Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 39

Kufatsa Sikutanthauza Kufooka

Kufatsa Sikutanthauza Kufooka

“Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.”—2 TIM. 2:24.

NYIMBO NA. 120 Tikhale Ofatsa Ngati Khristu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi tingathe kufunsidwa chiyani tikakhala kuntchito kapena kusukulu?

 KODI mumamva bwanji mnzanu wakuntchito kapena kusukulu akakufunsani zimene mumakhulupirira? Kodi mumachita mantha? Ambirife timachita mantha. Komatu funso limene angatifunse lingatithandize kudziwa zimene amaganiza kapena kukhulupirira ndipo zingatipatse mpata woti timuuze uthenga wabwino. Komabe nthawi zina munthu angatifunse funso n’cholinga choti tikangane. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa ena anamva zolakwika zokhudza zimene timakhulupirira. (Mac. 28:22) Kuwonjezera pamenepo, tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ ndipo anthu ambiri ‘safuna kugwirizana ndi anzawo’ komanso ndi “oopsa.”—2 Tim. 3:​1, 3.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ofatsa?

2 Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingakhale bwanji wodekha komanso wokoma mtima pamene munthu wina akufuna kukangana nane pa zimene ndimakhulupirira?’ Kukhala wofatsa n’kumene kungakuthandizeni. Munthu wofatsa samakwiya msanga koma amadziletsa ena akamuputa ndiponso akakhala kuti sakudziwa zoti ayankhe. (Miy. 16:32) Koma mwina munganene kuti zimenezi sizophweka. Ndiye mungatani kuti mukhale ofatsa? Kodi mungayankhe bwanji mofatsa munthu wina akamafuna kukangana nanu pa zimene mumakhulupirira? Ngati ndinu kholo, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azifotokozera ena zimene amakhulupirira, koma mofatsa? Tiyeni tione.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKHALE OFATSA

3. N’chifukwa chiyani tingati kukhala ofatsa sikutanthauza kufooka? (2 Timoteyo 2:​24, 25)

3 Munthu akakhala wofatsa sizitanthauza kuti ndi wofooka. Pamafunika kukhala wamphamvu kuti ukhale wodekha ukakumana ndi vuto linalake. Kufatsa ndi limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:​22, 23) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kufatsa” nthawi zina ankawagwiritsa ntchito pofotokoza za hatchi yam’tchire yomwe ikuwetedwa. Taganizirani za hatchi yam’tchire yomwe yaphunzitsidwa kukhala yodekha. Hatchiyo ingakhale yodekha, koma imakhalabe yamphamvu. Ndiye kodi anthufe tingakhale bwanji ofatsa, pa nthawi imodzimodziyo n’kukhalanso amphamvu? Sitingathe kuchita zimenezi patokha. Chomwe chingatithandize ndi kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake womwe ungatithandize kuti tikhale ndi khalidwe labwinoli. Pali umboni wosonyeza kuti zimenezi ndi zotheka. Abale ndi alongo ambiri amayankha mofatsa anthu otsutsa ndipo izi zimathandiza kuti anthu akhale ndi maganizo oyenera okhudza a Mboni za Yehova. (Werengani 2 Timoteyo 2:​24, 25.) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife amphamvu pokhala ofatsa?

4. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Isaki pa nkhani yokhala ofatsa?

4 M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kufunika kokhala ofatsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Isaki. Iye atakakhala m’dera la Afilisiti la Gerari, anthu ansanje a kumeneko anakwirira zitsime zimene antchito a bambo ake anakumba. M’malo momenyana nawo kuti alanditse zitsimezo, Isaki ndi banja lake anangosamukira kutali ndipo anakumba zitsime zina. (Gen. 26:​12-18) Koma Afilisiti anapitiriza kunena kuti madzi a m’deralo analinso awo. Ngakhale zinali choncho, Isaki anapitiriza kuchita zinthu mwamtendere. (Gen. 26:​19-25) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupitirizabe kukhala wofatsa ngakhale kuti ena ankafuna kumakangana naye? Ayenera kuti ankatengera chitsanzo cha makolo ake ndipo anaphunzira mmene Abulahamu ankachitira zinthu mwamtendere komanso ankaona “mzimu wabata ndi wofatsa” wa Sara.—1 Pet. 3:​4-6; Gen. 21:​22-34.

5. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza kuti makolo angaphunzitse ana awo kufunika kokhala ofatsa?

