Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 37

Tizigonjera Yehova ndi Mtima Wonse

Tizigonjera Yehova ndi Mtima Wonse

“Kodi sitiyenera kuwagonjera [Atate] koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?”​—AHEB. 12:9.

NYIMBO NA. 9 Yehova Ndi Mfumu Yathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kugonjera Yehova?

TIYENERA kugonjera * Yehova chifukwa ndi amene anatilenga. Choncho ndi woyenera kutipatsa mfundo zoti tiziyendera. (Chiv. 4:11) Koma chifukwa china chotichititsa kumumvera n’chakuti ulamuliro wake ndi wabwino kuposa wina uliwonse. Kuyambira kale, anthu ambiri akhala akulamulira anzawo. Koma Yehova ndi Wolamulira wanzeru, wachikondi komanso wachifundo kuposa olamulira ena onsewo.​—Eks. 34:6; Aroma 16:27; 1 Yoh. 4:8.

2. Kodi lemba la Aheberi 12:9-11 limafotokoza zifukwa ziti zotichititsa kugonjera Yehova?

2 Yehova amafuna kuti tizimumvera chifukwa choti timamukonda komanso timaona kuti ndi Atate wathu wachikondi osati chifukwa chomuopa basi. M’kalata yake yopita kwa Aheberi, Paulo ananena kuti ‘tiyenera kugonjera Atate’ chifukwa amatiphunzitsa n’cholinga choti “tipindule.”​—Werengani Aheberi 12:9-11.

3. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timagonjera Yehova? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Timagonjera Yehova poyesetsa kumumvera pa chilichonse komanso popewa kudalira luso lathu lomvetsa zinthu. (Miy. 3:5) Sitivutika kumvera Yehova tikadziwa bwino makhalidwe ake. Zili choncho chifukwa makhalidwe akewo amaonekera pa zonse zimene amachita. (Sal. 145:9) Tikamudziwa bwino Yehova m’pamene timamukonda kwambiri. Ngati timakonda Yehova sitifunika malamulo ambirimbiri otiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zosayenera. Timayesetsa kuti tizikonda zimene Yehova amakonda komanso kudana ndi zimene iye amadana nazo. (Sal. 97:10) Koma nthawi zina zimativuta kumumvera. N’chifukwa chiyani zili choncho? Nanga kodi akulu, abambo komanso amayi angaphunzire chiyani kwa Nehemiya, Mfumu Davide komanso Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.

N’CHIFUKWA CHIYANI ZINGATIVUTE KUGONJERA YEHOVA?

4-5. Mogwirizana ndi Aroma 7:21-23, n’chifukwa chiyani tingavutike kugonjera Yehova?

4 Chifukwa chimodzi chimene chimachititsa kuti tizivutika kumvera Yehova n’chakuti si ife angwiro. Choncho nthawi zina sitifuna kumvera Mulungu. Pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Yehova n’kudya chipatso choletsedwa, anasonyeza kuti akufuna kumasankha okha chabwino ndi choipa. (Gen. 3:22) Masiku anonso, anthu ambiri samvera Yehova ndipo amasankha okha kuti izi n’zoyenera, izi n’zosayenera.

5 Ngakhale anthu amene amadziwa Yehova komanso kumukonda angavutike kumugonjera pa zinthu zina. Nayenso mtumwi Paulo ankavutika. (Werengani Aroma 7:21-23.) Mofanana ndi Paulo, timafuna kuchita zinthu zimene Yehova amaona kuti n’zabwino. Koma nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kudziletsa kuti tisachite zoipa.

6-7. Kodi ndi chifukwa china chiti chimene chingachititse kuti tizivutika kugonjera Yehova? Perekani chitsanzo.

6 Tingavutikenso kugonjera Yehova chifukwa chakuti timasokonezedwa ndi chikhalidwe cha kumene tinakulira. Maganizo a anthu ambiri amasiyana ndi maganizo a Yehova choncho tiyenera kuyesetsa kwambiri kuti tisamatengere maganizo a anthuwo. Tiyeni tione chitsanzo chimodzi.

