Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 37

Tizidalira Yehova Ngati Mmene Samisoni Ankachitira

Tizidalira Yehova Ngati Mmene Samisoni Ankachitira

“Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, chonde, ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu.”—OWER. 16:28.

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1-2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira nkhani ya Samisoni?

 KODI n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva dzina lakuti Samisoni? N’kutheka kuti mumaganizira za munthu wamphamvu kwambiri. Zimenezotu ndi zoona. Komatu pa nthawi ina Samisoni anasankha zinthu molakwika, zomwe zinamubweretsera mavuto aakulu. Komabe Yehova ankaganizira zinthu zambiri zimene Samisoni anachita pomutumikira mokhulupirika ndipo analemba m’Baibulo kuti zizitithandiza.

2 Yehova anagwiritsa ntchito Samisoni pochita zinthu zodabwitsa n’cholinga chofuna kuthandiza Aisiraeli, omwe anali anthu ake. Patapita zaka zambiri Samisoni atamwalira, Yehova anauzira mtumwi Paulo kuti alembe dzina la Samisoni pagulu la anthu omwe anasonyeza chikhulupiriro. (Aheb. 11:​32-34) Chitsanzo cha Samisoni chingatilimbikitse. Iye ankadalira Yehova ngakhale pa nthawi zovuta kwambiri. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Samisoni komanso mmene chitsanzo chake chingatilimbikitsire.

SAMISONI ANKADALIRA YEHOVA

3. Kodi Samisoni anapatsidwa utumiki wotani?

3 Samisoni anabadwa pa nthawi imene Afilisiti ankalamulira komanso kupondereza Aisiraeli. (Ower. 13:1) Ulamuliro wankhanzawu unachititsa kuti Aisiraeli azivutika kwambiri. Yehova anasankha Samisoni kuti ‘adzakhale patsogolo populumutsa Isiraeli m’manja mwa Afilisiti.’ (Ower. 13:5) Imeneyitu inali ntchito yovuta. Kuti athe kugwira ntchitoyi, Samisoni ankafunika kudalira Yehova.

Samisoni ankadalira Yehova ndipo anali wokonzeka kusintha. Iye anagwiritsa ntchito chinthu chimene chinapezeka kuti akwaniritse chifuniro cha Yehova (Onani ndime 4-5)

4. Kodi Yehova anathandiza bwanji Samisoni kuti adzipulumutse kwa Afilisiti? (Oweruza 15:​14-16)

4 Taganizirani chitsanzo chimodzi chosonyeza kuti Samisoni ankadalira Yehova ndiponso mmene Mulungu anamuthandizira. Pa nthawi ina, gulu la asilikali la Afilisiti linabwera kuti lidzagwire Samisoni ku Lehi. N’kutheka kuti kumeneku kunali ku Yuda. Anthu a ku Yuda anachita mantha ndipo anaganiza zopereka Samisoni kwa adaniwo. Choncho anthu a mtundu wake anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano n’kukamupereka kwa Afilisiti. (Ower. 15:​9-13) Koma “mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito” pa Samisoni ndipo iye anadula zingwezo. Kenako “anapeza fupa laliwisi lansagwada za bulu wamphongo” ndipo analitola n’kuligwiritsa ntchito popha Afilisiti okwana 1,000.—Werengani Oweruza 15:​14-16.

5. Kodi kugwiritsa ntchito fupa lansagwada za bulu kunasonyeza bwanji kuti Samisoni ankadalira Yehova?

5 N’chifukwa chiyani Samisoni anagwiritsa ntchito fupa lansagwada za bulu? Chimenechitu sichinali chida chomwe anthu ankagwiritsa ntchito kunkhondo. N’zosachita kufunsa kuti Samisoni ankadziwa kuti angapambane chifukwa chodalira Yehova osati chida chimene akanagwiritsa ntchito. Munthu wokhulupirikayu anagwiritsa ntchito chinthu chomwe chinapezeka kuti akwaniritse cholinga cha Yehova. Chifukwa choti anadalira Yehova, Samisoni anadalitsidwa ndipo anapambana pankhondoyo.

6. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Samisoni tikapatsidwa utumiki winawake?

6 Yehova angathe kutipatsanso mphamvu kuti tikwanitse kugwira ntchito ngakhale zimene zimaoneka kuti n’zovuta. Mulungu akhoza kuchita zimenezi m’njira imene ingatidabwitse. Musamakayikire kuti Yehova amene anapatsa mphamvu Samisoni, angakuthandizeni inuyo kuchita chifuniro chake ngati nanunso mumamudalira.—Miy. 16:3.

