Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 38

Achinyamata, Kodi Mudzachita Chiyani pa Moyo Wanu?

Achinyamata, Kodi Mudzachita Chiyani pa Moyo Wanu?

“Kuzindikira kudzakuteteza.”—MIY. 2:11.

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi Yehoasi, Uziya ndi Yosiya anakumana ndi mavuto otani?

 KODI mungamve bwanji mutaikidwa kukhala mfumu ya anthu a Mulungu muli mwana kapenanso musanakwanitse n’komwe zaka 20? Kodi mungagwiritse ntchito bwanji udindo wanu? Baibulo limatifotokozera za achinyamata angapo amene anakhala mafumu a Yuda. Mwachitsanzo Yehoasi anakhala mfumu ali ndi zaka 7 zokha, Uziya ali ndi zaka 16 komanso Yosiya ali ndi zaka 8. Zimenezi ziyenera kuti zinali zovuta. Ngakhale zinali choncho, Yehova ndi anthu ena anawathandiza kuti athe kulimbana ndi mavuto komanso azichita zabwino.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira zitsanzo za Yehoasi, Uziya ndi Yosiya?

2 N’zoona kuti ifeyo si mafumu komabe tikhoza kuphunzira zinthu zofunika kwambiri kwa anthu atatuwa. Iwo ankasankha zinthu mwanzeru koma pa nthawi ina analakwitsa zinthu. Zitsanzo zawo zitithandiza kuona kufunika kosankha bwino anzathu, kukhalabe odzichepetsa komanso kupitiriza kudalira Yehova.

MUZISANKHA ANZANU MWANZERU

Masiku anonso n’zotheka kutengera chitsanzo cha Yehoasi mukamamvetsera malangizo ochokera kwa anzanu abwino (Onani ndime 3, 7) c

3. Kodi Yehoyada anathandiza bwanji Mfumu Yehoasi kuti asankhe zinthu mwanzeru?

3 Muzitsanzira Yehoasi yemwe anasankha zinthu mwanzeru. Ali mwana, Mfumu Yehoasi anasankha zinthu mwanzeru. Iye analibe bambo ndipo anatsatira malangizo a Mkulu wa Ansembe Yehoyada amene anali wokhulupirika. Mkulu wa ansembeyo ankalangiza Yehoasi ngati mwana wake. Potengera chitsanzo cha Yehoyada, Yehoasi anasankha kuti azitumikira Yehova komanso kuthandiza anthu ena kuti azimutumikira. Yehoasi anakonzanso zoti kachisi wa Yehova akonzedwe.—2 Mbiri 24:​1, 2, 4, 13, 14.

4. Kodi timapindula bwanji tikamakonda malamulo a Yehova ndiponso kuwatsatira? (Miyambo 2:​1, 10-12)

4 Ngati mukuphunzitsidwa kuti muzikonda Yehova komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wanu, dziwani kuti mukupatsidwa mphatso yapadera. (Werengani Miyambo 2:​1, 10-12.) Makolo akhoza kuphunzitsa ana awo m’njira zambiri. Taganizirani mmene bambo ake a mlongo wina dzina lake Katya anamuthandizira kuti azisankha zinthu mwanzeru. Tsiku lililonse bambo akewo akamamuperekeza kusukulu, ankakambirana naye lemba la tsiku. Iye anati, “Zimenezi zinkandithandiza kuti ndizichita zoyenera ndikakumana ndi mavuto.” Koma bwanji ngati mfundo za m’Baibulo zimene makolo anu akukuuzani zikuoneka ngati zikukupherani ufulu? N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzimvera malangizo awo? Mlongo wina dzina lake Anastasia amakumbukira kuti makolo ake ankamufotokozera chifukwa chake anakhazikitsa malamulo ena ake. Iye anati, “Zimenezi zinandithandiza kuona kuti iwo ankandiletsa kuchita zinthu zina pofuna kunditeteza osati pofuna kundipanikiza.”