7 M’madera ena, anthu ambiri amalimbikitsa achinyamata kuti aziyesetsa kuti adzapeze ndalama zambiri. Mlongo wina dzina lake Mary * anakumana ndi vuto limeneli. Iye asanaphunzire za Yehova anapita kuyunivesite ina yapamwamba m’dziko lawo. Achibale ake ankamukakamiza kuti adzapeze ntchito yolemekezeka komanso ya ndalama zambiri. Poyamba, nayenso ankafuna zimenezi. Koma ataphunzira za Yehova n’kuyamba kumukonda, anasintha zolinga zake. Ngakhale zili choncho, iye anati: “Nthawi zina, ndimapeza mwayi wopanga ndalama zambiri koma umene ungandilepheretse kutumikira Yehova mmene ndikuchitira panopa. Ndipo chifukwa cha mmene ndinakulira, zimakhala zovuta kuti ndikane. Ndimafunika kupempha Yehova kuti andithandize kukana ntchito imene ingandilepheretse kumutumikira bwinobwino.”​—Mat. 6:24.

8. Kodi tikambirana chiyani tsopano?

8 Kugonjera Yehova kumatithandiza kwambiri. Koma anthu amene ali ndi udindo woyang’anira monga akulu, abambo komanso amayi ali ndi chifukwa china chowachititsa kutsatira malangizo a Yehova. Chifukwa chake n’chakuti akamachita zimenezi amathandizanso anthu ena. Tiyeni tikambirane zitsanzo zochokera m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tiziyang’anira anthu m’njira imene ingasangalatse Yehova.

KODI AKULU ANGAPHUNZIRE CHIYANI KWA NEHEMIYA?

Akulu amathandiza pa ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu ngati mmene Nehemiya anathandizira pa ntchito yomanganso Yerusalemu (Onani ndime 9-11) *

9. Kodi Nehemiya anakumana ndi mavuto ati?

9 Yehova wapereka kwa akulu udindo wofunika woyang’anira anthu ake. (1 Pet. 5:2) Ndipo akulu angaphunzire zambiri kwa Nehemiya pa nkhani yoyang’anira anthu a Yehova. Nehemiya anali ndi udindo waukulu chifukwa anali bwanamkubwa ku Yuda. (Neh. 1:11; 2:7, 8; 5:14) Taganizirani za mavuto amene ankakumana nawo. Iye anaona kuti anthu aipitsa kachisi komanso sankatsatira Chilamulo pa nkhani yothandiza Alevi kupeza zofunika pa moyo. Ayuda sankasunganso Sabata komanso anakwatira akazi amitundu ina. Ndiye kodi Nehemiya anatani ataona mavuto amenewa?​—Neh. 13:4-30.

10. Kodi Nehemiya anatani atakumana ndi mavuto?

10 Nehemiya sankagwiritsa ntchito molakwika udindo wake pokakamiza anthu a Mulungu kuti aziyendera maganizo ake. M’malomwake, ankapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kuti azimuthandiza komanso ankaphunzitsa anthu Chilamulo cha Yehova. (Neh. 1:4-10; 13:1-3) Iye anadzichepetsanso n’kumagwira ntchito ndi abale ake yomanga mpanda wa Yerusalemu.​—Neh. 4:15.

11. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 2:7, 8, kodi akulu ayenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu mumpingo?

11 Mwina akulu sangakumane ndi mavuto ngati amenewa, koma angatsanzire Nehemiya m’njira zambiri. Mwachitsanzo, ayenera kuyesetsa kuthandiza abale ndi alongo. Komanso sayenera kudziona kuti ndi apamwamba chifukwa cha udindo wawo. M’malomwake ayenera kuchita zinthu mwachikondi ndi anthu mumpingo. (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Chikondi komanso kudzichepetsa ziyenera kuwathandiza kuti azilankhula ndi abale ndi alongo mokoma mtima. M’bale wina dzina lake Andrew, yemwe wakhala mkulu kwa zaka zambiri, ananena kuti: “Ndimaona kuti akulu akamachita zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi amathandiza kwambiri abale ndi alongo. Makhalidwe amenewa amathandiza kuti abale ndi alongo azigwirizana ndi akulu.” M’bale wina dzina lake Tony, amene wakhalanso mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Ndimayesetsa kutsatira malangizo a pa Afilipi 2:3 oti tiziona ena kukhala otiposa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipewa kupondereza anthu ena.”

12. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kukhala odzichepetsa?

12 Akulu ayenera kukhala odzichepetsa ngati Yehova. Ngakhale kuti Yehova ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse, iye “amatsika m’munsi” kuti adzutse “munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.” (Sal. 18:35; 113:6, 7) Ndipo Yehova amanyansidwa ndi anthu onyada komanso odzikweza.​—Miy. 16:5.