7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tiyenera kudalira Yehova kuti azititsogolera?

7 Abale ndi alongo ambiri amene amagwira ntchito zomangamanga m’gulu la Yehova, amasonyezanso kuti amamudalira. M’mbuyomu, abale ankalemba mapulani komanso kumanga Nyumba za Ufumu ndi malo ena. Koma patapita nthawi, panafunika kusintha chifukwa cha kuwonjezereka kwa anthu m’gulu la Yehova. Abale amene amatsogolera m’gulu lathu anapempha Yehova kuti awatsogolere ndipo anayesa njira zatsopano, monga kugula nyumba n’kuzikonza. Robert, yemwe wakhala akugwira ntchito zomangamanga m’mayiko ambiri ananena kuti: “Poyamba sizinali zophweka kwa anthu ena kuti atsatire njira yatsopanoyi. Njirayi inali yosiyana kwambiri ndi zimene takhala tikuchita kwa zaka zambiri. Koma abale ankafunitsitsa kusintha ndipo zikuonekeratu kuti Yehova akudalitsa njira yatsopanoyi.” Ichi ndi chitsanzo chimodzi chokha chosonyeza kuti Yehova akutsogolera anthu ake kuti akwaniritse cholinga chake. Tonsefe tingachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndimalola kuti Yehova azinditsogolera komanso ndimakhala wokonzeka kusintha kuti ndizimutumikira m’njira yoyenera?’

SAMISONI ANKADALIRA YEHOVA KUTI AZIMUTHANDIZA

8. Kodi pa nthawi ina Samisoni anachita chiyani atamva ludzu kwambiri?

8 Mwina mukukumbukira zinthu zina zodabwitsa zimene Samisoni anachita. Iye anapha mkango ndipo kenako anapha Afilisiti 30 mumzinda wa Asikeloni. (Ower. 14:​5, 6, 19) Samisoni ankadziwa kuti sakanatha kuchita zinthu ngati zimenezi popanda kuthandizidwa ndi Yehova. Umboni wa zimenezi unaonekera pa nthawi ina pamene anamva ludzu kwambiri, pambuyo popha Afilisiti 1,000. Kodi iye anatani? M’malo modzidalira kuti apeze madzi akumwa, anapempha Yehova kuti amuthandize.—Ower. 15:18.

9. Kodi Yehova anachita chiyani Samisoni atapempha kuti amuthandize? (Oweruza 15:19 ndi mawu a m’munsi)

9 Yehova anayankha pempho la Samisoni pochititsa kuti nthaka itulutse madzi. Samisoni atamwa madziwo, “anapezanso mphamvu ndi kutsitsimulidwa.” (Werengani Oweruza 15:19 ndi mawu a mmunsi.) N’kutheka kuti madzi ankatulukabe pamalowa kwa zaka zambiri, mpaka pa nthawi imene mneneri Samueli anauziridwa kulemba buku la Oweruza. Aisiraeli amene anaona madziwa ankakumbukira kuti Yehova ndi wodalirika ndipo amathandiza atumiki ake okhulupirika pa nthawi yomwe avutika.

Samisoni anapeza mphamvu atamwa madzi amene Yehova anapereka. Ifenso tingachite bwino kumagwiritsa ntchito zinthu zimene Yehova amatipatsa n’cholinga choti tipitirize kukhala okhulupirika kwa iye (Onani ndime 10)

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atithandize? (Onaninso chithunzi.)

10 Kaya tili ndi luso lotani kapena tachita zambiri potumikira Yehova, ifenso tiyenera kudalira Yehova kuti azitithandiza. Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumavomereza kuti zinthu zikhoza kutiyendera bwino pokhapokha ngati tikudalira Yehova. Mofanana ndi Samisoni yemwe anapeza mphamvu atamwa madzi omwe Yehova anamupatsa, nafenso tikhoza kupeza mphamvu mwauzimu tikamadalira zinthu zonse zomwe Yehova amatipatsa.—Mat. 11:28.

11. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito zinthu zimene Yehova amatipatsa kuti zitithandize? Perekani chitsanzo.