5. Kodi zochita zanu zimakhudza bwanji makolo anu komanso Yehova? (Miyambo 22:6; 23:​15, 24, 25)

5 Makolo anu adzasangalala ngati mutamatsatira malangizo a m’Malemba amene amakupatsani. Chofunika kwambiri n’chakuti mudzasangalatsa Mulungu ndipo mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba. (Werengani Miyambo 22:6; 23:​15, 24, 25.) Zimenezitu ndi zifukwa zabwino zokuchititsani kutsanzira zimene Yehoasi anachita ali mwana.

6. Kodi Yehoasi anayamba kutsatira malangizo a ndani, nanga zotsatira zake zinali zotani? (2 Mbiri 24:​17, 18)

6 Muziphunzirapo kanthu pa zimene Yehoasi analakwitsa. Yehoyada atamwalira, Yehoasi ankagwirizana ndi anthu olakwika. (Werengani 2 Mbiri 24:​17, 18.) Iye anayamba kumvera akalonga a Yuda omwe sankakonda Yehova. Kodi mukuona kuti iye anachita bwino kugwirizana ndi anthu osokonezawa? (Miy. 1:10) Komatu iye ankawaona ngati anzake ndipo ankawamvera. Komanso msuweni wake Zekariya atayesa kumulangiza, Yehoasi analamula kuti aphedwe. (2 Mbiri 24:​20, 21; Mat. 23:35) Kumenekutu kunali kuipa mtima komanso kupusa kwambiri. Poyamba Yehoasi anali munthu wabwino koma n’zomvetsa chisoni kuti anasintha n’kukhala wampatuko komanso wakupha. Pamapeto pake atumiki ake anamupha. (2 Mbiri 24:​22-25) Zinthu zikanamuyendera bwino ngati akanapitiriza kumvera Yehova komanso anthu amene ankamukonda. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chake?

7. Kodi ndi anthu ati amene muyenera kusankha kuti akhale anzanu? (Onaninso chithunzi.)

7 Nkhani ya Yehoasi ikutiphunzitsa kuti tizisankha anzathu omwe angatithandize kuti tizichita zabwino. Tizisankha anthu omwe amakonda Yehova komanso amafuna kumusangalatsa. Tisamangocheza ndi anthu amsinkhu wathu okha. Kumbukirani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi mnzake Yehoyada. Mukamasankha anzanu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iwo amandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Kodi amandilimbikitsa kuti ndizitsatira mfundo zake? Kodi amakonda kulankhula za Yehova komanso choonadi chake chamtengo wapatali? Kodi amalemekeza mfundo za Mulungu? Kodi iwo amangondiuza zinthu kuti andisangalatse kapena amalimba mtima n’kundiuza zimene ndikulakwitsa?’ (Miy. 27:​5, 6, 17) Kunena zoona anthu amene sakonda Yehova sayenera kukhala anzanu. Koma ngati muli ndi anzanu omwe amakonda Yehova, pitirizani kucheza nawo chifukwa azikuthandizani.—Miy. 13:20.

8. Ngati timagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi tiyenera kuganizira zinthu ziti?

8 Malo ochezera a pa intaneti angakhale njira yabwino yolumikizirana ndi achibale komanso anzanu. Komabe anthu ambiri amagwiritsa ntchito malo amenewo pofuna kugometsa anzawo. Amaika zithunzi ndi mavidiyo a zimene agula kapena zimene achita. Ngati mumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti dzifunseni kuti: ‘Kodi cholinga changa ndi kugometsa anthu ena? Kodi ndikufuna kulimbikitsa ena kapena kuoneka wapamwamba? Kodi ndimalola kuti anthu omwe amagwiritsa ntchito malowa asokoneze maganizo anga, zolankhula komanso zochita zanga?’ M’bale Nathan Knorr, yemwe anatumikirapo m’Bungwe Lolamulira, anapereka malangizo awa: “Musamayese kusangalatsa anthu. Mukamatero mudzapeza kuti simunasangalatse aliyense. Muzisangalatsa Yehova ndipo mudzasangalatsanso anthu onse amene amakonda Yehova.”

