Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Wamphamvuyonse Koma Amaganizira Ena

Yehova Ndi Wamphamvuyonse Koma Amaganizira Ena

“[Yehova] akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.”​—SAL. 103:14.

NYIMBO: 30, 10

1, 2. (a) Kodi Yehova amachita bwanji zinthu mosiyana ndi anthu? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

ANTHU amphamvu komanso otchuka nthawi zambiri “amapondereza anthu” ena. (Mat. 20:25; Mlal. 8:9) Koma zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi Yehova. Ngakhale kuti ndi Wamphamvuyonse, amachita zinthu moganizira anthu ochimwafe. Iye ndi wachikondi komanso wokoma mtima. Amaganizira mmene tikumvera ndipo amadziwa zimene tikufunikira. Komanso samayembekezera kuti tizichita zimene sitingakwanitse chifukwa “amakumbukira kuti ndife fumbi.”​—Sal. 103:13, 14.

2 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza mmene Yehova anachitira zinthu moganizira atumiki ake. Munkhaniyi tikambirana zitsanzo zitatu. Chitsanzo choyamba ndi chokhudza mmene Yehova anathandizira Samueli ali mwana kuti apereke uthenga wachiweruzo kwa Eli yemwe anali mkulu wa ansembe. Chachiwiri, tiona mmene Yehova anachitira zinthu moganizira Mose pamene ankaopa kutsogolera mtundu wa Aisiraeli. Chachitatu ndi cha zimene Yehova anachita potsogolera Aisiraeli kuchoka ku Iguputo. Tikamakambirana zitsanzozi, tiziganizira zimene tikuphunzira zokhudza Yehova komanso zimene tingachite kuti tizimutsanzira.

ANACHITA ZINTHU MOGANIZIRA SAMUELI

3. (a) Kodi n’chiyani chinachitika tsiku lina Samueli akugona? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi zimenezi zingatichititse kufunsa funso liti?

3 Samueli anayamba “kutumikira Yehova” kuchihema ali wamng’ono kwambiri. (1 Sam. 3:1) Tsiku lina akugona panachitika zinthu zodabwitsa. * (Werengani 1 Samueli 3:2-10.) Iye anamva munthu akumuitana. Poyamba ankaganiza kuti akuitanidwa ndi Eli ndipo anathamanga kupita kwa iye n’kunena kuti: “Ndabwera mbuyanga, ndamva kuitana.” Koma Eli anamuuza kuti sanamuitane. Zimenezi zinachitikanso maulendo ena awiri ndipo Eli anazindikira kuti Mulungu ndi amene ankaitana Samueli. Choncho anamuuza mmene angayankhire ndipo Samueli anachita zomwezo. N’chifukwa chiyani Yehova sanathandize Samueli kuzindikira ulendo woyamba womwewo kuti iye ndi amene ankamuitana? Baibulo silinena, koma zimene zinachitika zikusonyeza kuti Yehova anachita zimenezi chifukwa choti ankamuganizira Samueliyo. N’chifukwa chiyani tikutero?

4, 5. (a) Kodi Samueli anamva bwanji Yehova atamuuza uthenga woti akauze Eli, nanga chinachitika n’chiyani kutacha? (b) Kodi nkhani ya Samueli ikusonyeza kuti Yehova ndi wotani?

4 Werengani 1 Samueli 3:11-18. Yehova analamula ana kuti azilemekeza achikulire, makamaka amene akutsogolera. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Ndiye kodi mukuganiza kuti Samueli akanakwanitsa kungodzuka m’mawa n’kupita kwa Eli kukamuuza uthenga woopsa wochokera kwa Mulungu? Ayi. Baibulo limanena kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Koma Mulungu anathandiza Eli kudziwa kuti ndi iyeyo amene ankamuitana Samueli. Choncho Eli ndi amene anauza Samueliyo kuti afotokoze zimene anauzidwa. Anamulamula kuti: ‘Usandibisire ngakhale mawu amodzi pa mawu onse amene iye wakuuza.’ Samueli anamvera ndipo “anamuuza mawu onse.”

5 Uthenga umene Samueli ananena sunali wachilendo kwambiri kwa Eli. Tikutero chifukwa chakuti “munthu wa Mulungu” wina anali atamuuzanso zofanana ndi zimenezi. (1 Sam. 2:27-36) Nkhani imeneyi ikusonyeza kuti Yehova ndi wanzeru komanso amaganizira anthu ake.

6. Kodi nkhani ya Samueli ikusonyeza kuti Mulungu ndi wotani?

6 Kodi inunso ndinu wamng’ono? Ngati ndi choncho, nkhani ya Samueli ikusonyeza kuti Yehova amamvetsa mavuto amene mukukumana nawo komanso mmene mumamvera mumtima mwanu. N’kutheka kuti ndinu wamanyazi ndipo zimakuvutani kulalikira kwa akuluakulu kapena kuchita zinthu mosiyana ndi anzanu. Koma dziwani kuti Yehova amafunitsitsa kukuthandizani. Choncho muzipemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima. (Sal. 62:8) Muziganizira za achinyamata otchulidwa m’Baibulo monga Samueli. Muzikambirananso ndi Akhristu anzanu, kaya achikulire kapena achinyamata, amene anakumana ndi mavuto ngati anuwo. Iwo akhoza kukufotokozerani mmene Yehova anawathandizira mwina m’njira imene sankayembekezera.