11 Taganizirani chitsanzo cha m’bale wathu wa ku Russia dzina lake Aleksey, yemwe akuzunzidwa kwambiri. Kodi n’chiyani chamuthandiza kukhalabe wolimba pa mavuto aakulu omwe akukumana nawo? Nthawi zonse iye ndi mkazi wake amachita zinthu zokhudza kulambira. Aleksey anati: “Ndimayesetsa kuti ndiziphunzira pandekha komanso kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. M’mawa uliwonse ine ndi mkazi wanga timakambirana lemba la tsiku komanso kupemphera kwa Yehova limodzi.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? M’malo modalira nzeru zathu tiyenera kumadalira Yehova. Tingachite zimenezi polimbitsa chikhulupiriro chathu tikamachita zinthu monga kuphunzira Baibulo, kupemphera, kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Tikatero, Yehova adzatidalitsa chifukwa cha khama lomwe timasonyeza pomutumikira. Mulungu anapatsa mphamvu Samisoni, ndipo mosakayikira nafenso angatipatse mphamvu.

SAMISONI SANAFOOKE

12. Kodi Samisoni analakwitsa chiyani, nanga zimenezi zikusiyana bwanji ndi zimene anachita m’mbuyo?

12 Mofanana ndi ifeyo, nayenso Samisoni sanali wangwiro, choncho nthawi zina ankasankha zinthu molakwika. Pa nthawi ina, iye anasankha zinthu zomwe zinayambitsa mavuto aakulu. Atatumikira kwa kanthawi monga woweruza, Samisoni “anayamba kukonda mkazi wina kuchigwa cha Soreki, ndipo dzina lake anali Delila.” (Ower. 16:4) M’mbuyomo iye ankafuna kukwatira mkazi wina wa Chifilisiti, koma Yehova ‘ndi amene anachititsa zimenezi,’ chifukwa “anali kufunafuna mpata woti amenyane ndi Afilisiti.” Kenako Samisoni anapita kukakhala kunyumba ya hule lina mumzinda wa Afilisiti wa Gaza. Pa nthawiyo, Yehova anapatsa mphamvu Samisoni kuti anyamule zitseko za geti la mzindawo, zomwe zinachititsa kuti ukhale wosavuta kuugonjetsa. (Ower. 14:​1-4; 16:​1-3) Koma nkhani ya Delila inali yosiyana chifukwa choti iye ayenera kuti anali Mwisiraeli, ndipo Yehova si amene anachititsa kuti ubwenzi wawo ukhalepo.

13. Kodi Delila anatani kuti Samisoni akumane ndi mavuto?

13 Delila analandira ndalama zambiri kuchokera kwa Afilisiti kuti apereke Samisoni. Kodi iye ankamukhulupirira kwambiri Delila chifukwa choti ankamukonda, moti iye sankadziwa zomwe ankafuna kuchita? Kaya zinthu zinali bwanji, mobwerezabwereza Delila anakakamiza Samisoni kuti amuululire kumene kunkachokera mphamvu zake, ndipo pamapeto pake Samisoni anamuuza. N’zomvetsa chisoni kuti zimene Samisoni anachita zinapangitsa kuti mphamvu zake zithe komanso Yehova asiye kumukonda kwa kanthawi.—Ower. 16:​16-20.

14. Kodi Samisoni anakumana ndi mavuto otani chifukwa chokhulupirira Delila?

14 Samisoni anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa chokhulupirira Delila m’malo modalira Yehova. Afilisiti anamugwira ndipo anamuboola maso. Iye anaikidwa m’ndende ku Gaza komwe anthu ake anawachititsa manyazi m’mbuyomo ndipo anakhala kapolo wopera tirigu. Kenako Afilisiti anamuchititsa manyazi pamene anasonkhana kuti achite phwando. Iwo anapereka nsembe kwa mulungu wawo Dagoni, ngati kuti iye ndi amene anapereka Samisoni m’manja mwawo. Afilisitiwo anatulutsa Samisoni m’ndende n’kubwera naye paphwandolo kuti “adzawasangalatse.”—Ower. 16:​21-25.

Yehova anapatsa Samisoni mphamvu kuti agonjetse Afilisiti (Onani ndime 15)

15. Kodi Samisoni anasonyeza bwanji kuti anayambiranso kudalira Yehova? (Oweruza 16:​28-30) (Onani chithunzi chapachikuto.)

15 Samisoni anali atalakwitsa zinthu kwambiri komabe sanasiye kutumikira Yehova. Iye anafunafuna mpata woti akwaniritse utumiki umene Mulungu anamupatsa, wogonjetsa Afilisiti. (Werengani Oweruza 16:​28-30.) Samisoni anapempha Yehova kuti: “Ndiloleni ndiwabwezere Afilisiti.” Mulungu woona anamuyankha ndipo anamupatsanso mphamvu zodabwitsa. Choncho pa nthawiyi, Samisoni anapha Afilisiti ambiri kuposa maulendo ena m’mbuyomo.

16. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Samisoni analakwitsa?

16 Ngakhale kuti Samisoni anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cholakwitsa zinthu, iye sanasiye kuchita chifuniro cha Yehova. Choncho kaya talakwitsa zinthu ndipo tikufunika kudzudzulidwa, kusiyitsidwa udindo kapena utumiki winawake, sitiyenera kufooka. Tizikumbukira kuti Yehova amakhala wokonzeka kutikhululukira. (Sal. 103:​8-10) Ngakhale kuti timalakwitsa zinthu, Yehova angatigwiritsebe ntchito ngati mmene anachitira ndi Samisoni.

N’kutheka kuti Samisoni sanasangalale chifukwa cha zimene analakwitsa, komabe sanataye mtima. Ifenso sitiyenera kutaya mtima (Onani ndime 17-18)

17-18. Kodi chitsanzo cha Michael chakulimbikitsani bwanji? (Onaninso chithunzi.)

17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira m’bale wina wachinyamata dzina lake Michael. Iye ankatumikira Yehova mwakhama ndipo anali mtumiki wothandiza komanso mpainiya wokhazikika. N’zomvetsa chisoni kuti iye analakwitsa zinthu, zomwe zinachititsa kuti asiyitsidwe utumiki wake. Michael anati: “M’mbuyo monsemu zinthu zinkandiyendera bwino potumikira Yehova. Koma mwadzidzidzi zinangokhala ngati ndaomba khoma. Sindinkaganiza kuti Yehova angandisiye, komabe ndinkakayikira ngati ndingadzakhalenso naye pa ubwenzi wabwino ngati poyamba kapenanso kumachita zambiri pomutumikira mumpingo.”

18 N’zosangalatsa kuti Michael sanataye mtima. Iye anati: “Ndinayesetsa kuti ndikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova popemphera kwa iye mochokera pansi pa mtima, kuphunzira Mawu ake komanso kuwaganizira mozama.” Patapita nthawi, iye anayambiranso kutumikira mumpingo ngati poyamba. Panopa iye ndi mkulu komanso mpainiya wokhazikika. Michael ananenanso kuti: “Zimene mpingo unachita makamaka akulu pondilimbikitsa, zinandithandiza kuzindikira kuti Yehova amandikondabe. Panopa ndikutumikiranso mumpingo ndili ndi chikumbumtima choyera. Zomwe zinandichitikirazi zinandiphunzitsa kuti Yehova amakhululukira aliyense yemwe walapa kuchokera pansi pa mtima.” Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa komanso kutigwiritsa ntchito ngakhale kuti tinalakwitsapo zinazake. Chongofunika ndi kuchita zonse zomwe tingathe kuti tikonze zomwe tinalakwitsazo, n’kupitiriza kumudalira.—Sal. 86:5; Miy. 28:13.

19. Kodi chitsanzo cha Samisoni chakulimbikitsani bwanji?

19 Munkhaniyi, taona zinthu zochititsa chidwi zomwe zinachitika pa moyo wa Samisoni. Iye sanali wangwiro, komabe sanasiye kuchita zonse zomwe akanatha potumikira Yehova ngakhale kuti analakwitsa zinthu pa nkhani yokhudza Delila. Yehova sanasiye kumugwiritsa ntchito. Anamugwiritsanso ntchito pochita zinthu zina zamphamvu. Yehova ankamuonabe monga munthu wokhulupirika ndipo analola kuti dzina lake lilembedwe pagulu la anthu okhulupirika otchulidwa mu Aheberi chaputala 11. N’zosangalatsa kudziwa kuti timatumikira Atate wathu wachikondi, yemwe amafunitsitsa kutipatsa mphamvu makamaka tikafooka. Choncho mofanana ndi Samisoni, tiyeni tizipempha Yehova kuti: “Chonde ndikumbukireni ndi kundipatsa mphamvu.”—Ower. 16:28.

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu Komanso Timakudalirani

a Samisoni ndi wodziwika kwambiri, ngakhale kwa anthu amene sadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Nkhani yake imapezeka m’masewero, nyimbo komanso mafilimu. Komabe nkhani yokhudza moyo wake si nthano chabe. Tingathe kuphunzira zambiri kwa munthu wachikhulupiriro ameneyu.