Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 36

Uthenga Wokhudza Aramagedo Ndi Wosangalatsa

Uthenga Wokhudza Aramagedo Ndi Wosangalatsa

‘Anawasonkhanitsa pamodzi ku Haramagedo.’—CHIV. 16:16.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti uthenga wokhudza Aramagedo ndi wosangalatsa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

MWINA munamvapo anthu akutchula mawu oti “Aramagedo” ponena za nkhondo yanyukiliya kapena zinthu zina zoopsa. Komatu zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Aramagedo n’zabwino komanso zosangalatsa. (Chiv. 1:3) Nkhondo imeneyi ndi yabwino chifukwa idzapulumutsa anthu. N’chifukwa chiyani tikutero?

2 Baibulo limasonyeza kuti nkhondoyi idzatipulumutsa pothetsa maboma a anthu. Nkhondo imeneyi idzapha anthu oipa onse n’kusiya olungama okhaokha. Idzatetezanso dzikoli kuti lisawonongeke. (Chiv. 11:18) Kuti timvetse mfundo zimenezi, tiyeni tikambirane mafunso 4 awa: Kodi Aramagedo n’chiyani? Kodi n’chiyani chidzachitike Aramagedo itatsala pang’ono kuyamba? Kodi tingatani kuti tidzapulumuke pa Aramagedo? Nanga tingatani kuti tikhalebe okhulupirika m’masiku otsirizawa?

KODI ARAMAGEDO N’CHIYANI?

3. (a) Kodi Aramagedo n’chiyani? (b) Malinga ndi Chivumbulutso 16:14, 16, n’chifukwa chiyani tinganene kuti Aramagedo si malo enieni?

3 Werengani Chivumbulutso 16:14, 16. Mawu akuti “Aramagedo,” kapena kuti “Haramagedo,” amapezeka kamodzi kokha m’Malemba ndipo amachokera ku mawu achiheberi omwe amatanthauza “Phiri la Megido.” (Chiv. 16:16; mawu am’munsi) Megido unali mzinda wa ku Isiraeli wakale. (Yos. 17:11) Koma Aramagedo si dzina la malo enaake padzikoli. Mawuwa kwenikweni amanena za nthawi pamene “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwe kuti alimbane ndi Yehova. (Chiv. 16:14) Koma munkhaniyi tizigwiritsa ntchito mawu oti “Aramagedo” ponena za nkhondo imene idzayambe mafumu apadziko lapansi akadzasonkhanitsidwa. Kodi tikudziwa bwanji kuti Aramagedo si malo enieni? Chifukwa choyamba n’chakuti padzikoli palibe malo kumene kuli phiri la Megido. Chachiwiri n’chakuti dera la Megido ndi laling’ono kwambiri moti sikungakwane “mafumu a dziko lonse lapansi,” asilikali awo komanso zida zawo zankhondo. Chachitatu n’chakuti, malinga ndi zomwe tione munkhaniyi, nkhondo ya Aramagedo idzayamba “mafumu” a dziko lapansi akadzaukira anthu a Mulungu, omwe ali m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse.

4. N’chifukwa chiyani Yehova anagwiritsa ntchito mawu oti Megido ponena za nkhondo yake yomaliza?

4 N’chifukwa chiyani Yehova anagwiritsa ntchito mawu akuti Megido pofotokoza za nkhondo yaikulu yomaliza? Ku Megido komanso chigwa cha Yezereeli kunkamenyedwa nkhondo zambiri. Ndipo nthawi zina Yehova ankathandiza athu ake pomenya nkhondozo. Mwachitsanzo, “pafupi ndi madzi a ku Megido,” Mulungu anathandiza Baraki, yemwe anali woweruza wa Aisiraeli, kuti agonjetse asilikali a ku Kanani omwe ankatsogoleredwa ndi Sisera. Baraki limodzi ndi mneneri wamkazi dzina lake Debora anathokoza Yehova chifukwa chowapulumutsa modabwitsa. Iwo anaimba kuti: “Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba, zinamenyana ndi Sisera . . . Mtsinje wa Kisoni unawakokolola.”​—Ower. 5:19-21.

5. Kodi nkhondo ya Aramagedo idzasiyana bwanji ndi nkhondo ya Baraki?

5 Baraki ndi Debora anamaliza nyimbo yawo ndi mawu akuti: “Adani anu onse afafanizidwe chimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuwa limakhalira.” (Ower. 5:31) Pa nkhondo ya Aramagedo, adani a Mulungu adzawonongedwanso ndipo anthu onse amene amakonda Mulungu adzapulumuka. Koma nkhondo ziwirizi zimasiyana pa mfundo imodzi yofunika. Pa Aramagedo, anthu a Mulungu sadzamenya nawo nkhondo ndipo sadzakhalanso ndi zida zankhondo. Koma adzakhala ‘amphamvu akadzakhala osatekeseka n’kumakhulupirira’ Yehova ndi gulu lake lankhondo lakumwamba.​—Yes. 30:15; Chiv. 19:11-15.