5 Makolo a Chikhristu, dziwani kuti mungaphunzitse ana anu kufunika kokhala ofatsa. Taganizirani chitsanzo cha Maxence, yemwe ali ndi zaka 17. Iye ankakumana ndi anthu okwiya kusukulu komanso mu utumiki. Makolo ake anamuthandiza moleza mtima kuti akhale wofatsa. Iwo anati: “Maxence waphunzira kuti pamafunika mphamvu zambiri kuti adziletse kusiyana ndi kuyankha mokwiya kapena kuchita chiwawa.” N’zosangalatsa kuti panopa Maxence amasonyeza mphamvu pokhala wofatsa.

6. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tipitirize kukhala ofatsa?

6 Kodi tingatani ngati ena atikhumudwitsa, mwachitsanzo ngati anena zoipa zokhudza Mulungu wathu kapena kunyoza Baibulo? Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake komanso nzeru kuti tichite zinthu mofatsa. Bwanji ngati pambuyo pake tazindikira kuti sitinayankhe bwino? Tiyenera kuipemphereranso nkhaniyo komanso kuganizira zimene tingadzachite kuti tiyankhe bwino nthawi ina. Tikatero, Yehova adzatipatsa mzimu wake womwe ungatithandize kuugwira mtima komanso kukhala ofatsa.

7. Kodi kuloweza mavesi enaake kungatithandize bwanji kuti tizidziletsa polankhula ndiponso pochita zinthu? (Miyambo 15:​1, 18)

7 Mavesi ena a m’Baibulo angatithandize kuti tilankhule modekha pa nthawi imene zili zovuta kuti tichite zinthu mofatsa. Mzimu wa Mulungu ungatithandize kukumbukira mavesi amenewo. (Yoh. 14:26) Mwachitsanzo, mfundo zimene timapeza m’buku la Miyambo zingatithandize kukhala ofatsa. (Werengani Miyambo 15:​1, 18.) Buku la m’Baibuloli limasonyezanso ubwino wodziletsa ngakhale pa nthawi imene n’zovuta kuchita zimenezo.—Miy. 10:19; 17:27; 21:23; 25:15.

KUZINDIKIRA KUNGATITHANDIZE KUKHALA OFATSA

8. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuganizira zomwe zachititsa munthu kutsutsa zimene timakhulupirira?

8 Kuzindikira n’kothandizanso kwambiri. (Miy. 19:11) Munthu wozindikira amadziletsa ena akamatsutsa zimene amakhulupirira. Mafunso ena tingawayerekezere ndi kholowa. Mbatata yeniyeniyo siioneka chifukwa imakhala munthaka. Mofanana ndi zimenezi, munthu angafunse funso kapena angafotokoze nkhawa inayake koma sitingazindikire cholinga chake. Choncho tisanayankhe tingachite bwino kuzindikira kuti nthawi zina sitingadziwe chimene chachititsa munthu kufunsa funsolo.—Miy. 16:23.

9. Kodi Gidiyoni anasonyeza bwanji kuzindikira komanso kufatsa pamene ankayankha amuna a ku Efuraimu?

9 Taganizirani mmene Gidiyoni anayankhira amuna a ku Efuraimu. Iwo anabwera kudzamufunsa mokwiya chifukwa chake sanawaitane kuti akawathandize pankhondo yolimbana ndi adani a Isiraeli. Kodi n’chifukwa chiyani iwo ankafuna kukangana naye? Kodi anachita zimenezi chifukwa chokwiya? Kaya iwo anachita zimenezi pa chifukwa chiti, Gidiyoni anachita zinthu mwanzeru, anamvetsa chifukwa chomwe chinawachititsa kuti akwiye ndiponso anawayankha mofatsa. Zotsatira zake n’zakuti iwo sanamenyane naye ndipo “mkwiyo wawo unaphwa.”—Ower. 8:​1-3.

10. Kodi n’chiyani chingatithandize kudziwa mmene tingayankhire anthu amene amafuna kudziwa zimene timakhulupirira? (1 Petulo 3:15)

10 Mwina mnzathu wakuntchito kapena kusukulu angatifunse chifukwa chake timatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani inayake. Tingachite bwino kumufotokozera zimene timakhulupirira koma m’njira yosonyeza kuti tikulemekeza maganizo ake. (Werengani 1 Petulo 3:15.) M’malo moganiza kuti watifunsa n’cholinga choti akangane nafe kapena kutitsutsa, tiziona kuti funso lakelo litithandiza kudziwa zimene zikumudetsa nkhawa. Kaya munthu wafunsa funso pa zifukwa ziti, tiyenera kumuyankha mofatsa komanso mokoma mtima. Yankho lathu likhoza kumuthandiza kuti asinthe maganizo ake. Ngakhale atafunsa mwachipongwe kapena monyoza, nthawi zonse tiziyankha mokoma mtima.—Aroma 12:17.

