Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 39

NYIMBO NA. 125 “Odala Ndi Anthu Achifundo”

Kupatsa Kumatichititsa Kukhala Osangalala

Kupatsa Kumatichititsa Kukhala Osangalala

“Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”MAC. 20:35.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tikambirana zimene tingachite kuti tizikhala osangalala kwambiri chifukwa cha kupatsa.

1-2. Kodi kulengedwa m’njira yoti tizisangalala chifukwa chopatsa kumatithandiza bwanji?

 YEHOVA anatilenga m’njira yoti tizisangalala kwambiri tikakhala opatsa. (Mac. 20:35) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitimasangalala tikalandira? Ayi. Tonse tikudziwa mmene timasangalalira tikalandira mphatso. Komabe, timasangalala kwambiri tikapatsa ena zinthu. Ndipo Yehova anatilenga m’njira imeneyi kuti zizitithandiza. N’chifukwa chiyani tikutero?

2 Njira imene Yehova anatilengera imatithandiza kuti tizitha kuwonjezera chimwemwe chathu. Tingawonjezere chimwemwe chathu tikamafunafuna mipata yoti tipereke zinthu kwa ena. Kunena zoona, njira imene Yehova anatilengerayi ndi yabwino kwambiri.—Sal. 139:14.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe”?

3 Malemba amatitsimikizira kuti kupatsa kumatithandiza kukhala osangalala, choncho n’zosadabwitsa kuti amafotokozanso kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Iye ndi wopatsa wamkulu komanso amene anayambitsa kupatsa. Mtumwi Paulo ananena kuti chifukwa cha iye, “tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:28) Ndipotu “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro” zimachokera kwa Yehova.—Yak. 1:17.

4. N’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala kwambiri?

4 Tonsefe timafuna kukhala osangalala kwambiri chifukwa cha kupatsa. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa. (Aef. 5:1) Tikambirananso zimene tingachite ngati ena sakuyamikira zimene tawapatsa. Zimenezi zitithandiza kuti tipitirize kukhala osangalala komanso kuwonjezera chimwemwe chathu chifukwa chopatsa.

TIZITSANZIRA YEHOVA PA NKHANI YOPATSA

5. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Yehova amatipatsa?

5 Kodi Yehova wasonyeza m’njira ziti kuti ndi wopatsa? Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo. Yehova amatipatsa zinthu zofunika pa moyo. N’zoona kuti sitingakhale ndi zinthu zonse zimene timalakalaka. Koma Yehova amatipatsa zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Mwachitsanzo, amatipatsa chakudya, zovala komanso pogona. (Sal. 4:8; Mat. 6:​31-33; 1 Tim. 6:​6-8) Kodi Yehova amangotipatsa zinthuzi chifukwa chakuti ndi udindo wake? Ayi. Ndiye n’chifukwa chiyani amatipatsa zinthu zimenezi?

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa Mateyu 6:​25, 26?

6 Mwachidule tingati Yehova amatipatsa zinthu zofunika pa moyo chifukwa chakuti amatikonda. Taganizirani mawu amene Yesu ananena pa Mateyu 6:​25, 26. (Werengani.) Yesu anaphunzitsa pogwiritsa ntchito zinthu zam’chilengedwe. Ponena za mbalame, Yesu anati: “Pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola kapenanso kusunga chakudya mʼnyumba zosungiramo zinthu.” Kenako iye ananena kuti: “Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa.” Ndiyeno anafunsa kuti: “Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?” Apa mfundo ndi yakuti Yehova amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali kuposa zinyama. Ndiye ngati Yehova amasamalira zinyama, sitiyenera kukayikira kuti adzatithandizanso kupeza zinthu zofunika. Iye ali ngati bambo wachikondi amene amayesetsa kupeza zofunika m’banja lake chifukwa cha chikondi.—Sal. 145:16; Mat. 6:32.

7. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yopatsa? (Onaninso chithunzi.)