TIYENERA KUKHALA ODZICHEPETSA

9. Kodi Yehova anathandiza Uziya kuchita zinthu ziti? (2 Mbiri 26:​1-5)

9 Muzitsanzira Uziya yemwe anasankha zinthu mwanzeru. Mfumu Uziya ali wachinyamata anali wodzichepetsa. Iye anaphunzira ‘kuopa Mulungu woona.’ Iye anakhala ndi moyo kwa zaka 68 ndipo Yehova anamudalitsa pa zaka zambiri za moyo wake. (Werengani 2 Mbiri 26:​1-5.) Uziya anagonjetsa adani ambiri a Aisiraeli ndipo ankaonetsetsa kuti mzinda wa Yerusalemu ndi wotetezeka. (2 Mbiri 26:​6-15) N’zosachita kufunsa kuti Uziya ankasangalala ndi zonse zimene Mulungu anamuthandiza kuchita.—Mlal. 3:​12, 13.

10. Kodi zinthu zinamuyendera bwanji Uziya?

10 Muziphunzirapo kanthu pa zimene Uziya analakwitsa. Uziya anali atazolowera kuuza ena zochita. Kodi mwina zimenezi ndi zimene zinamuchititsa kuti aziganiza kuti angathe kuchita chilichonse chomwe ankafuna? Tsiku lina Uziya anachita zinthu modzikuza. Iye analowa m’kachisi wa Yehova n’kuyamba kupereka nsembe zofukiza paguwa, zimene mafumu sankaloledwa kuchita. (2 Mbiri 26:​16-18) Mkulu wa Ansembe Azariya anayesa kumuletsa koma iye anakwiya kwambiri. N’zomvetsa chisoni kuti Uziya anawononga mbiri yake yokhala wokhulupirika ndipo Yehova anamulanga pomuchititsa khate. (2 Mbiri 26:​19-21) Zinthutu zikanamuyendera bwino akanakhalabe wodzichepetsa.

M’malo modzitama chifukwa cha zimene tachita, tiyenera kulola kuti ulemerero wonse upite kwa Yehova (Onani ndime 11) d

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze kuti ndife odzichepetsa? (Onaninso chithunzi.)

11 Uziya atakhala wamphamvu anaiwala kuti Yehova ndi amene anamupatsa mphamvuzo komanso kumuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tizikumbukira kuti Yehova ndi amene amatipatsa zabwino zonse zimene timasangalala nazo pa moyo wathu komanso pomutumikira. M’malo modzitama chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita, tizipereka ulemerero wonse kwa Yehova. b (1 Akor. 4:7) Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumazindikira kuti si ife angwiro ndipo timafunika kulangizidwa. M’bale wina yemwe ali ndi zaka za m’ma 60 analemba kuti: “Ndaphunzira kuti ndisamakhumudwe kapena kukwiya msanga ena akandiuza kuti ndalakwitsa penapake. Ena akandipatsa malangizo chifukwa chakuti ndachita zinthu mosaganiza bwino, ndimayesetsa kusintha n’kumachita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova.” Zoona n’zakuti tikamaopa Yehova n’kumapitirizabe kukhala odzichepetsa, zinthu zimatiyendera bwino pa moyo wathu.—Miy. 22:4.

PITIRIZANI KUFUNAFUNA YEHOVA

12. Kodi Yosiya ali wachinyamata anafunafuna bwanji Yehova? (2 Mbiri 34:​1-3)

12 Muzitsanzira Yosiya yemwe anasankha zochita mwanzeru. Yosiya anayamba kufunafuna Yehova ali wachinyamata. Ankafuna kuphunzira za Yehova n’kumachita chifuniro chake. Komabe zinthu sizinali zophweka kwa mfumu yachinyamatayi. Iye ankafunika kusankha kukhala kumbali ya kulambira koona pa nthawi imene anthu ambiri ankalambira milungu yabodza. Ndipo iye anachitadi zimenezo. Asanakwanitse zaka 20, Yosiya anayamba kuthetsa kulambira kwabodza.—Werengani 2 Mbiri 34:​1-3.