Tingayankhe bwino ngati choyamba titadziwa chifukwa chake wina watiitana kuti tikasangalale nawo paphwando lokumbukira tsiku lobadwa (Onani ndime 11-12)

11-12. (a) Kodi tiyenera kuganizira chiyani tisanayankhe funso linalake lovuta? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza mmene funso la munthu lingathandizire kuti tiyambe kukambirana naye. (Onaninso chithunzi.)

11 Ngati mnzathu wakuntchito watifunsa chifukwa chake sitikondwerera tsiku lobadwa, tingadzifunse kuti: Kodi n’kutheka kuti iye akufuna kudziwa ngati timaloledwa kukhala ndi nthawi yosangalala? Kapena akuona kuti tichititsa kuti anthu asamagwirizane pakampanipo? Tingayambe ndi kumuyamikira chifukwa choganizira anzake ogwira nawo ntchito ndipo kenako tingamutsimikizire kuti ifenso tikakhala kuntchito timafuna kuti tizisangalala. Izi zingachititse kuti mukambirane bwino zimene Baibulo limanena pa nkhani yokondwerera tsiku lobadwa.

12 Tikhozanso kugwiritsa ntchito njira imeneyi anthu akatifunsa mafunso ena ovuta. Mnzanu wakusukulu anganene kuti a Mboni za Yehova ayenera kusintha maganizo awo pa nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Kodi akunena zimenezo chifukwa chakuti anamva zolakwika zokhudza a Mboni? Kodi mwina ali ndi mnzake kapena wachibale yemwe amachita zimenezi? Kapenanso akuganiza kuti timadana ndi anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha? Tiyenera kumutsimikizira kuti timakonda anthu onse komanso timadziwa kuti aliyense ali ndi ufulu, ndipo timalemekeza zimene ena asankha. b (1 Pet. 2:17) Kenako tingakambirane naye mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira ifeyo kukhala osangalala.

13. Kodi mungathandize bwanji munthu yemwe amaganiza kuti si nzeru kukhulupirira kuti kuli Mulungu?

13 Mukakumana ndi munthu yemwe akukutsutsani kwambiri musamafulumire kuganiza kuti mukudziwa zimene amakhulupirira. (Tito 3:2) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mnzanu wakusukulu wakuuzani kuti si nzeru kukhulupirira kuti kuli Mulungu. Kodi muyenera kuganiza kuti iye amakhulupirira kwambiri kuti zamoyo zinachita kusintha komanso kuti akudziwa zambiri pa nkhaniyo? Mwina zenizeni zingakhale zakuti iye anangomva kwa anthu ena ndipo sanafufuzepo. M’malo mokangana naye pa nkhaniyo, mukhoza kupeza njira yomufotokozera zinthu zina zoti akaziganizire. Mungamusonyeze nkhani zokhudza chilengedwe pa jw.org. Pambuyo pake mwina angakonde kuti mukambirane nkhani inayake kapenanso vidiyo yopezeka pawebusaitiyi. Kukambirana naye mwaulemu kungachititse kuti asinthe maganizo ake.

14. Kodi Naill anagwiritsa ntchito bwanji webusaiti yathu pothandiza mnzake yemwe anamva zolakwika zokhudza a Mboni?

14 Wachinyamata wina dzina lake Naill anagwiritsa ntchito webusaiti yathu poyankha mnzake yemwe anali ndi maganizo olakwika okhudza a Mboni. Iye anati: “Mnzanga wina wam’kalasi ankakonda kundiuza kuti sindikhulupirira sayansi chifukwa ndimakhulupirira Baibulo, lomwe lili ndi nkhani zongopeka.” Popeza kuti mnzakeyo sanamulole kufotokoza zimene amakhulupirira, Naill anamuonetsa gawo la pa jw.org lakuti “Sayansi Komanso Baibulo.” Kenako Naill anazindikira kuti mnzakeyo anawerenga nkhanizi ndipo ankafunitsitsa kuti akambirane zambiri zokhudza mmene moyo unayambira. Njira imeneyi ingakuthandizeninso inuyo.

MUZIKONZEKERA MONGA BANJA

15. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti aziyankha mofatsa anzawo a kusukulu akamatsutsa zimene amakhulupirira?