7 Mofanana ndi Yehova, ifenso tingapatse ena zinthu chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, kodi mukudziwa Mkhristu wina yemwe akufunika chakudya kapena zovala? Yehova angagwiritse ntchito inuyo kuti mumuthandize kupeza zimene akufunikira. Anthu a Yehova amadziwika kuti amathandizana pakagwa mavuto. Mwachitsanzo, pa nthawi ya mliri wa COVID-19, abale ndi alongo ankapereka chakudya, zovala komanso zinthu zina kwa anthu amene akuvutika. Ndipo ambiri ankapereka ndalama zothandiza pa ntchito ya padziko lonse. Izi zinathandiza kuti gulu lizipereka chithandizo padziko lonse. Abale ndi alongo anachita mogwirizana ndi lemba la Aheberi 13:​16, lomwe limati: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo, chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.”

Tonsefe tikhoza kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa (Onani ndime 7)


8. Kodi mphamvu za Yehova zimatithandiza bwanji? (Afilipi 2:13)

8 Yehova amapereka mphamvu. Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, ndipo amasangalala kupereka mphamvu zake kwa atumiki ake. (Werengani Afilipi 2:13.) Kodi munayamba mwapempherapo kuti Yehova akupatseni mphamvu n’cholinga choti mukane mayesero kapenanso kuti mupirire vuto lalikulu? Mwinanso munamupemphapo kuti akupatseni mphamvu zoti muthe kuchita zofunika patsikulo. Ngati iye anakupatsani mphamvu mutamupempha, mukhoza kuvomereza zimene mtumwi Paulo analemba. Iye anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.”—Afil. 4:13.

9. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pothandiza ena ndi mphamvu zathu? (Onaninso chithunzi.)

9 Ngakhale kuti si ife angwiro, tingatsanzire Yehova pothandiza ena ndi mphamvu zathu. N’zoona kuti sitingathe kupatsa munthu mphamvu koma tikhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zathu kuti tiwathandize. Mwachitsanzo, ngati pali Mkhristu amene ndi wachikulire kapena amene akudwala, tingamuthandize ntchito zapakhomo kapena kukamugulira zinthu. Ngati tingakwanitse tikhoza kugwira nawo ntchito yoyeretsa kapena kukonza Nyumba ya Ufumu. Tikamagwiritsa ntchito mphamvu zathu m’njira zimenezi, timathandiza ena omwe amalambira Yehova.

Tikhoza kugwiritsa ntchito mphamvu zathu pothandiza ena (Onani ndime 9)


10. Kodi tingalimbikitse bwanji ena ndi mawu athu?

10 Muzikumbukira kuti mawu ndi amphamvu. Kodi pali winawake amene mukudziwa kuti angamve bwino mutamuyamikira kuchokera pansi pa mtima? Kodi mukudziwa munthu wina amene akufunika kulimbikitsidwa? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kulankhula ndi munthuyo. Mungachite zimenezo popita kukalankhula naye, kumuimbira foni, kumulembera khadi, imelo kapena kumutumizira meseji. Sikuti mufunika kulankhula mwaluso kwambiri. Mawu ochepa koma ochokera pansi pa mtima akhoza kuthandiza Mkhristu mnzanuyo kuti akhalebe wokhulupirika kapena kuti ayambe kumva bwino pa mavuto amene akukumana nawo.—Miy. 12:25; Aef. 4:29.

11. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji nzeru zake?

11 Yehova amapereka nzeru. Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu ndipo adzamupatsa, chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka popanda kupezera aliyense zifukwa.” (Yak. 1:5) Lembali likusonyeza kuti Yehova saumira nzeru zake. Iye amazipereka kwa anthu mowolowa manja. Ndipo lanenanso kuti Yehova akamapereka nzeru amachita zimenezo “mosatonza” kapena kuti “popanda kupezera aliyense zifukwa.” Iye satichititsa kuti tizidziona ngati osafunika chifukwa chakuti tamupempha kuti atitsogolere. Ndipotu amatilimbikitsa kuti tizimupempha nzeru.—Miy. 2:​1-6.

12. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe tingapatse ena nzeru?

12 Kodi ifenso tingatsanzire Yehova pa nkhani yopatsa ena nzeru? (Sal. 32:8) Anthu a Yehova amakhala ndi mwayi wambiri wophunzitsa ena zimene akudziwa. Mwachitsanzo, timaphunzitsa atsopano mmene angalalikirire. Akulu amathandiza moleza mtima atumiki othandiza komanso abale obatizidwa kuti azisamalira bwino maudindo awo mumpingo. Komanso ena amene ali ndi luso la zomanga amaphunzitsa anzawo kuti azigwira nawo ntchito zomangamanga za gulu lathu.