13. Kodi muyenera kuchita chiyani mukadzipereka kwa Yehova?

13 Ngakhale kuti ndinu wamng’ono mungathe kusankha kuti muzitsanzira Yosiya pofunafuna Yehova komanso kuphunzira makhalidwe ake. Kuchita zimenezi kudzakulimbikitsani kuti mudzipereke kwa iye. Kodi kudzipereka kumeneko kudzakhudza bwanji moyo wanu? Luke yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 14 ananena kuti, “Kuyambira tsopano, ndiziika kutumikira Yehova pamalo oyamba ndipo ndiziyesetsa kuti ndizimusangalatsa.” (Maliko 12:30) Ngati inunso mutachita zimenezi Yehova adzakudalitsani.

14. Perekani zitsanzo zosonyeza zimene achinyamata ena akuchita potsanzira Mfumu Yosiya.

14 Kodi ndi mavuto ati omwe mungakumane nawo mukamatumikira Yehova muli wachinyamata? Johan yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 12, anafotokoza mmene anzake a m’kalasi ankamukakamizira kugwiritsa ntchito shisha kapena kuti kuvepa. Kuti alimbe mtima n’kukana, Johan amadzikumbutsa kuti kuvepa kukhoza kuwononga moyo wake komanso kusokoneza ubwenzi wake ndi Yehova. Rachel yemwe anabatizidwa ali ndi zaka 14, anafotokoza chimene chimamuthandiza kupirira mavuto omwe amakumana nawo kusukulu. Iye anati: “Zinazake zikachitika, ndimayesetsa kuganizira zinthu zokhudza Baibulo komanso Yehova. Mwachitsanzo, tikamaphunzira mbiri yakale ndimakumbukira nkhani ya m’Baibulo kapena ulosi winawake. Kapenanso ndikamacheza ndi winawake, ndimayesa kukumbukira lemba lomwe ndingamuwerengere.” Mungakumane ndi mavuto osiyana ndi amene Mfumu Yosiya inakumana nawo komabe mungathe kuchita zinthu mwanzeru komanso kukhalabe wokhulupirika ngati mmene iye anachitira. Kulimbana ndi mavuto muli wachinyamata, kungakuthandizeni kudzalimbana ndi mavuto omwe mungakumane nawo m’tsogolo.

15. N’chiyani chinathandiza Yosiya kuti azitumikira Yehova mokhulupirika? (2 Mbiri 34:​14, 18-21)

15 Atakula, Mfumu Yosiya anayamba kukonzanso kachisi. Pogwira ntchitoyi “anapeza buku la Chilamulo cha Yehova loperekedwa ndi dzanja la Mose.” Mfumuyi itamva zimene zinawerengedwa, nthawi yomweyo inasintha kuti itsatire malangizo a m’bukuli. (Werengani 2 Mbiri 34:​14, 18-21.) Kodi mumafuna kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse? Ngati mukuyesa kale kuchita zimenezi kodi zinthu zikukuyenderani bwanji? Kodi mumasunga mavesi ena ake omwe mukuona kuti angakuthandizeni? Luke yemwe tamutchula kale uja amalemba m’buku lake mfundo zosangalatsa zomwe wapeza. Kodi kuchita zofanana ndi zimenezi kungakuthandizeninso inuyo kuti muzikumbukira mavesi kapena mfundo zimene zakusangalatsani? Mukamaphunzira komanso kukonda kwambiri Baibulo, m’pamenenso mumafuna kwambiri kutumikira Yehova. Ndipo mofanana ndi Mfumu Yosiya, inunso Mawu a Mulungu adzakuthandizani kuchita zoyenera.

16. N’chifukwa chiyani Yosiya analakwitsa zinthu kwambiri, nanga tikuphunzirapo chiyani?

16 Muziphunzirapo kanthu pa zimene Yosiya analakwitsa. Yosiya ali ndi zaka pafupifupi 39, analakwitsa zinthu ndipo zinachititsa kuti aphedwe. Iye anadzidalira m’malo mopempha malangizo kwa Yehova. (2 Mbiri 35:​20-25) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kaya ndife wamkulu kapena wamng’ono kapenanso takhala tikuphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kufunafuna Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kupempha Yehova nthawi zonse kuti atipatse malangizo, kuphunzira Mawu ake komanso kumvera malangizo a Akhristu olimba mwauzimu. Tikamachita zimenezi tidzapewa kulakwitsa kwambiri zinthu ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25.