6. Kodi Yehova angadzagwiritse ntchito zinthu ziti powononga adani ake pa Aramagedo?

6 Kodi Mulungu adzagonjetsa bwanji adani ake pa Aramagedo? Iye akhoza kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, akhoza kugwiritsa ntchito zivomezi, matalala komanso mphenzi. (Yobu 38:22, 23; Ezek. 38:19-22) Apo ayi, akhoza kuchititsa kuti adani ake aziphana okhaokha. (2 Mbiri 20:17, 22, 23) Akhozanso kugwiritsa ntchito angelo ake kuti awononge anthu oipa. (Yes. 37:36) Kaya Mulungu adzagwiritsa ntchito njira iti, mfundo ndi yakuti adzawonongeratu adani ake n’kupulumutsa anthu olungama.​—Miy. 3:25, 26.

KODI CHIDZACHITIKE N’CHIYANI ARAMAGEDO ITATSALA PANG’ONO KUYAMBA?

7-8. (a) Malinga ndi 1 Atesalonika 5:1-6, kodi atsogoleri am’dzikoli adzalengeza uthenga wapadera uti? (b) N’chifukwa chiyani uthenga wabodzawu udzakhala woopsa?

7 “Tsiku la Yehova” lisanafike anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (Werengani 1 Atesalonika 5:1-6.) Pa 1 Atesalonika 5:2, mawu oti “tsiku la Yehova” akunena za ‘chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:14) Kodi tidzadziwa bwanji kuti chisautsochi chatsala pang’ono kuyamba? Baibulo limafotokoza za uthenga winawake wapadera umene udzalengezedwe. Uthengawu udzakhala chizindikiro chakuti chisautso chachikulu chatsala pang’ono kuyamba.

8 Uthenga umene udzalengezedwewo udzakhala wakuti “bata ndi mtendere.” N’chifukwa chiyani atsogoleri am’dzikoli adzanene mawu amenewa? Nanga atsogoleri a zipembedzo adzalengeza nawo uthengawu? Mwina adzatero. Mulimonse mmene zidzakhalire, mawuwa adzangokhala uthenga wina wouziridwa ndi ziwanda. Koma uthenga wabodzawu udzakhala woopsa chifukwa chakuti udzachititsa anthu kuganiza kuti ndi otetezeka pa nthawi imene chisautso chachikulu kwambiri chatsala pang’ono kuyamba. Paja Baibulo limanena kuti “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati.” Koma kodi n’chiyani chidzachitikire atumiki okhulupirika a Yehova? Mwina akhoza kudzadabwa kuti tsiku la Yehova layamba modzidzimutsa kwambiri, koma adzakhala atakonzeka.

9. Kodi Mulungu adzawononga bwanji dziko la Satanali?

9 Yehova sadzawononga mbali zonse za dziko la Satana kamodzin’kamodzi ngati mmene anachitira m’nthawi ya Nowa. Koma adzayamba ndi mbali imodzi, kenako mbali ina. Choyamba, adzawononga Babulo Wamkulu, kapena kuti zipembedzo zonse zonyenga. Kenako pa Aramagedo, adzawononga mbali zina zonse za dziko la Satana, zomwe ndi zandale, zankhondo komanso zamalonda. Tiyeni tsopano tikambirane mwatsatanetsatane zinthu ziwiri zimene Mulungu adzachitezi.

10. Malinga ndi Chivumbulutso 17:1, 6; 18:24, kodi Yehova adzawononga Babulo Wamkulu chifukwa chiyani?

10 “Chiweruzo cha hule lalikulu.” (Werengani Chivumbulutso 17:1, 6; 18:24.) Babulo Wamkulu wachititsa kuti dzina la Mulungu linyozeke kwambiri. Iye wakhala akuphunzitsa mabodza ambiri okhudza Mulungu. Wakhala akuchitanso uhule wauzimu pochita zinthu mogwirizana ndi atsogoleri am’dzikoli. Iye amagwiritsanso ntchito mphamvu zake kuti apondereze anthu ake komanso kutenga ndalama zawo. Komanso wachititsa kuti anthu ambiri aphedwe, kuphatikizapo atumiki ena a Mulungu. (Chiv. 19:2) Ndiye kodi Yehova adzawononga bwanji Babulo Wamkulu?

11. Kodi ‘chilombo chofiira’ n’chiyani, nanga chidzagwiritsidwa ntchito bwanji pokwaniritsa cholinga cha Mulungu chokhudza Babulo Wamkulu?