13. Pophunzitsa ena, kodi tingatsanzire bwanji mmene Yehova amaperekera nzeru?

13 Anthu amene akuphunzitsa anzawo ayenera kutsanzira mmene Yehova amaperekera nzeru. Kumbukirani kuti Yehova amapereka nzeru mowolowa manja. Ifenso timaphunzitsa ena ndi mtima wonse zimene tikudziwa. Tisamaope kuphunzitsa ena zinthu poopa kuti adzatilanda malo. Si bwinonso kuganiza kuti, ‘Ndinaphunzira ndekha, nayenso aphunzire yekha.’ Mtima umenewo ndi wosafunika pakati pa anthu a Mulungu. M’malomwake, timachita zonse zomwe tingathe kuti tiwaphunzitse chilichonse chomwe tikudziwa, ngati kuti ‘tikuwapatsa miyoyo yathu yeniyeniyo.’ (1 Ates. 2:8) Timayembekezera kuti “nawonso adzakhala oyenerera kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:​1, 2) Tikatero timathandiza ena kuti akhale owolowa manja komanso osangalala.

NGATI ENA SAYAMIKIRA TIKAWAPATSA ZINTHU

14. Kodi anthu ambiri amatani tikawapatsa zinthu?

14 Tikapereka zinthu makamaka kwa abale ndi alongo, nthawi zambiri amayamikira. Angatilembere kakhadi kapenanso kutithokoza m’njira ina. (Akol. 3:15) Munthu akathokoza chonchi zimatisangalatsa kwambiri.

15. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati anthu ena sanatiyamikire?

15 Zoona n’zakuti si nthawi zonse pomwe anthu amayamikira zimene tachita. Nthawi zina tingapereke nthawi, mphamvu ndi zinthu zathu koma pambuyo pake n’kudabwa kuti munthu sakuyamikira zimene tamuchitira. Ngati izi zitatichitikira, kodi tingatani kuti tisakwiye n’kupitirizabe kukhala osangalala? Tizikumbukira mawu a mulemba limene pachokera nkhaniyi, la Machitidwe 20:35. Sikuti timasangalala chifukwa cha zimene munthu amachita tikamupatsa zinthu. Tikhoza kumasangalalabe ngakhale zitaoneka kuti munthuyo sakuyamikira. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize? Tiyeni tione zinthu zingapo.

16. Kodi tiziganizira chiyani tikamapatsa anthu zinthu?

16 Maganizo athu azikhala pa kutsanzira Yehova. Iye amapereka zinthu zabwino kwa anthu kaya iwo ayamikira kapena ayi. (Mat. 5:​43-48) Yehova amalonjeza kuti tikamapereka zinthu “osayembekezera kulandira kalikonse” ndiye kuti ‘mphoto yathu idzakhala yaikulu.’ (Luka 6:35) Mawu akuti “kalikonse” akhoza kutanthauzanso zimene ena angachite posonyeza kuyamikira. Kaya atiyamikira kapena ayi, nthawi zonse Yehova adzatibwezera chifukwa cha zabwino zimene timachitira ena komanso chifukwa ‘chopereka mosangalala.’—Miy. 19:17; 2 Akor. 9:7.

17. N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera? (Luka 14:​12-14)

17 Mfundo ya pa Luka 14:​12-14, ikhoza kutithandiza kukhala ndi maganizo oyenera popereka zinthu. (Werengani.) Si kulakwa kupereka zinthu kwa anthu amene akhoza kudzatipatsanso zinthu m’tsogolo. Koma bwanji ngati tazindikira kuti nthawi zina timapereka zinthu pofuna kuti tidzapezepo kenakake m’tsogolo? Tingachite bwino kuyesa kuchita zimene Yesu ananena. Tingayese kupereka zinthu kwa munthu amene tikudziwa kuti sangatipatse kenakake. Tikatero tidzasangalala chifukwa tidzakhala tikutsanzira Yehova. Maganizo amenewa angatithandize kuti tikhalebe osangalala ngakhale pamene ena sakutiyamikira.

18. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

18 Tizipewa kukayikira zolinga za ena. (1 Akor. 13:7) Ngati wina sanasonyeze kuyamikira zimene tamuchitira, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi wosayamikadi, kapena wangoiwala kuyamikira?’ N’kutheka kuti pali zimene zachititsa kuti asayamikire m’njira imene timaganizira. Ena amakhala akuyamikira mumtima koma amalephera kusonyeza kuyamikirako. Ena angamachite manyazi akathandizidwa makamaka ngati m’mbuyomo iwowo ndi amene ankathandiza ena. Kaya zinthu zili bwanji, chikondi ndi chimene chingatithandize kuti tisamakayikire zolinga za Akhristu anzathu n’kupitirizabe kukhala osangalala.—Aef. 4:2.

19-20. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji tikamapereka zinthu kwa ena? (Onaninso chithunzi.)

19 Tizikhala oleza mtima. Pa nkhani ya kuwolowa manja, Mfumu Solomo inalemba kuti: “Ponya mkate wako pamadzi chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.” (Mlal. 11:1) Lembali likusonyeza kuti anthu ena akhoza kuyamikira zimene tawachitira patapita nthawi yaitali, kapena kuti “masiku ambiri.” Tiyeni tikambirane chitsanzo pa nkhaniyi.

20 Zaka zambiri m’mbuyomo, mkazi wa woyang’anira dera wina anatumiza kakhadi kwa mlongo wina yemwe anali atangobatizidwa kumene pomulimbikitsa kuti akhalebe wokhulupirika. Patapita zaka 8, mlongoyo anamulembera kalata yonena kuti: “Ndaganiza kuti ndikulembereni kuti ndikuuzeni kuti mwakhala mukundithandiza kwa zaka zambiri, ngakhale kuti inuyo simukudziwa.” Anapitiriza kuti: “Uthenga wanu unali wolimbikitsa, koma lemba lomwe munaikamo ndi limene linandifika pamtima moti sindimaiwala.” a Atafotokoza mavuto amene anakumana nawo, mlongoyo ananena kuti: “Nthawi zina ndinkangofuna nditasiya chili chonse kuphatikizapo choonadi, koma lemba limene munaikamo linkandilimbikitsa moti . . . sindinabwerere m’mbuyo.” Anawonjezeranso kuti: “Pa zaka 8 zonsezi, palibenso china chimene chandilimbikitsa kwambiri kuposa lembali.” Mkazi wa woyang’anira derayo ayenera kuti anasangalala kwambiri kulandira kalatayi ngakhale kuti panali ‘patapita masiku ambiri.’ Ifenso tikhoza kudzayamikiridwa patapita nthawi yaitali kuchokera pamene tapatsa munthu wina zinthu.

Anthu ena akhoza kuyamikira zimene tawachitira patapita nthawi yaitali (Onani ndime 20) b


21. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kupitiriza kutsanzira Yehova pa nkhani yopatsa?

21 Mu nkhaniyi, taona kuti Yehova anatilenga m’njira yapadera. Ngakhale kuti timasangalala tikalandira, timasangalala kwambiri tikapatsa anthu ena zinthu. Timamva bwino tikathandiza Akhristu anzathu ndipo timasangalala akayamikira. Koma kaya munthu atiyamikira kapena ayi, ifeyo timasangalala chifukwa tachita zinthu zoyenera. Musamaiwale kuti mukapereka zinthu “Yehova akhoza kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.” (2 Mbiri 25:9) Sitingapereke zinthu kuposa zimene Yehova angatipatse. Ndipo palibe chinthu chosangalatsa ngati kubwezeredwa ndi Yehova. Choncho tiyeni tipitirize kutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wopatsa.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

a Lemba limene linkalimbikitsa mlongoyo ndi la 2 Yohane 8, lomwe limati: “Samalani kuti musataye zinthu zimene tinakuthandizani kuti muzipeze nʼcholinga choti mudzalandire madalitso onse amene Mulungu wakukonzerani.”

b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pa chithunzi choyerekezerachi, mkazi wa woyang’anira dera akulemba khadi kuti alimbikitse mlongo. Patapita zaka, akulandira kalata yoyamikira.