Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zothandiza Pofufuza

Mfundo Zothandiza Pofufuza

Zoti Ana Achite

Makolo ali ndi udindo waukulu wophunzitsa ana zokhudza Yehova. (Aef. 6:4) Pofuna kuthandiza makolo, gulu la Yehova latulutsa zinthu zambiri monga nkhani, mavidiyo komanso nyimbo. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zinthu zimenezi pophunzitsa ana anu?

  • Pezani zinthu zimene zingathandize. Pa JW. ORG, mungapeze zinthu zonse zimene zafalitsidwa zomwe zingathandize ana, monga mavidiyo komanso zoti ana achite pophunzira. a Kuti mupeze zinthu zimenezi, lembani mawu akuti “Ana” kapena “Achinyamata” pamalo ofufuzira.

  • Sankhani zogwirizana ndi ana anu. Pa zinthu zomwe zaikidwa pansi pa kamutu kakuti “Ana,” mungasankhe zimene zingathandize mwana wanu. Kuti mupeze zinthu zimenezi, fufuzani pamalo akuti, “Zochita pa Kulambira kwa Pabanja.”

  • Muzipeza nthawi yokambirana ndi ana anu. Musamangowasiya kuti azionera mavidiyo kapena kuchita zinthu zina n’cholinga choti angotanganidwa nazo. M’malomwake muzikambirana zinthuzo ndi ana anu kuti muwathandize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.

a Panopa, pa JW Library pali mavidiyo onse okhudza achinyamata, koma pa mbali yakuti “Zochita” pali zochepa.