11 Yehova adzawononga “hule lalikulu” pogwiritsa ntchito “nyanga 10” za ‘chilombo chofiira.’ Chilombo chophiphiritsira chimenechi chimaimira bungwe la United Nations. Nyanga 10 zikuimira maulamuliro omwe amagwirizana ndi bungweli. Nthawi imene Mulungu wasankha ikadzakwana, maulamulirowo adzaukira Babulo wophiphiritsirayu. Iwo ‘adzamusakaza ndi kumusiya wamaliseche’ pomulanda chuma chake komanso kusonyeza kuti ndi woipa kwambiri. (Chiv. 17:3, 16) Iye adzawonongedwa mwamsanga moti zidzakhala ngati zachitika tsiku limodzi lokha ndipo anthu onse amene ankagwirizana naye adzadabwa. Paja iye wakhala akudzitama ponena kuti: “Ine ndine mfumukazi. Sindine mkazi wamasiye, ndipo sindidzalira ngakhale pang’ono.”​—Chiv. 18:7, 8.

12. Kodi Yehova sadzalola kuti olamulira am’dzikoli achite chiyani? Perekani chifukwa.

12 Mulungu sadzalola kuti olamulira am’dzikoli awononge anthu ake, omwe amasangalala kudziwika ndi dzina lake ndipo anamvera lamulo lake loti atuluke m’Babulo Wamkulu. (Mac. 15:16, 17; Chiv. 18:4) Ayesetsanso kuthandiza anthu ena kuti achoke m’Babulo Wamkulu. Choncho atumiki a Yehova ‘sadzalandira nawo miliri yake.’ Komabe chikhulupiriro chawo chidzayesedwa.

Anthu a Mulungu adzamudalira kulikonse kumene adzapezeke pa nthawi imene azidzaukiridwa (Onani ndime 13) *

13. (a) Kodi Gogi ndi ndani? (b) Malinga ndi Ezekieli 38:2, 8, 9, kodi n’chiyani chidzafikitse Gogi kumalo otchedwa Aramagedo?

13 Gogi adzatiukira. (Werengani Ezekieli 38:2, 8, 9.) Zipembedzo zonse zonyenga zikadzawonongedwa, anthu a Mulungu adzaoneka ngati mtengo umodzi wokha umene wapulumuka mphepo yamkuntho. N’zosachita kufunsa kuti Satana adzakwiya kwambiri. Iye adzasonyeza mkwiyo wake pogwiritsa ntchito “mauthenga ouziridwa ndi ziwanda,” kapena kuti mabodza a ziwanda, kuti mgwirizano wa mayiko uukire atumiki a Yehova. (Chiv. 16:13, 14) Mgwirizano umenewu umatchedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” Mayiko amenewa akadzangoyamba kuukira anthu a Mulungu adzakhala kuti afika pamalo ophiphiritsira otchedwa Aramagedo.​—Chiv. 16:16.

14. Kodi Gogi adzazindikira chiyani?

14 Gogi adzadalira “mphamvu za anthu” kapena kuti mphamvu za asilikali ake. (2 Mbiri 32:8) Koma ifeyo tidzadalira Yehova Mulungu wathu ndipo anthu enawo adzaganiza kuti ndife opusa. Adzaganiza choncho poona kuti milungu ya Babulo Wamkulu sinamuteteze pamene ankawonongedwa ndi “chilombo” komanso ‘nyanga zake 10.’ (Chiv. 17:16) Choncho Gogi adzaganiza kuti sadzavutika kutigonjetsa. Iye adzaukira anthu a Yehova ngati ‘mitambo yophimba dziko.’ (Ezek. 38:16) Koma Gogi adzazindikira kuti wadziputira tsoka lalikulu. Mofanana ndi Farao pa Nyanja Yofiira, Gogi adzazindikira kuti akulimbana ndi Yehova.​—Eks. 14:1-4; Ezek. 38:3, 4, 18, 21-23.

15. Kodi Khristu adzachita zotani pa nkhondo ya Aramagedo?

15 Khristu limodzi ndi gulu la angelo ake adzateteza anthu a Mulungu n’kuwonongeratu Gogi ndi asilikali ake. (Chiv. 19:11, 14, 15) Koma kodi Satana, yemwe ndi mdani wamkulu wa Yehova komanso amene mabodza ake achititsa mayiko kuti afike pa Aramagedo, zidzamuthera bwanji? Yesu adzatsekera m’phompho Satana ndi ziwanda zake ndipo adzakhala mmenemo kwa zaka 1,000.​—Chiv. 20:1-3.

KODI TINGATANI KUTI TIDZAPULUMUKE PA ARAMAGEDO?

16. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timadziwa Mulungu’? (b) Kodi kudziwa Mulungu kudzatithandiza bwanji pa Aramagedo?

16 Kaya takhala m’choonadi kwa zaka zambiri kapena ayi, kuti tidzapulumuke tifunika kusonyeza kuti ‘timadziwa Mulungu’ komanso ‘timamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.’ (2 Ates. 1:7-9) ‘Kudziwa Mulungu’ kumatanthauza kudziwa zimene zimamusangalatsa, zimene sizimusangalatsa komanso mfundo zake. Timasonyezanso kuti timamudziwa tikamamukonda, kumumvera ndiponso kukhala odzipereka kwa iye yekha. (1 Yoh. 2:3-5; 5:3) Tikamachita zimenezi tidzakhalanso ‘odziwika kwa Mulungu,’ kutanthauza kuti azisangalala nafe. (1 Akor. 8:3) Izi n’zimene zidzapangitse kuti adzatipulumutse pa Aramagedo.

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu’?

17 “Uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu” umatanthauza zinthu zonse zimene iye anaphunzitsa zomwe zimapezeka m’Mawu a Mulungu. Timasonyeza kuti timamvera uthenga wabwino tikamatsatira mfundo zake pa moyo wathu. Timasonyezanso kumvera tikamaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, kutsatira mfundo zachilungamo za Mulungu komanso kuuza ena za Ufumu wa Mulungu. (Mat. 6:33; 24:14) Kuwonjezera pamenepa, timathandiza Akhristu odzozedwa kugwira ntchito yaikulu imene anapatsidwa.​—Mat. 25:31-40.

18. Kodi atumiki a Mulungu odzozedwa adzayamikira bwanji zinthu zabwino zimene achitiridwa?

18 Posachedwapa, atumiki a Mulungu odzozedwa adzasonyeza kuyamikira zinthu zabwino zimene a “nkhosa zina” awachitira. (Yoh. 10:16) Kodi adzachita bwanji zimenezi? Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, odzozedwa onse okwana 144,000 adzakhala atapita kumwamba ndipo adzakhala ndi matupi auzimu osakhoza kufa. Iwo adzakhala m’gulu la asilikali akumwamba amene adzawononge Gogi n’kupulumutsa “khamu lalikulu” la anthu a Mulungu. (Chiv. 2:26, 27; 7:9, 10) Choncho ndi mwayi waukulu kuthandiza atumiki a Yehova odzozedwa pa nthawi imene adakali padziko lapansi.

KODI TINGATANI KUTI TIKHALEBE OKHULUPIRIKA M’MASIKU OTSIRIZAWA?

19-20. Ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, kodi tingatani kuti tikhalebe okhulupirika pamene Aramagedo ikuyandikira?

19 M’masiku otsirizawa anthu a Yehova ambiri akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Koma n’zotheka kupirira n’kumakhalabe osangalala. (Yak. 1:2-4) Kupemphera nthawi zonse kungatithandize kwambiri. (Luka 21:36) Tiyeneranso kuphunzira Mawu a Mulungu tsiku lililonse komanso kusinkhasinkha Mawuwo, kuphatikizapo maulosi ake omwe akukwaniritsidwa masiku ano. (Sal. 77:12) Tikamachita zimenezi komanso kulalikira mwakhama tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso chiyembekezo champhamvu.

20 Kunena zoona, tidzasangalala kwambiri Babulo Wamkulu akadzawonongedwa komanso nkhondo ya Aramagedo ikadzatha. Koma chimene chidzatisangalatse kwambiri n’chakuti aliyense azidzalemekeza dzina la Yehova komanso ulamuliro wake. (Ezek. 38:23) Apa tinganenedi kuti uthenga wokhudza Aramagedo ndi wosangalatsa kwa anthu amene amadziwa Mulungu, kumvera Mwana wake komanso amene adzapirire mpaka mapeto.​—Mat. 24:13.

NYIMBO NA. 143 Pitirizani Kugwira Ntchito, Kukhala Maso ndi Kudikira

^ ndime 5 Anthu a Yehova akhala akuyembekezera Aramagedo kwa nthawi yaitali. Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi Aramagedo n’chiyani? Kodi n’chiyani chidzachitike Aramagedo itatsala pang’ono kuyamba? Nanga tingatani kuti tikhalebe okhulupirika m’masiku otsirizawa?

^ ndime 71 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pamene zinthu zodabwitsa zizidzachitika, ifeyo (1) tidzayesetsa kulalikira ngati n’zotheka, (2) tidzapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu komanso (3) tidzapitiriza kudalira Yehova kuti atiteteze.

^ ndime 85 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Apolisi akufuna kulowa m’nyumba ya banja lina lachikhristu limene silikukayikira kuti Yesu ndi angelo ake akuona zimene zikuchitika.