15 Makolo angaphunzitse ana awo mmene angayankhire mofatsa ena akamatsutsa zimene amakhulupirira. (Yak. 3:13) Makolo ena amayeserera zimenezi pa nthawi ya kulambira kwa pabanja. Amaganizira nkhani zimene anawo akhoza kukumana nazo kusukulu. Kenako amakambirana nawo ndi kuwasonyeza mmene angayankhire, n’kuwaphunzitsa mmene angachitire zimenezo mofatsa ndiponso m’njira yabwino kwambiri.—Onani bokosi lakuti “ Kuyeserera Kungathandize Banja Lanu.”

16-17. Kodi kuyeserera pa kulambira kwa pabanja kungathandize bwanji achinyamata?

16 Kukonzekera kungathandize Akhristu kudziwa mmene angafotokozere mogwira mtima zimene amakhulupirira. Kungathandizenso achinyamata kutsimikizira kuti ali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira mfundo za m’Baibulo. Pa jw.org pa gawo lakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,” pali zoti achinyamata achite. Zimenezi zinakonzedwa kuti zizithandiza achinyamata kulimbitsa chikhulupiriro chawo komanso kuwakonzekeretsa kuti azitha kuyankha m’mawu awoawo ena akamawafunsa. Kuphunzira nkhani zimenezi monga banja kungatithandize tonsefe kuti tizitha kufotokoza zimene timakhulupirira mofatsa komanso m’njira yabwino kwambiri.

17 Wachinyamata wina dzina lake Matthew anafotokoza mmene kuyeserera pa kulambira kwa pabanja kunamuthandizira. Iye ndi makolo ake amafufuziratu nkhani zimene anthu akhoza kuyamba kukambirana m’kalasi. Matthew anati: “Timaganizira mafunso amene angabwere ndipo kenako timayeserera mmene tingawayankhire pogwiritsa ntchito mfundo zomwe tafufuza. Ndikamvetsa zimene timakhulupirira pa nkhani inayake, sindimachita mantha ndipo ndimaona kuti sizindivuta kukhala wofatsa ndikamachita zinthu ndi ena.”

18. Kodi lemba la Akolose 4:6 likusonyeza kufunika kwa chiyani?

18 N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kupereka zifukwa zomveka, kungachititse kuti ena avomereze zimene tikuwauza. (Werengani Akolose 4:6.) Koma kufotokoza mwaluso ndiponso mofatsa kungathandize. Kufotokozera ena zimene timakhulupirira tingakuyerekezere ndi kuponyerana mpira. Tikhoza kuponyera munthu wina mpira pang’onopang’ono kapena mwamphamvu. Tikauponya mwapang’onopang’ono, mnzathu angathe kuwakha mosavuta ndipo tikhoza kupitiriza kusewera. Mofanana ndi zimenezi, tikamafotokoza zimene timakhulupirira mwaluso komanso mofatsa, anthu angafune kumvetsera ndipo tingapitirize kukambirana nawo. N’zoona kuti munthu akafuna kuti tizitsutsana kapena kunyoza zimene timakhulupirira sitiyenera kupitiriza kukambirana naye. (Miy. 26:4) Komabe si onse amene amachita zimenezi, ambiri angamvetsere.

19. Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuti tizikhala ofatsa tikamafotokoza zimene timakhulupirira?

19 Kunena zoona, timapindula kwambiri tikamayesetsa kuti tikhale ofatsa. Muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu zimene zimafunikira kuti mupitirize kukhala ofatsa mukamayankha mafunso ovuta kapena ena akamakutsutsani. Kumbukirani kuti kukhala ofatsa kungathandize kuti kusiyana maganizo pa nkhani inayake kusafike mpaka pokhala mkangano waukulu. Ndipo kuyankha mofatsa komanso mwaulemu kungachititse kuti anthu asinthe mmene amationera ndiponso mmene amaonera mfundo za m’Baibulo. Tiyeni ‘tizikhala okonzeka nthawi zonse’ kuyankha aliyense amene akufuna kudziwa zomwe timakhulupirira, ndipo tizichita zimenezo “ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.” (1 Pet. 3:15) Pajatu kufatsa sikutanthauza kufooka.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

a Nkhaniyi itithandiza kudziwa mmene tingayankhire mofatsa ena akamatsutsa zimene timakhulupirira.

b Mungapeze mfundo zina zothandiza munkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limalola Kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?” mu Galamukani! Na. 4, 2016.

c Mungapeze mfundo zina zothandiza pa jw.org munkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa” komanso “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri.”