ACHINYAMATA ZINTHU ZIKHOZA KUKUYENDERANI BWINO

17. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani za mafumu atatu a Yuda?

17 Pali zinthu zosangalatsa zambiri zimene mungachite muli achinyamata. Nkhani ya Yehoasi, Uziya komanso Yosiya ikusonyeza kuti achinyamata angathe kusankha zinthu mwanzeru komanso kusangalatsa Yehova pa moyo wawo. N’zoona kuti zitsanzo zawo zikusonyeza kuti si nthawi zonse pamene zinthu zimayenda bwino. Komabe tingathe kutsanzira zinthu zabwino zimene mafumuwa anachita n’kumapewa zimene analakwitsa. Tikatero zinthu zikhoza kutiyendera bwino.

Davide anakhala pa ubwenzi ndi Yehova kuyambira ali wamng’ono. Yehova ankasangalala naye ndipo zinthu zinamuyendera bwino pa moyo wake (Onani ndime 18)

18. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Malemba zomwe zikusonyeza kuti zinthu zingakuyendereni bwino? (Onaninso chithunzi.)

18 M’Baibulo muli nkhani za achinyamata enanso omwe anakhala pa ubwenzi ndi Yehova. Iye ankawakonda ndipo zinthu zinawayendera bwino pa moyo wawo. Davide anali mmodzi wa achinyamatawa. Iye anasankha kutumikira Mulungu ali wachinyamata ndipo kenako anadzakhala mfumu yokhulupirika. N’zoona kuti Davide ankalakwitsa zinthu zina koma Mulungu ankamuona kuti ndi wokhulupirika. (1 Maf. 3:6; 9:​4, 5; 14:8) Mukamaphunzira za Davide, chitsanzo chake chikhoza kukulimbikitsani kuti muzitumikira Yehova mokhulupirika. Mukhozanso kukonza zoti muphunzire zambiri zokhudza Maliko kapena Timoteyo. Mudzaona kuti iwo anayamba kutumikira Yehova ali achinyamata ndipo anapitiriza kumusangalatsa komanso zinthu zinawayendera bwino pa moyo wawo.

19. Kuti zinthu zikuyendereni bwino pa moyo kodi zikudalira chiyani?

19 Zimene mukuchita panopa ndi zomwe zingachititse kuti zinthu zidzakuyendereni bwino kapena ayi. Mukamakhulupirira Yehova osati kudalira luso lanu lomvetsa zinthu, iye adzakuthandizani kuti muzisankha zinthu mwanzeru. (Miy. 20:24) Mukatero, mudzakhala wosangalala ndipo moyo wanu udzakhala wabwino. Kumbukirani kuti Yehova amayamikira zonse zimene mumachita pomutumikira. Palibenso njira ina yabwino yogwiritsira ntchito moyo wanu imene ingapose kutumikira Atate wathu wachikondi Yehova.

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

a Achinyamata, Yehova amadziwa kuti mumakumana ndi mavuto amene angachititse kuti musakhale naye pa ubwenzi. Kodi mungatani kuti muzisankha mwanzeru zinthu zomwe zingasangalatse Atate wanu wakumwamba? Munkhaniyi tikambirana zitsanzo za anyamata atatu amene anadzakhala mafumu a Yuda. Tiyeni tione zimene mungaphunzire pa zimene iwo anasankha.

b Onani bokosi lakuti “Musamanamizire kuti Ndinu Wodzichepetsa” munkhani yakuti “Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?” pa jw.org

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wolimba mwauzimu akupereka malangizo anzeru kwa mlongo wachitsikana.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo yemwe ali ndi mbali pamsonkhano akudalira Yehova ndipo akupereka ulemerero wonse kwa iye.