

15 Pali njira zambiri zimene tingasonyezere kuti timaganizira anthu mu utumiki. Mwachitsanzo, kufunsa mafunso kumathandiza kwambiri tikamaphunzitsa anthu. Koma tiyenera kufunsa mafunsowo mokoma mtima komanso mwaulemu. Mpainiya wina amene ankalalikira m’dera limene anthu ake si omasuka kwambiri, anaona kuti si bwino kufunsa mafunso amene angawachititse manyazi. Amapewa mafunso amene munthu angalephere kuyankha kapena amene angawayankhe molakwika. Mwachitsanzo, sawafunsa kuti: ‘Kodi dzina la Mulungu mumalidziwa?’ kapena kuti ‘Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?’ M’malomwake amangonena kuti: “Ndawerenga m’Baibulo kuti Mulungu ali ndi dzina lenileni. Mungakonde kuti ndikusonyezeni dzina lake?” Sitingachite kuika malamulo pa nkhani imeneyi chifukwa anthu komanso zikhalidwe zimakhala zosiyanasiyana. Koma nthawi zonse tiyenera kuchita zinthu mwaulemu komanso moganizira anthu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kuwadziwa bwino anthu a m’gawo lathu.

16, 17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zinthu izi tikamalalikira? (a) nthawi imene tiyenera kuwapeza anthu. (b) kutalika kwa nthawi imene tingakambirane nawo.

16 Nthawi imene tiyenera kuwapeza. Tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, timapita kwa anthu omwe sanatiitane. Choncho ndi bwino kuwapeza pa nthawi imene angamasuke kukambirana nafe. (Mat. 7:12) Mwachitsanzo, kodi anthu m’gawo lanu amadzuka mochedwa Loweruka kapena Lamlungu? Ngati ndi choncho, ndi bwino kuyamba utumiki wathu ndi kulalikira mumsewu kapena m’malo opezeka anthu ambiri. Apo ayi, tingapite kwa anthu amene tikudziwiratu kuti tikawapeza atadzuka.

17 Kutalika kwa nthawi imene tingakambirane nawo. Anthu ambiri masiku ano amatanganidwa choncho si bwino kulankhula nawo kwa nthawi yaitali pa maulendo oyambirira. Ndi bwino kuwasiya msanga kusiyana ndi kuwachedwetsa. (1 Akor. 9:20-23) Anthu akaona kuti tikuzindikira zoti atanganidwa angalole mosavuta kuti tidzawapezenso ulendo wina. Tikakhala mu utumiki tiyenera kusonyeza makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. Tikamatero timakhaladi “antchito anzake a Mulungu” ndipo iye akhoza kutigwiritsa ntchito pokokera anthu ena m’gulu lake.​—1 Akor. 3:6, 7, 9.

18. Kodi chingachitike n’chiyani tikamachita zinthu moganizira ena?

18 Choncho tiyeni tiziyesetsa kuganizira anthu m’banja lathu, mumpingo komanso mu utumiki. Tikamatero tidzadalitsidwa kwambiri panopa komanso m’tsogolo. Paja lemba la Salimo 41:1, 2 limati: “Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa. . . . Adzatchedwa wodala padziko lapansi.”