13. N’chifukwa chiyani akulu amayenera ‘kulamulira lilime lawo’?

13 Mkulu yemwe amagonjera Yehova ayenera ‘kulamulira lilime lake.’ Kupanda kutero sangalankhule bwino ngati munthu sakumupatsa ulemu. (Yak. 1:26; Agal. 5:14, 15) Andrew, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Nthawi zina, ngati m’bale kapena mlongo sanandilemekeze, ndimavutika kudziletsa kuti ndisamulankhule mawu olakwika. Koma kuganizira zitsanzo za anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo kwandithandiza kuzindikira ubwino wokhala wodzichepetsa komanso wofatsa.” Akulu amasonyeza kuti amagonjera Yehova akamalankhula mwachikondi komanso mwaulemu kwa abale ndi alongo ndiponso akulu anzawo.​—Akol. 4:6.

KODI ABAMBO ANGAPHUNZIRE CHIYANI KWA MFUMU DAVIDE?

14. Kodi Yehova wapereka udindo wotani kwa abambo, nanga amafuna kuti azichita chiyani?

14 Yehova anapatsa abambo udindo woyang’anira banja ndipo amafuna kuti aziphunzitsa komanso kulangiza ana ake. (1 Akor. 11:3; Aef. 6:4) Koma udindo wa abambo uli ndi malire. Tikutero chifukwa chakuti Yehova ndi amene anayambitsa banja ndipo akhoza kuimba bambo mlandu pa zimene amachita ndi anthu a m’banja lake. (Aef. 3:14, 15) Abambo amasonyeza kuti amagonjera Yehova potsogolera banja lawo m’njira imene imasangalatsa Mulungu. Iwo angaphunzire zambiri ngati amawerenga za moyo wa Mfumu Davide.

Abambo ayenera kusonyeza kudzichepetsa akamapemphera kwa Yehova (Onani ndime 15-16) *

15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mfumu Davide ndi chitsanzo chabwino kwa abambo?

15 Kuwonjezera pa kuyang’anira banja lake, Yehova anasankha Davide kuti aziyang’anira mtundu wonse wa Isiraeli. Popeza anali mfumu, Davide anali ndi mphamvu zambiri. Koma nthawi zina sankagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake ndipo anachita machimo aakulu. (2 Sam. 11:14, 15) Koma anasonyeza kuti amagonjera Yehova polandira chilango chimene anapatsidwa. Iye anapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova ndipo ankayesetsa kutsatira malangizo ake. (Sal. 51:1-4) Davide anasonyezanso kudzichepetsa pomvera malangizo othandiza ochokera kwa amuna komanso akazi. (1 Sam. 19:11, 12; 25:32, 33) Iye anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsa ndipo ankaika kutumikira Yehova pamalo oyamba.

16. Kodi abambo angaphunzire chiyani kwa Mfumu Davide?

16 Ngati ndinu abambo, kodi mungaphunzire chiyani kwa Mfumu Davide? Simuyenera kugwiritsa ntchito molakwika udindo umene Yehova wakupatsani. Muyeneranso kuvomereza zimene mwalakwitsa n’kulandira malangizo ochokera m’Malemba amene mungapatsidwe. Mukamachita zimenezi anthu a m’banja lanu adzayamikira kudzichepetsa kwanu ndipo azikulemekezani. Popemphera ndi banja, muyenera kufotokoza zinthu kuchokera pansi pa mtima kuti anthu a m’banja lanu aziona kuti mumadalira kwambiri Yehova. Koma chofunika kwambiri n’chakuti muziika kutumikira Yehova pamalo oyamba. (Deut. 6:6-9) Chitsanzo chanu chabwino n’chimene chingathandize kwambiri anthu a m’banja lanu.

KODI AMAYI ANGAPHUNZIRE CHIYANI KWA MARIYA?

17. Kodi Yehova wapereka udindo wotani kwa amayi?

17 Yehova wapatsa amayi udindo wolemekezeka m’banja ndipo iwo ayeneranso kuyang’anira ana awo. (Miy. 6:20) Kunena zoona, zimene mayi amachita zimakhudza kwambiri moyo wa ana. (Miy. 22:6) Tiyeni tsopano tione zimene amayi angaphunzire kwa Mariya, yemwe anali mayi ake a Yesu.

18-19. Kodi amayi angaphunzire chiyani kwa Mariya?

18 Mariya ankadziwa bwino Malemba. Iye ankalemekezanso kwambiri Yehova ndipo anali naye pa ubwenzi wolimba. Iye anali ndi mtima wofuna kuchita zimene Yehova ankafuna ngakhale kuti zimenezi zinasinthiratu moyo wake.​—Luka 1:35-38, 46-55.