ANACHITA ZINTHU MOGANIZIRA MOSE

7, 8. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankamuganizira Mose?

7 Mose ali ndi zaka 80, Mulungu anamupatsa ntchito yovuta. Anamuuza kuti akapulumutse Aisiraeli ku Iguputo. (Eks. 3:10) Mose anali m’busa kwa zaka 40 ku Midiyani, choncho ayenera kuti anadabwa atapatsidwa ntchitoyi. Iye anati: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” Koma Mulungu anamutsimikizira kuti: “Ndidzakhala nawe.” (Eks. 3:11, 12) Iye anamulonjezanso kuti: ‘Akulu a Isiraeli adzamvera mawu ako.’ Komabe Mose anafunsa kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira ndi kumvera mawu anga?” (Eks. 3:18; 4:1) Apatu Mose ankatsutsa zimene Mulungu anamuuza. Koma Yehova anapitiriza kumulezera mtima. Ndipo anamupatsa mphamvu yochitira zozizwitsa moti anali munthu woyamba kukhala ndi mphamvu zimenezi.​—Eks. 4:2-9, 21.

8 Koma ananenabe kuti sangakwanitse kugwira ntchitoyi chifukwa ankalankhula movutikira. Mulungu anamuyankha kuti: “Ine ndidzakhala nawe polankhula ndipo ndidzakuuza zonena.” Kodi zimenezi zinathandiza kuti mtima wa Mose ukhale m’malo? Zikuoneka kuti ayi chifukwa anapemphanso Mulungu kuti atumize munthu wina osati iyeyo. Ndiyeno Yehova anamukwiyira koma anakhalabe wololera. Iye anachitanso zinthu moganizira Mose ndipo anapempha Aroni kuti akakhale womulankhulira.​—Eks. 4:10-16.

9. Kodi zimene Yehova anamuchitira Mose zinamuthandiza bwanji?

9 Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova? Popeza ndi wamphamvuyonse akanatha kuopseza Mose kuti amvere msangamsanga. Koma m’malomwake, anamumvetsera moleza mtima ndipo anayesetsa kulimbikitsa Mose yemwe anali wodzichepetsa kwambiri. Kodi zimene Mulungu anachitazi zinathandiza? Inde. Mose anadzakhala mtsogoleri wabwino komanso wofatsa ndipo ankachita zinthu moganizira ena ngati mmene Yehova anachitira.​—Num. 12:3.

Kodi mumatsanzira Yehova pochita zinthu ndi anthu ena? (Onani ndime 10)

10. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatsanzira Yehova pa nkhani yoganizira ena?

10 Ngati ndinu mwamuna, kholo kapena mkulu mumpingo, kodi mungaphunzirepo chiyani pa nkhaniyi? Popeza kuti mumayang’anira anthu ena, muyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yochita zinthu mokoma mtima, moleza mtima komanso moganizira anthuwo. (Akol. 3:19-21; 1 Pet. 5:1-3) Mukamayesetsa kutsanzira Yehova komanso Yesu Khristu, yemwe ndi Mose Wamkulu, anthu azimasuka nanu ndipo mukhoza kuwalimbikitsa. (Mat. 11:28, 29) Mudzakhalanso chitsanzo chabwino kwambiri kwa anthu ena.​—Aheb. 13:7.

YEHOVA ANACHITA ZINTHU ZOOPSA KOMA MOGANIZIRA ANTHU AKE

11, 12. Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli kuti asamachite mantha pochoka ku Iguputo?

11 Aisiraeli amene anapulumutsidwa ku Iguputo mu 1513 B.C.E. ayenera kuti anali oposa 3 miliyoni. Pa gululi panali ana, achikulire komanso mwina anthu odwala kapena olumala. Kuti munthu atsogolere bwinobwino gulu lalikulu chonchi, anafunika kukhala womvetsa komanso woganizira ena. Yehova anali mtsogoleri wotereyu ndipo anagwiritsa ntchito Mose. Izi zinathandiza kuti Aisiraeli asachite mantha pochoka ku Iguputo kumene anabadwira.​—Sal. 78:52, 53.

12 Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake kuti asamachite mantha pa ulendowu? Choyamba, anawauza kuti aziyenda “mwa dongosolo lomenyera nkhondo.” (Eks. 13:18) Dongosolo limeneli linathandiza Aisiraeliwo kudziwa kuti Yehova awayendetsa bwino. Yehova anawathandizanso kudziwa kuti ali nawo chifukwa ankawatsogolera ndi “mtambo masana” ndipo usiku ankawatsogolera ndi “kuwala kwa moto.” (Sal. 78:14) Apa zinali ngati Yehova akuwauza kuti: “Musaope. Ndili nanu. Ndizikutsogolerani komanso kukutetezani.” Zimenezi zinawathandiza kwambiri pa mavuto amene anadzakumana nawo.

Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankaganizira Aisiraeli pa Nyanja Yofiira? (Onani ndime 13)

13, 14. (a) Kodi Yehova anachita bwanji zinthu moganizira Aisiraeli pa Nyanja Yofiira? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali wamphamvu kuposa Aiguputo?

13 Werengani Ekisodo 14:19-22. Tayerekezerani kuti munali m’gulu la Aisiraeli ndipo kutsogolo kwanu kuli Nyanja Yofiira, kumbuyo kwanu kukubwera Farao ndi asilikali ake. Ndiyeno Yehova akuyamba kukuthandizani. Mtambo uja ukubwera kumbuyo kwanu n’kuchititsa mdima mbali imene kuli Aiguputo. Koma mbali imene kuli inuyo kukuwala modabwitsa. Kenako mukuona Mose akuloza Nyanja Yofiira ndi ndodo yake ndipo mphepo yamphamvu yakum’mawa ikubwera n’kuyamba kugawa nyanjayo moti njira yaikulu ikutseguka. Ndiyeno inuyo, anthu a m’banja lanu, ziweto zanu komanso Aisiraeli onse mukudutsa mwadongosolo. Mukudabwa kuti pansi pamene mukudutsapo palibe matope ndipo munthu sangaterereke. Malo amene mukuponda ndi ouma gwa moti mukuyendapo bwinobwino. Ngakhale anthu oyenda pang’onopang’ono akuwoloka bwinobwino n’kupita tsidya lina.

14 Werengani Ekisodo 14:23, 26-30. Kenako Farao, yemwe ndi wokula mtima komanso wopusa akulowa pampatawo kuti akuthamangireni. Ndiyeno Mose akulozanso nyanjayo. Nthawi yomweyo makoma a madziwo akugwa ndipo madzi a mbali ziwirizo akuwombana mwamphamvu. Farao ndi asilikali ake akuthera pomwepo.​—Eks. 15:8-10.

15. Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?

15 Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo ndipo zimenezi zingatithandizenso kuti tisamachite mantha kapena kuda nkhawa. (1 Akor. 14:33) Ikusonyezanso kuti Yehova ndi m’busa wabwino amene amasamalira anthu ake. Iye amawateteza mwachikondi kwa adani awo. Mfundo zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli.​—Miy. 1:33.

16. Kodi kuganizira mmene Yehova anapulumutsira Aisiraeli kungatithandize bwanji?

16 Masiku anonso, Yehova amasamalira gulu lake m’njira zosiyanasiyana. Ndipo apitiriza kuchita zimenezi mpaka pa chisautso chachikulu chimene chikubwera posachedwapa. (Chiv. 7:9, 10) Choncho kaya ndife aang’ono kapena achikulire, athanzi kapena olumala, sitidzafunika kuopa pa nthawi ya chisautso chachikulu. * M’malomwake tidzangokumbukira mawu a Yesu akuti: “Mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.” (Luka 21:28) Tidzapitiriza kudalira Yehova ngakhale pa nthawi imene tidzaukiridwe ndi Gogi, yemwe akuimira mgwirizano wa mitundu ya anthu womwe udzakhala wamphamvu kwambiri kuposa Farao. (Ezek. 38:2, 14-16) Koma kodi n’chiyani chidzathandize anthu a Mulungu kuti asachite mantha? Iwo amadziwa kuti Yehova sasintha ndipo adzachitanso zinthu mowaganizira n’kuwapulumutsa.​—Yes. 26:3, 20.

17. (a) Kodi nkhani za m’Baibulo zosonyeza mmene Yehova amasamalirira anthu ake zingatithandize bwanji? (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 M’Baibulo muli zitsanzo zambirimbiri zosonyeza kuti Yehova amachita zinthu mokoma mtima komanso moganizira anthu ake akamawasamalira, kuwatsogolera komanso kuwapulumutsa. Mukamaganizira nkhani ngati zimenezi, muziyesetsa kuona zimene mukuphunzira zokhudza makhalidwe a Yehova. Mukamatero, makhalidwewo adzakhazikika mumtima ndi m’maganizo anu ndipo mudzayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kumukhulupirira ndi mtima wonse. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti tizitsanzira Yehova pa nkhani yoganizira ena. Tidzaona mmene tingachitire zimenezi m’banja, mumpingo komanso mu utumiki.

^ ndime 3 Katswiri wa mbiri ya Ayuda dzina lake Josephus ananena kuti pa nthawiyi Samueli anali ndi zaka 12.

^ ndime 16 N’zodziwikiratu kuti anthu ena amene adzapulumuke nkhondo ya Aramagedo adzakhala olumala. Yesu ali padzikoli, anachiritsa anthu okhala ndi “zofooka zilizonse” ndipo zimenezi zikusonyeza zimene iye adzachitire anthu opulumuka pa Aramagedo, osati oukitsidwa. (Mat. 9:35) N’zosakayikitsa kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa ndi matupi abwinobwino.