Ngati mayi watopa kapena kukwiya, angafunike kuyesetsa kwambiri kuti azisonyezabe chikondi kwa anthu a m’banja lake (Onani ndime 19) *

19 Ngati ndinu amayi, kodi mungatsanzire bwanji Mariya? Choyamba, muyenera kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo komanso kupemphera panokha. Chachiwiri, muyenera kulolera kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti musangalatse Yehova. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti munaleredwa ndi makolo amtima wapachala omwe ankakonda kukalipira ana. Ndiye inuyo munakula mukuganiza kuti njira yabwino yolerera ana ndi imeneyo. Ndipo ngakhale kuti mwaphunzira mfundo za Yehova, zingakuvutenibe kuugwira mtima makamaka ngati ana anu akuvuta inu mutatopa. (Aef. 4:31) Pa nthawi ngati imeneyo, muyenera kudalira kwambiri Yehova n’kupemphera kwa iye. Mayi wina dzina lake Lydia anati: “Nthawi zina ndimafunika kupemphera kwa Yehova mochonderera kuti ndisakalipire mwana wanga ngati sakundimvera. Pena ndimadula chiganizo nditachiyamba kale kenako n’kupempha Yehova kuti andithandize. Kupemphera kumandithandiza kwambiri kuti mtima wanga ukhale m’malo.”​—Sal. 37:5.

20. Kodi amayi ena amakhala ndi vuto liti, nanga angathane nalo bwanji?

20 Koma amayi ena amakhala ndi vuto lina. Zimawavuta kuti asonyeze chikondi kwa ana awo. (Tito 2:3, 4) Mwina analeredwa m’banja limene makolo sankasonyeza chikondi kwenikweni kwa ana awo. Ngati inunso munaleredwa m’banja lotere, muziyesetsa kupewa zimene makolo anu ankalakwitsazo. Mayi amene amagonjera Yehova ayenera kuyesetsa kuti azisonyeza chikondi kwa ana ake. N’zoona kuti kusintha maganizo, mtima komanso zochita kumakhala kovuta. Koma zimenezi n’zotheka ndipo n’zothandiza kwa mayiyo komanso banja lonse.

PITIRIZANI KUGONJERA YEHOVA

21-22. Malinga ndi Yesaya 65:13, 14, kodi kugonjera Yehova kuli ndi ubwino wotani?

21 Mfumu Davide ankadziwa ubwino wogonjera Yehova. Iye analemba kuti: “Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso. Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo. Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.” (Sal. 19:8, 11) Masiku ano, tingaone kusiyana pakati pa anthu amene amagonjera Yehova ndi amene amakana kutsatira malangizo ake. Anthu amene amagonjera Yehova ‘amafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima.’​—Werengani Yesaya 65:13, 14.

22 Akulu, abambo komanso amayi akamagonjera Yehova amakhala ndi moyo wabwino, mabanja awo amakhala osangalala komanso mpingo wonse umakhala wogwirizana. Koma chofunika kwambiri n’chakuti amasangalatsa mtima wa Yehova. (Miy. 27:11) Ndipo zimenezi n’zosangalatsa kuposa chinthu china chilichonse.

NYIMBO NA. 123 Tizigonjera Mulungu Mokhulupirika

^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kugonjera Yehova. Tikambirananso zimene anthu omwe ali ndi udindo woyang’anira monga akulu, abambo komanso amayi angaphunzire kwa Nehemiya, Mfumu Davide ndi Mariya.

^ ndime 1 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Anthu ena amaona kuti mawu oti kugonjera amatanthauza kumvera munthu wina mokakamizika. Koma anthu a Mulungu saona kugonjera m’njira imeneyi chifukwa iwo amasankha okha kumumvera.

^ ndime 7 Mayina ena munkhaniyi asinthidwa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mkulu akugwira ntchito limodzi ndi mwana wake pokonza zinthu ku Nyumba ya Ufumu ngati mmene Nehemiya anathandizira pa ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Bambo akupemphera kuchokera pansi pa mtima limodzi ndi banja lake.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mwana wakhala akusewera magemu apakompyuta kwa maola ambiri ndipo sanagwire ntchito zake zapakhomo kapena kulemba homuweki yake. Mayi ake akumulangiza popanda kumupsera mtima kapena kumukalipira ngakhale kuti angoweruka kumene kuntchito ndipo atopa.